Chakudya ndi nkhani yofunika kwambiri imene imapezeka kangapo m’Baibulo. Uku mu Genesis, mukupezeka nkhani ya zipatso ndi zomera monga chakudya cha munthu.
Mu Chipangano Chakale, mulinso malamulo okhudza zakudya, omwe amatiuza zamitundu ya nyama zomwe tingadye. Ndipo mu Chipangano Chatsopano, pali nkhani zambiri zomwe Yesu anadya limodzi ndi otsatira ake, kusonyeza kufunika kwa ubale wathu ndi Mulungu ndi anzathu pamene tidya limodzi.
Komanso, Baibulo limatiphunzitsa kuti thupi lathu ndi kachisi wa Mzimu Woyera, choncho tiyenera kulisamalira bwino. Ndipo kusamalira thupi lathu kumaphatikizapo kudya bwino.
Zonsezi zimatiphunzitsa kuti chakudya si chongotipatsa mphamvu zokha, koma ndi njira yoti tilimbikitse ubale wathu ndi Mulungu komanso ndi anzathu. Monga mwambi umati, “M’mimba mulibe m’bale”. Koma ife, monga Akhristu, tiyenera kuona chakudya ngati njira yoti tigwirizanitse anthu, monga momwe Yesu anachitira.
Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala. Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala.
Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira.
Mtima wokhuta upondereza chisa cha uchi; koma wakumva njala ayesa zowawa zonse zotsekemera.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'chilamulo changa kapena iai.
Ndamva madandaulo a ana a Israele; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m'mawa padagwa mame pozungulira tsasa. Ndipo atakamuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati chipale panthaka. Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu.
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake. Pamenepo adzavomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pochita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine, Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzichepetsa, ndipo avomereza kulanga kwa mphulupulu zao; pamenepo ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isaki, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukira; ndipo ndidzakumbukira dzikoli. Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ake, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzavomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga. Ndiponso pali ichinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kuthyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wao. Koma chifukwa cha iwo ndidzawakumbukira pangano la makolo ao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova. Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa Iye ndi ana a Israele m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose. Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.
Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m'kamwa mwa Yehova.
ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m'nyengo yake, ya chizimalupsa ndi ya masika, kuti mutute tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu. Ndipo ndidzapatsa msipu wa zoweta zanu podyetsa panu; mudzadyanso nimudzakhuta.
Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.
Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala. Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!
Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.
Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chao m'nyengo zao. Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.
Misona ya mkango isowa nimva njala, koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.
Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha.
Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, mudye. Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadye ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.
Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.
Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo. Koma nyama, m'mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.
Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndalama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo wake. Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira. Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao. M'malo mwa mithethe mudzatuluka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamchisu; ndipo chidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati chizindikiro chosatha, chimene sichidzalikhidwa. Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.
Ndipo anawavumbitsira mana, adye, nawapatsa tirigu wa kumwamba. Yense anadya mkate wa angelo, anawatumizira chakudya chofikira.
Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka; ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.
Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.
Koma chakudya sichitivomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tilibe kupindulako.
Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:
Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.
Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;
Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu: Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero.
Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.
Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.
natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu.
Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala? Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?
Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo. nanena kwa anyamata ake, Uyo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye. Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri.
Ndipo Iye analamulira anthuwo akhale pansi onse; natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu. Ndipo onsewa anadya, nakhuta: ndipo anatola makombo otsala madengu asanu ndi awiri odzala.
Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!
Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.
Koma sanadzisiyire Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.
Iye wakusamalira tsiku, alisamalira kwa Ambuye: ndipo iye wakudya, adya mwa Ambuye, pakuti ayamika Mulungu; ndipo iye wosadya, mwa Ambuye sakudya, nayamikanso Mulungu.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
Pakuti cholengedwa chonse cha Mulungu nchabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi chiyamiko; pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.