M’Baibulo muli nkhani zambiri zokhudza vinyo, ndipo limagwira ntchito yofunika kwambiri. Nthawi zambiri vinyo limatanthauza chikondwerero ndi chisangalalo, koma palinso mavuto ake. Vinyo lingatanthauze madalitso komanso mavuto, kutengera mmene likugwiritsidwira ntchito m’Baibulo.
Mu Chipangano Chakale, vinyo limasonyeza kuchuluka kwa madalitso ochokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, m’buku la Genesis, Nowa atabwera kuchokera m’Chigumula, anabzala mpesa napanga vinyo. Vinyo limeneli linasonyeza madalitso ndi zipatso za dziko zimene Mulungu anapatsa anthu.
Komabe, m’Malemba onse tikuchenjezedwa za kuipa kwa kumwa vinyo mopitirira muyeso. M’buku la Miyambo, tikuuzidwa kuti vinyo lingatikoke m’mayesero ndi kutitsogolera kuledzera ndi kusowa kwa nzeru. Tikuuzidwanso kuti tipewe kumwa mopitirira muyeso ndi kulamulira zochita zathu.
Mu Chipangano Chatsopano, Yesu anachita chozizwitsa chake choyamba pa ukwati ku Kana, pomwe anasandutsa madzi kukhala vinyo. Izi zikusonyeza mphamvu zake komanso chikhumbo chake chobweretsa chisangalalo ndi chimwemwe m’miyoyo yathu. Komabe, ndikofunikira kukumbukira kuti Yesu nthawi zonse anatilimbikitsa kukhala odekha komanso osaledzera. Choncho, tiyenera kuchita zinthu zonse moyenera ndi mwadongosolo.
Ndiye iwe usaope, uzidya chakudya chako mokondwa, uzimwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti Mulungu wavomereza kale zochita zakozo.
Adaŵamwetsa chambiko wochokera ku ng'ombe ndiponso mkaka wankhosa, adaŵadyetsa nkhosa ndi mbuzi zonenepa, ndiponso nkhosa zamphongo zabwino za ku Basani, pamodzi ndi tirigu wabwino ndi vinyo wokoma.
Nowa anali mlimi ndipo anali woyamba kulima munda wamphesa. Tsiku lina atangomwa vinyo, adaledzera, ndipo adavula zovala zake zonse, nakagona ali maliseche m'hema mwake.
Potsata nzeruzo ndidaayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewo unali uchitsiru. Ndinkati mwina kapena njira yotere nkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku oŵerengeka a moyo wao.
Ndipo Melkizedeki, mfumu ya ku Salemu, wansembe wa Mulungu Wopambanazonse, adabwera kwa Abramu atatenga buledi ndi vinyo.
Uleke kumangomwa madzi okha. Koma uzimwako vinyo pang'ono, paja umavutika ndi m'mimba, ndiponso chifukwa cha kudwaladwala kwako kuja.
Isaki adayankha Esauyo kuti, “Ndamudalitsa kale iyeyo kuti akhale mbuyako, ndipo abale ake onse ndaŵasandutsa atumiki ake. Ndampatsa chakudya ndi chomwera chake. Nanga tsopano chatsalanso nchiyani choti ndikuchitire iwe mwana wanga?”
Pamodzi ndi mwanawankhosa woyambayo, uzipereka kilogaramu limodzi la ufa wosalala watirigu wosakaniza ndi lita limodzi la mafuta abwino, ndiponso lita limodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.
“Usamwe vinyo kapena chakumwa china champhamvu, iwe ndi ana ako uli nawoŵa, pamene mukupita ku chihema chamsonkhano, kuwopa kuti mungafe. Limeneli likhale lamulo losatha pa mibadwo yanu yonse.
Chopereka cha chakudya yopereka pamodzi ndi nkhosayo ikhale makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, kuti ikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa yopereka pamodzi ndi nkhosayo, ikhale ya vinyo wokwanira ngati lita limodzi.
asamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa. Asamwe vinyo wopangidwa ndi mphesa kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo asamwe madzi amphesa kapena kudya mphesa zaziŵisi kapena zouma.
Ndalamazo mugulire zilizonse zimene mufuna, monga nyama yang'ombe, nyama yankhosa, vinyo ndiponso zakumwa zaukali, malinga nkukhosi kwanu. Tsono inuyo pamodzi ndi mabanja anu, mudzadye ndi kusangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu.
Anthuwo amagona pambali pa malo aliwonse opembedzerapo, pa zovala zimene adalandira kwa osauka ngati chikole. M'nyumba ya Mulungu amamweramo zakumwa za anthu amene adaŵalipitsa pa mlandu.
Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka. Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.
Tsoka kwa inu amene mumamwera vinyo m'zipanda zodzaza, inu amene mumadzola mafuta abwino kwambiri, koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa dziko la Yosefe.
Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.
“Ndidzaŵabwezeranso pabwino anthu anga Aisraele. Adzamanganso mizinda yamabwinja ndi kumakhalamo. Adzalima minda ya mphesa ndipo adzamwa vinyo wake. Adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
Anthu okhuta vinyo amanyodola anzao, omwa zaukali amautsa phokoso. Aliyense wosokera nazo zimenezi ndi wopanda nzeru.
Nkwabwino kusadya nyama, kusamwa vinyo, ndiponso kusachita kanthu kalikonse kamene kangachimwitse mbale wako.
Adzaperekenso vinyo wa chopereka cha chakumwa wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense, kuwonjezera pa nsembe yopsereza kapena pa nsembe yopembedzera.
Ndi amene amakhalitsa pamene pali vinyo, amene amamwa nawo vinyo wosanganiza ndi zina. Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akututuma m'chikho namakoma poloŵa ku m'mero. Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amanjenjedula ngati mphiri. Maso ako adzaona zinthu zachilendo, maganizo ndi mau ako adzakhala okhotakhota. Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja, kapena ngati munthu wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalaŵa. Iwe udzati, “Adanditchaya, koma sadandipweteke. Adandimenya, koma ine osamvako. Kodi ine ndidzatsitsimuka liti? Ndiye ndithamangira chakumwa china.”
Adzakukondani ndi kukudalitsani, kotero kuti mudzachuluka ndi kubereka ana ambiri. Minda yanu adzaidalitsa, kotero kuti tirigu, vinyo ndi mafuta, mudzakhala nazo zonsezo. Adzakudalitsaninso pa zoŵeta pokupatsani ng'ombe zambiri ndi zoŵeta zina zomwe. Madalitso onseŵa, adzakupatsani muli m'dziko limene adalonjeza makolo anu.
Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa.
Kumeneko adapatsa Yesu vinyo wosanganiza ndi ndulu kuti amwe. Koma atalaŵa, adakana kumwa.
“Nthaŵi imeneyo ikadzafika, mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndipo kuzitunda kudzayenderera mkaka. Mitsinje yonse ya ku Yuda idzadzaza ndi madzi. Kasupe adzatumphuka ku Nyumba ya Chauta ndi kuthirira chigwa cha Sitimu.
Kunena za aneneri, mtima wanga wasweka, m'nkhongono mwachita kuti zii! Ndakhala ngati munthu woledzera, munthu wosokonezeka ndi vinyo, chifukwa cha Chauta ndi mau ake oyera.
Chauta akunena kuti, “Inu nonse omva ludzu, bwerani, madzi ali pano. Ndipo inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule chakudya, kuti mudye. Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka, osalipira ndalama, osalipira chilichonse.
Atatha kudya, adaŵapatsanso chikho, nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira.
Apo Isaki adati, “Bwera nayo kuno nyama yako, kuti ndidye ndipo ndikudalitse.” Yakobe adabwera ndi nyamayo, Isaki nkudya. Yakobe adampatsanso vinyo woti amwe.
Anthuwo adzabwera akuimba mofuula pa mapiri a Ziyoni, adzakhala osangalala kwambiri chifukwa cha zabwino zochuluka zochokera kwa Chauta. Zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano, mafuta, anaankhosa ndi anaang'ombe. Moyo wao udzakhala ngati munda wothirira, ndipo sadzamvanso chisoni.
Koma inu mudakondwa ndi kusangalala, mudapha ng'ombe ndi nkhosa ndi kuzidya, ndiponso mudamwa vinyo. Mudati, “Tidye, timwe, poti maŵa tifa.”
Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, matumbawo amaphulika, vinyoyo natayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso. Apo zonse ziŵiri zimasungika bwino.”
Pa phiri ili la Ziyoni Chauta Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse phwando la zakudya zokoma ndi la vinyo wabwino, phwando la nyama yonona ndi la vinyo amene wafikapo.
Amene amakondetsa zosangalatsa, adzasanduka munthu wosauka. Amene amakondetsa vinyo ndi mafuta, sadzalemera.
Kunena zoona, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano pamodzi nanu mu Ufumu wa Atate anga.”
Kunena zoona, sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.”
Munalibe buledi woti muzidya, ngakhalenso vinyo kapena chakumwa chaukali, koma Chauta adakupatsani zonse zokusoŵani, kuti mudziŵe kuti Iye ndi Chauta, Mulungu wanu.
Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, vinyoyo amaphulitsa matumba aja, ndipo choncho vinyo uja amatayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso.”
“Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba aja. Choncho vinyoyo adzatayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso.
Mwana wa Munthu adabwera, nkumadya ndi kumwa ndithu, inu mumvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’
Ndithu ndikunenetsa kuti kuyambira tsopano sindidzamwanso konse chakumwa cha mtengo wamphesa, mpaka Mulungu atadzakhazikitsa ufumu wake.”
Patapita masiku aŵiri, kunali ukwati ku mudzi wa Kana m'dera la Galileya. Amai ake a Yesu anali komweko. namuuza kuti, “Anzanu amapereka vinyo wabwino kwambiri poyamba, kenaka anthu atakhuta, amaŵapatsa vinyo wokoma pang'ono. Koma inu mwasunga vinyo wabwino kwambiri kufikira tsopano.” Yesu adaonetsa chizindikiro chake choyambachi m'mudzi wa Kana m'dera la Galileya. Pamenepo adaonetsa ulemerero wake, ndipo ophunzira ake adamkhulupirira.
Simungathe kumwera m'chikho cha Ambuye nkumweranso m'chikho cha Satana. Simungathe kudyera pa tebulo la Ambuye nkudyeranso pa tebulo la Satana.
Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthaŵi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.”
Ndipo moyo wanu udzakhala wodzaza ndi zipatso za chilungamo zimene mudzaonetsa mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti anthu onse alemekeze ndi kutamanda Mulungu.
Chimodzimodzinso azimai achikulire, uŵauze kuti azikhala ndi makhalidwe oyenera azimai oyera mtima. Asakhale osinjirira anzao kapena akapolo a zoledzeretsa. Akhale alangizi abwino,
Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo.
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
M'manja mwa Chauta mulitu chikho cha vinyo wofanizira chilango chake, vinyo wotutuma ndi wothirako dzoŵaŵa. Adzatsanyula vinyoyo, ndipo oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa, nadzagugudiza mpaka ndungundungu zake.
Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona. Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta, mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.
Pomaliza Ambuye adachita ngati kudzuka kutulo, ngati munthu wamphamvu wofuula chifukwa choledzera. Tsono Mulungu adaŵapirikitsa adani ake, naŵachititsa manyazi anthaŵizonse.
Inu mwalola anthu anu kuti aone mavuto aakulu. Mwatipatsa vinyo wachilango kuti timwe, ndipo tikudzandira naye.
Munthu amene ali pafupi kufa, uzimpatsa chakumwa chaukali, ndipo munthu amene ali pa mavuto oopsa, uzimpatsa vinyo. Amwe kuti aiŵale umphaŵi wake asakumbukirenso kuvutika kwake.
Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona.
Tsono ndidaika mbiya zodzaza ndi vinyo ndi zikho zomwera pamaso pa Arekabuwo, ndipo ndidaŵauza kuti, “Nayu vinyo, imwani.” Koma iwowo adati, “Ife sitimwa vinyoyu, poti kholo lathu Yonadabu mwana wa Rekabu adatilamula kuti, ‘Musadzamwe vinyo, inuyo ndi ana anu omwe.
Anthu a ku Damasiko ankagula kwa iwe chifukwa cha kuchuluka kwa zamalonda zako ndi katundu wako wosiyanasiyana. Ankakugulitsa vinyo wa ku Heliboni ndi ubweya wa nkhosa wambee.
Dzukani inu zidakwa, ndipo mulire. Mulire modandaula inu nonse okonda vinyo: mphesa zotchezera vinyo watsopano zaonongedwa,
Munthu wina atamapita uku ndi uku akulalika zabodza kuti, ‘Ndithudi mudzakhala ndi vinyo ndi zakumwa zamphamvu zambiri,’ mlaliki wotere ndi amene anthu aŵa angamkonde.
Pamenepo Aefuremu adzakhala ngati ankhondo amphamvu, adzasangalala ngati anthu okhuta vinyo. Ana ao adzaziwona zimenezi, nawonso nkusangalala, mumtima mwao mudzadzaza chimwemwe, chifukwa cha zimene Chauta wachita.
Mwana wa Munthu adabwera nkumadya ndi kumwa ndithu, anthu amvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’ Komabe chilungamo cha nzeru za Mulungu chimatsimikizika ndi zochita zake.”
Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adaŵauza kuti, “Imwani nonsenu.
popeza kuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Sazidzamwa konse vinyo kapena choledzeretsa china chilichonse. Adzakhala wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ngakhale asanabadwe nkomwe.
Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino.
Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana.
Inu mumati mukamadya, aliyense angoyambapo kudya chakudya chakechake, kotero kuti wina amakhala ndi njala, m'menemo wina waledzera. Zokuwonerani zimenezi! Kodi mulibe nyumba zomakadyeramo ndi kumweramo? Kodi kapena mufuna kunyazitsa Mpingo wa Mulungu ndi kuŵachititsa manyazi amene alibe kanthu, eti? Ndikuuzeni chiyani tsono? Ndingakuyamikeni ngati? Iyai, pa zimenezi sindingakuyamikeni konse.
Nanga chikho chimene timachidalitsa mothokoza Mulungu, kodi suja timaphatikizana ndi magazi a Khristu tikamweramo? Nanga mkate umene timaunyema, kodi suja timaphatikizana ndi thupi la Khristu tikaudya?
Chikondi cha Khristu ndicho chimatiwongolera mokakamiza, popeza kuti tikudziŵa mosakayika konse kuti Munthu mmodzi adafera anthu onse, ndiye kuti pamenepo onse adafa.
Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lao lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake.
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera. Anthu ogona tulo, amagona usiku, anthu oledzera amaledzera usiku. Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.
Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zao, iwoŵa adadzizoloŵeza kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.
Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu. Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye.
Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa.
nadzalangidwa molingana ndi kuipa kwao. Chimene chimaŵakomera nkumangochita zokondweretsa thupi nthaŵi yamasana. Ali ngati mathotho ndi maŵanga onyansa, chifukwa podya nanu pamodzi amakondwera kuchita zonyenga.
Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Kukondwa ndi kusangalala kwalekeka ku minda yadzinthu. Nyimbo sizikuimbidwa, palibenso kufuula m'minda yamphesa. Palibe wopsinya vinyo mopondera mphesa, kufuula kwachimwemwe kwa nthaŵi yotchera mphesa kwalekeka.
Iyeyo sadyera nao ku zitunda zachipembedzo. Sapembedza mafano a ku Israele. Saipitsa mkazi wa munthu wina. Sakhudza mkazi pamene ali wosamba.
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene mlimi adzabzola wokolola, ndipo woponda mphesa adzabzola wobzala mbeu. M'mapiri mudzatuluka vinyo wokoma, azidzachita kuyenderera pa zitunda zonse.
Mudzabzala, koma simudzakolola, Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzaŵadzola. Mudzaponda mphesa, koma vinyo wake simudzamulaŵa.
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, azikhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, azikhala kapolo wa onse.
Yesu adauzanso Mfarisi uja amene adaamuitana kudzadya naye kuti, “Ukamakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamaitana abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anzako achuma, chifukwa mwina iwonso adzakuitanako, motero udzalandiriratu mphotho yako. Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu. Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.”
namuuza kuti, “Anzanu amapereka vinyo wabwino kwambiri poyamba, kenaka anthu atakhuta, amaŵapatsa vinyo wokoma pang'ono. Koma inu mwasunga vinyo wabwino kwambiri kufikira tsopano.”
Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.
Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama.
Musalole zophunzitsa zosiyanasiyana ndiponso zachilendo kuti zikusokeretseni. Choyenera kutilimbitsa mtima ndi kukoma mtima kwa Mulungu, osati malamulo onena za chakudya ai. Malamulo ameneŵa sadaŵapindulitsepo anthu amene ankaŵatsata.
Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.
mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga.
Munthu woyenda mwaungwiro, amayenda mosatekeseka. Koma woyenda njira zoipa, adzadziŵika.
Phwando ndi lokondwetsa anthu, ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo. Komatu zonsezo nzolira ndalama.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.