Ndizovuta kusiya munthu kapena malo omwe timawakonda, chifukwa cha chikondi chimene tili nacho pa iwo. Tonse timadutsamo nthawi yosiyana ndi anthu kapena zinthu, koma ndikofunika kukumbukira kuti sikulakwa kumva chisoni ndi kulira.
Tiyenera kufotokoza zomwe tikumva m'nthawi imeneyi yachisoni ndi kutulutsa mitima yathu pamaso pa Mulungu, kuti tipeze chitonthozo, mphamvu ndi kuchita chifuniro chake moyenera.
Komabe, sitiyenera kulola chisoni ndi ululu kuti zitilamulire kwa nthawi yaitali. Tilole Mulungu apukute misozi yathu ndi kubweretsa chimwemwe mumtima mwathu, chifukwa Iye adzatibwezeretsa kumwetulira kumaso kwathu.
Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Ndili nawe, ndidzakutchinjiriza kulikonse kumene udzapite, ndipo ndidzakubwezanso ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zonse ndakuuzazi.”
Labani adanenanso kuti, “Chauta atiyang'anire ife tonse aŵiri pamene tikulekana. Motero malowo adaŵatcha Mizipa. Atafikako, iye adaŵauza kuti, “Ndaona kuti bambo wanu tsopano sakundipenya ndi maso abwino ngati kale. Koma Mulungu wa atate anga wakhala nane. Labani adapitirira kunena kuti, Ukamakaŵazunza ana angaŵa, kapena ukakakwatira akazi ena, ngakhale palibe wina ali nafe pano, ukumbukire kuti Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi iwe.”
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Madalitso a Ambuye Yesu Khristu ndi chikondi cha Mulungu ndiponso chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.
Ambuye, eniake mtendere amene, akupatseni mtenderewo nthaŵi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
Usiku womwewo Farao adaitana Mose ndi Aroni, ndipo adaŵalamula kuti, “Inu pamodzi ndi Aisraele onse, fulumirani, mutuluke. Asiyeni anthu anga, pitani mukapembedze Chauta monga momwe mudanenera.
“Tsopano ndikudziŵa kuti inu nonse amene ndidakuyenderani kumakulalikirani za ufumu wa Mulungu, simudzaonanso nkhope yanga ai.
Koma wantchitoyo adati, “Chonde musandichedwetse. Chauta wandithandiza kwambiri pa ulendo wangawu. Loleni tsono ndibwerere kwa mbuyanga.”
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.” Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa. Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
Apo Mose adauza Chauta kuti, “Mukapanda kupita nafe limodzi, musatilole kuti tichoke pano.
Chauta ndiye amene ali kothaŵirako ndipo pa dziko lapansili amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adathaŵitsa adani anu onse pamene munkayenda, ndipo adakuuzani kuti muŵaononge onse.
Tsono Chauta adauza Yoswa, mwana wa Nuni, kuti, “Khala wamphamvu ndipo ulimbe mtima. Udzaŵatsogolera Aisraele kukaloŵa m'dziko lomwe ndidaŵalonjeza. Ndipo ndidzakhala nawe.”
Tsono mnyamatayo atapita, Davide adatulukira ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, ndipo adadzigwetsa pansi nagunditsa nkhope yake pansi katatu. Adampsompsonana, nayamba kulira onse aŵiriwo, koma Davide adalira koposa. Pamenepo Yonatani adauza Davide kuti, “Pita ndi mtendere, pakuti aŵirife tidalonjezana molumbira m'dzina la Chauta kuti, ‘Chauta ndiye adzakhale mboni pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa zidzukulu zanga ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.’ ” Pompo Davide adanyamuka nachokapo, ndipo Yonatani adabwerera kumzinda kuja.
Loti adadzisankhira chigwa chonse cha Yordani, napita kukakhala chakuvuma. Umu ndimo m'mene anthu aŵiriwo adasiyanirana.
Eliya atachoka kumeneko, adakapeza Elisa akulima ndi pulawo yokokedwa ndi ng'ombe. Panali magoli khumi ndi aŵiri, mwiniwakeyo nkumakuyenda ndi goli lotsiriza. Eliya adabwera kumene kunali iyeko, namuveka mwinjiro wake. Pomwepo Yezebele adatuma munthu kukauza Eliya kuti, “Milungu indilange ngakhale kundipha kumene, ngati sindikupha iweyo maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, monga momwe udaphera aneneriwo.” Pomwepo Elisa adasiya ng'ombe zakezo, adathamangira Eliya uja nampempha kuti, “Mundilole kuti ndikatsazike bambo wanga ndi mai wanga, ndipo pambuyo pake ndidzakutsatani.” Eliya adamuyankha kuti, “Chabwino, pita. Ndakuletsa ngati?” Apo Elisa adabwerera, ndipo adatenga ng'ombe zake ziŵiri nazipha. Kenaka adatenga magoli a ng'ombezo nasonkhera moto nkuphikira nyamayo, ndipo adaipereka kwa anthu kuti adye. Pambuyo pake adanyamuka namayenda ndi Eliya ndi kumamtumikira.
Akadakhala mdani wanga wondinyozayo, ndikadatha kupirira. Akadakhala mdani wanga wondichita chipongweyo, ndikadangobisala basi. Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye, bwenzi langa wozoloŵerana naye, ndi amene ukuchita zimenezi. Tinkakambirana nkhani zokoma tili aŵiri, tinkapembedza limodzi m'Nyumba ya Mulungu.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu.
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu: Ndaziwona ntchito zimene Mulungu adapatsa anthu kuti azizigwira. Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira. Ndikudziŵa kuti kwa anthu palibe chabwino china choposa kukhala osangalala ndi kumadzikondweretsa nthaŵi yonse ya moyo wao. Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa. Ndikudziŵa kuti zimene Mulungu amazichita zimakhazikika mpaka muyaya. Palibe zimene zingathe kuwonjezedwa kapena kuchotsedwapo pa zimenezo. Mulungu adazipanga motero, kuti choncho anthu azimumvera. Zimene zilipo tsopano zidaaliponso kale. Zimene zidzakhalepo kutsogolo, zidaaliponso kale. Mulungu amabwezanso zakale zimene zidapita kuti zichitikenso. China chimene ndidachiwona pansi pano ndi ichi: Koyenera kukhala chiweruzo chabwino, komwekonso kumapezeka kuipa mtima. Koyenera kukhala chilungamo, komwekonso kumapezeka zoipa. Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.” Kunena za anthu, ndinkalingaliranso kuti, “Mulungu amaŵayesa ndi cholinga choti aŵaonetse kuti iwowo sasiyana konse ndi nyama. Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake. pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Koma Iye adandiyankha kuti, “Usati, ‘Ndine mwana.’ Udzapita ndithu kwa anthu onse kumene ndidzakutuma, ndipo chilichonse chimene ndidzakulamula udzachilankhula. Usaŵaope, Ine ndili nawe, ndidzakupulumutsa,” akuterotu Chauta.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo. Nthaŵi imeneyo mudzandiitana ndi kumanditama mopemba, ndipo ine ndidzakumverani. Mudzandifunafuna, ndipo mudzandipeza. Mukadzandifunafuna ndi mtima wanu wonse,
“Iwe mwana wa munthu, ndakuika kuti ukhale mlonda woyang'anira Aisraele. Uzikati ukamva mau anga, uzikaŵachenjeza.
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.
“Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Ulibenso ntchito mpang'ono pomwe, koma kungoutaya kunja basi, anthu nkumauponda. “Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Munthu aliyense akakana kukulandirani kapena kumvera mau anu, musanse fumbi la kumapazi kwanu potuluka m'nyumbamo kapena m'mudzimo.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ndiponso chifukwa cha Uthenga Wabwino, Koma Yesu poyankha adati, “Kodi Mose adakulamulani zotani?” ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale: nyumba, abale, alongo, amai, ana, minda, komanso mazunzo. Ndipo kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.
Yesu adati, “Munthu amene wayambapo kulima, tsono nkumachewukiranso kumbuyo, Mulungu alibe naye ntchito mu Ufumu wake.”
Yesu adati, “Tsono kapitao wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake?
Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Iyai, kunena zoona, osati mtendere koma kugaŵikana. Kuyambira tsopano m'banja limodzi mudzakhala anthu asanu ogaŵikana, atatu adzakangana ndi aŵiri, ndipo aŵiri adzakangana ndi atatu. Bambo adzakangana ndi mwana wake wamwamuna, mwana wamwamuna adzakangana ndi bambo wake. Mai adzakangana ndi mwana wake wamkazi, mwana wamkazi adzakangana ndi mai wake. Apongozi adzakangana ndi mkazi wa mwana wao, ndipo mkaziyo adzakangana ndi apongozi akewo.”
Ana anga, ndili nanube kanthaŵi pang'ono. Mudzandifunafuna, koma ndikukuuzani tsopano, monga ndidauziranso akulu a Ayuda kuti, ‘Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako.’
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso. Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao. Mundikhulupirire kuti Ine ndimakhala mwa Atate ndipo Atate amakhala mwa Ine. Kupanda apo, khulupiriranitu chifukwa cha ntchito zanga zomwezo. Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate. Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.” “Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu. Sindidzakusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ndidzabweranso kwa inu. Kwangotsala kanthaŵi pang'ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu. “Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.” Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. “Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. “Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine.
Nthaŵi ilikudza, ndipo yafika kale, pamene mudzabalalikana aliyense kunka kwao, Ine kundisiya ndekha. Komabe sindili ndekha, pakuti Atate ali nane. Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Onsewo adalira kwambiri. Adamkumbatira Pauloyo namumpsompsona polaŵirana naye. Makamaka adachita chisoni chifukwa cha mau ake aja onena kuti iwo sadzaonanso nkhope yake. Pambuyo pake adamperekeza kuchombo.
Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa, pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona. Anthu onse adaimva mbiri ya kumvera kwanu. Tsono ine ndikunyadira inuyo, koma ndifuna kuti mukhale anzeru pa zabwino, ndi othaŵa zoipa.
Mipingo ya ku dziko la Asiya ikuti moni. Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi mpingo umene umasonkhana m'nyumba mwao, akuti moni kwa inu nonse, akhristu anzao. Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera. Abale onse akuti moni. Mupatsane moni mwa chikondi chenicheni.
Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziŵa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya. Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa. Tsono popeza tikudziŵa kuti Ambuye ngoyenera kuŵaopa, timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziŵa kwathunthu, ndipo tikhulupirira kuti inunso mumatidziŵa kwenikweni m'mitima mwanu. Sitikuyesa kudzichitiranso umboni pamaso panu ai, koma tingofuna kukupatsani chifukwa choti muzitinyadira. Tikufuna kuti mukhale ndi kanthu koŵayankha amene angonyadira zooneka ndi maso, osati zamumtima. Ngati tidachita ngati tapenga, tidachita zimenezi kuti tilemekeze Mulungu. Koma ngati tikuchita zanzeru, tikuchita zanzeru kuti tikuthandizeni. Chikondi cha Khristu ndicho chimatiwongolera mokakamiza, popeza kuti tikudziŵa mosakayika konse kuti Munthu mmodzi adafera anthu onse, ndiye kuti pamenepo onse adafa. Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adaŵafera, nauka kwa akufa chifukwa cha iwowo. Nchifukwa chake kuyambira tsopano ife sitiganiziranso za munthu aliyense potsata nzeru za anthu chabe. Ngakhale kale tinkaganiza za Khristu potsata nzeru za anthu chabe, koma tsopano sitiganizanso za Iye motero. Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano. Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho. Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike. Nchifukwa chake tsono tikubuula ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu yakumwambayo, Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu. Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu. kuti titaivala, tisadzapezeke amaliseche. Ife amene tili mu msasa uno timalemedwa ndipo timabuula. Sitifuna kuuvula msasawu ai, koma kwenikweni tikadakonda kuvala nyumba ija ya Kumwamba pamwamba pake, kuti chimene chili chakufa chimizidwe ndi moyo.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.
Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu. Ndi cholinga chimenechi ndikugwiradi ntchito kwambiri ndi mphamvu ya Khristu imene ikugwira ntchito kolimba mwa ine.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani. Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.
Koma tidakhala ofatsa pakati panu ngati mai wosamalira ana ake. Tinkakukondani, ndipo chifukwa cha kukulakalakani kwambiri, tidatsimikiza zogaŵana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso ngakhale moyo wathu womwe.
Abale, tsopano tikukulamulani m'dzina la Ambuye Yesu Khristu kuti muziŵapewa abale onse a makhalidwe aulesi, osafuna kutsata mwambo umene tidaŵapatsa.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Nchifukwa chake ine adandiika kuti ndikhale mlaliki wake ndiponso mtumwi, wophunzitsa anthu a mitundu ina mau a chikhulupiriro choona. Sindikunamatu ai, ndikunena zoona.
Uŵagwiritse mau oona amene udamva kwa ine, kuti akhale chitsanzo choti uzitsata. Uzichita zimenezi mwa chikhulupiriro ndi mwa chikondi, zimene zili mwa Khristu Yesu. Usunge bwino zokoma zimene adakusungitsa pakutsata Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.
Nchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti mphatso imene Mulungu adakupatsa pamene ndidakusanjika manja, uiyatsenso ngati moto. Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira.
Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro. Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira. Ambuye amene ali Woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphothoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso.
Uziŵakumbutsa anthu onse kuti azigonjera akulu oweruza ndi olamulira. Aziŵamvera ndipo azikhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino. Munthu woyambitsa mipatuko, utamdzudzula kaŵiri konse, usakhale nayenso nkanthu. Paja ukudziŵa kuti munthu wotere ngwosokonezeka ndipo ngwochimwa. Mwini wake yemwe amadziimba mlandu yekha. Ndikadzamtuma Aritema kapena Tikiko kwanuko, uchite chotheka kudzandipeza ku Nikopoli, chifukwa ndatsimikiza kuti ndikakhala kumeneko nyengo yachisanu ikubwerayi. Uyesetse kuthandiza Zena, katswiri wa malamulo uja ndiponso Apolo, kuti apitirize ulendo wao. Uwonenso kuti asasoŵe kanthu. Anthu athunso aziphunzira kudzipereka pa ntchito zabwino, kuti azithandiza pamene pali kusoŵa kwenikweni. Azitero kuti moyo wao usakhale wopanda phindu. Onse amene ali nane kuno akuti moni. Uperekeko moni kwa onse amene amatikonda chifukwa cha chikhulupiriro. Mulungu akukomereni mtima nonse. Uŵauze kuti asamakamba zoipa za wina aliyense, apewe kukangana, akhale ofatsa, ndipo nthaŵi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Pitirizani kukondana monga abale. Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo. Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa. Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake. Tiyeni tsono tipite kwa Iye kunja kwa misasa kuti tikanyozekere naye limodzi. Paja ife tilibe mzinda wokhazikika pansi pano, tikufunafuna wina umene ulikudza. Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera. Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu. Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe. Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo. Ndikukupemphani makamaka kuti mupemphere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga. Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo. Mulungu wopatsa mtendere, adaukitsa kwa akufa Ambuye athu Yesu, amene ndiye Mbusa wamkulu wa nkhosa, chifukwa cha imfa yake yotsimikizira Chipangano chamuyaya. Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen. Ndikukupemphani, inu abale anga, kuti muŵalandire bwino mau okulimbitsani mtimaŵa, pakuti ndangokulemberani mwachidule. Ndikufuna kuti mudziŵe kuti Timoteo, mbale wathu, amtulutsa m'ndende. Akafika msanga, ndidzabwera naye kwanuko podzakuwonani. Mutiperekereko moni kwa atsogoleri anu onse, ndi kwa anthu onse a Mulungu. Abale a ku Italiya akuti moni. Mulungu akukomereni mtima nonse. Muzikumbukira am'ndende, ngati kuti mukuzunzikira nawo limodzi m'ndendemo. Muzikumbukira ovutitsidwa, pakuti inunso muli ndi thupi.
Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza, Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu. dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.
Paja mau a Mulungu amanena kuti, “Anthu onse ali ngati udzu, ulemerero wao uli ngati duŵa lakuthengo. Udzu umauma, ndipo duŵa limathothoka, koma mau a Ambuye ngokhala mpaka muyaya.” Mau ameneŵa ndi Uthenga Wabwino umene walalikidwa kwa inu.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha. Iye ndiye mwini mphamvu mpaka muyaya. Amen.
Koma mukule m'chifundo ndi m'nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen.
Chimene tidachiwona ndi kuchimva, tikukulalikirani, kuti inunso mukhale a mtima umodzi ndi ife. Kuyanjana kwathu tikuyanjana ndi Atate, ndiponso ndi Mwana wao, Yesu Khristu.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Inu Chauta, ndikudziŵa kuti kuweruza kwanu nkolungama, ndipo mwandilanga potsata kukhulupirika kwanu.
Ndaima pakhomo pano, ndipo ndikugogoda. Wina akamva mau anga, nkutsekula chitseko, ndiloŵa, ndipo Ine ndi iye tidyera limodzi.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la atate ako. Usachite kupita ku nyumba ya mbale wake, ukakhala pa mavuto. Mnzako wokhala naye pafupi amaposa mbale wako wokhala kutali.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake?
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.”
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Popeza kuti Mulungu adachita kundituma, ndidakhazika maziko monga mmsiri waluso, ndipo wina akumanga pa mazikowo. Koma aliyense azichenjera pomanga.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Ndikufuna kuti zimenezi ziŵalimbitse mtima, ndipo azilunzana pamodzi m'chikondi, azikhala odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu. Motero adzatha kudziŵa mozama chinsinsi cha Mulungu chonena za Khristu. Mudafa pamodzi ndi Khristu, ndiye kuti simulamulidwanso ndi miyambo ya dziko lapansi. Tsono bwanji mukuchita ngati kuti moyo wanu ukudalirabe zapansipano? Bwanji mukuŵamvera malamulo onga aŵa akuti, “Usagwire chakuti”, “Usakhudze chakuti”? Malamulo ameneŵa ndi zophunzitsa zimenezi ndi za anthu chabe, ndipo zimangokhudza zinthu zimene zimatha, anthu akamazigwiritsa ntchito. Kwinaku mauwo amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamula anthu zambiri pa za kupembedza, za kudzichepetsa ndi za kuzunza thupi lao. Komabe malamulowo alibe phindu, ndipo sathandiza konse kugonjetsa khalidwe longosangalatsa thupi. Mwa Iyeyu mudzapeza chuma chonse chobisika, ndiye kuti nzeru ndi luntha.
Abale, tifuna kuti mudziŵeko za anthu amene adamwalira, kuti chisoni chanu chisakhale ngati cha anthu ena amene alibe chiyembekezo. Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.
Iwe Timoteo, mwana wanga, ndikukupatsa malangizo ameneŵa molingana ndi zimene aneneri adaanenapo kale za iwe. Mau amenewo akuthandize kumenya nkhondo yabwino, uli ndi chikhulupiriro ndiponso ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa. Ena sadamvere pamene mtima wao unkaŵatsutsa, motero chikhulupiriro chao chidaonongeka.
Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu: “Ngati tidafa pamodzi naye, tidzakhala moyonso pamodzi naye. Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye. Ngati ife timkana, Iyenso adzatikana. Ngati ndife osakhulupirika, Iye amakhalabe wokhulupirika, pakuti sangathe kudzitsutsa.”
Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse. Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu. Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake. Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Koma ndimadalira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu Mulungu wanga.” Masiku anga ali m'manja mwanu. Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse. Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Ngwodala munthu amene amatchera khutu kwa ine, amene amakhala pakhomo panga tsiku ndi tsiku, amene amadikira pa chitseko changa. Paja wondipeza ine, wapeza moyo, ndipo amapeza kuyanja pamaso pa Chauta.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu. Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72, naŵatuma aŵiriaŵiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene Iye ankati apiteko. Koma kumudzi kumene mukaloŵe, anthu nkupanda kukulandirani bwino, mukapite m'miseu yam'mudzimo, nkukanena kuti, ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la m'mudzi mwanu muno limene linamamatira ku mapazi athu. Komabe dziŵani kuti ufumu wa Mulungu wafika.’ Kunena zoona, pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga mudzi umenewo. “Uli ndi tsoka, iwe Korazini! Uli ndi tsoka, iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima. Koma pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu. Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.” Yesu adauza anthu 72 aja kuti, “Wokumverani inu, akumvera Ine amene. Wokukanani inu akukana Ine amene. Ndipo wondikana Ine, akukananso Atate amene adandituma.” Anthu 72 aja adabwerako ndi chimwemwe nati, “Ambuye, ngakhale mizimu yoipa yomwe imatigonjera tikamailamula m'dzina lanu.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndidaona Satana alikugwa ngati mphezi kuchokera Kumwamba. Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni. Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo. Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa Kumwamba.” Nthaŵi yomweyo Mzimu Woyera adadzaza Yesu ndi chimwemwe, mwakuti Yesuyo adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu. “Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.” Pambuyo pake Yesu adatembenukira ophunzira ake, naŵauza iwo okha kuti, “Ngodala maso amene akuwona zimene mukuwonazi. Kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu ambiri adaafunitsitsa kuwona zimene inu mukupenyazi, koma sadaziwone. Adaafunitsitsa kumva zimene inu mukumvazi, koma sadazimve.” Katswiri wina wa Malamulo adaimirira kuti ayese Yesu. Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mudalembedwa chiyani? Mumaŵerengamo zotani?” Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” Yesu adati, “Mwayankha bwino. Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.” Koma munthu uja pofuna kudziwonetsa ngati wolungama, adafunsa Yesu kuti, “Nanga mnzangayo ndani?” Pitani tsono. Ndikukutumani ngati anaankhosa pakati pa mimbulu.
Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo. Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao. Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.” Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”