Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 9:2 - Buku Lopatulika

2 Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga, ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pansomba zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Zamoyo zonse za pa dziko lapansi pamodzi ndi mbalame zomwe, nyama zokwaŵa ndi zonse zam'nyanja zidzakuwopani. Zonsezi ndaziika kuti muzilamule.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Nyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za mlengalenga, ndi chamoyo chilichonse chokwawa, ndiponso nsomba zonse za ku nyanja; zidzakuopani ndipo ndazipereka kuti muzilamulire.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 9:2
16 Mawu Ofanana  

Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.


Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi.


Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.


Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.


Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera mizinda yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo.


Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.


Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.


Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yake njaikulu? Udzaisiyira ntchito yako kodi?


Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.


Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.


Popeza ndidzatumiza chilombo chakuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu ndipo chidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.


Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.


Pakuti mtundu uliwonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam'nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa