Timatamanda Mulungu chifukwa cha tsiku lililonse lapadera limene timakumana nalo, ndi masiku osangalala ndi kukondwerera. Mulungu amasangalala tikamayenda mu mtendere ndi chimwemwe. Muzimutamanda Yehova m'masiku amenewa ndipo musaiwale kuti ndi Mulungu amene amakuchititsani kukhala ndi nthawi zapadera.
Masalimo 30:11-12 amati, “Munasintha kulira kwanga kukhala kuvina; Munandichotsa chiguduli, n’kundiveka chokondwerera; kuti moyo wanga uziyimba nyimbo zotamanda Inu, osakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakutamandani nthawi zonse.” M’Baibulo muli mavesi ambiri okhudza zochitika zapadera.
“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu.
Anthu ochuluka amene anali patsogolo, ndi amene anali m'mbuyo, adayamba kufuula kuti, “Ulemu kwa Mwana wa Davide. Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye. Ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”
“Inu Ambuye Chauta, mwangondiwonetsa chiyambi chake chokha cha ntchito za ukulu wanu ndi mphamvu zanu. Kumwambako, ngakhalenso pansi pano, palibe Mulungu wina amene angathe kuchita zinthu zamphamvu zonga zimene inu mumachita.
Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona.
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Pambuyo pake ku mpando wachifumu uja kudachoka mau akuti, “Tamandani Mulungu wathu, inu nonse atumiki ake, inu nonse omuwopa, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe.”
Nchifukwa chake Davide adatamanda Chauta pamaso pa msonkhano wonse. Adati, “Mutamandike mpaka muyaya Inu Chauta, Mulungu wa Israele, kholo lathu.
Tamandani Chauta! Tamandani Mulungu m'malo ake opatulika. Mtamandeni ku thambo lake lamphamvu.
Mtamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu, mtamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.
Mtamandeni pomuimbira lipenga, mtamandeni ndi gitara ndi zeze.
Mtamandeni poimba ng'oma ndi povina, mtamandeni ndi zipangizo zansambo ndi mngoli.
Mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira, mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira kwambiri.
Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Chauta. Tamandani Chauta!
Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaaŵauzira.
“Palibe woyera wina wofanafana ndi Chauta, palibe wina koma Iye yekha. Palibe thanthwe lina lotchinjiriza lofanafana ndi Mulungu wathu.
Kenaka Ezara adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wamkulu!” Ndipo anthu onse adakweza manja nayankha kuti, “Inde momwemo, inde momwemo.” Pambuyo pake adaŵeramitsa mitu pansi ndipo adapembedza Chauta ali chizyolikire.
Adatenganso pena pathupi, nabala mwana winanso wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano ndidzatamanda Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Yuda. Apo adayamba walekeza kubala.
“Zoonadi, ndinu aakulu, Inu Chauta Wamphamvuzonse. Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha.
Ine ndine Chauta, dzina langa nlimenelo. Ulemerero wanga sindidzapatsa wina aliyense. Mayamiko oyenera Ine, sindidzalola kuti mafano alandireko.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta amene amakhala ku Ziyoni. Lalikani za ntchito zake kwa anthu a mitundu yonse.
Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse.
Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa.
Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha.
Pamenepo Simeoni adalandira mwanayo m'manja mwake, nayamba kutamanda Mulungu ndi mau akuti,
“Ambuye, tsopano mundilole ine mtumiki wanu, ndipite ndi mtendere, pakuti mwachitadi zija mudaalonjezazi.
Motero anthu onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mudzi kwao.
Ndi maso angaŵa ndachiwonadi chipulumutso chija,
Ndidzayamika Chauta nthaŵi zonse, pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza.
Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.
Bwerani ana anga, mundimvere, ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta.
Ndani mwa inu amakhumba moyo ndi kulakalaka kuti akhale masiku ambiri, kuti asangalale ndi zinthu zabwino?
Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa, pakamwa pako pasakambe zonyenga.
Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino. Funafuna mtendere ndi kuulondola.
Ngati mumvera Chauta, adzakuyang'anirani ndipo adzayankha kupempha kwanu.
Koma Chauta amaŵakwiyira anthu ochita zoipa, anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano.
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse.
Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.
Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.
Moyo wanga umanyadira Chauta. Anthu ozunzika amve ndipo akondwere.
Chauta amasunga thupi la munthuyo, palibe fupa limene limasweka.
Choipa chitsata mwini, anthu odana ndi munthu wa Mulungu adzalangidwa.
Chauta amaombola moyo wa atumiki ake. Palibe wothaŵira kwa Iye amene adzalangidwe.
Lalikani pamodzi nane ukulu wa Chauta, tiyeni limodzi tiyamike dzina lake.
Tsono Alevi aŵa, Yesuwa, Kadimiyele, Bani, Hasabeniya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya adalengeza kuti, “Imirirani, mumtamande Chauta, Mulungu wanu, nthaŵi zonse. Litamandike dzina lake laulemerero limene anthu sangathe kulilemekeza ndi kulitamanda mokwanira.”
Iwo adampembedza, pambuyo pake nkubwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu.
Tsono ankasonkhana m'Nyumba ya Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi akutamanda Mulungu.
Ndidzakuyamikani, Inu Mulungu wanga, mfumu yanga, ndidzalemekeza dzina lanu nthaŵi zonse mpaka muyaya.
Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta, anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani.
Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu, adzasimba za mphamvu zanu,
kuti adziŵitse anthu onse za ntchito zanu zamphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu.
Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ulamuliro wanu ndi wa pa mibadwo yonse. Chauta ndi wokhulupirika pa mau ake onse, ndi wokoma mtima pa zochita zake zonse.
Chauta amachirikiza onse ogwa m'mavuto, amakweza onse otsitsidwa.
Maso onse amayang'anira kwa Inu, ndipo mumaŵapatsa chakudya pa nthaŵi yake.
Mumafumbatula dzanja lanu, ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake.
Chauta ndi wolungama m'zochita zake zonse, ndi wachifundo pa zonse zimene achita.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
Ndidzakuthokozani tsiku ndi tsiku, ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya.
Onse amene amakonda Chauta, amaŵasunga, koma Chauta adzaononga oipa onse.
Pakamwa panga padzayamika Chauta, zamoyo zonse zitamande dzina lake loyera mpaka muyaya.
Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera.
Mwadzidzidzi kudachita chivomezi champhamvu, kotero kuti maziko a ndende adagwedezeka. Nthaŵi yomweyo zitseko zonse zidatsekuka, maunyolo a mkaidi aliyense nkumasuka.
Ngakhale mikuyu ipande kuchita maluŵa, mipesa ipande kukhala ndi mphesa, mitengo ya olivi ipande kubala zipatso, m'minda musatuluke kanthu, ndipo nkhosa ndi ng'ombe zithe m'khola,
komabe kwanga nkukondwerera mwa Chauta, kwanga nkusangalala chifukwa cha Mulungu Mpulumutsi wanga.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano! Imbirani Chauta, anthu a m'dziko lonse lapansi!
Uzani mitundu ya anthu kuti, “Chauta ndiye Mfumu. Dziko lonse lidakhazikitsidwa molimba, silidzagwedezeka konse. Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.”
Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere, nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo.
Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam'menemo. Mitengo yam'nkhalango idzaimba mokondwa
pamaso pa Chauta, pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi. Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo, adzalamulira anthu a mitundu yonse moona.
Imbirani Chauta, tamandani dzina lake! Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.
Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri. Nwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa.
Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.”
Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo.
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.
Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu.
Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta.
Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi.
Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo.
Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake.
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.
Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.
Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Tamandani Chauta. Tamandani dzina la Chauta, Perekani matamando, inu atumiki a Chauta,
Ndiye amene adaononga mitundu yambiri ya anthu, ndi kupha mafumu amphamvu aja,
Sihoni, mfumu ya Aamori, ndi Ogi, mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi maufumu onse a ku Kanani.
Adapereka dziko lao kuti likhale choloŵa, choloŵa cha Aisraele, anthu ake.
Dzina lanu, Inu Chauta, nlamuyaya, kutchuka kwanu ndi kwa pa mibadwo yonse.
Pakuti Chauta adzaweruza anthu ake kuti alibe mlandu, adzachitira chifundo atumiki ake.
Mafano a mitundu ina ya anthu ndi asiliva ndi agolide chabe, ndi opangidwa ndi manja a anthu.
Pakamwa ali napo, koma salankhula, maso ali nawo, koma sapenya.
Makutu ali nawo, koma saamva, ndipo alibe mpweya m'kamwa mwao.
Anthu amene amapanga mafanowo afanefane nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.
Inu a m'banja la Israele, tamandani Chauta! Inu a m'banja la Aroni, tamandani Chauta!
inu amene mumatumikira m'Nyumba ya Chauta, m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu!
Inu a banja la Levi, tamandani Chauta! Inu amene mumaopa Chauta, tamandani Chauta!
Atamandike ku Ziyoni Chauta, amene amakhala ku Yerusalemu! Tamandani Chauta!
Tamandani Chauta, pakuti ngwabwino. Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nlokoma kwambiri.
Tamandani Chauta! Nkwabwino kuimba nyimbo zotamanda Mulungu wathu, nkokondwetsa mtima kumtamanda moyenera.
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.
Aisraele asangalale ndi Mlengi wao. Anthu a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yao.
Atamande dzina lake povina, amuimbire nyimbo yokoma ndi ng'oma ndi pangwe.
Imbirani Chauta, inu anthu a dziko lonse lapansi. Lengezani tsiku ndi tsiku za m'mene Iye adapulumutsira anthu ake.
Lalikani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.
Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri, ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
nafunsa Yesu kuti, “Kodi mukumva zimene akunenazi?” Yesu adaŵayankha kuti, “Inde. Kani simudaŵerenge konse mau a Mulungu aja akuti, ‘Mudaphunzitsa ana ndi makanda omwe kukutamandani kotheratu?’ ”
Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Inu Mulungu, mwatiyesa, mwatiyeretsa monga m'mene amayeretsera siliva.
Inu mudatiloŵetsa mu ukonde wa adani, mudatisenzetsa katundu wolemera pamsana pathu.
Inu mudalola kuti adani atikwere pa mutu, tidaloŵa m'moto ndiponso m'madzi, komabe Inu mwatifikitsa ku malo opulumukirako.
Ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzachitadi zimene ndidazilumbira kwa Inu,
zimene ndidalankhula ndi pakamwa panga, ndiponso zimene ndidalonjeza pamene ndinali pa mavuto.
Ndidzapereka kwa Inu nsembe zopsereza za nyama zonenepa, utsi wa nsembe za nkhosa zamphongo udzafika kwa Inu. Ndidzaperekanso ngati nsembe ng'ombe zamphongo ndi mbuzi.
Bwerani mudzamve, inu nonse amene opembedza Mulungu, ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira.
Ndidafuula kwa Iye, ndipo ndidamtamanda ndi pakamwa panga.
Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera.
Koma zoonadi, Mulungu wandimvera, wasamala mau a pemphero langa.
Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu.
Ndiponso akuti, “Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye, anthu a mitundu yonse amtamande.”
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.
Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta amene amakhala ku Ziyoni. Lalikani za ntchito zake kwa anthu a mitundu yonse.
Paja Iye amachitira chifundo anthu ozunzika, salephera kumva kulira kwao ndipo amalanga anthu oŵazunzawo.
Mundikomere mtima, Inu Chauta. Onani m'mene akundisautsira anthu ondida. Inu mumandipulumutsa ku imfa,
kuti ndithe kuyamika ntchito zanu zonse, pakati pa anthu anu a mu Ziyoni. Zoonadi ndidzakondwa chifukwa mwandipulumutsa.
Akunja agwera m'mbuna yokumba iwo omwe. Phazi lao lakodwa mu ukonde wobisika wotcha iwo omwe.
Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe.
Tsono anthu oipa adzapita ku dziko la anthu akufa, ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu.
Koma anthu aumphaŵi Mulungu saŵaiŵala nthaŵi zonse, anthu osauka Mulungu saŵagwiritsa mwala mpang'ono pomwe.
Dzambatukani, Inu Chauta, munthu asakunyozeni. Azengeni mlandu anthu akunja.
Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Ndidamva angelowo akuimba mokweza mau kuti, “Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko.”
Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi. Kumwamba amaimba nyimbo zotamanda ulemerero wanu.
Komabe Inu ndinu oyera, mumakhala pa mpando wanu waufumu, ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani.
Muimbireni Mulungu, imbani nyimbo zotamanda dzina lake. Kwezani nyimbo yotamanda Iye amene amayenda pa mitambo. Dzina lake ndi Chauta, musangalale pamaso pake.
Ndidzaimbira Chauta moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Chauta, nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse. Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu.
Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta, anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani.
Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo.
Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera.
Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga. Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu. Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa mokhulupirika ndi motsimikiza, zinthu zimene mudakonzeratu kalekale.
Tsono ndidzakuthokozani pa msonkhano waukulu, ndidzakutamandani pa chinamtindi cha anthu anu.
Lemekezani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthunu, mau omtamanda Iye amveke.
Iye watchinjiriza moyo wathu, sadalole kuti mapazi athu aterereke.
Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse.
Sitidzabisira ana ao, koma tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo ntchito zotamandika za Chauta, tidzaŵasimbira mphamvu zake ndi zodabwitsa zimene wakhala akuchita.
Tamandani Chauta. Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Tamandani Chauta! Mtamandeni, inu atumiki ake, tamandani dzina la Chauta.
Yamikani Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Dzina la Chauta litamandike kuyambira ku matulukiro a dzuŵa mpaka ku maloŵero ake.
Okhulupirika akondwerere chigonjetso chopambanachi, aziimba mokondwa ali gone pa mabedi.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Tamandani Chauta, inu angelo ake, inu amphamvu amene mumamva mau ake, amene mumachita zimene amalamula.
Tamandani Chauta, inu magulu a ankhondo ake onse, atumiki ake ochita zimene Iye afuna.
Tamandani Chauta, inu zolengedwa zake zonse, ku madera onse a ufumu wake. Nawenso mtima wanga, tamanda Chauta!
Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera, njenjemerani pamaso pake, inu anthu onse a pa dziko lapansi.