Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


38 Mau a Mulungu Okhudza Kumvera Olamulira

38 Mau a Mulungu Okhudza Kumvera Olamulira

Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, tili ndi udindo wotsatira malamulo a Mulungu omwe ali m'Malemba Opatulika.

Kutsatira malamulo amenewa kumaphatikizapo kumvera olamulira athu, anthu omwe ali pafupi nafe kuti atiphunzitse ndikutitsogolera, kaya kutchalitchi, kunyumba, kuntchito kapena kudziko lathu lonse. Tikamachita izi, tikutsatira mfundo yofunika kwambiri imene Mulungu anatipatsa m’Mawu ake, chifukwa kumvera Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse.

Kumvera olamulira athu kudzatibweretsera madalitso ambiri m'miyoyo yathu, ndikutithandiza kukula mbali zonse, chifukwa khalidwe lathu lidzalimbitsidwa ndipo tidzakhala okonzeka kulandira zambiri kuposa zomwe talandirapo kale. Mulungu amadalitsa anthu omwe amatsatira chifuniro chake ndikulemekeza malamulo ake.

Choncho, n’kofunika kulemekeza olamulira athu mwa kuwapempherera kapena m’njira ina iliyonse yabwino yosonyeza ulemu.




Eksodo 22:28

“Musanyoze Mulungu, ndipo musatemberere mtsogoleri wa anthu anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 17:12

Aliyense wosamvera wansembe amene akutumikira Chauta, Mulungu wanu, kapena wosamvera muweruzi, aphedwe. Mwa njira imeneyi mudzachotsa choipa pakati pa Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:21

Mwana wanga, uziwopa Chauta ndiponso mfumu, usagwirizane ndi anthu okonda kuŵachitira mwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 8:2-5

Uzimvera lamulo la mfumu, ndipo chifukwa cha lumbiro lako kwa Mulungu usade nkhaŵa. Zinthu zikapanda kuikondweretsa mfumu, uchoke pamaso pake mwamsanga, pakuti imachita chilichonse chimene chikuikomera. Pajatu mau a mfumu ndi opambana. Ndani angafunse kuti, “Kodi mukuchita chiyani?” Womvera malamulo ake sadzaona vuto lililonse. Munthu wanzeru amadziŵa nthaŵi yake ndi njira yake yochitira zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:7

Muzikometsa ku mizinda kumene ndidakupirikitsirani ku ukapoloko, kuti zonse zizikuyenderani bwino. Muzipempherera mizindayo kwa Chauta, chifukwa choti mizindayo ikakhala pa mtendere, inunso mudzakhala pabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:21

Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumuyo, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:2-3

Adaŵauza kuti, “Aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi ali ndi udindo wotanthauzira malamulo a Mose. Tsonotu munthu akalumbira kuti, Pali guwa la nsembe, walumbiranso pa zonse zimene zili paguwapo. Akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, walumbiranso pa zonse zimene zili m'Nyumbamo. Ndipo akalumbira kuti, Kumwambadi, walumbiranso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndiponso pa Iye amene amakhala pampandopo. “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo. Inu atsogoleri akhungu, mumasuza zakumwa zanu kuti muchotsemo kanchenche, koma mumameza ngamira. “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumatsuka kunja kwa chikho ndi kwa mbale koma m'kati mwake m'modzaza ndi nzeru zakuba, ndi zaumbombo. Afarisi akhungu inu, yambani mwatsuka m'kati mwa chikho, ndipo kunja kwakenso kudzayera. “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Muli ngati manda opaka njeresa, amene amaoneka okongola kunja, pamene m'kati mwake m'modzaza ndi mafupa a anthu akufa ndi zoola zina zilizonse. Inunso muli chimodzimodzi: pamaso pa anthu mumaoneka olungama, pamene m'kati mwanu m'modzaza ndi chiphamaso ndi zoipa zina. “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumakonza bwino manda a aneneri, ndipo mumakongoletsa ziliza za anthu olungama. Nchifukwa chake muzichita ndi kutsata zonse zimene iwo amakuphunzitsani. Komatu musamatsanzira zimene amachita, pakuti sachita zimene amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:1-3

Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu. Kwenikweni adzikongoletse ndi ntchito zabwino, monga ayenera kuchitira akazi amene amati ndi opembedza Mulungu. Akazi pophunzitsidwa, azikhala chete ndi a mtima wodzichepetsa. Sindilola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala ndi ulamuliro pa amuna. Mkazi kwake nkukhala chete. Paja Adamu ndiye adaayambira kulengedwa, pambuyo pake Heva. Ndiponso si Adamu amene adaanyengedwa, koma mkaziyo ndiye adaanyengedwa, naphwanya lamulo la Mulungu. Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima. Muziŵapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza. Zimenezi nzabwino ndi zokondweretsa pamaso pa Mulungu, Mpulumutsi wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1-2

Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu. Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena. Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira. Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa. Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:3-4

Olamulira sachititsa mantha anthu a makhalidwe abwino, koma a makhalidwe oipa. Kodi ufuna kukhala wosaopa wolamulira? Uzichita zolungama, ndipo iye adzakuyamikira, pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:13-14

Chifukwa cha Ambuye, muzimvera akulu onse olandira ulamuliro. Ngati ndi mfumu yaikulu koposa ija, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro pa mafumu ena onse. Ngati ndi nduna, zimvereni chifukwa zidachita kutumidwa ndi mfumu kuti zizilanga ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:3-5

Olamulira sachititsa mantha anthu a makhalidwe abwino, koma a makhalidwe oipa. Kodi ufuna kukhala wosaopa wolamulira? Uzichita zolungama, ndipo iye adzakuyamikira, pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga. Nchifukwa chake muziŵamvera olamulira, osati chifukwa cha kuwopa mkwiyo wa Mulungu chabe, komanso chifukwa chomvera umboni wa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:17

Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:40

Koma tsono, zonse zizichitika moyenera ndi molongosoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:22

Inu antchito, muziŵamvera pa zonse ambuye anu apansipano. Musamangochitatu zimenezi pamene muli pamaso pao kuti akuyamikireni, koma muziŵamvera ndi mtima wonse, chifukwa choopa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5

Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:5-8

Inu akapolo, ambuye anu a pansi pano muziŵamvera mwamantha ndi monjenjemerera. Muzichita zimenezi ndi mtima woona, ngati kuti mukuchitira Khristu yemwe. Musazichite mwachiphamaso chabe, ngati kuti mukungofuna kukondweretsa anthu. Koma ngati akapolo a Khristu, muzichita ndi mtima wonse zimene Mulungu afuna. Muzitumikira mosangalala, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu chabe. Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:15

Paja Mulungu amafuna kuti ndi zochita zanu zabwino muthetse kulankhula kosadziŵa kwa anthu opusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-3

Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:14-15

Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:17

Wosamala malangizo amayenda pa njira ya moyo, koma wokana chidzudzulo amasokera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:22-24

Inu antchito, muziŵamvera pa zonse ambuye anu apansipano. Musamangochitatu zimenezi pamene muli pamaso pao kuti akuyamikireni, koma muziŵamvera ndi mtima wonse, chifukwa choopa Ambuye. Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 82:3-4

Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi. “Landitsani ofooka ndi osoŵa. Apulumutseni kwa anthu oipa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:12-13

Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani. Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:2

Mu dziko mukakhala chilungamo, anthu amakondwa, koma chilungamo chikasoŵa, anthu amadandaula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:5

Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1

Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:19

Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:1-2

Uziŵakumbutsa anthu onse kuti azigonjera akulu oweruza ndi olamulira. Aziŵamvera ndipo azikhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino. Munthu woyambitsa mipatuko, utamdzudzula kaŵiri konse, usakhale nayenso nkanthu. Paja ukudziŵa kuti munthu wotere ngwosokonezeka ndipo ngwochimwa. Mwini wake yemwe amadziimba mlandu yekha. Ndikadzamtuma Aritema kapena Tikiko kwanuko, uchite chotheka kudzandipeza ku Nikopoli, chifukwa ndatsimikiza kuti ndikakhala kumeneko nyengo yachisanu ikubwerayi. Uyesetse kuthandiza Zena, katswiri wa malamulo uja ndiponso Apolo, kuti apitirize ulendo wao. Uwonenso kuti asasoŵe kanthu. Anthu athunso aziphunzira kudzipereka pa ntchito zabwino, kuti azithandiza pamene pali kusoŵa kwenikweni. Azitero kuti moyo wao usakhale wopanda phindu. Onse amene ali nane kuno akuti moni. Uperekeko moni kwa onse amene amatikonda chifukwa cha chikhulupiriro. Mulungu akukomereni mtima nonse. Uŵauze kuti asamakamba zoipa za wina aliyense, apewe kukangana, akhale ofatsa, ndipo nthaŵi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:17

Muzilemekeza anthu onse. Muzikonda akhristu anzanu. Khalani anthu oopa Mulungu. Mfumu yaikulu koposa ija muziipatsa ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:1-2

Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu. Kwenikweni adzikongoletse ndi ntchito zabwino, monga ayenera kuchitira akazi amene amati ndi opembedza Mulungu. Akazi pophunzitsidwa, azikhala chete ndi a mtima wodzichepetsa. Sindilola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala ndi ulamuliro pa amuna. Mkazi kwake nkukhala chete. Paja Adamu ndiye adaayambira kulengedwa, pambuyo pake Heva. Ndiponso si Adamu amene adaanyengedwa, koma mkaziyo ndiye adaanyengedwa, naphwanya lamulo la Mulungu. Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima. Muziŵapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:28

Pakuti ulamuliro ndi wake wa Chauta, Iye amalamula anthu a mitundu yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1-4

Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu. Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena. Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira. Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa. Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango. Olamulira sachititsa mantha anthu a makhalidwe abwino, koma a makhalidwe oipa. Kodi ufuna kukhala wosaopa wolamulira? Uzichita zolungama, ndipo iye adzakuyamikira, pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:1

Uziŵakumbutsa anthu onse kuti azigonjera akulu oweruza ndi olamulira. Aziŵamvera ndipo azikhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:13-15

Chifukwa cha Ambuye, muzimvera akulu onse olandira ulamuliro. Ngati ndi mfumu yaikulu koposa ija, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro pa mafumu ena onse. Ngati ndi nduna, zimvereni chifukwa zidachita kutumidwa ndi mfumu kuti zizilanga ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino. Paja Mulungu amafuna kuti ndi zochita zanu zabwino muthetse kulankhula kosadziŵa kwa anthu opusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:18

Inu antchito, muzimvera ndi ulemu wonse anthu okulembani ntchito, osati okhawo amene ali abwino ndi ofatsa ai, koma ndi ovuta omwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate, Inu ndinu Wamphamvuyonse, muli ndi ulamuliro pa zonse, chifukwa ndinu Woyera ndi Wokwezeka. Ndikupempha kuti atsogoleri ndi akuluakulu a maboma adziwe kuti Inu ndinu Mfumu ya mafumu, ndipo agonjetse ulamuliro wawo pansi pa chitsogozo cha Mzimu Woyera wanu, ndipo ndi nzeru zanu azilamulira mitundu yonse mwachilungamo. Mawu anu amati: "Aliyense agonjere olamulira akuluakulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu, ndipo uliwonse umene ulipo, Mulungu ndiye anauuika." Ambuye, mundiphunzitse kugonjera olamulira amene mwaiika pa moyo wanga, onse a dziko lapansi ndi auzimu. Mtima wanga ukhale womvera, wokonzeka kulandira uphungu, osakana, koma uzindikire olamulira amene inu mwaiika, kaya panyumba, kuntchito, kutchalitchi, kapena kudziko. Mundiphunzitse kusonyeza nthawi zonse mzimu womvera ndi kukhala chitsanzo kwa iwo amene ali pafupi nane, chifukwadi mu kumvera muli madalitso anga. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa