Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

108 Mauthenga a Baibulo Okhudza Imfa ya Yesu

Imfa ya Yesu inali yowawa kwambiri komanso yochititsa manyazi. Koma pakati pa kuzunzika kwakeko, zinthu zodabwitsa zinachitika zomwe zinasonyeza kuti Yesu sanali munthu wamba ayi. Mwachitsanzo, mawu ake akuti: “Atate, awakhululukireni, pakuti sadziwa chimene achita.” (Luka 23:34)

Yesu Khristu anamwalira pa mtanda atazunzidwa kwambiri. Chilango chimene analandira m’malo mwathu chinali champhamvu kwambiri, chinam’vulaza kwambiri ndipo chinam’taya magazi ambiri, magazi amenewo omwe anandigula ine ndi kundiombola ku uchimo.

Malinga ndi Mauthenga Abwino, Yesu anamwalira patapita maola ochepa atapachikidwa pa mtanda, ngakhale kuti atsimikizire kuti wafadi, msilikali anamubaya mkondo m’mbali mwake. Poona zimenezi, ndikofunikira kukumbukira izi ndi kuyesetsa kukhala moyo wolungama pamaso pa Mulungu, poyamikira nsembe ya Yesu, yemwe anandipulumutsa ine ndi kundimasula ku chilango chosatha chimene ndinayenera kulandira.

Tiyeni tilambire dzina lake ndi kuyamikira chikondi chake chosatha.


Yohane 19:30

Yesu atalandira vinyo wosasayo adati, “Zonse ndakwaniritsa.” Kenaka adaŵeramitsa mutu, napereka mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 23:21

Koma iwo adafuulirafuulira kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 5:15

Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adaŵafera, nauka kwa akufa chifukwa cha iwowo.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 5:30

Mulungu wa makolo athu adaukitsa Yesu kwa akufa, Iye amene inu mudaamupha pakumpachika pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 26:2

“Pajatu chikondwerero cha Paska chiyambika patangopita masiku aŵiri, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kuti akapachikidwe pa mtanda.”

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 14:8

Iyeyu wachita zimene akadatha kuchita. Wadzozeratu thupi langa ndi mafuta onunkhira, kuti alikonzeretu lisanaikidwe m'manda.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:10

Kufa kumene adafako kunali kufa kolekana ndi uchimo, ndipo adafa kamodzi kokhako. Tsono moyo umene ali nawo tsopano ndi moyo woperekedwa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 27:50

Koma Yesu adafuulanso kwakukulu, napereka mzimu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 19:33

Koma pamene adafika pa Yesu, poona kuti wafa kale, sadathyole miyendo yake.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 8:31

Yesu adayamba kuphunzitsa ophunzira ake kuti, “Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda, ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma patapita masiku atatu adzauka.”

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 4:10

Nthaŵi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu m'thupi mwathu, kuti moyo wake uwonekenso m'thupi mwathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 26:28

Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 27:46

Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 11:51

(Kwenikwenitu sadanene zimenezi ndi nzeru za iye yekha ai. Koma popeza kuti anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho, ankalosa kuti Yesu adzafera mtundu wa Ayuda.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 15:43

Yosefe wa ku Arimatea adafika. Adaali mkulu wodziŵika ndithu, wa m'Bwalo Lalikulu la Ayuda. Nayenso ankayembekeza Ufumu wa Mulungu. Tsono iye adalimba mtima, napita kwa Pilato kukapempha kuti ampatsire mtembo wa Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 15:39

Mkulu wa asilikali amene adaaimirira pomwepo kuyang'anana naye, ataona kuti Yesu watsirizika akufuula chotero, adati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 27:51

Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 1:20

Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 27:54

Mkulu wa asilikali ndiponso amene anali naye polonda Yesu, ataona chivomezi chija ndi zina zonse zimene zidaachitika, adachita mantha kwambiri nati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 20:18-19

“Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe,

ndipo akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamkwapula, nkumupachika pa mtanda; koma mkucha wake Iye adzauka kwa akufa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 17:22-23

Tsiku lina ophunzira atasonkhana onse ku Galileya, Yesu adaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu.

Iwo adzamupha, koma mkucha wake Iye adzauka.” Ophunzirawo atamva zimenezi, adagwidwa ndi chisoni chachikulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 15:37

Koma Yesu adafuula kwakukulu, natsirizika.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 14:24

Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 22:19-20

Kenaka Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.”

Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti aphere Yesu. Paja iwo ankaopa anthu.

Atatha kudya, adaŵapatsanso chikho, nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 23:46

Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti, “Atate ndikupereka mzimu wanga m'manja mwanu.” Atanena zimenezi, adatsirizika.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 24:7

Paja adaakuuzani kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja mwa anthu ochimwa, kupachikidwa pa mtanda, ndi kuuka kwa akufa patapita masiku atatu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 23:34

Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 22:37

Ndithu ndikunenetsa kuti ziyenera kuchitikadi mwa Ine zimene Malembo adanena kuti, ‘Ankamuyesa mmodzi mwa anthu ophwanya malamulo.’ Ndipo zonse zimene zidalembedwa za Ine zikuchitikadi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 1:29

M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 10:11

“Ine ndine mbusa wabwino. Mbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 10:15

monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 12:32-33

Ndipo Ine, akadzandipachika, ndidzakokera anthu onse kwa Ine.”

(Adaanena mau ameneŵa kuti aŵadziŵitse za m'mene analikudzafera.)

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 19:34

Koma mmodzi mwa asilikali aja adamubaya m'nthiti mwake ndi mkondo, ndipo nthaŵi yomweyo mudatuluka magazi ndi madzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 2:23

Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m'mene Iye amadziŵiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 2:24

Koma Mulungu adammasula ku zoŵaŵa za imfa, namuukitsa kwa akufa, chifukwa kunali kosatheka kuti agonjetsedwe ndi imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 2:36

“Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 4:10

Mudziŵetu tsono inu nonse, ndi Aisraele ena onse, kuti munthuyu akuima wamoyo pamaso panu chifukwa cha mphamvu ya dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete. Amene uja inu mudaampachika pa mtanda, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:8

Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:6

Tidziŵa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:9

Paja Khristu adamwalira nakhalanso ndi moyo, kuti akhale Mbuye wa anthu akufa ndiponso wa anthu amoyo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 15:3

Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 5:21

Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 2:20

Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:14

Koma ine sindinganyadire kanthu kena kalikonse, koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu basi. Popeza kuti Iye adafa pa mtanda, tsopano zapansipano kwa ine zili ngati zakufa, ndipo inenso kwa zapansipano, ndili ngati wopachikidwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 1:7

Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 2:14

Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:24

Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 3:18

Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 2:2

Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 1:5

Akukomereninso mtima ndi kukupatsani mtendere Yesu Khristu, mboni yokhulupirika, amene ali woyambirira kulandira moyo waulemerero, amenenso ali Mfumu yolamula mafumu onse a pa dziko lapansi. Iyeyo amatikonda, ndipo ndi magazi ake adatimasula ku machimo athu.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 5:9

Ankaimbira Mwanawankhosa uja nyimbo yatsopano iyi yakuti: “Ndinu oyenera kulandira bukuli ndi kumatula zimatiro zake. Pakuti mudaaphedwa, ndipo ndi imfa yanu mudaombolera Mulungu anthu a fuko lililonse, a chilankhulo chilichonse, ndi a mtundu uliwonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 7:14

Ine ndidati, “Mbuyanga, mukudziŵa ndinu.” Ndipo iye adandiwuza kuti, “Ameneŵa ndi amene adapambana m'masautso aakulu aja. Adachapa mikanjo yao ndi kuiyeretsa m'magazi a Mwanawankhosa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 28:5-6

Koma mngeloyo adalankhula ndi azimai aja naŵauza kuti, “Inu musaope ai. Ndikudziŵa kuti mukufuna Yesu, uja adaampachika pa mtandayu.

Sali muno ai, wauka monga muja adaaneneramu. Bwerani, dzaoneni pamene adaagona.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 26:39

Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa choŵeramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 14:36

Adanenanso kuti, “Abba, Atate, mungathe kuchita chilichonse. Mundichotsere chikho cha masautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 22:42

Adati, “Atate, ngati mukufuna, mundichotsere chikho chamasautsochi. Komabe muchite zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 3:14-15

“Monga momwe Mose adaapachikira njoka pa mtengo m'chipululu muja, momwemonso Mwana wa Munthu ayenera kudzapachikidwa,

kuti aliyense wokhulupirira akhale ndi moyo wosatha mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 6:51

Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikulipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 12:24

Kunena zoona, mbeu ya tirigu imakhalabe imodzi yomweyo ngati siigwa m'nthaka nkufa. Koma ikafa, imabala zipatso zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 19:25-27

Pafupi ndi mtanda wa Yesu padaaimirira amai ake, ndi mbale wa amai akewo, Maria mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa ku Magadala.

Pamene Yesu adaona amai ake ndi wophunzira uja amene Iye ankamukonda kwambiri, akuimirira pafupi, adauza amai ake kuti, “Mai, nayu mwana wanu.”

Adauzanso wophunzirayo kuti, “Naŵa amai ako.” Ndipo kuyambira pamenepo wophunzirayo adaŵatenga amaiwo kumakaŵasamala kwao.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 27:29

Adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake, ndipo adamgwiritsa ndodo m'dzanja lake lamanja. Kenaka adayamba kumgwadira, namaseŵera naye mwachipongwe nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 27:35

Atampachika pa mtanda, adagaŵana zovala zake pakuchita maere.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 15:25

Pamene adampachika pa mtanda, nkuti nthaŵi ili 9 koloko m'maŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 23:32-33

Asilikali aja adaatenganso anthu ena aŵiri, amene anali zigaŵenga, kuti akaphedwe pamodzi ndi Yesu.

Pamene adafika ku malo otchedwa Chibade cha Mutu, adapachika Yesu komweko pa mtanda. Komwekonso adapachika zigaŵenga zija, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 23:39-43

Chigaŵenga chimodzi chimene chidaapachikidwa nao, chidayamba kunyoza Yesu nkumanena kuti, “Ha! Kodi iwe sindiwe Mpulumutsi Wolonjezedwa uja? Udzipulumutse wekha ndi ife tomwe.”

Pamenepo Pilato adauza akulu a ansembe ndi anthu onse aja kuti, “Sindikumpeza mlandu munthuyu.”

Koma mnzake uja adamdzudzula, adati, “Kodi iwe, suwopa ndi Mulungu yemwe, chidziŵirecho kuti nawenso ukulandira chilango chomwechi?

Tsonotu ife zikutiyeneradi zimenezi, tikulandira zolingana ndi zimene tidachita. Koma aŵa sadachite cholakwa chilichonse.”

Ndipo adati, “Inu, mukandikumbikire mukakafika mu Ufumu wanu.”

Yesu adamuyankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 19:23-24

Asilikali aja atapachika Yesu, adatenga zovala zake, nazigaŵa panai, msilikali aliyense chigawo chake. Adatenganso mkanjo wake. Mkanjowo unali wolukidwa kuyambira pamwamba mpaka pansi, opanda msoko.

Tsono asilikaliwo adauzana kuti, “Tisaung'ambe, koma tichite mayere kuti tiwone ukhala wa yani.” Zidaayenda choncho kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Adagaŵana zovala zanga, ndipo mkanjo wanga adauchitira mayere.” Zimenezi adachitadi asilikali aja.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 26:65-66

Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake nati, “Kunyoza Mulungu koopsatu kumeneku! Kodi pamenepa nkufunanso mboni zina ngati? Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku.

Ndiye inu mukuganiza bwanji?” Iwo aja adayankha kuti, “Ayenera kuphedwa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 27:1-2

M'maŵa kutacha, akulu onse a ansembe ndi akulu a Ayuda adapanga upo kuti aphe Yesu.

nagulira munda wa mmisiri wa mbiya, monga momwe Ambuye adaandilamulira.”

Tsono Yesu adaimirira pamaso pa bwanamkubwa. Iyeyo adamufunsa kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adati, “Mwanena nokha.”

Koma pamene akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda aja ankamuneneza, Yesu sadayankhepo kanthu.

Apo Pilato adamufunsa kuti, “Kodi sukumva zonse akukunenezazi?”

Koma Yesu sadamuyankhe kanthu, kotero kuti bwanamkubwa uja adadabwa kwambiri.

Pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska, bwanamkubwa ankaŵamasulira anthu mkaidi mmodzi, yemwe iwo ankafuna.

Pa nthaŵi imeneyo panali mkaidi wina wodziŵika, dzina lake Barabasi.

Tsono anthu atasonkhana, Pilato adaŵafunsa kuti, “Mukufuna kuti ndikumasulireni uti, Barabasi kapena Yesu, wotchedwa Khristu?”

Adaatero chifukwa adaadziŵa kuti Yesuyo anthuwo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe.

Pilato ali pa mpando woweruzira milandu, mkazi wake adamtumizira mau. Adati, “Musaloŵerepo pa nkhani ya munthu wolungamayo. Inetu maloto andivuta kwambiri usiku chifukwa cha Iyeyo.”

Adammanga, napita naye kwa Pilato, bwanamkubwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 15:1

M'maŵa kutangocha, akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi aphunzitsi a Malamulo, pamodzi ndi ena onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda adapanga upo. Adammanga Yesu napita naye kwa Pilato.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 22:54

Anthu aja adamugwira Yesu, napita naye ku nyumba ya mkulu wa ansembe onse. Petro ankaŵatsatira chapatali.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 23:4

Pamenepo Pilato adauza akulu a ansembe ndi anthu onse aja kuti, “Sindikumpeza mlandu munthuyu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 23:13-16

Pilato adasonkhanitsa akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi anthu wamba.

Adaŵauza kuti, “Mwadzampereka munthuyu kwa ine kuti ndi munthu wosokeza anthu. Ndipo onani, ine ndamufunsa pamaso panu, koma sindikumpeza mlandu pa zonse zimene mukumnenezazi.

Herode yemwe sadampeze mlandu, nchifukwa chake wamubweza kwa ife. Ameneyu sadachite kanthu koyenera kumuphera.

Motero ndingomukwapula kenaka nkumumasula.” [

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 19:12

Atamva mau ameneŵa, Pilato adafuna ndithu kummasula Yesu. Koma Ayuda adafuula kuti, “Mukammasula ameneyu, sindinu bwenzi la Mfumu ya ku Roma. Aliyense wodziyesa mfumu, ngwoukira Mfumu ya ku Romayo.”

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 3:15

Mudapha Wopatsa moyo, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 10:39

Ife ndife mboni za zonse zimene Iye adachita mu Yerusalemu ndi m'dziko lonse la Ayuda. Iwo adamupha pakumpachika pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 3:25

Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:32

Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 1:18

Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 2:2

Koma ndidaatsimikiza kuti pamene ndili pakati panu, ndiiŵale zina zonse, kupatula Yesu Khristu yekha, koma tsono amene adapachikidwa pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 1:4

Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 2:16

Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:8

Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:3

Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:10

Iwo adatifera kuti tikakhale ndi moyo pamodzi naye, ngakhale pamene tili amoyo kapena titafa kale.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 2:9

Komatu tikuwona kuti Yesu, amene pa kanthaŵi pang'ono adaasanduka wochepera kwa angelo, adalandira mphotho ya ulemerero ndi ulemu chifukwa adamva zoŵaŵa za imfa. Zidatero chifukwa mwa kukoma mtima kwake Mulungu adaafuna kuti afere anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 9:26

Zikadatero, akadayenera kumamva zoŵaŵa kaŵirikaŵiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma monga zilirimu, waoneka kamodzi kokha pakutha pake pa nthaŵi yotsiriza, kuti achotse uchimo pakudzipereka yekha nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 9:28

Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:10

Chifukwa chakuti Yesu Khristu adachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:18-19

Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai,

adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:21

Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:1

Tsono popeza kuti Khristu adamva zoŵaŵa m'thupi mwake, valani dzilimbe ndi maganizo omwewo, chifukwa munthu amene wamva zoŵaŵa m'thupi mwake, ndiye kuti walekana nawo machimo.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 12:11

Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:40

Monga Yona uja anali m'mimba mwa chinsomba chija masiku atatu, usana ndi usiku, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala m'kati mwa nthaka masiku atatu, usana ndi usiku.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 9:22

Adati, “Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma mkucha wake adzauka kwa akufa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 7:30

Pamenepo anthu adafuna kumgwira Yesu, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene adamkhudza, chifukwa nthaŵi yake inali isanafike.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 8:59

Pamenepo Ayuda aja adayamba kutola miyala kuti amlase. Koma Yesu adazemba natuluka m'Nyumba ya Mulunguyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 11:49-53

Koma mmodzi mwa iwo, dzina lake Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho, adaŵauza kuti, “Inu simudziŵa kanthu konse ai.

Ndiye kuti Yesu ankakonda Marita ndi mng'ono wake Maria ndiponso Lazaro.

Monga inu simukuwona kuti nkwabwino koposa kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu onse, m'malo moti mtundu wathu wonse uwonongeke?”

(Kwenikwenitu sadanene zimenezi ndi nzeru za iye yekha ai. Koma popeza kuti anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho, ankalosa kuti Yesu adzafera mtundu wa Ayuda.

Tsono osati kungofera fuko chabe, komanso kusonkhanitsa pamodzi ana a Mulungu amene adabalalika.)

Kuyambira tsiku limenelo akulu aja a Ayuda adayamba kupangana zoti amuphe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 18:4-6

Yesu adaadziŵiratu zonse zimene zinalikudzamugwera. Nchifukwa chake Iye adaima poyera, naŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna yani?”

Pamenepo iwo adafuulanso kuti, “Ameneyu ai, koma Barabasi.” (Barabasiyo anali chigaŵenga.)

Adamuyankha kuti, “Tikufuna Yesu wa ku Nazarete.” Yesu adati, “Ndine, ndilipo.” Yudasi, wompereka kwa adani ake uja, anali nao pomwepo.

Pamene Yesu adaŵayankha kuti, “Ndine, ndilipo,” iwo adabwerera m'mbuyo nagwa pansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 19:11

Yesu adati, “Akadapanda kukupatsani mphamvu zimenezo Mulungu, sibwenzi mutakhala nazo konse mphamvu pa Ine. Nchifukwa chake amene wandipereka kwa inu ali ndi tchimo lalikulu koposa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 1:3

Iye ataphedwa, adadziwonetsa wamoyo kwa iwo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adaŵaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 2:30

Paja iye anali mneneri, ndipo ankadziŵa zimene Mulungu adamlonjeza molumbira zakuti mmodzi mwa zidzukulu zake ndiye adzaloŵe ufumu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:12

Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 15:21-22

Pakuti monga imfa idadza pansi pano kudzera mwa munthu wina, momwemonso kuuka kwa akufa kudadza kudzera mwa munthu wina.

Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 3:13

Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.”

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:2

Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 9:22

Malinga ndi Malamulo a Mosewo pafupifupi zonse zimayeretsedwa ndi magazi, ndipo machimo sakhululukidwa popanda kukhetsa magazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 21:4

Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse! Ndikubwera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu, Inu nokha ndinu woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa kwapamwamba. Atate Woyera, zikomo chifukwa cha imfa yanu pa mtanda chifukwa cha ine, chifukwa kudzera mu nsembe yanu ndili ndi moyo wosatha pamodzi ndi Inu. Ambuye, ngakhale munali wopanda tchimo, munathira magazi anu chifukwa cha machimo anga onse ndipo munandiyeretsa ku zoipa zonse, munagonjetsa imfa ndipo pa tsiku lachitatu munauka kwa akufa, ndipo tsopano muli ndi moyo ndipo mukulamulira. Ambuye, ndikupemphani kuti mutsegule mtima wanga ndikulola uthenga wa mtanda kulowa mozama mwa ine kotero kuti pamoyo wanga pakhale kubadwanso kwatsopano, chikhulupiriro chatsopano ndi chiyembekezo. Ambuye Yesu, zikomo chifukwa cha imfa yanu pa mtanda ndi chikhululukiro, moyo wosatha ndi kukwaniritsidwa kwa malonjezo onse a Mulungu pa moyo wanga ndi anthu onse. Pakuti monga momwe Mulungu anakukwezerani kwa akufa, momwemonso ndidzakwezedwa ndi Mphamvu yanu. M'dzina la Yesu. Ameni.