Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 103:5 - Buku Lopatulika

5 Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino; nabweza ubwana wako unge mphungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino; nabweza ubwana wako unge mphungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndiye amene amakupatsa zabwino nthaŵi zonse za moyo wako, choncho umakhalabe wa mphamvu zatsopano ngati mphungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino, kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 103:5
12 Mawu Ofanana  

Mnofu wake udzakhala see, woposa wa mwana; adzabwerera kumasiku a ubwana wake.


Chimene muzipatsa zigwira; mufumbatula dzanja lanu, zikhuta zabwino.


Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka, nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.


Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.


Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.


Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.


koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.


Ndipo ndidzampatsa minda yake yampesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m'dziko la Ejipito.


Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.


Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;


Koma lero lino ndili wamphamvu monga tsiku lija anandituma Mose; monga mphamvu yanga pamene paja, momwemo mphamvu yanga tsopano, kugwira nkhondo, ndi kutuluka ndi kulowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa