Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 8:2 - Buku Lopatulika

2 kuti m'chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 kuti m'chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Anthu a m'mipingoyo adayesedwa kwambiri ndi masautso, komabe adakondwa kwakukulu, kotero kuti adapereka moolowa manja kwenikweni, ngakhale anali amphaŵi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 8:2
20 Mawu Ofanana  

Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.


Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?


kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.


Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse.


monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.


polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.


popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;


ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu;


Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;


Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala mu Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda;


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa