Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 136:12 - Buku Lopatulika

12 Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka; pakuti chifundo chake nchosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka; pakuti chifundo chake nchosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambalitsa, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 136:12
10 Mawu Ofanana  

Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,


Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.


Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu, dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.


Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;


ndipo munatulutsa anthu anu Israele m'dziko la Ejipito ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;


Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro mu Ejipito, ndi mu Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai.


Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa