Kodi ndani amene angakukonde ngati Yesu? Ndani angakukonde mmene iye anakukondera? Pamene onse anakutasiya, iye anakukumbatira. Pamene anakunenera zoipa ndipo anakutsutsa, chisomo chake chinakufikira.
Kuchokera kumwamba, anakupenya utatayika ndipo anasankha kutenga malo ako. Sikuti unamukonda poyamba, koma asanakudziwe, anakukonda kale. N’chifukwa chake anasankha kufera pamtanda, kusiya mpando wachifumu wake ndi ulemerero wake, kukhetsa mwazi wake pamtanda kuti akutsuke ku uchimo wako ndi kukulola kukhala woyera.
Iye anatenga chilango cha mtendere wako, ndipo ndi mabala ake wachiritsidwa ku matenda ako onse. Sanalemedwe ndi nsembe yake chifukwa cha iwe. Pa chikwapulo chilichonse, anatchula dzina lako chifukwa chakuti amakukonda ndipo chifuniro chake ndi chakuti ukhale ndi moyo wabwino mwa iye, kusangalala ndi madalitso amene anakupatsa mwa kufera pamtanda chifukwa cha iwe.
Choncho, usanyoze chikondi chake chachikulu. Mukonde ndi mtima wako wonse ndipo ukhale moyo wako wonse kuti umusangalatse. Usachoke pafupi naye, khalani pa ubwenzi ndi Mzimu Woyera. Chifukwa lero uli ndi ufulu womulambira: chomwe chinkakulekanitsa naye sichilinso, chifukwa waomboledwa ndi mwazi wake.
Pumira kuti ulemekeze dzina lake ndipo umutumikire ndi moyo wako wonse. Yesu amatikonda ndipo chifukwa cha chikondi anapereka moyo wake kuti atipatse moyo wosatha pamodzi naye. Kupyolera mu nsembe yake, tingapulumuke ku machimo athu. Monga mmene lemba la Aheberi 9:28 limatiuza, Khristu anaperekedwa nsembe kamodzi kokha kuti achotse machimo a anthu ambiri; ndipo adzabweranso kachiwiri, osati kunyamula machimo, koma kudzapulumutsa onse amene akumuyembekezera.
Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera. Nanga pamenepo ifenso timakhaliranji m'zoopsa nthaŵi zonse? Abale anga, imfa ndimayenda nayo tsiku ndi tsiku. Ndikunenetsa zimenezi chifukwa ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu. Nanga pamene ndidalimbana ndi zilombo ku Efeso, ndidapindulapo chiyani, ngati ndinkatsata maganizo a anthu chabe? Ndiyetu ngati akufa sauka, tizingochita monga amanenera kuti, “Tiyeni tizidya ndi kumwa, pakuti maŵa tikufa.” Musadzinyenge. “Paja kuyanjana ndi anthu ochimwa kumaononga khalidwe.” Mudzidzimuke mumtima mwanu, ndipo muleke kuchimwa. Ena mwa inu sadziŵa Mulungu konse. Ndikukuuzani zimenezi kuti muchite manyazi. Koma kapena wina nkufunsa kuti, “Kodi akufa adzauka bwanji? Kodi adzakhala ndi thupi lotani?” Ati kupusa ati! Mbeu imene umafesa, siingamere ndi kukhala moyo itapanda kufa. Ndipo chimene ufesa, si mmera umene udzatuluka ai, koma ndi njere chabe, kaya ndi ya tirigu, kapena ya mtundu wina uliwonse. Koma Mulungu amaisandutsa mmera monga momwe Iye akufunira, mbeu iliyonse mmera wakutiwakuti. Mnofu sukhala wa mtundu umodzi. Pali mnofu wina wa anthu, wina wa nyama, wina wa mbalame, ndi wina wa nsomba. Adaikidwa m'manda, mkucha wake adauka, monga Malembo anenera.
Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi.
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.
Ndidamva angelowo akuimba mokweza mau kuti, “Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko.”
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Pakuti moyo wake wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi, ndipo ndaŵapereka kwa inu kuti muzichitira mwambo wopepesera machimo a moyo wanu pa guwa. Pajatu magazi ndiwo amene amachotsa machimo, chifukwa cha moyo umene umakhala m'magazimo.
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Adamuvula zovala zake, namuveka chovala chofiira. Adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake, ndipo adamgwiritsa ndodo m'dzanja lake lamanja. Kenaka adayamba kumgwadira, namaseŵera naye mwachipongwe nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.”
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Adanenanso kuti, “Abba, Atate, mungathe kuchita chilichonse. Mundichotsere chikho cha masautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti, “Atate ndikupereka mzimu wanga m'manja mwanu.” Atanena zimenezi, adatsirizika.
“Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe, ndipo akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamkwapula, nkumupachika pa mtanda; koma mkucha wake Iye adzauka kwa akufa.”
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa. Tonse tidaasokera ngati nkhosa. Aliyense mwa ife ankangodziyendera. Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu.
Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha.
Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Pa nthaŵi imene Mulungu adaikonzeratu, pamene ife tikusoŵabe pogwira, Khristu adatifera anthu ochimwafe.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo.
Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.
Chifukwa chakuti Yesu Khristu adachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako.
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi.
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Komabe ndi Chauta yemwe amene adaafuna kuti amuzunze, ndipo adamsautsadi. Iye adapereka moyo wake kuti ukhale nsembe yokhululukira machimo. Choncho adzaona zidzukulu zake, adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Chauta chidzachitika mwa iye. Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula.
Komatu tikuwona kuti Yesu, amene pa kanthaŵi pang'ono adaasanduka wochepera kwa angelo, adalandira mphotho ya ulemerero ndi ulemu chifukwa adamva zoŵaŵa za imfa. Zidatero chifukwa mwa kukoma mtima kwake Mulungu adaafuna kuti afere anthu onse.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera.
Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu. Iyeyo adadzipereka kuti akhale momboli wa anthu onse. Umenewu unali umboni umene udaperekedwa pa nthaŵi yake.
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake.
Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.
Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu.
Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Ankaimbira Mwanawankhosa uja nyimbo yatsopano iyi yakuti: “Ndinu oyenera kulandira bukuli ndi kumatula zimatiro zake. Pakuti mudaaphedwa, ndipo ndi imfa yanu mudaombolera Mulungu anthu a fuko lililonse, a chilankhulo chilichonse, ndi a mtundu uliwonse.
Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Yesu ameneyu sali ngati akulu a ansembe ena aja. Palibe chifukwa chakuti tsiku ndi tsiku azipereka nsembe poyamba chifukwa cha machimo ake, kenaka chifukwa cha machimo a anthu. Zimenezi adachitiratu kamodzi kokha, pakudzipereka yekha ngati nsembe.
Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.
Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake.
“Ndithudi, iye adapirira masautso amene tikadayenera kuŵamva ifeyo, ndipo adalandira zoŵaŵa zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumlanga, ndi kumkantha ndi kumsautsa.
Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu.
Inu kale munali akufa chifukwa cha machimo anu, ndiponso chifukwa munali osaumbalidwa mu mtima. Koma tsopano Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu zonse. Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.
Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”
Malinga ndi Malamulo a Mosewo pafupifupi zonse zimayeretsedwa ndi magazi, ndipo machimo sakhululukidwa popanda kukhetsa magazi.
Yesu atalandira vinyo wosasayo adati, “Zonse ndakwaniritsa.” Kenaka adaŵeramitsa mutu, napereka mzimu.
“Anthu adamsautsa ndi kumzunza, koma iye sadalankhule kanthu. Monga momwe amachitira mwanawankhosa wopita naye kuti akamuphe, ndiponso monga momwe nkhosa imakhalira duu poimeta, nayenso adangokhala chete.
Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.
Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera.
Nchifukwa chake pamene Khristu adadza pansi pano, adati, “Inu Mulungu simudafune nsembe kapena zopereka, koma thupi mudandikonzera. Nsembe zoocha kwathunthu ndi nsembe zoperekera machimo, simudakondwere nazo. Tsono ine ndidati, ‘Inu Mulungu, ndabweratu kuti ndichite zimene mukufuna, paja zidalembedwa choncho ponena za Ine m'buku la Malamulo.’ ”
Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikulipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo.”