Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, kugwira ntchito sikuti kumatipindulitsa pa chuma chokha ayi. Kumatithandizanso m'mbali zina za moyo wathu. Kutipangitsa kugwiritsa ntchito bwino mphatso ndi nzeru zomwe Mulungu watipatsa.
Baibulo limati, “Perekeza ntchito zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.” (Miyambo 16:3). Tili ndi lonjezo la Atate wathu, ngati tipempha, Iye atitsogolera ndi kutidalitsa.
Ngakhale ntchito ikhale yovuta bwanji, tidzaona dzanja la Mulungu likugwira ntchito m'miyoyo yathu. Zinthu zidzayenda bwino chifukwa tamupereka kwa Iye zisankho zathu. Mulungu adzatipatsa chipambano m'zonse zomwe tichite, chifukwa munthu aliyense amene amapereka mapazi ake kwa Yehova, amayenda motetezeka ndipo sadzasowa kanthu. Zonse zomwe zikuzungulira zidzagwirira ntchito limodzi kuti zibweretse zabwino, mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
Koma Yesu adaŵauza kuti, “Atate anga akugwira ntchito mpaka tsopano, nanenso ndikugwira ntchito.”
M'maŵa, Inu Chauta, mumamva mau anga. M'maŵa ndimapemphera kwa Inu, ndi kudikira kuti mundiyankhe.
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Paja nthaŵi imene tinali nanu pamodzi, tidaakulamulani kuti munthu wosafuna kugwira ntchito, kudyanso asadye.
Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.
Inu Ambuye, Mulungu wathu, mutikomere mtima, ndi kudalitsa zonse zimene timachita, ndithu mudalitse ntchito zonse za manja athu.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.
Ukonzeretu ntchito zako zonse makamaka zakumunda, pambuyo pake mpamene ungayambe kumanga nyumba.
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Inu akapolo, ambuye anu a pansi pano muziŵamvera mwamantha ndi monjenjemerera. Muzichita zimenezi ndi mtima woona, ngati kuti mukuchitira Khristu yemwe. Musazichite mwachiphamaso chabe, ngati kuti mukungofuna kukondweretsa anthu. Koma ngati akapolo a Khristu, muzichita ndi mtima wonse zimene Mulungu afuna. Muzitumikira mosangalala, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu chabe. Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.
Chuma chochipeza mofulumira chidzanka chitha pang'onopang'ono, koma chochipeza pang'onopang'ono chidzanka chichulukirachulukira.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Kodi ukumuwona munthu wochita ntchito zake mwaluso? Iye adzatumikira mafumu, sadzatumikira anthu wamba.
Ntchito iliyonse imene ukuti uigwire, uigwire ndi mphamvu zako zonse. Pajatu kumanda kumene ukupitako kulibe ntchito, kulibe malingaliro, kulibe nzeru, ndiponso kulibe luntha.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso. Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Muzitumikira mosangalala, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu chabe. Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.