Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 136:11 - Buku Lopatulika

11 Natulutsa Israele pakati pao; pakuti chifundo chake nchosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Natulutsa Israele pakati pao; pakuti chifundo chake nchosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ndipo adatulutsa Aisraele pakati pao, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Natulutsa Israeli pakati pawo, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 136:11
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anawatulutsa pamodzi ndi siliva ndi golide: ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa.


Koma anatulutsa anthu ake ngati nkhosa, nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'chipululu.


Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anatuluka m'dziko la Ejipito.


Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, chifukwa cha kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israele ku mibadwo yao.


Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.


Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;


Ndipo chizikhala ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chapamphumi pakati pamaso ako; pakuti Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.


Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chikumbutso pakati pamaso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa