Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 132:2 - Buku Lopatulika

2 Kuti analumbira Yehova, nawindira Wamphamvuyo wa Yakobo, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Kuti analumbira Yehova, nawindira Wamphamvuyo wa Yakobo, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adalumbira kwa Inu Chauta, nalonjeza kwa Mulungu Wamphamvuzonse wa Yakobe kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye analumbira kwa Yehova ndi kulonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 132:2
15 Mawu Ofanana  

Koma uta wake unakhala wamphamvu, ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa. Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo. (Kuchokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israele.)


Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwake, atampumulitsa Yehova pa adani ake onse omzungulira,


mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndilikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu lili m'kati mwa nsalu zotchinga.


Ndipo mfumu Davide anaima chilili, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangira likasa la chipangano la Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi.


Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.


kufikira nditapezera Yehova malo, chokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?


Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.


Zowindira Inu Mulungu, zili pa ine, ndidzakuchitirani zoyamika.


Mu Ziyoni akulemekezani Inu mwachete, Mulungu, adzakuchitirani Inu chowindachi.


Ndipo ndidzadyetsa iwo amene atsendereza iwe ndi nyama yaoyao; ndi mwazi waowao; iwo adzaledzera monga ndi vinyo wotsekemera; anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndili Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.


Iwe udzayamwanso mkaka wa amitundu, nudzayamwa bere la mafumu, nudzadziwa kuti Ine Yehova ndine Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu ya Yakobo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa