Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:35 - Buku Lopatulika

35 Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo analemera kwakulukulu; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golide, ndi akapolo ndi adzakazi, ndi ngamira ndi abulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo analemera kwakulukulu; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golide, ndi akapolo ndi adzakazi, ndi ngamira ndi abulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Chauta adamdalitsa kwambiri mbuyanga, ndipo adamkuza kwambiri. Ali ndi nkhosa ndi mbuzi ndi ng'ombe zochuluka. Alinso ndi siliva ndi golide, akapolo aamuna ndi aakazi, ndiponso ngamira ndi abulu ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Yehova wadalitsa mbuye wanga kwambiri, ndiponso walemera. Wamupatsa nkhosa ndi ngʼombe, siliva ndi golide, antchito aamuna ndi antchito aakazi, komanso ngamira ndi abulu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:35
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu aakazi, ndi ngamira.


ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;


ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.


Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golide.


Ndipo Abrahamu anali wokalamba, nagonera zaka zambiri; ndipo Yehova anadalitsa Abrahamu m'zinthu zonse.


Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isaki mwana wake; ndipo Isaki anakhala pa Beere-Lahai-Roi.


Ndipo Abrahamu anampatsa Isaki zonse anali nazo.


Munthuyo ndipo analemera kwambiri, nali nazo zoweta zambiri, ndi akapolo aamuna ndi aakazi, ndi ngamira, ndi abulu.


Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba.


Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamira zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu aakazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum'mawa.


Ndipo awadalitsa, kotero kuti achuluka kwambiri; osachepsanso zoweta zao.


M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.


Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine.


Madalitso a Yehova alemeretsa, saonjezerapo chisoni.


Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.


Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.


Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;


pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa