Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;
Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.
Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.
Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.
Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu, ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,
Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.
Misona ya mkango isowa nimva njala, koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.
Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.
Alipo wogawira, nangolemerabe; aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka. Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.
Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu; tinapyola moto ndi madzi; koma munatifikitsa potitsitsimutsa.
ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.
Popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzachepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova padziko lapansi. Ndipo iye anakachita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m'nyumba ake, masiku ambiri. Mbiya ya ufa siidathe, ndi nsupa ya mafuta siinachepe, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.
Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi;
Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;
Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.
M'malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi chitonzo iwo adzakondwera ndi gawo lao; chifukwa chake iwo adzakhala nacho m'dziko mwao cholowa chowirikiza, adzakhala nacho chikondwerero chosatha.
Koma mukumbukire Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera chuma; kuti akhazikitse chipangano chake chimene analumbirira makolo anu, monga chikhala lero lino.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.
Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.
Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikulu, ndi zopambana, zimene suzidziwa.
Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.
Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.
Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa Iye yekha;
Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri; koma wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.
M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.
Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndalama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo wake. Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira. Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao. M'malo mwa mithethe mudzatuluka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamchisu; ndipo chidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati chizindikiro chosatha, chimene sichidzalikhidwa. Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.
Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.
ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israele.
Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka.
Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.
Ndipo pamene Iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza. Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka. Ndipo pamene anachita ichi, anazinga unyinji waukulu wa nsomba; ndipo makoka ao analinkung'ambika;
Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe.
kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.
Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wake, Nditengere chotengera china. Nanena naye, Palibe chotengera china. Ndipo mafuta analeka. Pamenepo anadza, namfotokozera munthu wa Mulungu. Nati iye, Kagulitse mafuta, ukabwezere mangawa ako, ndi zotsalapo zikusunge iwe ndi ana ako.
Dziko lapansi lapereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa. Mulungu adzatidalitsa; ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye.
Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri.
Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ake a izo adazigulitsa, nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagawira yense monga kusowa kwake.
Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakuchulukitsirani ntchito zonse za dzanja lanu, zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za zoweta zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zikukomereni; popeza Yehova Mulungu wanu adzakondweranso kukuchitirani zokoma; monga anakondwera ndi makolo anu;
Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Pakuti ndidzaika izi ndi midzi yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m'nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso.
Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.
Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo.
Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala. Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha. Nyama za m'thengo zidzandilimekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; chifukwa ndipatsa madzi m'chipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;
Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.
Ndiponso zimene sunazipemphe adakupatsa, ndipo chuma ndi ulemu, kuti pakati pa mafumu sipadzakhala ina yolingana ndi iwe masiku ako onse.
Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho.
Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalire, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowe; yense anaola monga mwa njala yake.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.
Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri, kulalikira kuti Yehova ngwolunjika; Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.
Katundu ndi ulemu zili ndi ine, chuma chosatha ndi chilungamo. Chipatso changa chiposa golide, ngakhale golide woyengeka; phindu langa liposa siliva wosankhika. Iima pamwamba pa mtunda, pa mphambano za makwalala; Ndimayenda m'njira ya chilungamo, pakati pa mayendedwe a chiweruzo, kuti ndionetse chuma akundikonda, chikhale cholowa chao, ndi kudzaza mosungira mwao.
Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.
koma mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusowa kwao nthawi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwao kukwanire kusowa kwanu. Kuti pakhale chilingano; monga kwalembedwa, Wosonkhetsa chambiri sichinamtsalire; ndi iye wosonkhetsa pang'ono sichinamsowe.
pakuti Yehova anasankha Ziyoni; analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti, Pampumulo panga mpano posatha, Pano ndidzakhala; pakuti ndakhumbapo. Ndidzadalitsatu chakudya chake; aumphawi ake ndidzawakhutitsa ndi mkate.
Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?
Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa. Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.
Ndipo makwangwala anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu; pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.
Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu. Chifukwa chake ngati simunakhale okhulupirika m'chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona? Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi zake za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?
Anatumizira anthu ake chipulumutso; analamulira chipangano chake kosatha; dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.
si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;
Ndipo anati kwa iwo, Pamene ndinakutumizani opanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba, ndi nsapato, munasowa kanthu kodi? Anati iwo, Iai.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.
Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.
Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.
Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.
Ndiye amene akhalitsa malire anu mumtendere; akukhutitsani ndi tirigu wakucha bwino.
koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho, tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),
Ndipo Iye, m'mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang'ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo. Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, madengu khumi ndi awiri.
polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.
nafese m'minda, naoke mipesa, ndiyo yakubala zipatso zambiri. Ndipo awadalitsa, kotero kuti achuluka kwambiri; osachepsanso zoweta zao.
Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; chifukwa anali wosawerengeka.
kuti m'chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao.
Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeretsa kwambiri; mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi, muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.
Ndipo chimene chilichonse mukafunse m'dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzachita.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monga ananena nanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha; nimudzachita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzachita ufumu pa inu.
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.
Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.
Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuluka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo aakulu.
Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.
Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova. Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwisi; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.
Mudzakhala odala m'mzinda, ndi odala kubwalo. Mudzapalana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m'mwemo; mudzaoka munda wampesa, osalawa zipatso zake. Adzapha ng'ombe yanu, pamaso panu, osadyako inu; adzalanda bulu wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani. Adzapereka ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu. Mtundu wa anthu umene simuudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse; nimudzakhala oyeruka chifukwa chomwe muchiona ndi maso anu. Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pamutu panu. Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simuudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala. Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi mwambi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko. Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha. Mudzaoka m'minda yampesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wake, kapena kutchera mphesa zake, popeza mbozi zidzaidya. Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu. Mudzakhala nayo mitengo ya azitona m'malire anu onse, osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo ya azitona zidzapululuka. Mudzabala ana aamuna ndi aakazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo. Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zaozao za dzombe. Mlendo wokhala pakati panu adzakulirakulira inu, koma inu mudzacheperachepera. Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mchira. Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake ndi malemba ake amene anakulamulirani; ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati chizindikiro ndi chozizwa, nthawi zonse. Popeza simunatumikire Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima, chifukwa cha kuchuluka zinthu zonse; chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani. Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao; Lidzakhala lodala dengu lanu, ndi choumbiramo mkate wanu. mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamchitira chifundo mwana; ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani. Ndipo adzakuzingani m'midzi mwanu monse, kufikira adzagwa malinga anu aatali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m'dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m'midzi mwanu monse, m'dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani. Ndipo mudzadya chipatso cha thupi lanu, nyama ya ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu. Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, diso lake lidzaipira mbale wake, ndi mkazi wa pa mtima wake, ndi ana ake otsalira; osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ake alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu monse. Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lake popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lake lidzamuipira mwamuna wa pamtima pake, ndi mwana wake wamwamuna ndi wamkazi; ndicho chifukwa cha matenda akutuluka pakati pa mapazi ake, ndi ana ake adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu. Mukapanda kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo Yehova Mulungu wanu; Yehova adzachita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwitsa, miliri yaikulu ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa. Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala potuluka inu.
Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu; pakuti sitinatenge kanthu polowa m'dziko lapansi, ndiponso sitingathe kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimene zitikwanire.
Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!
Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo analemera kwakulukulu; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golide, ndi akapolo ndi adzakazi, ndi ngamira ndi abulu.
nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.
Ndipo anawatulutsa pamodzi ndi siliva ndi golide: ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa.
Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!
nusunge chilangizo cha Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zake, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wake, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, kuti ukachite mwa nzeru m'zonse ukachitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako;
komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa. Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani. Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.
Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake. Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? Kapena, Tidzamwa chiyani? Kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
koma monga kulembedwa, Zimene diso silinazione, ndi khutu silinazimve, nisizinalowe mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.
Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sangathe kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.