Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 3:8 - Buku Lopatulika

8 Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sangathe kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndakutsekulirani pa khomo, ndipo palibe amene angatsekepo. Ndikudziŵa kuti mphamvu zanu nzochepa, komabe mwasunga mau anga, ndipo simudandikane.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa ntchito zako. Taona, ndakutsekulira pa khomo ndipo palibe wina amene angatseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa komabe wasunga mawu anga ndipo sunandikane.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 3:8
25 Mawu Ofanana  

ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.


Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling'ono; koma ambiri adzaphatikizana nao ndi mau osyasyalika.


Koma iye wondikana Ine pamaso pa anthu, iye adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.


Kumbukirani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.


Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu.


Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.


Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.


Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,


Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.


Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro:


Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.


Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.


Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sungathe kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;


Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a chinenero cha buku ili.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.


Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza padziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.


Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba: Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa