Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


93 Mau a Mulungu Okhudza Yesu Mneneri

93 Mau a Mulungu Okhudza Yesu Mneneri

Ndikufuna tikambirane za Yesu, mneneri wofunika kwambiri m'mbiri ya Baibulo. Iye anali wolankhula wa Mulungu, ndipo zimenezi zimamupanga munthu wofunika kwambiri pa uzimu wathu.

Chinthu chimodzi chodabwitsa chomwe Yesu anachita monga mneneri chinali kutanthauzira Malemba. Anali ndi mphamvu ya Mulungu yofotokozera tanthauzo lenileni la mawu a Mulungu ndi kutithandiza kumvetsa ubale wathu ndi Mulungu.

Nkhani zake ndi maulaliki ake zimasonyeza kuti ankadziwa bwino chifuniro cha Mulungu ndi chikondi chake chopanda malire kwa ife. Tangoganizani zimenezo!

Yesu analosera zinthu zimene zidzachitike m'tsogolo. Analankhula za zinthu zimene zidzachitike atatha kupita, ndipo anatiuza za mavuto amene tingakumane nawo m'dziko lino.

Zozizwitsa zimene anachita, monga kuchiritsa odwala, kuukitsa akufa, ndi kuchulukitsa chakudya, zimasonyeza kuti anatumidwa ndi Mulungu. Izi zinatsimikizira kuti iye anali mneneri wa Mulungu.

Yesu sanachite mantha kudzudzula chinyengo m'chipembedzo. Analankhula molimba mtima kwa atsogoleri achipembedzo, kuwavumbulira zolakwa zawo, ndi kuwalimbikitsa kukhala ndi moyo woyera ndikutumikira Mulungu.

Mau ake amphamvu anakhudza mitima ya anthu amene anali ofunitsitsa kumvera. Uthenga wake wa chikondi, chilungamo, ndi chipulumutso wafika mpaka pano lero. Ndi uthenga umene ungatisinthe ife tonse.




Mateyu 21:11

Tsono onse aja adayankha kuti, “Ameneyu ndi mneneri Yesu wochokera ku Nazarete, ku Galileya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:18-19

Ndidzaŵatumizira mneneri wonga iwe, wochokera mwa iwo amene. Ndidzamuuza zoti anene, ndipo iyeyo azidzauza anthu zonse zimene ndikumlamula. Mneneriyo akalankhula m'dzina langa, Ine ndidzalanga aliyense wosamvera mau angawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:22

Paja Mose adati, ‘Ambuye Mulungu adzasankhula mmodzi pakati pa abale anu, kuti akhale Mneneri wanu monga ine. Mudzamvere zonse zimene Iye adzakuuzeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:15

Iye adzakutumizirani mneneri wonga ine wochokera mwa inu amene, ndipo mudzayenera kumumvera iyeyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:37

Mose yemweyo ndiye amene adauza Aisraele kuti, ‘Mulungu adzatuma wina kuchokera mwa abale anu kuti akhale Mneneri wanu monga ine.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:57

Choncho adakhumudwa naye. Koma Yesu adaŵauza kuti, “Mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao ndiponso kubanja kwao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:16

Anthu onse adachita mantha, nayamba kutamanda Mulungu. Adati, “Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu.” Adatinso, “Mulungu wadzathandiza anthu ake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:19

Maiyo adati, “Bambo, ndadziŵa tsopano kuti ndinu mneneri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:46

motero adafuna kumugwira. Koma ankaopa anthu, popeza kuti ochuluka ankakhulupirira kuti Yesu ndi mneneri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:14

Pamene anthu aja adaona chizindikiro chozizwitsa chimene Yesu adachitacho, adati, “Zoonadi ameneyu ndi Mneneri uja amene ankanena kuti adzabwera pansi panoyu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 7:40

Pamene khamu la anthu lidamva mau ameneŵa, ena mwa iwo ankati, “Zoonadi munthuyu ndiye Mneneri uja.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 6:4

Koma Yesu adaŵauza kuti, “Mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao, pakati pa achibale ake, ndiponso kubanja kwao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:37

“Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri, nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:5

Akulankhula choncho, kudadza mtambo woŵala nuŵaphimba. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 9:17

Tsono Afarisi aja adamufunsanso munthu uja kale sankapenyayu, adati, “Kodi iweyo ukuti chiyani za Iyeyo, m'mene wakuchiritsamu?” Iye adati, “Ndi mneneritu basi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:21

Adamufunsanso kuti, “Nanga ndiwe yani? Ndiwe Eliya kodi?” Iye adati, “Iyai, sindine Eliya.” Iwo adati, “Kodi ndiwe Mneneri tikumuyembekeza uja?” Koma Yohane adayankha kuti, “Ainso.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:19

Yesu adaŵafunsa kuti, “Zotani?” Iwo adati, “Za Yesu wa ku Nazarete. Iye anali mneneri amene mau ake ndi zochita zake zinali zamphamvu pamaso pa Mulungu ndi pa anthu omwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:49

Pajatu sindidalankhule zochokera mwa Ine ndekha, koma Atate amene adandituma ndiwo adandilamula zoti ndinene, ndi momwe ndilankhulire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:22-23

Paja Mose adati, ‘Ambuye Mulungu adzasankhula mmodzi pakati pa abale anu, kuti akhale Mneneri wanu monga ine. Mudzamvere zonse zimene Iye adzakuuzeni. Aliyense amene sadzamvera Mneneriyo, amchotseretu mwa Aisraele ndi kumuwononga.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 6:15

Koma ena ankati, “Iyai, ameneyu ndi Eliya.” Enanso ankati, “Iyai, koma ndi mneneri wonga aneneri akale aja.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 8:28

Iwo adayankha kuti, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu mmodzi mwa aneneri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:14

Iwo adati, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu Yeremiya kapena mmodzi mwa aneneri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:39

Koma Mfarisi amene adaaitana Yesu uja ataona zimenezi, adayamba kuganiza kuti, “Munthuyu akadakhaladi mneneri, bwenzi atamdziŵa mai amene akumkhudzayu, kuti ndi wachiwerewere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 1:1-2

Kale lija pa nthaŵi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Adatinso, “Inu Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lapansi pachiyambi pomwe, zakumwambaku ndi ntchito ya manja anu. Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu achikhalire. Zonsezi zidzafwifwa ngati chovala. Mudzazipindapinda ngati mwinjiro, ndipo zidzasinthika ngati chovala, koma Inu ndinu osasinthika, zaka zanu sizidzatha konse.” Nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.” Nanga angelo, kodi suja iwo ndi mizimu yotumikira chabe, imene Mulungu amaituma chifukwa cha anthu odzalandira chipulumutso? Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati choloŵa chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:2

Koma Yesu adaŵauza kuti, “Nanga simukuziwona zonsezi? Ndithu ndikunenetsa kuti sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:24

Adaŵauzanso kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti palibe mneneri amene amalandiridwa bwino kumudzi kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 13:33

Komabe ndiyenera kupitirira ndi ulendo wanga lero ndi maŵa ndi mkucha, pakuti mneneri sangafere kwina koma ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 14:65

Ena adayamba kumthira malovu, namuphimba m'maso nkumamuwomba makofi, namanena kuti, “Lotatu, wakumenya ndani?” Alonda aja nawonso adayamba kummenya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:17

“Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:45

Filipo adakapeza Natanaele namuuza kuti, “Tampeza Ujayu amene Mose adalemba za Iye m'buku la Malamulo, uja anenerinso adalemba za Iye. Ndi Yesu Mwana wa Yosefe, wa ku Nazarete.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:15

“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:21-22

Koma tsopano yaoneka njira yopezera chilungamo pamaso pa Mulungu, ndipo njira yake si kutsata Malamulo ai. Malamulowo ndi aneneri omwe amaichitira umboni. Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:9

Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri amene.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:37

“Aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Ndipo wondilandira Ine bwino, ndiye kuti akulandira bwino osati Ineyo, koma Atate amene adandituma.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:19-20

Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:25

Mvetsetsani, Ine ndiye ndakuuziranitu zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 26:22-23

Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero. Motero ndaimirira pano kuti ndichite umboni pamaso pa anthu onse, aakulu ndi ang'ono omwe. Zimene ndikuŵauza si zina ai, koma ndi zomwezo zimene aneneri ndi Mose adanena kuti zidzachitika. Paja iwo adati Mpulumutsi wolonjezedwa uja adzamva zoŵaŵa, ndipo popeza kuti Iye adzakhala woyamba kuuka kwa akufa, adzalengeza Ayuda ndi amene sali Ayuda za kuŵala kwa chipulumutso.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:49-50

Pajatu sindidalankhule zochokera mwa Ine ndekha, koma Atate amene adandituma ndiwo adandilamula zoti ndinene, ndi momwe ndilankhulire. “Kodi bwanji mafuta ameneŵa sadaŵagulitse ndalama mazana atatu kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?” Ndipo ndikudziŵa kuti zimene amandilamula nzolinga ku moyo wosatha. Nchifukwa chake zimene ndimalankhula, ndimalankhula monga momwe Atate amandiwuzira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:21

Paja mau a aneneri sadadze konse ndi kufuna kwa munthu yekha, koma Mzimu Woyera adaŵalankhulitsa mau ochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:29

chifukwa ankaŵaphunzitsa monga munthu waulamuliro osati monga m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:18-19

“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa, ndi kukalalika za nthaŵi imene Ambuye adzapulumutsa anthu ao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1-2

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:3

Tsono Yesu atakhala pansi, pa Phiri la Olivi, ophunzira ake adadza kwa Iye paokha. Adamufunsa kuti, “Tatiwuzani, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti nthaŵi yakwana ya kubweranso kwanu, ndiponso ya kutha kwa dziko lapansi?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:11

Kudzaoneka aneneri onama ambiri, amene azidzasokeza anthu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:28

Tsono Yesu adaŵauza kuti, “Mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Ndilipo. Mudzadziŵanso kuti sindichita kanthu pandekha, ndimalankhula zimene Atate adandiphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:41

Pa tsiku la chiweruzo anthu a ku Ninive adzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzaŵatsutsa. Paja iwowo adaatembenuka mtima, atamva malaliko a Yona. Ndipotu pano pali woposa Yona amene.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:41-44

Yesu atayandikira, nkuwona Yerusalemu, adalira chifukwa cha mzindawo. Adati, “Ha, iwenso ukadangodziŵa lero lino zinthu zopatsa mtendere! Koma ai, tsopano maso ako sangathe kuziwona. Nthaŵi idzakufikira pamene adani ako adzakuzinga ndi machemba, nadzakuzungulira, nkukutsekereza ponseponse. Adzakusakaziratu iweyo pamodzi ndi anthu ako onse. Sadzasiya mwa iwe mwala pamwamba pa unzake, chifukwa chakuti sudazindikire nthaŵi imene Mulungu adaati adzakupulumutse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:15

Sindikutchulaninso antchito ai, pakuti wantchito sadziŵa zimene mbuye wake akuchita. Koma ndikukutchulani abwenzi, chifukwa zonse zimene ndidamva kwa Atate anga, ndidakudziŵitsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:64

Yesu adamuyankha kuti, “Mwanena nokha. Komanso ndikukuuzani kuti kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:29-30

Pamene anthu ankachulukirachulukira, Yesu adati, “Anthu a mbadwo uno ngoipa, amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzachiwona chizindikirocho, kupatula cha mneneri Yona chija. Mutipatse ife tsiku lililonse chakudya chathu chamasikuwonse. Monga Yona uja anali chizindikiro kwa anthu a ku Ninive, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mbadwo uno.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:41

Munthu wolandira nthumwi ya Mulungu chifukwa choti ndi nthumwi, adzalandira mphotho ya nthumwi ya Mulungu. Wolandira munthu wolungama chifukwa choti ngwolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:46

Mukadakhulupirira Mose moona, bwenzi mutakhulupiriranso Ine, pakuti iye adaalemba za Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:37-39

“Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri, nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana! Ndithu nyumba yanu yaikuluyi idzasanduka bwinja. Ndipo ndikunenetsa kuti simudzandiwonanso konse mpaka mudzati, ‘Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:23-24

Apo Yesu adaŵauza kuti, “Ndithudi mudzandiwuza mwambi uja wakuti, ‘Iwe sing'anga, dzichiritse wekha.’ Mudzatinso, ‘Tidamva zimene mudachita ku Kapernao, tsono muchitenso zomwezo kwanu kuno.’ ” Adaŵauzanso kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti palibe mneneri amene amalandiridwa bwino kumudzi kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:2

adadza kwa Yesu usiku. Adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe munthu wotha kuchita zizindikiro zozizwitsa zimene Inu mukuzichita, ngati Mulungu sali naye.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:16

Yesu adauza anthu 72 aja kuti, “Wokumverani inu, akumvera Ine amene. Wokukanani inu akukana Ine amene. Ndipo wondikana Ine, akukananso Atate amene adandituma.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:44-50

Yesu adanena mokweza mau kuti, “Munthu wondikhulupirira, sakhulupirira Ine ndekha ai, koma amakhulupiriranso Iye amene adandituma. Ndipo munthu woona Ine, amaonanso Iye amene adandituma. Ine ndine kuŵala, ndipo ndidadza pansi pano, kuti munthu aliyense wokhulupirira Ine, asamayende mu mdima. Munthu akamva mau anga koma osaŵagwiritsa ntchito, Ine sindimzenga mlandu ai. Pakuti sindidadzere kudzazenga anthu mlandu, koma kudzaŵapulumutsa. Munthu amene akana Ine, ndipo salandira mau anga, alipo amene adzamuweruze. Adzazengedwa mlandu pa tsiku lomaliza chifukwa cha mau omwe ndakhala ndikulankhulaŵa. Pajatu sindidalankhule zochokera mwa Ine ndekha, koma Atate amene adandituma ndiwo adandilamula zoti ndinene, ndi momwe ndilankhulire. “Kodi bwanji mafuta ameneŵa sadaŵagulitse ndalama mazana atatu kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?” Ndipo ndikudziŵa kuti zimene amandilamula nzolinga ku moyo wosatha. Nchifukwa chake zimene ndimalankhula, ndimalankhula monga momwe Atate amandiwuzira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:40

Monga Yona uja anali m'mimba mwa chinsomba chija masiku atatu, usana ndi usiku, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala m'kati mwa nthaka masiku atatu, usana ndi usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 7:16

Yesu adati, “Zimene ndimaphunzitsa si zangatu ai, ndi za Atate amene adandituma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:10

Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:20-23

Yesu adayang'ana ophunzira ake, naŵauza kuti, “Ndinu odala, inu osaukanu, Ufumu wa Mulungu ndi wanu. “Ndinu odala, inu amene mukumva njala tsopano, chifukwa mudzakhuta. “Ndinu odala, inu amene mukulira tsopano, chifukwa mudzakondwa. “Ndinu odala anthu akamadana nanu, akamakusalani ndi kukuchitani chipongwe, ndipo akamaipitsa dzina lanu chifukwa cha Ine Mwana wa Munthu. Nthaŵi imeneyo sangalalani ndi kuvina ndi chimwemwe, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi zomwenso makolo ao ankaŵachita aneneri kale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:57-58

Choncho adakhumudwa naye. Koma Yesu adaŵauza kuti, “Mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao ndiponso kubanja kwao.” Motero sadachite zamphamvu zambiri kumeneko, chifukwa cha kusakhulupirira kwa anthuwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:21

Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kudziŵitsa ophunzira ake kuti, “Ndiyenera kupita ku Yerusalemu, kumeneko akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzandizunza kwambiri. Ndidzaphedwa koma mkucha wake ndidzauka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:12

Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 8:31

Yesu adayamba kuphunzitsa ophunzira ake kuti, “Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda, ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma patapita masiku atatu adzauka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:27

Kenaka Yesu adayamba kuŵatanthauzira zimene zidalembedwa za Iye m'Malembo onse, kuyambira pa mabuku a Mose mpaka mabuku a aneneri onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:16-21

Nthaŵi ina Yesu adafika ku Nazarete kumene adaaleredwa. Ndipo pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapemphero, monga adaazoloŵera, naimirira kuti aŵerenge mau. Adampatsa buku la mneneri Yesaya. Tsono Iye adafutukula bukulo, napeza pamene padalembedwa kuti, “Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa, ndi kukalalika za nthaŵi imene Ambuye adzapulumutsa anthu ao.” masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala. Yesu adatseka bukulo nkulipereka kwa mtumiki wa nyumba yamapemphero, nakhala pansi. Anthu onse amene adaasonkhana m'nyumbamo ankangomupenyetsetsa. Tsono Yesu adaŵauza kuti, “Lero zachitikadi zimene adaaneneratu Malembo amene mwamvaŵa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 7:28-29

Pamene Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, adalankhula mokweza mau kuti, “Ine mukundidziŵa, ndipo kumene ndidachokera mukudziŵakonso. Koma sindidabwere mwa kufuna kwanga ai. Atate amene ali wokhulupirika ndiwo adandituma. Inu simukuŵadziŵa. Koma Ine ndikuŵadziŵa, chifukwa ndine wochokera kwa Iwo, ndipo ndiwo adandituma.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:4

Tsono Yesu adamuuza kuti, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyi ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 13:23

Koma inu chenjerani. Ine ndiye ndakuuziranitu zonse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:10

Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzafunafuna ndi kudzapulumutsa amene adatayika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:40

“Munthu wokulandirani inu, amandilandira Ine ndemwe. Ndipo wondilandira Ine, amalandiranso Iye uja amene adandituma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 18:37

Pilato adati, “Tsono ndiye kuti ndiwedi mfumu, ati?” Yesu adati, “Mwanena nokha kuti ndine mfumu. Ine ndidabwera pansi pano ndipo ndidabadwa kuti ndidzachitire umboni choona. Aliyense wokonda choona amamva mau anga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:36

“Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa; amadziŵa ndi Atate okha basi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:13

Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:23-24

Yesu adaŵauza kuti, “Inu ndinu ochokera pansi pano, Ine ndine wochokera Kumwamba. Inu ndinu a dziko lino lapansi, Ine sindine wa dziko lino lapansi ai. Nchifukwa chake ndakuuzani kuti mudzafera m'machimo anu. Pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine Ndilipo, mudzaferadi m'machimo anu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:6

Ndipotu ndikunenetsa kuti pali wina pano woposa Nyumba ya Mulunguyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:30

Ine ndi Atate ndife amodzi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:14-15

Ndipo ngati mukufunadi kukhulupirira zimenezi, Yohaneyo ndiye Eliya uja ankati adzabwerayu. Amene ali ndi makutu, amve!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:6

Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:3

Moyo wosathawo ndi wakuti akudziŵeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziŵenso Yesu Khristu amene mudamtuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:46-49

“Bwanji mumangoti, ‘Ambuye, Ambuye,’ koma chonsecho simuchita zimene ndimanena? Munthu aliyense wodza kwa ine, namva mau anga nkumaŵagwiritsa ntchito, ndikuuzani amene amafanafana naye. Amafanafana ndi munthu womanga nyumba, amene adaakumba mozama, naika maziko pa thanthwe. Tsono chigumula chitafika, madzi ake adagunda nyumbayo, koma sadaigwedeze, chifukwa adaaimanga bwino. Koma munthu wongomva mau anga, osaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu amene adaamanga nyumba pamwamba pa nthaka, osakumba maziko. Pamene madzi a chigumula adagunda nyumbayo, pompo idagwa, ndipo kuwonongeka kwake kunali kotheratu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:17-18

“Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:9

Khomo ndine. Munthu akaloŵera pa Ine, adzapulumuka. Azidzaloŵa ndi kutuluka, ndipo adzapeza chakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:64

Adammanga nsalu m'maso nkumamufunsa kuti, “Lota, wakumenya ndani?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:18

Chikhalire palibe munthu amene adaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekha uja, amene ali wapamtima wa Atate, ndiye adaulula za Mulunguyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:24

Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:19

Ndikukuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire kuti Ine ndinedi Ndilipo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 14:62

Yesu adayankha kuti, “Inde, ndinedi. Ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:25

Yesu adati, “Ndidakuuzani kale, komabe simukhulupirira. Ntchito zimene ndimachita m'dzina la Atate anga, ndizo zimandichitira umboni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:24

“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:31

Pambuyo pake Yesu adaŵauza kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya usiku uno. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa za msambiwo zidzangoti balala.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:50-51

Motero anthu amakono adzakhala ndi mlandu chifukwa cha aneneri onse amene adaphedwa chilengedwere dziko lapansi, kuyambira kuphedwa kwa Abele, mpaka kuphedwa kwa Zakariya amene adaphedwera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa la nsembe ndi malo opatulika kopambana. Ndithu ndikunenetsa kuti anthu amakono adzakhaladi ndi mlandu chifukwa cha ophedwawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, ndikukutamandani ndi mtima wonse, ulemerero wonse ukhale kwa inu. Muli Woyera katatu, kuzunguliridwa ndi ulemerero ndi chiyero. Mukukhala mu nthawi yosatha, kasupe wosatha wa moyo, Mpulumutsi wanga ndi wochirikiza wanga. Ndinu zonse zimene ndikufuna. Pamaso panu ndipo ndifuna kukhala nthawi zonse, pakuti palibe chabwino kuposa kukhala nanu. Zikomo Ambuye chifukwa ndinu mtsogoleri wanga, mawu anu amaunikira moyo wanga, ndipo ndazindikira kuti simunalakwitsepo kalibino. Ndinu choonadi, maganizo anu onse ndi olungama, njira zanu ndi zoyera. Mwawona tsogolo langa, mukudziwa zam'mbuyomu, ndipo mukuwongolera zamakono. Ndikukhulupirirani Ambuye, ndikupumula mu malonjezano anu. Sindidzataya mtima ngakhale sindinawone zomwe mwandionjeza, chifukwa ndikudziwa kuti simuli mwana wa munthu kuti muname, simundilola kuti ndichotsedwe manyazi. Ndinu Mfumu ya mafumu, Ambuye wa ambuye. Ulemerero, ulemu ndi mphamvu zikhale zanu, nthawi zonse. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa