Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 89:11 - Buku Lopatulika

11 Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu; munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu; munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Zakumwamba ndi zanu, dziko lapansi nalonso ndi lanu. Mudapanga dziko lonse ndi zonse zam'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Mayiko akumwamba ndi anu ndiponso dziko lapansi ndi lanu; munapanga dziko lonse ndi zonse zili mʼmenemo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 89:11
11 Mawu Ofanana  

Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse.


Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.


Kodi unazindikira chitando cha dziko lapansi? Fotokozera, ngati uchidziwa chonse.


Ndaniyo anayamba kundipatsa Ine kuti ndimthokoze? Zilizonse pansi pa thambo ponse ndi zanga.


Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.


Ndikamva njala, sindidzakuuza, pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwake komwe.


Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?


pakuti dziko lapansi lili la Ambuye, ndi kudzala kwake.


Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbumtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa