Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 9:3 - Buku Lopatulika

3 Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsopano mungathe kudya nyama zonse, monga ndidakulolani kudya ndiwo zamasamba. Ndakupatsani zonsezi kuti zikhale chakudya chanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsopano chamoyo chilichonse chidzakhala chakudya chanu. Monga momwe ndinakupatsirani ndiwo zamasamba, tsopano ndikupatsaninso nyama iliyonse.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 9:3
18 Mawu Ofanana  

Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga, ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pansomba zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.


Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.


Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa.


Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.


Usapasule ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Zinthu zonse zili zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.


Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira.


Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.


Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.


Koma monga mwa chikhumbo chonse cha moyo wanu muiphe ndi kudya nyama m'midzi yanu yonse, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani; odetsa ndi oyera adyeko, monga yamphoyo ndi yangondo.


Chifukwa chake munthu aliyense asakuweruzeni inu m'chakudya, kapena chakumwa, kapena m'kunena tsiku la chikondwerero, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa