Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 9:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Nyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za mlengalenga, ndi chamoyo chilichonse chokwawa, ndiponso nsomba zonse za ku nyanja; zidzakuopani ndipo ndazipereka kuti muzilamulire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga, ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pansomba zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Zamoyo zonse za pa dziko lapansi pamodzi ndi mbalame zomwe, nyama zokwaŵa ndi zonse zam'nyanja zidzakuwopani. Zonsezi ndaziika kuti muzilamule.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 9:2
16 Mawu Ofanana  

Choncho Mulungu analenga zamoyo zikuluzikulu za mʼnyanja ndi chamoyo chamtundu uliwonse chokhala mʼmadzi ndi mbalame iliyonse ya mapiko monga mwa mtundu wake. Mulungu anaona kuti zinali bwino.


Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”


Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.”


Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake.


Pamenepo ananyamuka, ndipo mtima woopa Mulungu unagwera anthu onse a mʼmizinda yozungulira, kotero kuti palibe aliyense amene anatsatira banja la Yakobo.


Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake aamuna nati kwa iwo, “Berekanani ndipo muchulukane ndi kudzaza dziko lapansi.


Tsopano chamoyo chilichonse chidzakhala chakudya chanu. Monga momwe ndinakupatsirani ndiwo zamasamba, tsopano ndikupatsaninso nyama iliyonse.


Kodi ungadalire njatiyo chifukwa champhamvu zake? Kodi ungayilekere kuti igwire ntchito zako zolemetsa?


“ ‘Ndidzapangana nazo pangano la mtendere. Ndidzachotsa mʼdzikomo zirombo zolusa. Choncho nkhosa zanga zidzakhala mu mtendere mu chipululu ngakhalenso mʼthengo.


Tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga. Ndidzachotsa mʼdzikomo uta, lupanga ndi zida zonse zankhondo, kuti onse apumule mwamtendere.


Ndidzabweretsa zirombo zolusa pakati panu, ndipo zidzakulandani ana anu ndi kuwononga ngʼombe zanu. Choncho zidzachepetsa chiwerengero chanu kotero kuti mʼnjira mwanu simudzapita anthu.


“ ‘Ndidzabweretsa mtendere mʼdziko lanu, ndipo muzidzagona popanda wokuopsezani. Ndidzachotsa nyama zakuthengo zoopsa mʼdziko mwanu, ndipo mʼdzikomo simudzakhala nkhondo.


Mitundu yonse ya nyama, ya mbalame, ya zokwawa ndi ya zolengedwa za mʼnyanja, zikuwetedwa ndipo munthu wakhala akuziweta,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa