Ine ndikufuna kukuuzani za chilungamo, chomwe ndi chofala kwambiri m'Baibulo. Tikamakhala olungama, timakhala moyo wotsatira malamulo ndi ziphunzitso za Mulungu. Ndi kuyenda m'njira yabwino, yopanda chinyengo, komanso yowona m'zonse zomwe timachita.
M'Baibulo muli mavesi ambiri ofotokoza kufunika kwa chilungamo. Mwachitsanzo, mu Miyambo 20:7, amati: "Wolungama amakhala ndi moyo wopanda banga; ana ake adzakhala odala pambuyo pake!" Apa tikumva kuti chilungamo sichingotipindulire tokha, komanso chidzapindulire mibadwo yotsatira.
Kukhala wolungama ndi kumvera malamulo a Mulungu ndikutsata njira zake. Salmo 119:11 imatilimbikitsa kusunga mawu a Mulungu mumtima mwathu kuti tisamuchimwire. Chilungamo chimatithandiza pa zochita zathu za tsiku ndi tsiku, kutsogolera zisankho zathu, ndi makhalidwe athu.
Baibulo limatiphunzitsanso kuti Mulungu amadalitsa anthu olungama. Mu Mateyu 5:6, Yesu anati: "Odala ali iwo akumva njala ndi ludzilo la chilungamo, pakuti adzakhutisidwa." Izi zikutanthauza kuti amene amafuna kukhala moyo wolungama adzadalitsidwa ndipo adzapeza chimwemwe mwa Mulungu.
Komabe, sitiyenera kuiwala kuti sitingathe kukhala olungama ndi mphamvu zathu zokha. Aroma 3:22 imatiuza kuti "Chilungamo cha Mulungu chimapezeka mwa chikhulupiriro mwa Yesu Khristu kwa onse okhulupirira." Sikuti ndi ntchito zathu, koma ndi kudalira nsembe ya Yesu pa mtanda ndikukhala moyo womvera Mulungu.
Chilungamo ndi khalidwe lofunika kwambiri lomwe limatiitana kuti tikhale moyo wotsatira mfundo za Atate wathu wakumwamba. Limatilimbikitsa kuti tichite zinthu mwachilungamo, mwaulemu, komanso mowona mtima nthawi zonse. Tikamakhala moyo wolungama, tidzalandira madalitso ndipo tidzapeza chimwemwe mwa Mulungu.
Paja Chauta ndi wolungama, amakonda ntchito zolungama, ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.
Ungwiro wa anthu olungama umaŵatsogolera, koma makhalidwe okhota a anthu onyenga ngoononga.
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
Mafano aowo ali ngati kangamunthu woopsera mbalame m'munda wa minkhaka, sangathe nkulankhula komwe. Ayenera kuŵanyamula, poti sangayende okha. Musaŵaope, chifukwa sangakuchiteni choipa. Alibenso mphamvu zochitira zabwino.”
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Ana anga, wina aliyense asakusokeretseni. Munthu amene amachita chilungamo, ngwolungama monga Khristu ali wolungama.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Ochita zoipa adzalephera, koma ochita chifuniro cha Chauta adzakhala ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwake.
Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai,
Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.
Anthu abwino atha pa dziko lapansi, palibe ndi mmodzi yemwe wolungama. Onse akubisalirana mwachiwembu. Aliyense akusakira mbale wake mu ukonde.
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Angathe kutero ndi amene amachita zolungama ndi kulankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga, amene amakutumula manja ake kuti angagwire chiphuphu, amene amatseka makutu kuti angamve mau opangana za kupha anzao, amene amatsinzina kuti angaone zoipa.
Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe.
Upenye munthu wopanda cholakwa ndi wolungama, ndipo udzapeza kuti munthu wamtendere ali ndi zidzukulu zambiri.
Ayenera kupita ku dziko la akufa ngati nkhosa, ndipo imfa idzakhala mbusa wao. Anthu olungama adzaŵapambana. Adzatsika kulunjika ku manda, matupi ao adzaola, kwao kudzakhala kumanda.
Ndipo moyo wanu udzakhala wodzaza ndi zipatso za chilungamo zimene mudzaonetsa mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti anthu onse alemekeze ndi kutamanda Mulungu.
Chauta adalitse anthu ake mtendere ndi chimwemwe zikhale nao, anthu akondwere chifukwa cha Chauta
Ngakhale nthaŵi ya mdima, munthu wochita chilungamo ayenda m'kuŵala, chifukwa ngwokoma mtima, wachifundo ndi woongoka.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni, ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro.
Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.
Paja anthu olungama ndiwo adzakhale m'dziko, anthu okhulupirika ndiwo adzakhazikike m'menemo.
Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa.
Munthu woyenda mwaungwiro, amayenda mosatekeseka. Koma woyenda njira zoipa, adzadziŵika.
“Mukatero, mudzaŵala ngati mbandakucha, ndipo mabala anu adzapola msanga. Ine, kulungama kwanu, ndidzakutsogolerani, ndipo ulemerero wanga udzakutchinjirizani kumbuyo kwanu.
Munthu wosauka amene amayenda mwaungwiro amaposa kwambiri munthu wolemera amene ali wonyenga.
Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
Koma kunena za ife, chifukwa cha kulandira Mzimu Woyera ndiponso pakukhulupirira, tikuyembekeza kuti Mulungu adzatiwona kuti ndife olungama pamaso pake.
Koma munthu atangokhulupirira, m'malo mwa kudalira ntchito zake, Mulungu amene amaŵaona kuti ngosapalamula anthu ochimwa, munthu ameneyo pakukhulupirira, Mulungu adzamuwona kuti ngwolungama pamaso pake.
Kulungama kwa munthu woyera mtima kumampulumutsa, koma zilakolako zoipa zimaŵaika mu ukapolo anthu onyenga.
Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.
Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.
Ngati mukudziŵa kuti Khristu ndi wolungama, musapeneke konse kuti aliyense wochita chilungamo, ndi mwana wa Mulungu.
Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo.
Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.
Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi.
Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira.
Chauta adandipatsa mphotho molingana ndi ntchito zanga zabwino, adandifupa molingana ndi ungwiro wanga.
Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu.
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Nowa adalandira machenjezo a Mulungu onena za zinthu zomwe mpaka nthaŵi imeneyo zinali zisanaoneke. Adamvera, napanga chombo kuti apulumutse onse a m'banja mwake. Potero adaŵatsutsa kuti ngolakwa anthu a dziko lapansi, nalandira chilungamo chimene Mulungu amapatsa anthu omkhulupirira.
Kulungama kwa anthu angwiro kumaŵathandiza pa moyo wao, koma kuipa mtima kumagwetsa mwiniwake yemweyo.
Apo Abramu adakhulupirira Chauta, ndipo chifukwa cha chimenecho, Chauta adamuwona kuti ndi wolungama.
koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino, ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse.
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu.
Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”
Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu, koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Pajatu pamene pali kuŵala, pamapezekanso ubwino wonse, chilungamo chonse ndi choona chonse.
kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,
Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu? Ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera? Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.
Chauta akunena kuti: “Tcherani khutu inu amene mufuna kupulumuka, inu amene mufuna kuti ndikuthandizeni. Taganizani za thanthwe kumene mudasemedwa, ku nkhuti ya miyala kumene adakukumbani.
Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta.
Anthu a mtima woipa amamnyansa Chauta, koma anthu a makhalidwe abwino amamkondweretsa.
Inu Chauta, ndinu olungama, munditsogolere pakati pa adani ondizonda. Mundikonzere njira yoongoka kuti ndidzeremo.
Khristu adafikitsa Malamulo a Mose ku mapherezero, kotero kuti aliyense wokhulupirira, amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira. Ambuye amene ali Woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphothoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso.
Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu.
Chauta akuuza anthu ake kuti, “Muzichita zabwino ndi zolungama, chifukwa ndikuwombolani posachedwa, chipulumutso changa chiwoneka.”
Mulungu ndiye adakulunzanitsani ndi Khristu Yesu, ndipo adamsandutsa kuti akhale nzeru yathu. Chifukwa cha Yesu, timapezeka olungama pamaso pa Mulungu. Ndi Yesuyo amene amatisandutsa anthu akeake a Mulungu, ndiye amatipulumutsa.
Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka.
Ndi amene amachita zabwino ndi manja ake, ndipo amaganiza zabwino mumtima mwake. Ndi amene salingalira zonama, ndipo salumbira monyenga. Adzalandira madalitso kwa Chauta, ndipo Mulungu Mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.
Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.
Mitambo ndi mdima waukulu zamzinga Chauta. Amalamulira molungama, mu ufumu wake mulibe tsankho.
Munthu wokoma mtima amasamalira zoyenerera osauka, koma munthu woipa salabadako za zimenezo.
Pamenepo mudzadziŵa kusankha zimene zili zabwino kotheratu. Apo pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu mudzapezeka oyera mtima, ndi opanda cholakwa chilichonse. Ndipo moyo wanu udzakhala wodzaza ndi zipatso za chilungamo zimene mudzaonetsa mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti anthu onse alemekeze ndi kutamanda Mulungu.
Munthu abwino amakhala mwachilungamo, ndipo Mulungu amadalitsa ana amene amatsata njira yake.
Choncho monga uchimo unkalamulira anthu ndi kudzetsa imfa pa iwo, momwemonso kunali koyenera kuti kukoma mtima kwa Mulungu kulamulire pakudzetsa chilungamo kwa anthu, ndi kuŵafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
Mudakonda chilungamo nkudana ndi zosalungama. Nchifukwa chake Ine, Mulungu wanu, ndakukwezani nkukudzozani ndi mafuta osonyeza chimwemwe, kupambana anzanu ena onse.”
Namondwe akaomba, oipa amachotsedwa, koma anthu ochita chilungamo amakhazikika mpaka muyaya.
Udzakhazikika m'chilungamo chenicheni. Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa palibe choopa, sudzakhalanso ndi mantha, chifukwa manthawo sadzakufikira.
Nayi mbiri ya Nowa. Nowa anali munthu wochita zokondweretsa Mulungu, wopanda cholakwa, ndipo pa nthaŵi imeneyo adaali yekhayo amene anali wabwino pamaso pa Mulungu.
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.
Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera. Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.
Koma amphaŵi adzaŵaweruza mwachilungamo, ndipo anthu otsika a pa dziko lapansi adzaŵagamulira mlandu wao mosakondera. Mau ochokera m'kamwa mwake adzakhala ngati ndodo yokanthira ochimwa, atalamula iyeyo anthu oipa adzaphedwa. Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake, ndipo kukhulupirika, ngati chomangira m'chiwuno mwake.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Maziko a ufumu wanu ndiwo kulungama ndi kuweruza mosakondera. Mumaonetsa chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika pa zonse zimene mumachita.
Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti ngati kukhulupirika kwanu sikuposa kukhulupirika kwa aphunzitsi a Malamulo ndi kwa Afarisi, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.