Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 132:6 - Buku Lopatulika

6 Taonani, tinachimva mu Efurata; tinachipeza kuchidikha cha kunkhalango.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Taonani, tinachimva m'Efurata; tinachipeza kuchidikha cha kunkhalango.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tidamva za bokosi lachipangano ku Efurata, tidalipeza m'minda ya ku Yaara.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata, tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 132:6
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anafa Rakele, naikidwa panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).


Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu ku Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko.


Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu ku Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana aamuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.


Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa