Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 16:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'chilamulo changa kapena iai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'chilamulo changa kapena iai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Apo Chauta adauza Mose kuti, “Chabwino, ndikupatsani chakudya chimene chidzagwa ngati mvula kuchokera kumwamba. Anthu azituluka tsiku ndi tsiku kukatola chakudya chokwanira tsiku limodzi, kuti ndiŵayese ndipo ndiwone ngati adzayenda motsata malamulo anga kapena ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzakupatsani buledi wogwa kuchokera kumwamba ngati mvula. Anthu azituluka tsiku lililonse kukatola buledi wokwanira tsiku limenelo. Ine ndidzawayesa mʼnjira imeneyi kuti ndione ngati adzatsatira malangizo anga.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 16:4
17 Mawu Ofanana  

Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oimbira chowathandiza, yense chake pa tsiku lake.


ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.


Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamane mana anu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao.


Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri, nawakhutitsa mkate wakumwamba.


Koma analamulira mitambo ili m'mwamba, natsegula m'makomo a kumwamba.


Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa;


Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu.


Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera;


Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.


tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku.


nadya onse chakudya chauzimu chimodzimodzi;


amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;


Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.


Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa