Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 132:11 - Buku Lopatulika

11 Yehova analumbira Davide zoona; sadzalibweza; ndi kuti, Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wachifumu wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Yehova analumbira Davide zoona; sadzalibweza; ndi kuti, Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wachifumu wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Chauta adalumbirira Davide momtsimikizira, ndipo sadzasintha, adati, “Ndidzakhazika pa mpando wachifumu mmodzi mwa ana ako aamuna.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Yehova analumbira kwa Davide, lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha: “Mmodzi wa ana ako ndidzamuyika pa mpando waufumu;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 132:11
21 Mawu Ofanana  

Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzatuluka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.


Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;


Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.


Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israele, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wachifumu, maso anga ali chipenyere.


Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga chimene chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wachifumu wa Israele; komatu ana ako achenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.


Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wachifumu wa Israele; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m'chilamulo changa, monga umo unayendera iwe pamaso panga.


pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu mu Israele.


Yehova walumbira, ndipo sadzasintha, Inu ndinu wansembe kosatha monga mwa chilongosoko cha Melkizedeki.


Koma sindidzamchotsera chifundo changa chonse, ndi chikhulupiriko changa sichidzamsowa.


Ndinalumbira kamodzi m'chiyero changa; sindidzanamizira Davide.


Udzakhazikika ngati mwezi kunthawi yonse, ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.


Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova; chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.


Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?


Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake:


Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m'chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake;


kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;


Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa