M’busa wabwino amagawana malangizo a Mawu a Mulungu chifukwa akufuna kutumikira ndi kutipatsa chakudya chauzimu chomwe chingatithandize kukhala ndi moyo wochuluka umene Yesu analonjeza: "Wakuba sabwera koma kudzaba, kupha ndi kuwononga; Ine ndinabwera kuti akhale nao moyo, ndi kuti akhale nao wochuluka." (Yohane 10:10).
Abusa ndi akulu ampingo apatsidwa udindo wotsogolera ndi kusamalira mamembala a mpingo. Choncho, tiyenera kuwamvera, monga momwe tikulimbikitsidwira pa Ahebri 13:17: "Mverani abusa anu, nimugonjere kwa iwo; pakuti iwo akuyang'anira miyoyo yanu, monga amene adzayankha mlandu; kuti achite ichi ndi chimwemwe, osati modandaula, pakuti ichi sichikupindulitsani."
Mulungu amasangalala ndi kumvera kwa ana ake, ndipo kumvera abusa athu ndi chizindikiro cha ubale wathu ndi Mulungu. Kumvera kumatanthauza kutsatira popanda kukayikira, popanda kudzudzula, ndi popanda tsankho, ndi mtima wonse. Mwanjira imeneyi, tidzalandira mphoto kuchokera kwa Yesu ndipo miyoyo yathu idzakhala yotetezeka m'malonjezo ake.
Tisaiwale kupempherera abusa athu nthawi zonse, kuti azitsogoleredwa ndi kulimbikitsidwa ndi Mzimu Woyera. Tilemekeze miyoyo yawo ndipo tikhale okonzeka kuwatumikira.
Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.
Muzikumbukira atsogoleri anu amene ankakulalikirani mau a Mulungu. Muzilingalira za moyo wao ndi m'mene adafera, ndipo muzitsanzira chikhulupiriro chao.
Tandimverani tsono, ndikulangizeni, ndipo Mulungu adzakhala nanu. Inu muyenera kuima m'malo mwa anthu pamaso pa Mulungu ndi kubwera ndi makangano ao kwa Iye.
Motero adabwera ndi Zipora, mkazi wa Mose, amene Moseyo anali atamsiya.
Muyenera kuŵaphunzitsa mau ndi malamulo a Mulungu, ndi kuŵafotokozera m'mene azikhalira ndi m'mene azichitira.
Komanso sankhulani amuna anzeru, ndipo muŵaike kuti akhale atsogoleri a anthu, motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe. Ayenera kukhala anthu oopa Mulungu, okhulupirika, ndiponso osakopeka ndi ziphuphu.
Iwo ndiwo aziweruza anthu nthaŵi zonse. Azibwera ndi milandu yovuta yokha kwa inu, koma timilandu ting'onoting'ono aziweruza okha. Adzakuchepetserani ntchito iwowo pakusenza katunduyo pamodzi nanu.
Mukachita zimenezi monga Mulungu akulamulira, simudzafooka, ndipo anthu onseŵa adzatha kumabwerera kwao, zao zonse zitakonzeka.”
Mose adamvera zonse zimene adanena Yetero zija.
Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa.
“Kumeneko ndidzakupatsani abusa a kukhosi kwanga. Adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha.
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu amene mzimu wa Mulungu uli mwa iye, ndipo umsanjike manja.
Umuimiritse pamaso pa wansembe Eleazara ndi pamaso pa mpingo wonse, tsono umlonge m'malo mwako, iwo akupenya.
Iwoŵa adakaima pamaso pa Mose, pa wansembe Eleazara, pa atsogoleri, ndiponso pamaso pa mpingo wonse, pakhomo pa chihema chamsonkhano, nati,
Umpatseko udindo wako, kuti mpingo wonse wa Aisraele uzimumvera.
Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani.
Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.
Aliyense wosamvera wansembe amene akutumikira Chauta, Mulungu wanu, kapena wosamvera muweruzi, aphedwe. Mwa njira imeneyi mudzachotsa choipa pakati pa Aisraele.
Onsewo adayankha Yoswa kuti, “Zonse zimene mwatilamulazi tidzachita, ndipo kulikonse kumene mudzatitume, tidzapita.
Tidzakumverani monga momwe tidamverera Mose. Chauta, Mulungu wanu, akhale nanu, monga momwe adakhalira ndi Mose!
Koma Samuele adati, “Kodi Chauta amakondwa ndi chiti: nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kapena kumvera mau ake? Ndithu, ndi kumvera ndi kupereka nsembe kwabwino kwambiri nkumvera. Ndi kutchera khutu ndi kupereka mafuta ankhosa kwabwino kwambiri nkutchera khutu.
Koma Chauta adauza Samuele kuti, “Usayang'ane maonekedwe ake, ngakhale kutalika kwa msinkhu wake, poti ndamkana ameneyo. Chauta sapenya monga m'mene apenyera anthu. Anthu amapenya zakunja, koma Chauta amapenya zamumtima.”
Tsono adauza anthu ake kuti, “Chauta andiletse kumchita choipa mbuyanga, wodzodzedwa wa Chauta. Ndisampweteke, popeza kuti ngwodzozedwa wa Chauta.”
Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi.
Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.
Tsono Davide adauza msonkhano wonse kuti, “Tamandani Chauta, Mulungu wanu.” Apo anthu onsewo adatamanda Chauta, Mulungu wa makolo ao. Adaŵeramitsa mitu yao napembedza Chauta, ndipo adalambira mfumu.
Tsono anthuwo adadzuka m'mamaŵa nakaloŵa m'chipululu cha ku Tekowa. Pamene ankatuluka, Yehosafati adaima nati, “Tamverani inu anthu a ku Yuda ndi inu okhala mu Yerusalemu. Khulupirirani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalimbika, khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzapambana.”
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu.
Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako.
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.
Basi, zonse zamveka. Mfundo yeniyeni ya zonsezi ndi iyi: Uzimvera Mulungu, ndipo uzitsata malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wake wonse wa munthu.
Ngodala anthu omvera Mulungu pakuti zinthu zidzaŵayendera bwino, adzakondwera ndi phindu la ntchito zao.
Koma tsoka kwa anthu oipa! Zinthu zidzaŵaipira. Zimene akhala akuchitira anzao zomwezo zidzaŵabwerera.
Ndidzazipatsa abusa oziŵeta bwino. Sizidzaopanso kapena kuchita mantha, kapena kusokera,” akuterotu Chauta.
Chauta Wamphamvuzonse akuuza anthu kuti, “Musamvere zimene akunena aneneri, iwowo amakuloserani zonyenga. Zimene amakuuzani kuti akuziwona m'masomphenya ndi maganizo ao chabe, si zolankhula Chauta ai.
Ndidzaziikira mbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala, ndipo adzakhala mbusa wake.
‘Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimadyetsa, ndipo Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.’ ”
“Pajatu ndi ntchito ya ansembe kuphunzitsa nzeru zoona za Mulungu, anthu ayenera kupita kwa iwo kuti akaphunzire zimene Ine ndifuna, chifukwa ansembewo ndiwo amithenga a Chauta Wamphamvuzonse.
“Munthu wokulandirani inu, amandilandira Ine ndemwe. Ndipo wondilandira Ine, amalandiranso Iye uja amene adandituma.
Munthu wolandira nthumwi ya Mulungu chifukwa choti ndi nthumwi, adzalandira mphotho ya nthumwi ya Mulungu. Wolandira munthu wolungama chifukwa choti ngwolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama.
Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti olamulira amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao.
Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu.
Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu.
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Nchifukwa chake muzichita ndi kutsata zonse zimene iwo amakuphunzitsani. Komatu musamatsanzira zimene amachita, pakuti sachita zimene amaphunzitsa.
“Tsono wantchito wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adamuika kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake?
Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi.
Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse.
Yesu adauza anthu 72 aja kuti, “Wokumverani inu, akumvera Ine amene. Wokukanani inu akukana Ine amene. Ndipo wondikana Ine, akukananso Atate amene adandituma.”
Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziŵa, ndipo izozo Ineyo zimandidziŵa,
monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.
Ndithu ndikunenetsa kuti wolandira aliyense amene ndamtuma, amalandira Ine. Ndipo wondilandira Ine, amalandira Iye amene adandituma.”
Tsono atumwi khumi ndi aŵiri aja adasonkhanitsa gulu lonse la ophunzira, naŵauza kuti, “Sibwino kuti ife tizisiya kulalika mau a Mulungu nkumayang'anira za chakudya.
Nchifukwa chake abale, pakati panupa sankhanipo amuna asanu ndi aŵiri, a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndiponso ndi nzeru. Tidzapatsa iwowo ntchitoyi.
Koma ife tidzadzipereka ku ntchito ya kupemphera ndi kulalika mau a Mulungu.”
Pa mpingo uliwonse adakhazika akulu a mpingo. Ndipo pakupemphera ndi kusala zakudya adaŵapereka kwa Ambuye amene anali atamkhulupirira tsopano.
Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao.
Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira.
Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera.
Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje.
Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.
Tsono muzipereka kwa onse zimene zikukhalira iwowo: msonkho kwa okhometsa msonkho, zolipira kwa oyenera kuŵalipira. Muzilemekeza oyenera kuŵalemekeza, ndi kuchitira ulemu oyenera kuŵachitira ulemu.
Momwemonso Ambuye adalamula kuti olalika Uthenga Wabwino, azilandira zoŵasunga pakulalika Uthengawo.
Abale, mukudziŵa kuti Stefanasi ndi a m'banja mwake ndiwo adayambirira kuloŵa chikhristu m'dziko la Akaiya. Ndipo akhala akudzipereka kutumikira anthu a Mulungu.
Tsono ndikukupemphani kuti inunso muziŵamvera anthu otere, ndiponso aliyense wogwira ntchito ndi kutumikira modzipereka pamodzi nawo.
Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.
Ndipotu ngakhale mwina ndikunyadira mokakata ulamuliro umene Ambuye adatipatsa woti tikulimbitse nawoni, osati kukuwonongani ai, ndithu sindidzachita manyazi.
Munthu amene akuphunzira mau a Mulungu, agaŵireko mphunzitsi wake zabwino zonse zimene iye ali nazo.
Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.
Mudaphunzira zimenezi kwa Epafra, mtumiki mnzathu wokondedwa. Iye uja akugwirira ntchito Khristu mokhulupirika m'malo mwathu.
Inu antchito, muziŵamvera pa zonse ambuye anu apansipano. Musamangochitatu zimenezi pamene muli pamaso pao kuti akuyamikireni, koma muziŵamvera ndi mtima wonse, chifukwa choopa Ambuye.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.
Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
Ambuye amatipatsa chikhulupiriro chakuti mukuchita zonse zimene timakuuzani, ndipo kuti mudzazichitabe.
Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu akuti, “Ngati munthu afuna ntchito ya kuyang'anira Mpingo, akukhumba ntchito yaulemu.”
Iwonso ayambe ayesedwa, ndipo pambuyo pake, ngati alibe chokayikitsa, ndiye asenze udindo wa atumiki.
Momwemonso akazi akhale ochita zachiukulu, osasinjirira, odzigwira, ndi okhulupirika pa zonse.
Atumiki a mpingo akhale a mkazi mmodzi yekha. Akhale olera ana ao bwino, oyendetsanso bwino mabanja ao.
Paja anthu ogwira bwino ntchito ya utumiki, amadzitengera mbiri yabwino, ndipo amalimba mtima kwenikweni pakuika chikhulupiriro chao mwa Khristu Yesu.
Pamene ndikukulembera zimenezi, ndikuyembekeza kudzafika kwanuko posachedwa.
Koma zina zikandichedwetsa, zimene ndanenazi zidzakudziŵitsa za m'mene anthu ayenera kukhalira m'banja la Mulungu, limene lili Mpingo wa Mulungu wamoyo, ndi mzati wochirikiza choona.
Ndithudi, chinsinsi cha chipembedzo chathu nchachikulu: “Iye uja adaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu Woyera adamchitira umboni kuti ndi wolungama, angelo adamuwona, adalalikidwa pakati pa anthu a mitundu yonse, anthu a pa dziko lonse lapansi adamkhulupirira, Iyeyo adatengedwa kunka kumwamba mu ulemerero.”
Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa.
Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
Udziyang'anire bwino wekha, ndi kusamala zimene umaphunzitsa. Ulimbikire kutero, chifukwa pakuchita zimenezi udzadzipulumutsa iwe wemwe, ndiponso anthu amene amamva mau ako.
Usamamvere mau oneneza mkulu wa mpingo, pokhapokha ngati pali mboni ziŵiri kapena zitatu.
Onse amene ali mu ukapolo aziwona ambuye ao ngati oyenera kuŵachitira ulemu ndithu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndiponso zimene timaphunzitsa.
Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.
Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene popereka umboni pamaso pa Ponsio Pilato, adaanena zoona zenizeni.
Ndikukulamula kuti, mopanda cholakwa kapena chokayikitsa, utsate bwino zonse zimene udalamulidwa, mpaka Ambuye athu Yesu Khristu adzabwerenso.
Pa nthaŵi yake Mulungu adzamuwonetsa kwa ife. Mulunguyo ngwodala ndipo Iye yekha ndiye Wolamula, ndiye Mfumu ya mafumu onse, ndiponso Mbuye wa ambuye onse.
Ndiye yekha wosafa, ndipo amakhala m'kuŵala kosayandikizika. Chikhalire palibe munthu amene adamuwona, palibenso amene angathe kumuwona. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Amen.
Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo.
Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.
Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.
Amene ambuye ao ndi akhristu, asaŵapeputse poona kuti ndi abale. Kwenikweni aziŵatumikira koposa, popeza kuti amene amapindula ndi ntchito yao, nawonso ndi akhristu, ndiponso okondedwa. Uziŵaphunzitsa anthu ndi kuŵalamula ntchito zimenezi.
Uŵagwiritse mau oona amene udamva kwa ine, kuti akhale chitsanzo choti uzitsata. Uzichita zimenezi mwa chikhulupiriro ndi mwa chikondi, zimene zili mwa Khristu Yesu.
Usunge bwino zokoma zimene adakusungitsa pakutsata Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.
Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto.
Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona.
uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.
Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira.
Asunge mogwiritsa mau okhulupirika, amene ali ogwirizana ndi zimene tidaphunzitsidwa. Pakutero adzatha kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona, ndiponso kugonjetsa otsutsana nacho.
Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu.
Mau ako akhale oona, kuti anthu asadzathe kuŵatsutsa. Motero wotsutsana nawe adzachita manyazi, atasoŵa kalikonse koipa kuti atinenere.
Zimenezi ndizo zimene uyenera kumaphunzitsa. Uziŵalimbikitsa anthu, ndi kuŵadzudzula komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ai.
Ndikukulembera zimenezi, popeza kuti ndikukhulupirira kuti udzachitadi zimene ndakupempha. Ndikudziŵa kuti udzachita kopitiriranso zimene ndapemphazi.
Mutiperekereko moni kwa atsogoleri anu onse, ndi kwa anthu onse a Mulungu. Abale a ku Italiya akuti moni.
Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse.
Chifukwa cha Ambuye, muzimvera akulu onse olandira ulamuliro. Ngati ndi mfumu yaikulu koposa ija, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro pa mafumu ena onse.
Ngati ndi nduna, zimvereni chifukwa zidachita kutumidwa ndi mfumu kuti zizilanga ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino.
Tsopano ndili nawo mau akulu a mpingo amene ali pakati panu, ine mkulu mnzao. Ndinenso mboni ya zoŵaŵa za Khristu, ndipo ndikuyembekeza kudzalandira nao ulemerero umene uti udzaoneke.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Iye ndiye mwini mphamvu mpaka muyaya. Amen.
Kalatayi ndalembetsa Silivano mwachidule. Ndimamuwona kuti ndi mbale wokhulupirika. Ndafuna kukulimbitsani mtima, ndi kuchita umboni wakuti kukoma mtima kwenikweni kwa Mulungu nkumeneku. Chifukwa cha kukoma mtimako, limbikani.
Anzanu a mu mpingo wa ku Babiloni akuti moni. Marko, mwana wanga, nayenso akuti moni.
Mupatsane moni mwachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli ake a Khristu.
Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira.
Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo.
Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”
Koma choyamba mumvetse kuti munthu payekha sangathe kumasulira mau a aneneri olembedwa m'Malembo.
Paja mau a aneneri sadadze konse ndi kufuna kwa munthu yekha, koma Mzimu Woyera adaŵalankhulitsa mau ochokera kwa Mulungu.
Komabe panali aneneri ena onama ngakhale pakati pa Aisraele omwe. Momwemonso pakati pa inu padzaoneka aphunzitsi onama. Iwowo adzaloŵetsa mwachinsinsi zophunzitsa zonama ndi zoononga, ngakhale kukana kumene Mbuye wao amene adaŵaombola, ndipo motero adzadziitanira chiwonongeko mwamsanga.
Koma ife ndife ake a Mulungu. Munthu wodziŵa Mulungu, amatimvera. Koma iye amene sali wake wa Mulungu, satimvera. Umu ndi m'mene timasiyanitsira pakati pa maganizo oona ndi maganizo onama.
Komabe anthu ameneŵa akuchita chimodzimodzi. Potsata maloto ao, amaipitsa matupi ao, amakana ulamuliro wa Mulungu, ndipo amachita chipongwe aulemerero a Kumwamba.
Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija zimene waziwona m'dzanja langa lamanja, ndi china chija cha ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide, tanthauzo lake ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija ndi atsogoleri a mipingo isanu ndi iŵiri; ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zija ndi mipingo isanu ndi iŵiri imene.”
“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Efeso umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa uja wanyamula nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m'dzanja lake lamanja, ndi kuyenda pakati pa ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide zija.
“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, ndidzampatsa mwai wodya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku Paradizo la Mulungu Kumwamba.”
Eliya adamuyankha kuti, “Chabwino, pita. Ndakuletsa ngati?” Apo Elisa adabwerera, ndipo adatenga ng'ombe zake ziŵiri nazipha. Kenaka adatenga magoli a ng'ombezo nasonkhera moto nkuphikira nyamayo, ndipo adaipereka kwa anthu kuti adye. Pambuyo pake adanyamuka namayenda ndi Eliya ndi kumamtumikira.
Pamene a m'gulu la aneneri amene ankakhala ku Yeriko adaona Elisayo akuwoloka, adati, “Mphamvu ndi nzeru za Eliya zaloŵa mwa Elisa.” Tsono adabwera kudzakumana naye, namgwadira Elisayo, nkuŵeramitsa mitu yao pansi.
Mulungu adasankhula Davide mtumiki wake, ndipo adakamtenga ku makola a nkhosa.
Adamtenga kumene ankaŵeta nkhosa zimene zinali ndi ana, kuti adzakhale mbusa wa Yakobe, fuko lake, wa Israele, choloŵa chake.
Davide adaŵasamala ndi mtima wolungama, naŵatsogolera ndi dzanja lake mwaluso.
Munthu wovomera malangizo, zinthu zidzamuyendera bwino, ndi wodala amene amadalira Chauta.
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
“Mudziŵe kuti iye uja ndidamsankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu, kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira anthu ambiri.
Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
“Tsoka kwa mbusa wanga wopandapakeyo, amene amasiya nkhosa! Amkanthe ndi lupanga pa mkono, ndi pa diso lake lakumanja. Mkono wakewo ufwape, ndipo diso lakelo lichite khungu kotheratu!”
Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika.
Pa zonse ndakuwonetsani kuti pakugwira ntchito kolimba motere, tiyenera kuthandiza ofooka. Kumbukirani mau aja a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupatsa kumadalitsa munthu koposa kulandira.’ ”
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu.
Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.
Mulungu mwa mphamvu zake adatipatsa zonse zotithandiza kukhala ndi moyo ndiponso opembedza, pakutidziŵitsa za Iyeyo amene adatiitana ku ulemerero ndi ubwino wake woposa.
Mulungu mwa chifundo chake adatipatsa ntchitoyi, nchifukwa chake sititaya mtima.
Nthaŵi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu m'thupi mwathu, kuti moyo wake uwonekenso m'thupi mwathu.
Pakuti nthaŵi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake uwonekenso m'matupi athu amene amafa.
Motero ife timaperekedwa ku imfa, koma chimenechi chimakupatsani moyo.
Malembo akuti, “Ndidakhulupirira, nchifukwa chake ndidalankhula.” Tsono popeza kuti ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timalankhula.
Pakuti tikudziŵa kuti Mulungu amene adaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa, adzatiwukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatifikitsa pamodzi nanu pamaso pake.
Cholinga cha zonsezi nchakuti inu mupindule, ndipo kuti monga momwe anthu olandira madalitso a Mulungu akunka nachulukirachulukira, momwemonso othokoza Mulungu achulukirechulukire ndi kumchitira ulemu.
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.
Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya.
Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
Takaniratu njira zonse zochititsa manyazi zimene anthu amatsata mobisika. Sitichita kanthu monyenga kapena kupotoza mau a Mulungu; koma pakulankhula zoona poyera pamaso pa Mulungu, tifuna kuti anthu onse ativomereze m'mitima mwao.