Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 1:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri. Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 1:31
21 Mawu Ofanana  

Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachitatu.


Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachinai.


Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu.


Ndipo Mulungu anatcha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.


Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.


Tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse.


Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri, naliyeretsa limenelo: chifukwa limenelo adapuma ku ntchito yake yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.


muja nyenyezi za m'mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?


Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.


Chimene muzipatsa zigwira; mufumbatula dzanja lanu, zikhuta zabwino.


Ulemerero wa Yehova ukhale kosatha; Yehova akondwere mu ntchito zake;


Inu ndinu wabwino, ndi wakuchita zabwino; mundiphunzitse malemba anu.


chifukwa m'masiku asanu ndi limodzi Yehova adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.


ndicho chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi ana a Israele; pakuti Yehova analenga kumwamba ndi dziko lapansi m'masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonanso mphamvu.


Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.


Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.


Kodi m'kamwa mwa Wam'mwambamwamba simutuluka zovuta ndi zabwino?


Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.


Pakuti cholengedwa chonse cha Mulungu nchabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi chiyamiko;


pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa