Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:49 - Buku Lopatulika

49 Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; chifukwa anali wosawerengeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

49 Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; chifukwa anali wosawerengeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

49 Adasonkhanitsa tirigu wochuluka ngati mchenga wakunyanja. Kunali tirigu wochuluka kotero kuti adaaleka nkumuyesa komwe, popeza kuti kunali kosatheka kumuyesa tirigu yenseyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

49 Yosefe anasunga tirigu wochuluka kwambiri ngati mchenga wa ku nyanja. Kunali tirigu wochuluka kwambiri motero kuti analeka nʼkulembera komwe.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:49
9 Mawu Ofanana  

kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;


Ndipo anasonkhanitsa chakudya chonse cha zaka zisanu ndi ziwiri chimene chinali m'dziko la Ejipito, nasunga chakudyacho m'mizinda; chakudya cha m'minda, yozinga mizinda yonse, anachisunga m'menemo.


Ndipo kwa Yosefe anabadwa ana aamuna awiri, chisanafike chaka cha njala, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.


Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamira zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu aakazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum'mawa.


Ndipo anawavumbitsira nyama ngati fumbi, ndi mbalame zouluka ngati mchenga wa kunyanja.


Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; chomwecho ndidzachulukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.


Pakuti anakwera nazo zoweta zao ndi mahema ao, analowa ngati dzombe kuchuluka kwao; iwowa ndi ngamira zao zomwe nzosawerengeka; ndipo analowa m'dziko kuliononga.


Ndipo Amidiyani ndi Aamaleke ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'chigwa, kuchuluka kwao ngati dzombe; ndi ngamira zao zosawerengeka, kuchuluka kwao ngati mchenga wa m'mphepete mwa nyanja.


Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa