Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

106 Mau a Mulungu Okhudza Kumvera

Kumvera Mulungu kuyenera kuchokera mumtima mwanga ngati kuyankha chikondi Chake ndi zonse zomwe wandichitira ndi zomwe akundichitira. Sikuti ndingongotsatira kapena kuvomereza mopanda chikhumbo chimene Iye akufuna, chifukwa nthawi zina sindimvetse chifukwa chake wandilamula kuchita kapena kusiya chinthu china. Komabe, ndimaonetsa chikhulupiriro changa ndi kudalira Mulungu mwa kumvera ngakhale sindikumvetsa zifukwa Zake.

Mwa kumvera malamulo a Mulungu, ndikudzikonzekeretsa moyo wosatha ndi kukwezedwa. Ndikukumbukira kuti ndine mtumiki wa amene ndikumvera, kaya ndi uchimo kapena Mulungu ndi Mawu Ake, ndipo ndimakhala mtumiki wa chilungamo.

Pomaliza, zilibe kanthu kuchuluka kwa ntchito zomwe ndimachita kapena utumiki womwe ndimapereka, khalidwe langa lofunika kwambiri pamaso pa Mulungu liyenera kukhala kumvera, chifukwa kwa Ambuye wanga, kumvera n’kofunika kwambiri kuposa nsembe zambiri (1 Samueli 15:22).


Yohane 14:23

Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:21-22

Inu okondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa, titha kuima mopanda mantha pamaso pa Mulungu.

Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 5:32

Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera Iye.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:15

“Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 11:1

Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndipo nthaŵi zonse muzimvera malamulo ndi malangizo ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:14

Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:22

Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:1

Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 7:23

Koma chimene ndidaalamula nchimodzi, ndidati, ‘Mukamandimvera, ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata malamulo anga onse kuti zinthu zikukomereni!’

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 15:22

Koma Samuele adati, “Kodi Chauta amakondwa ndi chiti: nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kapena kumvera mau ake? Ndithu, ndi kumvera ndi kupereka nsembe kwabwino kwambiri nkumvera. Ndi kutchera khutu ndi kupereka mafuta ankhosa kwabwino kwambiri nkutchera khutu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 128:1

Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 23:22

Koma mukamvera iyeyo ndi kuchita zonse zimene ndinena, Ineyo ndidzadana ndi adani anu, ndipo onse amene atsutsana nanu ndidzalimbana nawo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 1:8

Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 5:33

Muziyenda m'njira imene Chauta, Mulungu wanu, wakulamulani, kuti zinthu zidzakuyendereni bwino, ndipo mudzapitirire kukhala ndi moyo m'dziko limene mukakhalemolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 6:3

Inu Aisraele, mutchere khutu, ndipo muchenjere, mumveredi malamuloŵa. Tsono zinthu zidzakuyenderani bwino, ndipo mudzakhala mtundu wochuluka zedi ndi kumakhala m'dziko lamwanaalirenji, monga momwe Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakulonjezerani.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:13

Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 19:5

Tsono mukamandimvera ndi kusunga chipangano changa, mudzakhala anthu anga pakati pa makamu onse, pakuti dziko lonse lapansi ndi langa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:21

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 10:12-13

Tsono inu Aisraele, tamvani zimene Chauta, Mulungu wanu, akukuuzani. Akufuna kuti muzimuwopa ndi kuchita zonse zimene amakulamulani. Muzikonda Chauta, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,

ndipo muzimvera malamulo ndi malangizo onse a Chauta amene ndikukulamulani lero lino, kuti zinthu zikukomereni.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 11:26-28

Lero ndikukupatsani zinthu ziŵiri kuti musankhepo, madalitso kapena matemberero.

Madalitso kwa inu, mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndikukupatsani leroŵa.

Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 13:4

Mutsate Chauta, Mulungu wanu, ndi kuwopa Iye yekha. Mutsate malamulo ake ndi kumvera mau ake. Mutumikire Iye ndi kuphathana naye.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:1-2

Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi.

Tsono anthu onse a pa dziko lonse lapansi adzaona kuti Chauta, Mulungu wanu, wakusankhani inu kuti mukhale anthu akeake, ndipo azidzakuwopani.

Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani.

Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense.

Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika.

Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira.

Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa:

Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu.

Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu.

Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe.

Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse.

Mverani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalandira madalitso onse aŵa:

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 30:16

Mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mukamamkonda Chauta, Mulungu wanu ndi kutsata mau ake onse, pamenepo mudzakhala pabwino ndipo mudzakhala mtundu wa anthu ochuluka. Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko mukukakhalamolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 1:7-8

Komatu ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti usunge malamulo onse amene Mose mtumiki wanga adakupatsa. Usatayepo ndi kagawo kamodzi komwe, ndipo kulikonse kumene udzapite, udzapambana.

Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 5:6

Aisraele adakhala akuyenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka adafa amuna onse amene potuluka ku Ejipito anali a msinkhu woyenera pa nkhondo. Adatha nkufa, popeza kuti sadamvere Chauta. Iye adaachita kuŵalumbirira kuti sadzaloŵamo m'dziko lamwanaalirenji lija limene adaalonjeza kwa makolo ao kuti adzaŵapatsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 22:5

Musamale bwino kuti mumvere ndithu malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Mulungu adakupatsani. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, muzichita zimene Iyeyo akufuna, muzimvera malamulo ake, muzikhala okhulupirika kwa Iye, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi mzimu wanu wonse.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 12:14-15

Mukamaopa Chauta ndi kumamtumikira ndi kumamvera mau ake, osakana malamulo ake, ndiponso ngati nonsenu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Chauta, Mulungu wanu, zonse zidzakuyenderani bwino.

Koma mukapanda kumvera mau a Chauta nkumakana malamulo ake, ndiye kuti Iye adzakulangani inu ndi mfumu yanu yomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 15:24

Pamenepo Saulo adauza Samuele kuti, “Ndachimwa, ndalakwira lamulo la Chauta ndiponso malangizo anu, chifukwa chakuti ndinkaopa anthu ndipo ndinkamvera mau ao.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 2:3

Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 3:14

Ndipo ukamadzandimvera ndi kumasunga malamulo anga, monga momwe ankachitira bambo wako Davide, udzakhala ndi moyo wautali kwabasi.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 8:61

Nchifukwa chake inu Aisraele, mitima yanu ikhale yodzipereka kwathunthu kwa Mulungu wathu, ndipo mumvere bwino mau ake, ndi kutsata malamulo ake monga lero lino.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 11:38

Ukamamvera zonse zimene ndikukulamula, ndi kumayenda m'njira zanga, ndi kumachita zimene Ine ndifuna, posunga malamulo anga monga m'mene ankachitira Davide, mtumiki wanga, ndiye kuti Ine ndidzakhala nawe. Ndipo zidzukulu zako zidzalamulira monga m'mene ndidalonjezera Davide. Chigawo cha Israele ndidzachipereka kwa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 18:6

Iyeyo ankakangamira kwa Chauta. Sadaleke kutsata Chauta, koma ankasunga malamulo amene Iye adapatsa Mose.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 28:8

“Tsono pamaso pa Aisraele onse ndiponso pamaso pa msonkhano umenewu, Mulungu wathu alikumva, ndikukuuzitsani kuti muzisunga ndi kusamala malamulo onse a Chauta Mulungu wanu, kuti mukhalitse m'dziko labwinoli, ndipo lidzakhale nthaŵi zonse choloŵa cha ana anu, inu mutapita.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 7:14

ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 31:21

Ntchito iliyonse imene ankachita potumikira ku Nyumba ya Chauta potsata malangizo ndi malamulo, ndi pofunafuna Mulungu wake, ankachita zimenezo ndi mtima wake wonse ndipo ankapeza mwai.

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 1:5

Ndidati, “Inu Chauta, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, mumasunga chipangano. Mumaonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu amene amakukondani ndi kutsata malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 10:29

tikuphatikana ndi abale athu olemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata Malamulo a Mulungu amene adaŵapereka Mose mtumiki wa Mulungu. Tidzamvera ndi kuchitadi zimene Malamulo a Chauta, Mulungu wathu, amanena. Tidzamveranso malangizo ndi miyambo yake yolamulidwa. Ndipo titembereredwe tikalephera kuchita zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 1:1-2

Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu,

koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:2

Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:60

Ndimafulumira, sindizengereza kutsata malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:112

Mtima wanga muuphunzitse kuti uzikonda malamulo anu nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:1-2

Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga.

Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo.

Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake.

Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.

Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,

pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe.

Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo.

Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu.

Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha.

Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika.

Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino.

Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:8

Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:17

Wosamala malangizo amayenda pa njira ya moyo, koma wokana chidzudzulo amasokera.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 13:13

Wonyoza malangizo amadziwononga, koma wosamala lamulo amalandira mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:16

Munthu womvera malamulo amadzisungira moyo, koma munthu wonyoza malangizo a Mulungu adzafa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:20

Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo, kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:19

Ngati muli okonzeka kundimvera, mudzalidyera dziko.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 48:18

Ukadamvera malamulo anga, bwenzi mtendere ukukufikira ngati madzi amumtsinje, ndipo bwenzi chilungamo chikukuphimba kosalekeza ngati mafunde apanyanja.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 50:10

Ndani mwa inu amaopa Chauta, ndi kumvera mau a mtumiki wake? Aliyense woyenda mu mdima, wopanda chomuunikira, akhulupirire dzina la Chauta, ndipo adalire Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 11:4

chimene ndidachita ndi makolo anu, nditaŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Nditaŵachotsa m'ng'anjo ya moto ija, ndidati, ‘Mukamandimvera ndi kumachita zimene ndikuuzani, inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 26:13

Ngati tsopano mukonza makhalidwe anu ndi ntchito zanu zomwe, ndi kuyamba kumvera mau a Chauta Mulungu wanu, ndiye kuti Iye adzakhululuka osakulangani monga m'mene adaaganizira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 38:20

Yeremiya adayankha kuti, “Iyai, sadzakuperekani. Ngati mumvera Chauta pa zonse, ndikukuuzani kuti zinthu zonse zidzakuyenderani bwino, ndipo mudzakhala ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 36:27

Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 6:6

Kunena zoona Ine ndimafuna chikondi chosasinthika, osati nsembe chabe. Ndifuna kuti anthu andidziŵe Ine Mulungu m'malo mwa kumangopereka nsembe zopsereza.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 6:8

Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 3:7

“Zimene akunena Chauta Wamphamvuzonse ndi izi, akuti, ‘Mukamayenda m'njira yanga, ndi kumamveradi malamulo anga, mudzalamulira m'nyumba mwanga, ndipo mudzayang'anira mabwalo anga. Tsono ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi aŵa ali panoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 19:17

Yesu adamuyankha kuti, “Bwanji ukundifunsa za chimene chili chabwino? Wabwino ndi Mmodzi yekha. Ngati ufuna kukaloŵa ku moyo, uzimvera Malamulo.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 28:20

Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 6:46

“Bwanji mumangoti, ‘Ambuye, Ambuye,’ koma chonsecho simuchita zimene ndimanena?

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 8:51

Ndithu ndikunenetsa kuti munthu akamvera mau anga, sadzafa konse.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:21

“Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 15:10

Ngati mutsata malamulo anga, mudzakhala m'chikondi changa, monga momwe Ine ndatsatira malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala m'chikondi chao.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 5:29

Koma Petro ndi atumwi enawo adati, “Tiyenera kumvera Mulungu koposa kumvera anthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:5

Mwa Khristuyo ife tidalandira mwai wokhala atumwi, kuti tithandize anthu a mitundu yonse kumkhulupirira ndi kumumvera, kuti choncho dzina lake lilemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 2:13

Pakuti amene ali olungama pamaso pa Mulungu si amene amangomva Malamulo chabe ai. Koma okhawo amene amachitadi zonenedwa m'Malamulo ndiwo amene Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:19

Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:16-18

Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.

Tiyamike Mulungu! Inu kale munali akapolo a uchimo, koma tsopano mukumvera ndi mtima wonse zoona za chiphunzitso chimene mudalandira.

Mudamasulidwa ku uchimo, ndipo tsopano mwasanduka atumiki a Mulungu ochita zachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:1-2

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka.

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.

Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.

Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai.

Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira.

Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.

Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino.

Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere.

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 2:9

Pamene ndinkakulemberani kalata ija, cholinga changa chinali chakuti ndikuyeseni, ndi kuwona ngati mudzandimvera pa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 10:5

ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:7

Munkathamanga bwino lomwe. Tsono adakuletsani ndani kuti musamverenso choona?

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:12-13

Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera.

Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:20

Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 4:1-2

Potsiriza tsono, abale, tifuna tikupempheni kanthu. Mudalandira kwa ife mau onena za m'mene muziyendera kuti mukondweretse Mulungu. Mukutsata mayendedwe otere kumene, koma tikukupemphani kolimba m'dzina la Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale.

Ndipo mumakondana nawodi abale onse a m'dziko lonse la Masedoniya. Koma tikukupemphani abale, kuti muchite zimenezi koposa kale.

Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja,

kuti akunja azikulemekezani, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.

Abale, tifuna kuti mudziŵeko za anthu amene adamwalira, kuti chisoni chanu chisakhale ngati cha anthu ena amene alibe chiyembekezo.

Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.

Tsopano tikuuzeni mau a Ambuye mwini. Ife amoyofe, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sikuti tidzaŵasiya kumbuyo amene adamwalira aja ai.

Padzakhala mfuu wa mau a mngelo wamkulu ndi wa lipenga la Mulungu. Ndipo pamenepo Ambuye mwini adzatsika kuchokera Kumwamba. Anthu amene adafa akukhulupirira Khristu, adzayamba ndiwo kuuka.

Pambuyo pake ife amoyofe, otsalafe, tidzatengedwa pamodzi nawo m'mitambo kuti tikakumane ndi Ambuye mu mlengalenga. Motero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse.

Nchifukwa chake tsono muzithuzitsana mtima pokambirana zimenezi.

Pakuti mukudziŵa malangizo amene tidakupatsani ochokera kwa Ambuye Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:18

Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 1:8

Adzabwera ndi moto woyaka, nadzalanga anthu amene sadziŵa Mulungu, ndi amene sadamvere Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:14

Ndikukulamula kuti, mopanda cholakwa kapena chokayikitsa, utsate bwino zonse zimene udalamulidwa, mpaka Ambuye athu Yesu Khristu adzabwerenso.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:15

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 3:1

Uziŵakumbutsa anthu onse kuti azigonjera akulu oweruza ndi olamulira. Aziŵamvera ndipo azikhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 5:9

Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye,

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:36

Pafunikadi kupirira, kuti muchite zimene Mulungu akufuna, kuti motero mukalandire zimene adalonjeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:17

Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:25

Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:7

Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:14

Muzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene munkalakalaka pamene munali osadziŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:22

Mwayeretsa mitima yanu pakumvera choona, kotero kuti muzikondana ndi akhristu anzanu mosanyenga. Nchifukwa chake muzikondana ndi mtima wonse, mosafookera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:13

Chifukwa cha Ambuye, muzimvera akulu onse olandira ulamuliro. Ngati ndi mfumu yaikulu koposa ija, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro pa mafumu ena onse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:17

Nthaŵi ndiye yafika yoti Mulungu ayambe kuweruza anthu ake. Tsono ngati chiweruzocho chiyambira pa ife, nanga podzafika pa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, ndiye kuti chidzakhala chotani?

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 2:3-5

Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziŵa.

Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona.

Koma munthu akamasunga mau a Mulungu, pamenepo chikondi cha Mulungu chafikadi pake penipeni mwa iyeyo. Chotitsimikizitsa kuti tili mwa Iye, ndi chimenechi.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:22

Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 5:2-3

Chodziŵira kuti timakonda ana a Mulungu nchakuti timakonda Mulungu ndi kutsata malamulo ake.

Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha.

Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Yohane 1:6

Chikondi chimene ndikunenachi nchakuti tikhale omvera malamulo a Mulungu. Lamulo limene ndikukulemberanilo, monga mudamva kuyambira pa chiyambi, ndi lakuti moyo wanu uzikhala wachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 1:3

Ngwodala munthu amene aŵerenga momveka mauŵa. Ngodalanso anthu amene amvera mau a m'buku limeneli loneneratu zam'tsogolo, ndi kutsata zimene zalembedwamo. Pakuti nthaŵi yoti zichitike zonsezi ili pafupi.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 2:26

Amene adzapambane ndi kuchita mpaka potsiriza zimene ndamlamula, ndidzampatsa ulamuliro pa mitundu yonse ya anthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 3:10

Popeza kuti mwasunga mau anga oti mupirire mosatepatepa, Inenso ndidzakusungani pa nthaŵi yamayeso imene ilikudza m'dziko lonse lapansi, kuti anthu onse okhalamo adzayesedwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 12:17

Apo chinjokacho chidamupsera mtima kwambiri mai uja, nkungochokapo kuti chikayambane ndi ana ena onse a maiyo, ndiye kuti anthu otsata malamulo a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni. Motero chidakaimirira pambali pa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 14:12

“Pamenepa mpofunika kuti anthu a Mulungu akhale opirira, amene amatsata malamulo ake ndipo ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:9

Chauta adzakusandutsani anthu opatulikira Iye monga adalonjezera, malinga mukachita zonse zimene akukulamulani ndi kuyenda m'njira yake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 103:17-18

Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.

Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:1

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Wamkulu ndi woyenera kulambiridwa, ndinu Mulungu wanga, mphamvu yanu ndi yosatheka kufotokoza, palibe angakuletseni kapena kukutsutsani, Inu Ambuye wamphamvu ndi woopsa, ndikulemekeza dzina lanu. Ndikuyandikirani chifukwa palibe Mulungu wofanana ndi inu, ndinu ndipo mudzakhala chitsanzo chachikulu cha kumvera, chikondi ndi kudzichepetsa. Mundiphunzitse kukhala moyo womvera mawu anu ndi malamulo anu, chifukwa ndikudziwa kuti ndiyo njira yokha yopezera moyo wathunthu. Mzimu Woyera mundithandize kuchita mawu anu osati kungokhala womvera wokha wodzinyenga, koma kusinkhasinkha kuti ndimvetse kuti ngakhale pakati pa zovuta ndi zofooka, muli nane. Ndikufuna kukhala ndi mtima wodzaza ndi chiyamiko, kumvera ndi kudzichepetsa kuti ndizindikire zolakwa zanga motero kuti chofunika kwambiri kwa ine chikhale kukusangalatsani, kuti mumtima mwanga mukhale kumvera kwenikweni kotero kuti zochita zanga zizilankhula osati mawu anga, chifukwa "si onse amene amanena, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu ufumu wakumwamba, koma yemene achita chifuniro chanu". Mzimu Woyera, mundithandize kukhala paubwenzi wolimba ndi inu, kulamulira maganizo ndi malingaliro anga, kuwaika pansi pa chifuniro chanu kuti ndipatule nthawi kukhala pamaso panu, chifukwa pamenepo ndi pomwe ndidzapeza chipambano changa. M'dzina la Yesu. Ameni.