Mulungu sanatilembere malangizo enieni a chilengedwe chake, koma adakhazikitsa malamulo achilengedwe kuti alamulire mphamvu za chilengedwe, zomwe zimagwirira ntchito nthawi zonse mogwirizana ndi chifuniro chake champhamvu. Chilengedwecho chimandiwonetsa kuti Mulungu aliko, monga momwe Salmo 19:1 imanenera: "Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo limasonyeza ntchito ya manja ake".
Monga wokhulupirira, ndikofunikira kumvetsa kuti zinthu zosaoneka za Mulungu, monga mphamvu zake ndi ulemerero wake, zimawululidwa kudzera mu chilengedwe chake. Mulungu amasangalala pamene ine ndimadabwa ndi ntchito zake, chifukwa chilichonse chotizinga chidalengedwa kuti ndizindikire kuchuluka kwa chikondi chake kwa ine komanso kuti ndidziwe kukongola kwake, zomwe zimandilola kumulambira ndi mtima wanga wonse.
Ndiyenera kuyamikira chilengedwe, kuganizira za Mulungu ndi kumuthokoza, chifukwa chifundo chake chimawonekera m'moyo wanga nthawi iliyonse dzuwa likamatuluka.
Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili m'menemo;
Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu; munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.
Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira. Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo. Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,
Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi; nyanja ibume mwa kudzala kwake. Munda ukondwerere ndi zonse zili m'mwemo; pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera.
Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.
Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.
Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.
Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa. Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo
Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake. Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo, m'kuzisunga izo muli mphotho yaikulu. Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika. Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu. Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga. Usana ndi usana uchulukitsa mau, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru. Palibe chilankhulidwe, palibe mau; liu lao silimveka. Muyeso wao wapitirira padziko lonse lapansi, ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu. Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,
Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;
Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.
Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu. Nyanja siyo, yaikulu ndi yachitando, m'mwemo muli zokwawa zosawerengeka; zamoyo zazing'ono ndi zazikulu.
ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake.
Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?
Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Edeni kuti aulime nauyang'anire.
Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao. M'malo mwa mithethe mudzatuluka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamchisu; ndipo chidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati chizindikiro chosatha, chimene sichidzalikhidwa.
Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu.
Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi? Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi? Ndipo muderanji nkhawa ndi chovala? Tapenyetsani maluwa akuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito, kapena sapota: koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake wonse sanavale monga limodzi la amenewa.
Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo. Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wa makamumakamu, ndiye Mfumu ya ulemerero. Pakuti Iye analimanga pazinyanja, nalikhazika pamadzi.
Iye ndiye wakukonda chilungamo ndi chiweruzo, dziko lapansi ladzala ndi chifundo cha Yehova.
Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo ndi zake za Yehova Mulungu wanu.
Kodi chikucheperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? Muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? Muyenera kumwa madzi odikha, ndi kuvundulira otsalawo ndi mapazi anu?
Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu.
Ndipo asaligulitse dziko chigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine. Potero muzilola liomboledwe dziko lonse muli nalo.
Atumiza akasupe alowe m'makwawa; ayenda pakati pa mapiri: Zimamwamo nyama zonse zakuthengo; mbidzi zipherako ludzu lao. Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo, zimaimba pakati pa mitawi. Iye amwetsa mapiri mochokera m'zipinda zake: Dziko lakhuta zipatso za ntchito zanu. Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka;
Tamverani ichi, Yobu. Taimani, mulingirire zodabwitsa za Mulungu. Kodi mudziwa umo Mulungu azilangizira zimenezi, nawalitsa mphezi ya m'mtambo mwake? Kodi mudziwa madendekeredwe ake a mitambo, zodabwitsa za Iye wakudziwa mwangwiro?
Amene aphimba thambo ndi mitambo, amene akonzera mvula nthaka, amene aphukitsa msipu pamapiri. Amene apatsa zoweta chakudya chao, ana a khwangwala alikulira.
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang'ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera. Ndipo ng'ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao aang'ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng'ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m'funkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m'phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.
Amene anayala dziko lapansi pamwamba pamadzi; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene analenga miuni yaikulu; pakuti chifundo chake nchosatha. Dzuwa liweruze usana; pakuti chifundo chake nchosatha. Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku; pakuti chifundo chake nchosatha.
Ndipo anati Mulungu, Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo; ndiika utawaleza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.
Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.
ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?
Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholowa changa chonyansa.
pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye. Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye.
Pakuti zamoyo zonse zakuthengo ndi zanga, ndi ng'ombe za pa mapiri zikwi. Ndidziwa mbalame zonse za m'mapiri, ndipo nyama zakuthengo zili ndi Ine.
Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako; koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.
Malo ozama a dziko lapansi ali m'dzanja lake; chuma cha m'mapiri chomwe ndi chake. Nyanja ndi yake, anailenga; ndipo manja ake anaumba dziko louma.
Dziko lirira nilifota, dziko lilefuka nilifota, anthu omveka a padziko alefuka. Dzikonso laipitsidwa ndi okhalamo ake omwe, chifukwa iwo alakwa pamalamulo nasinthanitsa malemba, nathyola chipangano cha nthawi zonse.
ndilo dziko loti Yehova Mulungu wanu alisamalira, maso a Yehova Mulungu wanu akhalapo chikhalire, kuyambira chaka mpaka kutsiriza chaka.
Mapiri aatali ndiwo ayenera zinkhoma; pamatanthwe mpothawirapo mbira. Anaika mwezi nyengo zake; dzuwa lidziwa polowera pake. muvala ulemu ndi chifumu. Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala; ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga. Muika mdima ndipo pali usiku; pamenepo zituluka zilombo zonse za m'thengo. Misona ya mkango ibangula potsata nyama yao, nifuna chakudya chao kwa Mulungu. Potuluka dzuwa, zithawa, zigona pansi m'ngaka mwao. Pamenepo munthu atulukira kuntchito yake, nagwiritsa kufikira madzulo. Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.
Udziwitsitse zoweta zako zili bwanji, samalira magulu ako; pakuti chuma sichili chosatha; kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo. Amatuta udzu, msipu uoneka, atchera masamba a kumapiri. Anaankhosa akuveka, atonde aombolera munda; mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya; ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.
Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.
Aleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m'misanje. Nyama zakuthengo ndi zoweta zonse; zokwawa, ndi mbalame zakuuluka. Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu; zinduna ndi oweruza onse a padziko. Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo. Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya. Mlemekezeni, angelo ake onse; mlemekezeni, makamu ake onse. Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira. Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo. Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala kunthawi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ake okondwa.
Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, Iyeyo ndiye Ambuye, mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja; satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;
Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake.
Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu: Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa. Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.
ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?
Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikire Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.