Zonsezonse zimene ndikufuna kuchita, ndi mapulani anga onse, zimayamba ndi Mulungu. Iye ndiye gwero la chilichonse chimene ndingathe kuchifika. Maloto anga onse ndi zokhumba zanga zimapezeka mwa Iye.
Kuyambira ndili mwana, ndakhala ndikulakalaka zinthu zosiyanasiyana, kukhala ndi zinthu zanga, ndiponso kupita patsogolo m'moyo, makamaka potsiriza maphunziro anga. Koma, tikudziwa kuti si onse amene amatsiriza ulendo umenewu, ngakhale ambiri amayamba.
Komabe, mphamvu ya Mulungu yandithandiza kufika pamlingo watsopano uwu. Chifukwa cha zimenezi, ndiyenera kuyamika ndi kukhulupirira malonjezo ake. Ndikupempha kwa Mulungu kuti nthawi yomaliza maphunziro anga ifike msanga.
Ndipo ngati ndatsiriza kale, zifukwa zanga zoyamikira n’zochulukirapo, chifukwa Mulungu wandithandiza kufika pano. Zikomo Ambuye.
Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro.
Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Akupatse zimene mtima wako ukukhumba, akuthandize kuti zonse zimene wakonza zichitikedi.
Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye. Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu:
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”
Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni. Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.