Ndikufuna kukuuzani nkhani yokhudza ulemu kwa makolo athu. Mulungu amafuna tonse, ana, achinyamata, ndi akuluakulu, kuti tiphunzire kulemekeza ndi kumvera makolo athu kuti tizikhala moyanjana ndi nzeru. Baibulo limati, "Lemekeza atate wako ndi amako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira, kuti masiku ako akhale ochuluka, ndi kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa." (Deuteronomo 5:16).
Mukadziwa, ngakhale Yesu, ali mwana, anamvera makolo ake a padziko lapansi ndipo anakulanso mu nzeru. Iye anali Mwana wa Mulungu, koma anasonyeza chitsanzo chabwino cha kumvera. Ndipo ife, kodi sitingatsanzire chitsanzo chake cha ulemu?
Tikamamvera makolo athu, timadalitsa kwambiri. Mulungu amatipatsa madalitso ambiri chifukwa chomvera mawu ake ndi mfundo zake zosatha. Ndikukhulupirira kuti tonse tingatsatire chitsanzo cha Yesu ndi kukhala odalitsidwa.
“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.
“Uzilemekeza atate ako ndi amai ako, monga momwe Chauta, Mulungu wako, adakulamulira, kuti pakutero masiku a moyo wako achuluke ndipo kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa iwe.
amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.
Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa.
Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’
Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti samkonda, koma amene amakonda mwana wake, sazengereza kumlanga.
Wina akatemberera bambo wake kapena mai wake, moyo wake udzatha ngati nyale yozima mu mdima wandiweyani.
Paja Mose adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’
Aliyense mwa inu aziwopa mai wake ndi bambo wake. Muzisunga masiku anga a Sabata, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera.
“Atembereredwe aliyense wosalemekeza atate ndi amai ake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako. Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako.
Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.
Amene amachita ndeu ndi atate ake ndi kupirikitsa amai ake, ameneyo ndi mwana wochititsa manyazi ndiponso wonyozetsa.
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
Bambo wa mwana waulemu adzakondwa kwambiri. Wobala mwana wanzeru adzasangalala naye. Atate ako ndi amai ako asangalale, mai amene adakubala iwe akondwe.
Amene amatsata malamulo ndiye mwana wanzeru, koma amene amayenda ndi anthu adyera, amachititsa atate ake manyazi.
Aliyense amene amaseka bambo ndi kumanyozera kumvera mai, makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso, ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
Uzikumbukanso Mlengi wako pa masiku a unyamata wako, masiku oipa asanafike, zisanafikenso zaka zoti uzidzati, “Moyowu wandikola.”
Anthu ako akhala akunyoza atate ao ndi amai ao. Akhala akuzunza alendo okhala nawe, akhalanso akusautsa ana amasiye ndi akazi amasiye.
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Mwana amapatsa ulemu bambo wake ndipo kapolo amaopa mbuye wake. Ngati Ine ndine bambo wanu, nanga ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiwopa kuli kuti, Ansembe inu, amene mumanyoza dzina langa. Komabe mumanena kuti, kodi dzina lanu timalinyoza bwanji?
Iyeyo adzayanjanitsa atate ndi ana ao, ana ndi atate ao, kuwopa kuti ndingadzabwere kudzatemberera dziko lanu kuti liwonongeke.”
lemekeza atate ako ndi amai ako, ndiponso konda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
“Kodi inu, mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana aamuna aŵiri. Adapita kwa woyamba, nakamuuza kuti, ‘Mwana wanga, pita ukagwire ntchito m'munda wamphesa lero.’ Iyeyo adati, ‘Toto ine.’ Koma pambuyo pake adasintha maganizo, napitadi. Wina akakakufunsani kanthu, inu mukati, ‘Ambuye ali nawo ntchito, akangothana nawo aŵatumiza nthaŵi yomweyo.’ ” Bambo uja adapita kwa mwana wina uja, nakamuuza mau omwe aja. Iyeyo adati, ‘Chabwino atate,’ koma sadapite. Kodi mwa aŵiriwo, yemwe adachita zimene bambo wake ankafuna ndi uti?” Iwo adati, “Woyamba uja.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti okhometsa msonkho ndi akazi adama akuloŵa mu Ufumu wa Mulungu inu nkumakusiyani m'mbuyo.
Malamulo ukuŵadziŵa: Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, usadyerere mnzako, lemekeza atate ako ndi amai ako.”
Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankaŵamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake.
Malamulo ukuŵadziŵa: Usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, lemekeza atate ako ndi amai ako.”
Pamene Yesu adaona amai ake ndi wophunzira uja amene Iye ankamukonda kwambiri, akuimirira pafupi, adauza amai ake kuti, “Mai, nayu mwana wanu.” Adauzanso wophunzirayo kuti, “Naŵa amai ako.” Ndipo kuyambira pamenepo wophunzirayo adaŵatenga amaiwo kumakaŵasamala kwao.
Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”
Koma ngati mai wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wao pa banja lao moopa Mulungu, kuti pakutero abwezere makolo ao zimene adalandira kwa iwo. Pakuti zimenezi Mulungu amakondwera nazo akamaziwona.
Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.
Koma ngati mai wina aliyense wachikhristu ali ndi achibale amene ali azimai amasiye, aziŵasamala iyeyo, osasenzetsa mpingo katundu wakeyo. Motero mpingo udzatha kusamala azimai amasiye opanda oŵathandiza.
Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu.
Tinali nawo azibambo athu apansipano amene ankatilanga, ndipo tinkaŵalemekeza. Kwenikweni tsono tikadayenera kugonjera Mulungu, Atate a mizimu, kuti tikhale ndi moyo.
Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”
Munthu aliyense wotemberera bambo wake ndi mai wake ayenera kuphedwa. Munthu ameneyo watemberera bambo wake ndi mai wake, tsono magazi ake akhale pa iyeyo.
Tiyese kuti wina ali ndi mwana wokanika ndiponso wachipongwe, mwana woti bambo ndi mai ake saŵamvera konse, ngakhale amlange chotani. Makolo ake a mwanayo amgwire ndi kupita naye kwa akuluakulu amumzinda ku chipata cha mzindawo. Akuluakulu anu ndi aweruzi anu apiteko, ndipo akayese kutalika kwake kuchokera pamalo pamene pali munthu wakufayo mpaka ku mizinda yoyandikana ndi malowo. Makolowo auze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu ndi wokanika ndipo ndi wachipongwe safuna kutimvera, ndi wadyera ndiponso chidakwa. Pamenepo anthu amumzindawo amuphe pakumponya miyala, motero mudzachotsa choipa pakati panu. Anthu onse a mu Israele muno akadzamva zimene zachitikazi, adzakhala ndi mantha.”
Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu.
Tsono Davide adanyamuka m'mamaŵa, nasiyira nkhosa munthu wina wozisunga. Adatenga zakudyazo napita, monga momwe bambo wake adaamlamulira. Adafika ku zithando pamene ankhondo ankandanda pa mzere wankhondo, nkufuula mfuu wankhondo.
Tsono zakudya zija Davide atasiyira munthu wosunga katundu, adathamangira kumene kunali ankhondo, nakalonjera abale ake.
Choncho Bateseba adapita kwa mfumu Solomoni kukalankhula naye m'malo mwa Adoniya. Solomoni adanyamuka kuti akumane naye, ndipo adaŵeramira mai wakeyo. Adakhala pa mpando wake waufumu, ndipo adaitanitsa mpando wina kuti mai wake akhalepo. Tsono mai uja adakhala ku dzanja lamanja la mfumuyo.
Yeremiya adauza Arekabu aja mau a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, “Chifukwa chakuti mudamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndipo mudatsata malangizo ake ndi kuchita zonse zimene adakuuzani kuti muchite, tsono Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasoŵa mdzukulu wonditumikira mpaka muyaya.’ ”
Aka nkachitatu tsopano kukonzeka kuti ndibwere kwanuko, ndipo sindidzakhala ngati katundu wokulemetsani. Sindikufuna zinthu zanu, koma ndikufuna inuyo. Pakuti si udindo wa ana kusungira makolo ao chuma, koma ndi udindo wa makolo kusungira ana ao chuma.
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.
Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa.
Patapita masiku atatu, adampeza m'Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera mau ao, ndi kumaŵafunsa mafunso. Onse amene ankamva mau ake, ankadabwa ndi mayankho ake anzeru.
“Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona. Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’ Koma bambo wake adauza antchito ake kuti, ‘Thamangani mukatenge mkanjo wabwino kwambiri, mumuveke. Mumuvekenso mphete ku chala, ndi nsapato ku mapazi. Ndipo katengeni mwanawang'ombe wonenepa uja, muphe kuti tidye, tikondwere. Chifukwa mwana wangayu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ Ndiye pompo chikondwerero chidayamba.
Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana, koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako.
Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru, koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi.
Uzimlanga mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere mu mtima, adzakondweretsa mtima wako m'tsogolo.
Sitidzabisira ana ao, koma tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo ntchito zotamandika za Chauta, tidzaŵasimbira mphamvu zake ndi zodabwitsa zimene wakhala akuchita. Kaŵirikaŵiri ankamuukira m'chipululu, ankamumvetsa chisoni. Kaŵirikaŵiri ankamuyesa, ankamputa Woyera wa Israele. Sadakumbukire mphamvu zake kapena tsiku limene adaŵaombola kwa adani ao, pamene Iye adachita zizindikiro zamphamvu ku Ejipito, ndiponso zozizwitsa zake ku dera la ku Zowani. Paja Mulungu adasandutsa madzi a mitsinje yao kuti akhale magazi, kotero kuti Aejipito sadathe kumwa madziwo. Adaŵatumira nthenje za ntchentche zimene zidaŵazunza, ndiponso achule amene adasakaza dziko lao. Adalola kuti kapuchi adye mbeu zao ndiponso kuti dzombe lidye zonse za m'minda mwao. Adaononga mphesa zao ndi matalala ndiponso mitengo yao yankhuyu ndi chisanu. Adalola kuti ng'ombe zao zife ndi matalala ndi kuti nkhosa zao zife ndi zing'aning'ani. Adagwetsa moto wa ukali wake pa iwo: adaŵapsera mtima naŵakwiyira nkuŵagwetsera mavuto. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo oononga. Adapereka mau odzichitira umboni kwa Yakobe, adakhazikitsa malamulo ake mu Israele. Adalamula makolo athu kuti aziŵaphunzitsa ana ao malamulowo. Adalola kukwiya, osadziletsa, sadaŵapulumutse ku imfa, koma adapereka moyo wao ku miliri. Adapha ana achisamba onse a Aejipito, ana oyamba a mphamvu zao, m'zithando za zidzukulu za Hamu. Tsono Mulungu adaŵatulutsa anthu ake ngati nkhosa, naŵatsogolera m'chipululu ngati zoŵeta. Adaŵatsogolera bwino lomwe kotero kuti sanalikuwopa, koma nyanja idamiza adani ao. Adaŵafikitsa ku dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene adaŵagonjetsera ndi dzanja lake lamphamvu. Adapirikitsa mitundu ina ya anthu, kuŵachotsa m'njira. Adagaŵagaŵa dziko la anthuwo kuti likhale la anthu ake, adakhazikitsa mafuko a Israele m'midzi ya anthuwo. Komabe Aisraele adamuputa ndi kumuukira Mulungu Wopambanazonse, sadasunge malamulo ake, koma iwo adakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo ao. Adapotoka ngati uta wosakhulupirika. Iwo adakwiyitsa Mulungu ndi akachisi ao opembedzerako mafano ku mapiri. Adamupsetsa mtima chifukwa cha mafano ao osemawo. Pamene Mulungu adamva zimenezi, adakwiya kwambiri, ndipo adakana Aisraele kotheratu. Motero mbadwo wakutsogolo wa ana amene sanabadwebe, udzaŵadziŵa, ndipo nawonso udzafotokozera ana ake. Adasiya malo ake a Silo kumene ankakhala, adasiya hema limene ankakhalamo pakati pa anthu, ndipo adalola adani athu kuti alande Bokosi la Chipangano chake, limene linali chizindikiro cha mphamvu zake ndi ulemerero wake. Chifukwa adakwiyira anthu ake, adalola kuti anthu akewo aphedwe pa nkhondo. Nkhondo yoyaka ngati moto idaononga anyamata ao, ndipo atsikana ao adasoŵa oŵaimbira nyimbo zaukwati. Ansembe ao omwe adaphedwa ndi lupanga, ndipo akazi ao amasiye sadaŵalole kulira maliro. Pomaliza Ambuye adachita ngati kudzuka kutulo, ngati munthu wamphamvu wofuula chifukwa choledzera. Tsono Mulungu adaŵapirikitsa adani ake, naŵachititsa manyazi anthaŵizonse. Adakana banja la Yosefe, sadasankhule fuko la Efuremu. Koma adasankhula fuko la Yuda, ndiponso phiri la Ziyoni limene amalikonda. Adamanga malo ake opatulika ngati malo ake akumwamba, okhazikika ngati dziko lapansi mpaka muyaya. Anawo aike chikhulupiriro chao pa Mulungu, ndipo asaiŵale ntchito za Mulungu, koma asunge malamulo ake.
Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.
Ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene muti mudzamtumikire, kapena ndi milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m'dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.”
Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.
Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka.
Mwana wanga, mvera mau anga, malamulo anga akhale chuma chako. Ndiye mkazi adadzakumana naye, atavala ngati mkazi wadama, wa mtima wonyenga. Mkaziyo ndi wosakhazikika ndi wopanda manyazi, kamwendom'njira wosakhala pakhomo. Mwina umpeza pa mseu, mwina pa msika, amachita kukhalizira munthu pa mphambano iliyonse. Tsono amamgwira mnyamata uja, nkumumpsompsona, amalankhula naye ndi nkhope yopanda manyazi kunena kuti, “Ndinayenera kupereka nsembe, ndipo lero ndachita zimene ndidazilumbirira. Motero tsopano ndabwera kuti ndidzakumane nawe, ndinkakufunafuna, tsono ndakupeza. Pabedi panga ndayalapo zofunda zabwino, pali nsalu zabafuta zamaŵangamaŵanga za ku Ejipito. Pomweponso ndawazapo zonunkhira za mure, ndi mankhwala a fungo lokoma a aloyi, ndi a sinamoni. Bwera tsono, tikhale malo amodzi mpaka m'maŵa, tisangalatsane ndi chikondi. Mwamuna wanga kulibe, ali pa ulendo wautali. Utsate malamulo anga, ndipo udzakhala ndi moyo. Usamale malangizo anga monga umachitira ndi maso ako. Adatenga thumba la ndalama, adzabwerako mwezi utakhwima.” Amamkopa mnyamatayo ndi mau onyengerera, amamkakamiza ndi mau ake oshashalika. Pamenepo mnyamatayo amatsatira mkaziyo monga momwe ng'ombe imapitira kokaphedwa, kapena monga momwe mbaŵala imakodwera mu msampha, mpaka muvi kuilasa m'mimba mwake. Amakhala ngati mbalame yothamangira m'khwekhwe, osadziŵako kuti aferapo. Ndiye tsopano ana inu, mundimvere ine, mutchere khutu pa zimene ndinene ine. Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyo, musasokere potsata njira zakezo. Paja iye uja adagwetsa amuna ambiri, anthu amene adaŵaphetsa ngosaŵerengeka. Nyumba yake ndi njira yakumanda, yotsikira ku dziko la anthu akufa. Achite ngati waŵamangirira ku chala, ngati waŵadinda mumtima mwako.
“Ndipo tsopano, ana anga, tamverani, ngodala anthu amene amasunga malangizo anga. Muzimva malangizo, kuti muzikhala anzeru, musamanyozere mau anga.
Wovutitsa a m'nyumba mwake adzaloŵa m'mavuto, chitsiru chidzasanduka kapolo wa munthu wanzeru.
Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake. Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu. Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba. Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali.
Wokonda nzeru amasangalatsa atate ake, koma amene amayenda ndi akazi adama amamwaza chuma chake.
Akhale wodziŵa kuyendetsa bwino banja lake, ndi kulera bwino ana ake, kuti akhale omvera ndi aulemu kwenikweni.
Atumiki a mpingo akhale a mkazi mmodzi yekha. Akhale olera ana ao bwino, oyendetsanso bwino mabanja ao.
Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu. Mau ako akhale oona, kuti anthu asadzathe kuŵatsutsa. Motero wotsutsana nawe adzachita manyazi, atasoŵa kalikonse koipa kuti atinenere.
Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.
Tandimverani tsono, ndikulangizeni, ndipo Mulungu adzakhala nanu. Inu muyenera kuima m'malo mwa anthu pamaso pa Mulungu ndi kubwera ndi makangano ao kwa Iye. Motero adabwera ndi Zipora, mkazi wa Mose, amene Moseyo anali atamsiya. Muyenera kuŵaphunzitsa mau ndi malamulo a Mulungu, ndi kuŵafotokozera m'mene azikhalira ndi m'mene azichitira. Komanso sankhulani amuna anzeru, ndipo muŵaike kuti akhale atsogoleri a anthu, motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe. Ayenera kukhala anthu oopa Mulungu, okhulupirika, ndiponso osakopeka ndi ziphuphu. Iwo ndiwo aziweruza anthu nthaŵi zonse. Azibwera ndi milandu yovuta yokha kwa inu, koma timilandu ting'onoting'ono aziweruza okha. Adzakuchepetserani ntchito iwowo pakusenza katunduyo pamodzi nanu. Mukachita zimenezi monga Mulungu akulamulira, simudzafooka, ndipo anthu onseŵa adzatha kumabwerera kwao, zao zonse zitakonzeka.” Mose adamvera zonse zimene adanena Yetero zija.
Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Akamadzandichimwira, ndizidzamulanga monga m'mene bambo amalangira ana ake.
Mwana wanga, uvomere mau anga, ndi kusunga bwino malamulo anga. Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako, kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa. Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza. Nzeruyo idzakupulumutsa ku mayendedwe oipa, idzakuteteza kwa amtherakuŵiri, amene amasiya njira zolungama, namayenda m'njira zamdima. Iwoŵa amakondwa pochita zoipa, amasangalala ndi ntchito zosalungama. Anthu ameneŵa njira zao nzokhotakhota, makhalidwe ao ngonyenga. Udzapulumuka kwa mkazi wadama, kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika, amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta, kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake. Pakuti nyumba yake imatsenderekera ku imfa, njira zake zimamufikitsa kwa anthu akufa. Opita kwa iye, palibe ndi mmodzi yemwe wobwerako, sazipezanso njira zopita ku moyo. Uzitchera khutu ku nzeru, uziikapo mtima pa kumvetsa zinthu.
Uzimlanga mwana wako chikhulupiriro chikadalipo, ukapanda kutero, wamuwononga. Munthu wa ukali woopsa adzalandira chilango chomuyenerera, pakuti ukamlekerera wotereyu, zidzaipa koposa kale.
Muyenera kuŵaphunzitsa mau ndi malamulo a Mulungu, ndi kuŵafotokozera m'mene azikhalira ndi m'mene azichitira.
ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.
Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu.
Ndipo amene adandituma, ali nane pamodzi. Iye sadandisiye ndekha, chifukwa nthaŵi zonse ndimachita zomkondweretsa.”
Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko.
Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.
Ndipo Yesu analikunka nakula m'nzeru ndi mu msinkhu, ndipo Mulungu ndi anthu omwe ankakondwera naye kwambiri.
Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani. Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.