Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 132:12 - Buku Lopatulika

12 Ana ako akasunga chipangano changa ndi mboni yanga imene ndidzawaphunzitsa, ana aonso adzakhala pa mpando wanu kunthawi zonse,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ana ako akasunga chipangano changa ndi mboni yanga imene ndidzawaphunzitsa, ana aonso adzakhala pa mpando wanu kunthawi zonse,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ngati ana ako aamuna asunga chipangano changa ndi malamulo anga amene ndidzaŵaphunzitsa, ana aonso adzakhala pa mpando wako wachifumu mpaka muyaya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 ngati ana ako azisunga pangano langa ndi malamulo amene ndiwaphunzitsa, pamenepo ana awo adzakhala pa mpando wako waufumu kwamuyaya ndi muyaya.”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 132:12
11 Mawu Ofanana  

kuti Yehova akakhazikitse mau ake adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wachifumu wa Israele.


Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga chimene chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wachifumu wa Israele; komatu ana ako achenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.


pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu mu Israele.


Ana a atumiki anu adzakhalitsa, ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.


Yehova akuonjezereni dalitso, inu ndi ana anu.


Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse.


Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.


Pakuti Yehova atero: Davide sadzasowa munthu wokhala pa mpando wachifumu wa nyumba ya Israele;


Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m'chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa