Mu buku la Aheberi, Yesu akufotokozedwa ngati Mkulu wa Ansembe wangwiro, wopambana aliyense amene anakhalako. Ntchito yaikulu ya mkulu wa ansembe inali kuyanjanitsa Mulungu ndi anthu, kupereka nsembe za machimo a anthu. Koma Yesu anapita patsogolo pa ntchito imeneyi, chifukwa iye mwini anakhala nsembe yangwiro ya machimo athu podzipereka yekha pa mtanda.
Imfa ndi kuuka kwake zinatsegula njira yoyanjanirana ndi Mulungu kwamuyaya. Monga Mkulu wa Ansembe, Yesu amatipempherera kwa Atate. Amadziwa zofooka zathu ndi mavuto athu, chifukwa anakhalanso munthu ngati ife. Chifundo ndi chikondi chake ndi chopanda malire, ndipo nthawi zonse ndi wokonzeka kutikhululukira ndi kutipatsa chikondi chake chosatha.
Kudzera mu nsembe yake, Yesu amatipatsa chisomo chofunikira kuti tipeze chipulumutso ndi kumasulidwa ku ukapolo wa uchimo. Ntchito ya mkulu wa ansembe ndi kuphunzitsa ndi kutsogolera anthu. Yesu anakwaniritsa udindo umenewu mwangwiro, potisiya ndi ziphunzitso zofunika zomwe zimatipatsa moyo wabwino komanso ubwenzi wolimba ndi Mulungu.
Iye ndiye njira, choonadi, ndi moyo, ndipo ndi chitsanzo chathu cha kukhala moyo wotsatira mfundo za Ufumu wa Kumwamba. Tikhulupirire Mulungu ndi kumtsatira Yesu, ndipo tidzapeza mtendere weniweni ndi chimwemwe.
Penanso Mulungu adati, “Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”
Yesu adatitsogolera kale nkuloŵamo chifukwa cha ife. Iye adasanduka mkulu wa ansembe onse wamuyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Chauta walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake akuti, “Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”
Tiyeni tsono, tigwiritse chikhulupiriro chimene timavomereza. Pakuti tili naye Mkulu wa ansembe wopambana, amene adapita mpaka kukafika kumwamba kwenikweni kwa Mulungu. Iyeyu ndi Yesu, Mwana wa Mulungu.
Nkhaniyi imamveka bwino koposa pamene tiwona kuti pafika wansembe wina wonga Melkizedeki.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Tsono padaafunika kuti tikhale naye wotere mkulu wa ansembe onse: woyera mtima, wopanda choipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kubzola zonse zakumwambaku.
Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa pakati pa anthu, namuika kuti aziŵaimirira pamaso pa Mulungu. Ntchito yake nkupereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo.
Paja Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene adampatsa udindowo, monga momwe Mosenso anali wokhulupirika m'nyumba yonse ya Mulungu.
Momwemonso Khristu sadadzikweze yekha ku ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma Mulungu ndiye adachita kumuuza kuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga, Ine lero ndakubala.”
Penanso Mulungu adati, “Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”
Yesu ameneyu sali ngati akulu a ansembe ena aja. Palibe chifukwa chakuti tsiku ndi tsiku azipereka nsembe poyamba chifukwa cha machimo ake, kenaka chifukwa cha machimo a anthu. Zimenezi adachitiratu kamodzi kokha, pakudzipereka yekha ngati nsembe.
Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo.
Nchifukwa chake adaayenera kusanduka wofanafana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe onse wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, ndipo kuti pakutero achotse machimo a anthu.
Melkizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wopambanazonse. Pamene Abrahamu ankabwerako kuchokera ku nkhondo, atagonjetsa mafumu aja, Melkizedeki adadzamchingamira, namdalitsa.
Pakuti iye anali akadali m'thupi la kholo lake Abrahamu pamene Melkizedeki adadzamchingamira.
Malamulo amene Aisraele adalandira, anali okhazikika pa unsembe wa Levi. Tsono achikhala kudaali kotheka kukhala angwiro mwa unsembe umenewu, sikukadafunikanso unsembe wina, wonga uja wa Melkizedeki, wosiyana ndi wonga uja wa Aroni.
Pakuti pakakhala kusintha pa unsembe, ndiye kuti pa Malamulonso sipangalephere kukhala kusintha.
Ambuye athu, amene mauŵa akunena za Iwo, anali a fuko lina. Ndipo palibiretu wa fuko limeneli amene adatumikirapo ku guwa lansembe.
Nchodziŵikiratu kuti Ambuye athu aja anali a fuko la Yuda, ndipo Mose pokamba za fuko limeneli, sadanenepo kanthu za ansembe.
Nkhaniyi imamveka bwino koposa pamene tiwona kuti pafika wansembe wina wonga Melkizedeki.
Iyeyo sadakhale wansembe chifukwa cha malamulo okhudza kubadwa kwa anthu, koma chifukwa cha mphamvu za moyo wake umene uli wosatha.
Paja mau a Mulungu pomuchitira umboni akuti, “Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”
Motero lamulo lakale lalekeka chifukwa linali lopanda mphamvu, linali lopanda phindu.
Pajatu Malamulo a Mose sankatha kusandutsa munthu kuti akhale wangwiro. Koma m'malo mwake mwaloŵa chiyembekezo choposa, ndipo mwa chiyembekezo chimenechi timayandikira kwa Mulungu.
Abrahamu adampatsa chigawo chachikhumi cha zonse zimene adaafunkha. Potsata tanthauzo la dzina lake, choyamba Melkizedeki ndi “Mfumu ya chilungamo,” pambuyo pake ndi “Mfumunso ya Salemu,” ndiye kuti, “Mfumu ya Mtendere”.
Chinanso nchakuti Mulungu adaachita kulumbira. Amene ankaloŵa unsembe kale lija ankatenga udindo waowo popanda lumbiro.
Koma Yesu adaloŵa unsembe wake ndi lumbiro, pamene Mulungu adamuuza kuti, “Ambuye adalumbira, ndipo sadzasintha maganizo ake akuti, ndiwe wansembe mpaka muyaya.”
Kusiyana kokhudza lumbiroku kukutiwonetsa kuti Yesu ndi Nkhoswe yotsimikizira Chipangano choposa.
Kusiyana kwina nkwakuti ansembe akale aja anali ambiri, chifukwa ankafa, sankatha kupitirira ndi udindo waowo.
Koma Yesu ngwamuyaya, motero unsembe wake ngwosasinthika.
Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.
Tsono padaafunika kuti tikhale naye wotere mkulu wa ansembe onse: woyera mtima, wopanda choipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kubzola zonse zakumwambaku.
Yesu ameneyu sali ngati akulu a ansembe ena aja. Palibe chifukwa chakuti tsiku ndi tsiku azipereka nsembe poyamba chifukwa cha machimo ake, kenaka chifukwa cha machimo a anthu. Zimenezi adachitiratu kamodzi kokha, pakudzipereka yekha ngati nsembe.
Malamulo a Mose amaika anthu amene ali ndi zofooka, kuti akhale akulu a ansembe onse. Koma mau a lumbiro la Mulungu lija limene lidabwera pambuyo pa Malamulowo, adaika Mwana wake, amene wakhala wangwiro kwamuyaya kuti akhale mkulu wa ansembe onse.
Za bambo wake kapena mai wake, kapena makolo ake, palibe chilichonse chidalembedwa. Chimodzimodzi za kubadwa kwake ndi imfa yakenso. Ali ngati Mwana wa Mulungu, akupitiriza kukhala wansembe mpaka muyaya.
Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha.
Malamulo amene Aisraele adalandira, anali okhazikika pa unsembe wa Levi. Tsono achikhala kudaali kotheka kukhala angwiro mwa unsembe umenewu, sikukadafunikanso unsembe wina, wonga uja wa Melkizedeki, wosiyana ndi wonga uja wa Aroni.
Koma Khristu adapereka nsembe imodzi yokha yochotsera machimo onse. Ndipo ataipereka, adakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
Nkhaniyi imamveka bwino koposa pamene tiwona kuti pafika wansembe wina wonga Melkizedeki.
Iyeyo sadakhale wansembe chifukwa cha malamulo okhudza kubadwa kwa anthu, koma chifukwa cha mphamvu za moyo wake umene uli wosatha.
Paja mau a Mulungu pomuchitira umboni akuti, “Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”
Tsono popeza kuti iye yemwe adazunzikapo ndi kuyesedwapo, ndiye kuti angathe kuŵathandiza anthu amene amayesedwa.
Kusiyana kokhudza lumbiroku kukutiwonetsa kuti Yesu ndi Nkhoswe yotsimikizira Chipangano choposa.
Kusiyana kwina nkwakuti ansembe akale aja anali ambiri, chifukwa ankafa, sankatha kupitirira ndi udindo waowo.
Koma Yesu ngwamuyaya, motero unsembe wake ngwosasinthika.
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.
Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.
Tsono padaafunika kuti tikhale naye wotere mkulu wa ansembe onse: woyera mtima, wopanda choipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kubzola zonse zakumwambaku.
Yesu ameneyu sali ngati akulu a ansembe ena aja. Palibe chifukwa chakuti tsiku ndi tsiku azipereka nsembe poyamba chifukwa cha machimo ake, kenaka chifukwa cha machimo a anthu. Zimenezi adachitiratu kamodzi kokha, pakudzipereka yekha ngati nsembe.
Mfundo yeniyeni pa zimene tikunenazi ndi iyi: tili naye wotere Mkulu wa ansembe onse, amene akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu Waulemerero Kumwamba.
Iye akutumikira m'Malo Opatulika am'katikati, ndiye kuti m'chihema chenicheni chimene adachimanga ndi Ambuye osati munthu ai.
Koma monga zilirimu, Yesu adalandira unsembe wopambana kutalitali unsembe wakale uja, monga momwe ndiyenso Nkhoswe ya chipangano chopambana, chifukwa malonjezo ake ngopambana malonjezo a chipangano chakale chija.
Koma Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso changwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano.
Nchifukwa chake Khristu ndi Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti amene Mulungu adaŵaitana, alandire madalitso osatha amene Mulunguyo adalonjeza. Izi zidatheka chifukwa cha imfa ya Khristu, imene imapulumutsa anthu ku zochimwa zozichita akali m'Chipangano choyamba chija.
Paja Khristu sadaloŵe m'malo opatulika omangidwa ndi anthu, malo ongofanizira malo enieni opatulika a Kumwamba. Iye adapita Kumwamba kwenikweniko, kuti tsopano aziwonekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.
Zikadatero, akadayenera kumamva zoŵaŵa kaŵirikaŵiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma monga zilirimu, waoneka kamodzi kokha pakutha pake pa nthaŵi yotsiriza, kuti achotse uchimo pakudzipereka yekha nsembe.
Chifukwa chakuti Yesu Khristu adachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako.
Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu.
Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe.
Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake.
Abale, ndinu oyera ake a Mulungu, inuyo adakuitanani kuti nanunso mukhale ndi moyo wakumwamba. Nchifukwa chake muzisinkhasinkha za Yesu, mtumwi wa Mulungu, ndiponso Mkulu wa ansembe onse wa chikhulupiriro chimene timavomereza.
Nchifukwa chake aumirizidwa kumapereka nsembe chifukwa cha machimo a iye yemwe, ndiponso machimo a anthu ena.
“Aroni ndi ana ake aamuna apatulidwe pakati pa Aisraele ndipo abwere kwa iwe, kuti akhale ansembe onditumikira. Abwere Aroni pamodzi ndi ana ake Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.
Wansembe amene wadzozedwa nayeretsedwa kuti akhale mkulu wa ansembe onse m'malo mwa bambo wake, adzachite mwambo wopepesera machimo, atavala zovala zopatulika zabafuta.
Adzachite mwambo wopepesera malo oyera. Adzachitenso mwambo wopepesera chihema chamsonkhano ndi guwa, ndiponso mwambo wopepesera machimo a ansembe anzake ndi a mpingo wonse.
Limeneli lidzakhala lamulo lanu lamuyaya, kuti muzidzachita mwambo wopepesera machimo onse a Aisraele kamodzi pa chaka.” Tsono Mose adachita monga momwe Chauta adamlamulira.
“Munthu amene ali mkulu wa ansembe onse, amene adamdzoza pa mutu ndi mafuta, ndiponso amene adapatulidwa pakumuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake, kapena kung'amba zovala zake kusonyeza kuti ali pamaliro.
Malamulo a Mose amaika anthu amene ali ndi zofooka, kuti akhale akulu a ansembe onse. Koma mau a lumbiro la Mulungu lija limene lidabwera pambuyo pa Malamulowo, adaika Mwana wake, amene wakhala wangwiro kwamuyaya kuti akhale mkulu wa ansembe onse.
Paja mkulu wa ansembe aliyense amaikidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu. Motero nkofunika kuti wathunso mkulu wa ansembe onse akhale nkanthu koti apereke.
Ndipo chifukwa cha iwoŵa ndikudzipereka kwa Inu, kuti iwonso akhale odzipereka moonadi kwa Inu.”
Tsono palibe amene angaŵaweruze kuti ngopalamula. Khristu Yesu amene adafa, kaya tinene kuti amene adauka kwa akufa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndiye amene akutinenera kwa Mulunguyo.
Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama.
Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Motero Ine ndidzampatsa ulemu woyenerera akuluakulu. Adzagaŵana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza kuti adapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo. Adasenza machimo a anthu ambiri, ndipo adaŵapempherera ochimwawo kuti akhululukidwe.
Ndiye amene adzamange Nyumba ya Chauta. Ndiye amene adzakhale ndi ukulu waufumu, ndi kumalamulira atakhala pa mpando wake waufumu. Pafupi ndi mpando wake padzakhala wansembe, ndipo aŵiriwo adzagwira ntchito mwamtendere ndi mogwirizana.
Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa.
Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana.
Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.”
“Atate, ndifuna kuti amene mudandipatsa, iwonso akhale pamodzi ndi Ine kumene ndili. Ndifuna kuti aone ulemerero wanga umene mudandipatsa, chifukwa mudandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.
Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.
Mwafika kwa Yesu, Nkhoswe yokonza za chipangano chatsopano, ndiponso mwafika ku magazi okhetsedwa, amene akutilonjeza zinthu zabwino koposa m'mene magazi a Abele ankachitira.
Mulungu wopatsa mtendere, adaukitsa kwa akufa Ambuye athu Yesu, amene ndiye Mbusa wamkulu wa nkhosa, chifukwa cha imfa yake yotsimikizira Chipangano chamuyaya.
Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.
Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.
Motero Yesu, ngakhale anali Mwana wa Mulungu, adaphunzira kumvera pakumva zoŵaŵa.
Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye,
Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu.
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera.
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.
Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda.
Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse.
Iyeyo sadakhale wansembe chifukwa cha malamulo okhudza kubadwa kwa anthu, koma chifukwa cha mphamvu za moyo wake umene uli wosatha.
“Ine ndikuŵapempherera. Sindikupempherera anthu ena onse, koma ndikupempherera iwoŵa amene mudandipatsa, chifukwa ndi anu.
Chauta adauza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja, mpaka nditasandutsa adani ako kukhala ngati chopondapo mapazi ako.”
adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.
Mulungu Atate adakusankhani, monga Iye adaziganiziratu kuyambira pa chiyambi, kuti Mzimu Woyera akuyeretseni ndipo kuti mumvere Yesu Khristu, ndi kutsukidwa ndi magazi ake. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wonka nuchulukirachulukira.
Iyeyo Mulungu adaamsankhiratu dziko lapansi lisanalengedwe, koma wamuwonetsa nthaŵi yotsiriza ino chifukwa cha inu.
Komatu tikuwona kuti Yesu, amene pa kanthaŵi pang'ono adaasanduka wochepera kwa angelo, adalandira mphotho ya ulemerero ndi ulemu chifukwa adamva zoŵaŵa za imfa. Zidatero chifukwa mwa kukoma mtima kwake Mulungu adaafuna kuti afere anthu onse.
Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati.
Palibe munthu amadzitengera yekha ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma amachita kuitanidwa ndi Mulungu, monga momwe adaaitanidwira Aroni.
Magazi a atonde ndi a ng'ombe zamphongo, ndiponso phulusa la mwanawang'ombe wamkazi zimawazidwa pa anthu amene ali odetsedwa chifukwa chosasamala mwambo wachiyuda. Zimenezi zimaŵayeretsa pakuŵachotsa litsiro lam'thupi.
Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo.
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.
Mfundo yeniyeni pa zimene tikunenazi ndi iyi: tili naye wotere Mkulu wa ansembe onse, amene akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu Waulemerero Kumwamba.
“Nachi tsono chipangano chimene ndidzachita ndi fuko la Israele atapita masiku ameneŵa,” akutero Ambuye: “Ndidzaika Malamulo anga m'maganizo ao ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Choncho Ine ndidzakhala Mulungu wao, iwowo adzakhala anthu anga.
Sipadzafunikanso kuti wina aliyense aphunzitse mnzake, kapena kuti wina aliyense auze mbale wake kuti, ‘Udziŵe Ambuye’. Pakuti onse adzandidziŵa, kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu.
Mwachifundo ndidzaŵakhululukira zochimwa zao, sindidzakumbukiranso machimo ao.”
Pakunena mau oti, “Chipangano chatsopano”. Mulungu akunena kuti chipangano choyamba nchotha ntchito. Paja chinthu chimene chayamba kutha ntchito nkumakalamba, ndiye kuti chili pafupi kuzimirira.
Iye akutumikira m'Malo Opatulika am'katikati, ndiye kuti m'chihema chenicheni chimene adachimanga ndi Ambuye osati munthu ai.
Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula.
Kufa kumene adafako kunali kufa kolekana ndi uchimo, ndipo adafa kamodzi kokhako. Tsono moyo umene ali nawo tsopano ndi moyo woperekedwa kwa Mulungu.
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Muziŵapatula ndi mau anu kuti akhale anthu anu. Mau anuwo ngoona zedi.
Monga mudandituma Ine pansi pano, Inenso ndaŵatuma pansi pano.
Ndipo chifukwa cha iwoŵa ndikudzipereka kwa Inu, kuti iwonso akhale odzipereka moonadi kwa Inu.”
Kenaka Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.”
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti aphere Yesu. Paja iwo ankaopa anthu.
Atatha kudya, adaŵapatsanso chikho, nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira.
Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika.
Nanji tsono munthu wonyoza Mwana wa Mulungu, munthu woyesa chinthu chachabe magazi achipangano amene adamuyeretsa, munthu wonyoza Mzimu wotipatsa madalitso a Mulungu! Chilango cha munthu wotere chidzakhala choopsa kopambana.
Aroni azidzachita mwambo wopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Ndi magazi a nyama zija za nsembe zopepesera machimo azidzayeretsera guwa limeneli kamodzi pa chaka. Zimenezi zizidzachitikanso m'mibadwo yanu yonse. Guwa limeneli lidzakhala loyera kwambiri, lopatulikira Chauta.”
Umu ndimo m'mene ng'ombe yamphongo aichitire. Monga adachitira ndi ng'ombe yamphongo yopereka pa nsembe yopepesera machimo, ndimo aichitirenso imeneyi. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimowu, mpingowo udzakhululukidwa.
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikulipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo.”
Kusiyana kokhudza lumbiroku kukutiwonetsa kuti Yesu ndi Nkhoswe yotsimikizira Chipangano choposa.
Pakunena mau oti, “Chipangano chatsopano”. Mulungu akunena kuti chipangano choyamba nchotha ntchito. Paja chinthu chimene chayamba kutha ntchito nkumakalamba, ndiye kuti chili pafupi kuzimirira.
Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai,
adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.
Paseri pa chochinga chachiŵiri panali chipinda chotchedwa “Malo Opatulika Kopambana”.
Chipindachi chinali ndi guwa lagolide lofukizirapo lubani. M'chipindamo munalinso bokosi lachipangano. Bokosi lonselo linali lokutidwa ndi golide. M'bokosimo munali kambiya kagolide m'mene munali mana uja, ndi ndodo ya Aroni, ija idaaphukayi. Munalinso miyala iŵiri ija yolembedwapo mau a chipangano.
Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.
Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira.
Zimenezi nzofanizira chabe, ndipo zimaloza ku nthaŵi ino. Potsata malongosoledwe ameneŵa mphatso ndi nsembe zimene munthu amapereka sizingathe konse kuusandutsa wangwiro mtima wa wopembedzayo.
Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu.