Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


46 Mauthenga a Baibulo Olimbikitsa Ochita Masewera

46 Mauthenga a Baibulo Olimbikitsa Ochita Masewera

Ndikukuuzani, mu 1 Akorinto 9:24-25, Baibulo limati, “Kodi simukudziwa kuti akuthamanga m’bwalo amayesetsa onse, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphoto? Thamangani kotero kuti muipeze. Aliyense wochita mpikisano amadziletsa pa zonse. Iwo amachita zimenezi kuti alandire korona yakuvunda, koma ife yosavunda.” Apa tikupatsidwa chithunzithunzi cha moyo wachikhristu ngati mpikisano wothamanga. Monga mmene masewera amafunira kudzipereka, khama, ndi kupirira, ifenso tifunika kuchita chimodzimodzi kuti tipambane nkhondo yabwino ya chikhulupiriro. Tiyeni tikhale odzipereka kupemphera ndi kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, chifukwa zimenezi zitilimbitsa pamene tikumenya nkhondoyi.

Kumbukirani kuti Mulungu akufuna kukugwiritsani ntchito ngati chitoliro cha madalitso kwanu kulikonse kumene muli ndi udindo umene muli nawo. Choncho, musadzipatule kwa Yesu, ndipo muonetsetse kuti mukutamanda dzina lake m’zonse zimene mukuchita.




2 Timoteyo 2:5

Munthu wothamanga pa mpikisano wa liŵiro, sangalandire mphotho ngati sathamanga motsata malamulo a mpikisanowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:24

Monga inu simudziŵa kuti pa mpikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti nkukalandira mphothoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:11-12

Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:23

Yesu adati, “Bwanji mukuti, ‘Ngati mungathe?’ Zinthu zonse nzotheka kwa amene ali ndi chikhulupiriro.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:24-27

Monga inu simudziŵa kuti pa mpikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti nkukalandira mphothoyo. Aliyense wothamanga pa mpikisano wa liŵiro amadziletsa pa zonse. Iwowo amachita zimenezi kuti akalandire mphotho ya nkhata yamaluŵa yotha kufota. Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota. Nchifukwa chake ndimathamanga monga munthu wodziŵa kumene walinga. Ndiponso ndikamachita mpikisano womenyana, sindichita ngati munthu amene angomenya mophonya. Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:8

Kuzoloŵeza thupi kumapindulitsapo pang'ono, koma moyo wolemekeza Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo wakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 31:6

Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:5

Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 3:6

Sindichita mantha ngakhale adani anga ndi osaŵerengeka, ngakhale andizinge ndi kundithira nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 23:12

Koma iyeyo adaima pakatimpakati pa mundawo nautchinjiriza, ndipo adapha Afilistiwo, chifukwa Chauta adampambanitsa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:7-8

Koma upewe nthano zachabe, monga zimene akazi okalamba amakonda kukamba. Udzizoloŵeze kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu. Kuzoloŵeza thupi kumapindulitsapo pang'ono, koma moyo wolemekeza Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo wakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:29-31

Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu. Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu. Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa. Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:5

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:17-18

Tsono muchenjere, musamati, “Ndapeza chuma chonsechi ndi mphamvu zanga ndi nyonga zanga.” Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:32-33

Mulungu wathu ndiye amene amandiveka mphamvu, wandichotsera zoopsa m'njira zanga. Amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbaŵala, ndipo amandisunga bwino m'mapiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 1:9

Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:32-34

Mulungu wathu ndiye amene amandiveka mphamvu, wandichotsera zoopsa m'njira zanga. Amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbaŵala, ndipo amandisunga bwino m'mapiri. Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:1

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:23-24

Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye. Ngakhale agwe sadzapweteka, popeza kuti Chauta amamgwira dzanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:10

Ukataya mtima pamene upeza zovuta, ndiye kuti mphamvu zako ndi zochepa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:16

Munthu wabwino amagwa kasanunkaŵiri, koma amadzukirira ndithu, m'menemo anthu oipa tsoka limaŵagwera chonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:7-8

“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:26

Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:12

Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:27

Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu nkosathekadi, koma ndi Mulungu ai, nkotheka. Paja ndi Mulungu zonse nzotheka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:37

Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:37

Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19-20

Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:31

Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:10

Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:13-14

Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:7

Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1-2

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:12

Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:6-7

Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni. Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Inu Mulungu wanga, ndinu wopereka moyo, amene mumandipulutsa ndi kundikhululukira zolakwa zanga. Sindikudziwa komwe ndikanakhala lero Mulungu wanga popanda inu m'moyo mwanga. Muli wabwino kwambiri, ndipo ndikuyamikira chifukwa cha chikondi chanu chosatha. Atate, dalitsani moyo wa osewera onse, awaphunzitseni kukhala olimba mtima komanso opikisana bwino mu masewera awo. Ndikupempha kuti aliyense wa iwo akhale ndi mtima wodzichepetsa kuti avomereze zotsatira za masewero, kaya kupambana kapena kugonja. Aathandizeni kuti akhulupirire inu osati luso lawo lokha, chifukwa chipambano chimachokera kwa inu. Ambuye, monganso osewera, ndikupemphani kuti mundipatse nzeru ndi mphamvu kuti ndizichita bwino ntchito yanga yamasewera. Ndikufuna kuchotsa mantha ndi nkhawa chifukwa ndimatha kuchita zonse mwa inu amene mumandipatsa mphamvu. Ndithandzeni kukhala wodzipangira dala, ndikuchita masewerowa nthawi zonse, osakhutira ndi zomwe ndikudziwa, koma kukonzekera nthawi zonse mpikisano uliwonse, ndi mtima wabwino wokonzeka kulandira malangizo ndi chitsogozo kuchokera kwa aphunzitsi anga. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa