Tsono Mulungu adalankhula mau onseŵa, adati, Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako. Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera. “Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa. “Usaphe.” “Usachite chigololo.” “Usabe.” “Usachite umboni womnamizira mnzako.” “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”
Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse. Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa.
Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe. Idatumanso antchito ena nkunena kuti, ‘Kaŵauzeni oitanidwa aja kuti chakudya chakonzeka. Ndapha ng'ombe ndi nyama zina zonenepa. Zonse zakonzeka, bwerani ku phwando laukwati.’ Malamulo onse a Mose ndiponso zonse zimene aneneri adaphunzitsa zagona pa malamulo aŵiriŵa.”
Ngati mutsata malamulo anga, mudzakhala m'chikondi changa, monga momwe Ine ndatsatira malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala m'chikondi chao.
Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.
Tsono inu Aisraele, tamvani zimene Chauta, Mulungu wanu, akukuuzani. Akufuna kuti muzimuwopa ndi kuchita zonse zimene amakulamulani. Muzikonda Chauta, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo muzimvera malamulo ndi malangizo onse a Chauta amene ndikukulamulani lero lino, kuti zinthu zikukomereni.
Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana.
Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.
Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.
Koma Samuele adati, “Kodi Chauta amakondwa ndi chiti: nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kapena kumvera mau ake? Ndithu, ndi kumvera ndi kupereka nsembe kwabwino kwambiri nkumvera. Ndi kutchera khutu ndi kupereka mafuta ankhosa kwabwino kwambiri nkutchera khutu.
“Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.”
“Mukamayenda motsata njira zanga ndi kumamvera malamulo anga onse ndi kuŵatsatadi, Ndidzaononga akachisi anu opembedzerako mafano ku mapiri ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo lubani, ndipo ndidzaponya mitembo yanu pa mafano opanda moyo, ndipo ndidzadana nanu. Ndidzasandutsa mizinda yanu kuti ikhale mabwinja, ndidzasandutsanso malo anu achipembedzo kuti akhale opanda anthu, ndipo sindidzalolanso kumva fungo lokoma la zopereka zanu. Ndidzaononga dziko lanu kotero kuti adani anu amene adzakhale m'menemo adzadabwa. Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzakupirikitsani, lupanga lili pambuyo. Dziko lanu lidzasanduka chipululu, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja. “Pa nyengo imeneyo nthaka idzakondwerera zaka zoipumitsa nthaŵi yonse pamene m'dzikomo mulibe anthu, inu muli m'dziko la adani anu. Pamenepo nthaka idzapuma ndi kukondwerera zaka zopumazo. Nthaŵi zonse pamene dzikolo lilibe anthu, nthaka idzapuma, kupuma kwake kumene sidapumepo pa zaka zonse pamene inu munkakhalamo. Ndipo ngakhale ena amene mudzatsalenu, ndidzaika mtima wa mantha mwa inu pamene muli m'dziko la adani anu. Mtswatswa wa tsamba louluka udzakuthaŵitsani. Mudzathaŵa monga m'mene munthu amathaŵira lupanga, ndipo mudzagwa pansi popanda okuthamangitsani. Mudzaphunthwitsana monga ngati mukuthaŵa nkhondo, ngakhale palibe amene akukupirikitsani. Ndipo simudzakhala ndi mphamvu zoti mulimbane ndi adani anu. Mudzatha, kuchita kuti psiti, pakati pa mitundu ya anthu, ndipo dziko la adani anu lidzakudyani. Ngakhale ena amene mudzatsalenu, nanunso mudzazunzika m'dziko la adani anu chifukwa cha machimo anu, ndipo mudzazunzikanso chifukwa cha machimo a makolo anu. ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake, ndipo nthaka idzakubalirani zokolola zochuluka, ndipo mitengo yam'minda idzakubalirani zipatso.
Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.
Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.
Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndipo nthaŵi zonse muzimvera malamulo ndi malangizo ake onse.
Koma mukamvera iyeyo ndi kuchita zonse zimene ndinena, Ineyo ndidzadana ndi adani anu, ndipo onse amene atsutsana nanu ndidzalimbana nawo.
Lero ndikukupatsani zinthu ziŵiri kuti musankhepo, madalitso kapena matemberero. Madalitso kwa inu, mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndikukupatsani leroŵa. Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo.
Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.”
Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite.
Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye,
Chikondi chimene ndikunenachi nchakuti tikhale omvera malamulo a Mulungu. Lamulo limene ndikukulemberanilo, monga mudamva kuyambira pa chiyambi, ndi lakuti moyo wanu uzikhala wachikondi.
Ine ndikufuna kuti aziganiza zimenezo masiku onse. Ndikufuna kuti azindiwopa nthaŵi zonse, ndipo kuti azimvera malamulo anga, kuti zinthu ziŵayendere bwino iwowo ndi zidzukulu zao mpaka muyaya.
Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling'ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng'ono ndithu mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wakumwamba.
Muzimvera malangizo ndi malamulo ake onse amene ndakupatsani leroŵa. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino inuyo ndi zidzukulu zanu, ndipo mudzakhalitsa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani kuti likhale lanu mpaka muyaya.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Mutsate Chauta, Mulungu wanu, ndi kuwopa Iye yekha. Mutsate malamulo ake ndi kumvera mau ake. Mutumikire Iye ndi kuphathana naye.
Adati, “Mukamandimvera Ine Chauta, Mulungu wanu, kumachita zolungama, kumasamala malamulo anga ndi kumamvera zimene ndikukulamulani, sindidzakulangani ndi nthenda zilizonse zimene ndidalanga nazo Aejipito. Ine ndine Chauta amene ndimakuchiritsani.”
Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.
Pakuti amene ali olungama pamaso pa Mulungu si amene amangomva Malamulo chabe ai. Koma okhawo amene amachitadi zonenedwa m'Malamulo ndiwo amene Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama.
Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Tsono anthu onse a pa dziko lonse lapansi adzaona kuti Chauta, Mulungu wanu, wakusankhani inu kuti mukhale anthu akeake, ndipo azidzakuwopani. Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani. Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense. Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika. Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira. Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa: Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu. Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu. Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe. Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse. Mverani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalandira madalitso onse aŵa:
Yesu adauza anthu amene adamkhulupirirawo kuti, “Ngati mumvera mau anga nthaŵi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga.
Basi, zonse zamveka. Mfundo yeniyeni ya zonsezi ndi iyi: Uzimvera Mulungu, ndipo uzitsata malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wake wonse wa munthu.
Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa.
Koma Yesu adati, “Iyai, odala ndi anthu amene amamva mau a Mulungu naŵagwiritsa ntchito.”
Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu.
Mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mukamamkonda Chauta, Mulungu wanu ndi kutsata mau ake onse, pamenepo mudzakhala pabwino ndipo mudzakhala mtundu wa anthu ochuluka. Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko mukukakhalamolo.
Muzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene munkalakalaka pamene munali osadziŵa. Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse.
Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta.
Pajatu munthu wotsata Malamulo onse, akangophonyapo ngakhale pa mfundo imodzi yokha, ndiye kuti wachimwira Malamulo onsewo.
ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.
Nchifukwa chake mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye yekha Mulungu, ndipo ndi Mulungu wokhulupirika. Iye adzasungadi chipangano chake ndipo adzaonetsa chifundo chake chosasinthika kwa anthu a mibadwo zikwi zambirimbiri amene amakonda Iye namamvera malamulo ake.
Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu, poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu.
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.
Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.
Tsono inu, muzichita monga momwe Chauta akulamulirani. Muziyenda m'njira zake ndipo muzimuwopa.
Komatu anthu ambirimbiri a mibadwo yosaŵerengeka amene amandikonda, namatsata malamulo anga, ndimaŵakonda ndi chikondi chosasinthika.
Monsemo Chauta adatuma amithenga ndi aneneri ake ku Israele ndi ku Yuda, okalalika kuti, “Musinthe makhalidwe anu auchimo ndipo mumvere Malamulo anga amene ndidaŵapereka kwa makolo anu, kudzera mwa aneneri, atumiki anga.”
adati: Mukumbukire bwino malamulo onse amene ndakupatsani leroŵa. Muuze ana anu kuti azimvera mosamala mau onse a malamuloŵa. Mauŵa sikuti ndi mau achabe. Mau ameneŵa ndiwo moyo wanu. Muŵamvere, ndipo mudzakhalitsa m'dziko mukukakhalamolo uko kutsidya kwa Yordani.
“Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika. Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling'ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng'ono ndithu mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wakumwamba.
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Tsono mukamandimvera ndi kusunga chipangano changa, mudzakhala anthu anga pakati pa makamu onse, pakuti dziko lonse lapansi ndi langa.
Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.
Madalitso kwa inu, mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndikukupatsani leroŵa. Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo.
Pambuyo pake adatenga buku lachipangano, naŵaŵerengera momveka anthuwo. Tsono anthuwo adati, “Tidzachita zonse zimene Chauta walamula. Tidzamumvera Iyeyo.”
Ndipo ukamadzandimvera ndi kumasunga malamulo anga, monga momwe ankachitira bambo wako Davide, udzakhala ndi moyo wautali kwabasi.”
Nchifukwa chake monga Atate anu akumwamba ali abwino kotheratu, inunso mukhale abwino kotheratu.
Malamulo anu onse amalungamitsa mayendedwe anga. Ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga.
atatewo adandiphunzitsa ndi mau akuti, “Ugwiritse mumtima mwako zimene ndikukuuzazi, usunge malamulo anga, kuti ukhale ndi moyo.
Anthuwo adayankha pamodzi kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.” Pambuyo pake Mose adakafotokozera Chauta zimene anthuwo adanena.
Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Mosakayika konse, Malamulo a Mose ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo lamulo lililonse mwa Malamulowo ndi loyera, lolungama ndi labwino.
Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Pamenepo Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi mudzakhalabe osamvera mau anga ndi malamulo anga mpaka liti?
Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona.
Musaonjezerepo kanthu kena pa zimene ndakulamulani, ndipo musachotsepo kanthu. Muzimvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndakupatsani.
Yesu adamuyankha kuti, “Bwanji ukundifunsa za chimene chili chabwino? Wabwino ndi Mmodzi yekha. Ngati ufuna kukaloŵa ku moyo, uzimvera Malamulo.”
Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu. Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni. Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa. M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo. ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere. Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutse kwathunthu. Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse. Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe.
Pafunikadi kupirira, kuti muchite zimene Mulungu akufuna, kuti motero mukalandire zimene adalonjeza.
Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula.
Mulungu adachita zimenezi, kuti chilungamo chimene Malamulo a Mose amatipempha, chiwoneke kwathunthu mwa ife amene sitimveranso khalidwe lathu lopendekera ku zoipa, koma timamvera Mzimu Woyera.
Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Inu Aisraele, musamale ndithu kuchita zimene Chauta, Mulungu wanu, wakulamulani, osapatukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere. Muziyenda m'njira imene Chauta, Mulungu wanu, wakulamulani, kuti zinthu zidzakuyendereni bwino, ndipo mudzapitirire kukhala ndi moyo m'dziko limene mukakhalemolo.
“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba. Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kunali koopsa.”
Tsono mumachita bwino ngati mumatsatadi lamulo lachifumu lija limene limapezeka m'Malembo, lonena kuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Koma Samuele adati, “Kodi Chauta amakondwa ndi chiti: nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kapena kumvera mau ake? Ndithu, ndi kumvera ndi kupereka nsembe kwabwino kwambiri nkumvera. Ndi kutchera khutu ndi kupereka mafuta ankhosa kwabwino kwambiri nkutchera khutu. Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”
“Ndipo tsopano, ana anga, tamverani, ngodala anthu amene amasunga malangizo anga. Muzimva malangizo, kuti muzikhala anzeru, musamanyozere mau anga.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Tsono mumvereni, ndipo musunge malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani leroŵa.
Sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, kuti nditsate malamulo anu.
Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.
Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu.
Musamale bwino kuti mumvere ndithu malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Mulungu adakupatsani. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, muzichita zimene Iyeyo akufuna, muzimvera malamulo ake, muzikhala okhulupirika kwa Iye, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi mzimu wanu wonse.”
Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”
Utsate malamulo anga, ndipo udzakhala ndi moyo. Usamale malangizo anga monga umachitira ndi maso ako.
Munthu aliyense wodza kwa ine, namva mau anga nkumaŵagwiritsa ntchito, ndikuuzani amene amafanafana naye. Amafanafana ndi munthu womanga nyumba, amene adaakumba mozama, naika maziko pa thanthwe. Tsono chigumula chitafika, madzi ake adagunda nyumbayo, koma sadaigwedeze, chifukwa adaaimanga bwino. Koma munthu wongomva mau anga, osaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu amene adaamanga nyumba pamwamba pa nthaka, osakumba maziko. Pamene madzi a chigumula adagunda nyumbayo, pompo idagwa, ndipo kuwonongeka kwake kunali kotheratu.”
Ndikukulamula kuti, mopanda cholakwa kapena chokayikitsa, utsate bwino zonse zimene udalamulidwa, mpaka Ambuye athu Yesu Khristu adzabwerenso.
Mudzaitane amuna onse, akazi, ana ndi alendo amene ali m'mizinda mwanu, kuti aliyense adzimvere yekha, ndipo aphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu, ndi kumamvera mau ake mosamala. Mwa njira imeneyi zidzukulu zanu zimene sizidamve malamulo a Chauta nkale lomwe, zidzamva, ndipo zidzaphunzira kuwopa Chauta nthaŵi yonse imene zidzakhale m'dziko limene mukukakhalamolo patsidya pa Yordani.”
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
“Tsono pamaso pa Aisraele onse ndiponso pamaso pa msonkhano umenewu, Mulungu wathu alikumva, ndikukuuzitsani kuti muzisunga ndi kusamala malamulo onse a Chauta Mulungu wanu, kuti mukhalitse m'dziko labwinoli, ndipo lidzakhale nthaŵi zonse choloŵa cha ana anu, inu mutapita.
Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa.
Yesu adaŵayankha kuti, “Nanga bwanji inuyo, chifukwa choumirira miyambo yanu, mumaphwanya lamulo la Mulungu? Anthu ambirimbiri adadza kwa Iye ndi anthu opunduka miyendo, akhungu, olumala, osalankhula, ndiponso ndi odwala ena ambiri. Adaŵakhazika pafupi ndi Yesu, Iye nkuŵachiritsa. Tsono anthu onse adadabwa poona kuti osalankhula aja akulankhula, olumala aja achira, opunduka miyendo aja akuyenda, ndipo akhungu aja akupenya. Choncho adatamanda Mulungu wa Israele. Yesu adaitana ophunzira ake, naŵauza kuti, “Ndikuŵamvera chifundo anthuŵa, chifukwa akhala nane masiku atatu tsopano, ndipo alibe chakudya. Sindifuna kuŵabweza kwao ali ndi njala chonchi, kuwopa kuti angalefuke pa njira.” Ophunzirawo adamufunsa kuti, “Anthu ochuluka chotereŵa tingaŵapezere kuti chakudya chokwanira, kuthengo ngati kuno?” Yesu adaŵafunsa kuti, “Kaya buledi muli naye mngati?” Iwo aja adati, “Msanu ndi muŵiri, ndiponso tinsomba toŵerengeka.” Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi. Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, ndi nsomba zija, adathokoza Mulungu, nazinyemanyema nkuzipereka kwa ophunzira ake, iwowo nakazigaŵira anthu aja. Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nkudzaza madengu asanu ndi aŵiri. Koma tsono anthu amene adaadyawo, analipo zikwi zinai amuna okha, osaŵerenga akazi ndi ana. Pambuyo pake Yesu adatsazikana nawo anthu aja, kenaka Iye adaloŵa m'chombo napita ku dera la Magadani. Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’ Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni, ndazipereka kwa Mulungu,” ameneyo sasoŵanso kulemekeza atate ake.’ Pakutero, chifukwa cha mwambo wanuwo, mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe. Inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaati, “ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutali ndi Ine. Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni ndi malamulo a anthu chabe.’ ”
Mwa Khristuyo ife tidalandira mwai wokhala atumwi, kuti tithandize anthu a mitundu yonse kumkhulupirira ndi kumumvera, kuti choncho dzina lake lilemekezedwe.
Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga.
Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma.
Komatu muzidzamvera Chauta, Mulungu wanu, ndi kusunga malamulo ndi malangizo ake onse amene ali m'buku lino la malamulo ake. Mutembenukire kwa Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Munthu womvera malamulo amadzisungira moyo, koma munthu wonyoza malangizo a Mulungu adzafa.
Nchifukwa chake abale, chitani changu koposa kale kutsimikiza kuti Mulungu adakuitanani ndipo adakusankhani. Mukatero simudzagwa konse.
Koma ndimachitira chifundo chosasinthika anthu zikwi zambirimbiri amene amandikonda namasunga malamulo anga.
Yesu adauza anthu amene adamkhulupirirawo kuti, “Ngati mumvera mau anga nthaŵi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziŵa zoona zenizeni, ndipo zoonazo zidzakusandutsani aufulu.”