Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 132 - Buku Lopatulika


Davide asamalira Kachisi ndi likasa. Lonjezano la Mulungu
Nyimbo yokwerera.

1 Yehova, kumbukirani Davide kuzunzika kwake konse.

2 Kuti analumbira Yehova, nawindira Wamphamvuyo wa Yakobo, ndi kuti,

3 Ngati ndidzalowa pakhomo pa nyumba yanga, ngati ndidzakwera pa kama logonapo;

4 ngati ndidzalola maso anga agone, kapena zikope zanga ziodzere;

5 kufikira nditapezera Yehova malo, chokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?

6 Taonani, tinachimva mu Efurata; tinachipeza kuchidikha cha kunkhalango.

7 Tidzalowa mokhalamo Iye; tidzagwadira kumpando wa mapazi ake.

8 Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu; Inu ndi hema wa mphamvu yanu.

9 Ansembe anu avale chilungamo; ndi okondedwa anu afuule mokondwera.

10 Chifukwa cha Davide mtumiki wanu musabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.

11 Yehova analumbira Davide zoona; sadzalibweza; ndi kuti, Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wachifumu wako.

12 Ana ako akasunga chipangano changa ndi mboni yanga imene ndidzawaphunzitsa, ana aonso adzakhala pa mpando wanu kunthawi zonse,

13 pakuti Yehova anasankha Ziyoni; analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti,

14 Pampumulo panga mpano posatha, Pano ndidzakhala; pakuti ndakhumbapo.

15 Ndidzadalitsatu chakudya chake; aumphawi ake ndidzawakhutitsa ndi mkate.

16 Ndipo ansembe ake ndidzawaveka ndi chipulumutso: Ndi okondedwa ake adzafuulitsa mokondwera.

17 Apo ndidzaphukitsira Davide nyanga; ndakonzeratu wodzozedwa wanga nyali.

18 Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi; koma pa iyeyu korona wake adzamveka.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa