Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 132:9 - Buku Lopatulika

9 Ansembe anu avale chilungamo; ndi okondedwa anu afuule mokondwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ansembe anu avale chilungamo; ndi okondedwa anu afuule mokondwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ansembe anu avale chilungamo ngati nsalu, anthu anu oyera mtima afuule ndi chimwemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ansembe anu avekedwe chilungamo; anthu anu oyera mtima ayimbe nyimbo mwachimwemwe.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 132:9
19 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, avale chipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.


Ndinavala chilungamo, ndipo chinandivala ine; chiweruzo changa chinanga mwinjiro ndi nduwira.


Lemekeza Yehova, moyo wanga; Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkulukulu;


Ndipo ansembe ake ndidzawaveka ndi chipulumutso: Ndi okondedwa ake adzafuulitsa mokondwera.


Okondedwa ake atumphe mokondwera mu ulemu: Afuule mokondwera pamakama pao.


Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu; fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa.


Koma olungama akondwere; atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu; ndipo asekere nacho chikondwerero.


Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; nanene kosalekeza iwo akukonda chipulumutso chanu, abuke Mulungu.


Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


taonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wachisoni; ndipo mudzafuula chifukwa cha kusweka mzimu.


Imba, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula, Israele; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu.


Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.


Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.


Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.


Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbuu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.


Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa