Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:7 - Buku Lopatulika

7 Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumtulutsa mu Uri wa kwa Akaldeya, ndi kumutcha dzina lake Abrahamu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumtulutsa m'Uri wa Ababiloni, ndi kumutcha dzina lake Abrahamu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Inu ndinu Chauta, Mulungu amene mudasankha Abramu, kumtulutsa ku Uri wa ku Kaldeya, ndi kumutcha dzina loti Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumutulutsa mʼdziko la Uri wa ku Kaldeya ndi kumutcha dzina lake Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:7
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko.


Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe mu Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako.


Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.


Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.


Abramu, (ndiye Abrahamu).


Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumchulukitsa.


Koma Yehova anakondwera nao makolo anu kuwakonda, nasankha mbeu zao zakuwatsata, ndiwo inu, mwa mitundu yonse ya anthu, monga kuli lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa