Nehemiya 9:6 - Buku Lopatulika6 Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Pamenepo Ezara adapemphera kuti, “Inu nokha ndiye Chauta. Inu mudalenga kumwamba, kumwambamwamba, ndiponso zonse zokhala komweko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Mudalenga nyanja ndi zonse zam'menemo. Zonse zakumwamba zimakupembedzani. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani. Onani mutuwo |