Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

NDIME ZA CHIYERO

Mulungu akuitana ana ake kukhala oyera. Kukhala oyera ndiko kukhala opulidwa, odzipereka kwa Mulungu. Kuti tikhalebe oyera tiyenera kupewa chilichonse chomwe Mulungu sachikonda, ndipo Mawu ake ndiye chitsogozo chathu chabwino kwambiri choti tidziwe zimenezo. Werengani Mawu ake tsiku lililonse ndipo mudzamudziwa bwino Mulungu. Mukatero, mudzadziwa chabwino ndi choipa, chomwe chimakufikitsani pafupi ndi Ambuye komanso chomwe chimakutalikirani.

(Masalimo 119:9) Mnyamata adzayeretse bwanji njira yake? Ndi kusunga mawu anu. Yesu Khristu anapereka moyo wake chifukwa cha ife kuti atiyeretse ndi kutikhala oyera. Ngati mumakondadi Atate wanu wakumwamba, mudzapewa chilichonse chomwe chimakutalikirani kwa Iye. Mudzakhala osamala tsiku lililonse ndipo mudzafune kukhala oyera pa chilichonse chomwe muchita.

Tsiku lililonse muyenera kufunafuna kuyera kumene Mulungu akuitanani kuti mukaone Iye. Mawu ake amati: Fufuzani mtendere ndi onse, ndi chiyero; popanda icho palibe munthu adzaona Ambuye. (Ahebri 12:14) Atate wanu wakumwamba akuyuna kuti mukaonekere pamaso pake muli oyera, kuti muchotse chilichonse chomwe chimadetsa thupi lanu ndi mzimu wanu. Mu gawo lino mupeza mavesi ambiri okhudza kuyera ndi kufunika kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


1 Yohane 5:21

Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 24:23

Yoswa adatinso, “Chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu, ndipo muzipembedza Chauta, Mulungu wa Israele, mokhulupirika.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 15:8-9

“ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutali ndi Ine.

Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni ndi malamulo a anthu chabe.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 10:18

Pakuti munthu wovomerezeka, si amene amadzichitira yekha umboni, koma amene Ambuye amamchitira umboni.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 4:5

Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 42:8

Ine ndine Chauta, dzina langa nlimenelo. Ulemerero wanga sindidzapatsa wina aliyense. Mayamiko oyenera Ine, sindidzalola kuti mafano alandireko.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:3-5

“Usakhale ndi milungu ina, koma Ine ndekha.

“Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko.

Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:4-5

“Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko.

Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 19:4

Musabwerere ku mafano, kapena kudzipangira nokha milungu ya zitsulo zosungunula. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:23

Musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide, kuti muziipembedzera kumodzi ndi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 5:8-9

“Usadzipangire fano kufanizira kanthu kolengedwa kalikonse kakumwamba, kapena ka pa dziko lapansi, kapena ka m'madzi a pansi pa dziko.

Usagwadire fano lililonse kapena kulipembedza, chifukwa Ine, Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, sindilola kuti wina apikisane nane. Ndimalanga amene adana nane. Ndimalanganso zidzukulu zao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 26:1

“Musadzipangire mafano ndipo musaimike zithunzi zosema kapena miyala yachipembedzo. Musaimiritse miyala yosema mwachithunzi m'dziko mwanu kuti muziipembedza. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 24:15

Ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene muti mudzamtumikire, kapena ndi milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m'dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 5:7-9

“Usapembedze Mulungu wina, koma Ine ndekha.

“Usadzipangire fano kufanizira kanthu kolengedwa kalikonse kakumwamba, kapena ka pa dziko lapansi, kapena ka m'madzi a pansi pa dziko.

Usagwadire fano lililonse kapena kulipembedza, chifukwa Ine, Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, sindilola kuti wina apikisane nane. Ndimalanga amene adana nane. Ndimalanganso zidzukulu zao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:10

Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 15:7-9

Inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaati,

“ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutali ndi Ine.

Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni ndi malamulo a anthu chabe.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 23:13

Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 4:8

Kale simunkadziŵa Mulungu, nchifukwa chake munkatumikira zomwe sizili milungu konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 4:24

Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 18:21

Eliya adasendera pafupi ndi anthu onsewo, naŵafunsa kuti, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iŵiri mpaka liti? Ngati Chauta ndiye Mulungu, mtsateni. Koma ngati Baala ndiye Mulungu, tsatani iyeyo.” Anthuwo sadamuyankhe ndi liwu limodzi lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 16:4

Amene amasankhula milungu ina, amadzichulukitsira mavuto. Sindidzatsira nawo nsembe zao zamagazi kapena kutchula maina a milungu yaoyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yona 2:8

Anthu opembedza milungu yachabe amataya kukhulupirika kwao.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 20:11

Ahabu, mfumu ya ku Israele, adayankha kuti, “Kamuuzeni kuti, ‘Mwamuna mnzako mpachulu, kulinga utakwerapo. Wankhondo weniweni ndi amene amadzitama atapambana, osati asanamenye nkhondo.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 4:8-9

Kale simunkadziŵa Mulungu, nchifukwa chake munkatumikira zomwe sizili milungu konse.

Koma tsopano mukumdziŵa Mulungu, makamaka ndinene kuti Mulungu ndiye akudziŵa inu. Nanga bwanji mukubwereranso ku miyambo yachabe ndi yopanda phindu ija? Bwanji mukufuna kukhalanso akapolo ake?

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 17:16

Motero adasiya malamulo onse a Chauta Mulungu wao, nadzipangira mafano aŵiri osungunula anaang'ombe. Adapanganso mafano ena a Asera namapembedza zinthu zakumlengalenga ndiponso Baala.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 11:2

Ine ndikamakangaza kumuitana, iye ndiye kumandithaŵa kunka kutali. Ankaperekabe nsembe kwa Baala ndi kulitenthera lubani fanolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:25

Adasiya zoona za Mulungu namatsata zabodza. Adayamba kupembedza ndi kutumikira zolengedwa m'malo mwa kupembedza ndi kutumikira Mlengi mwini, amene ali woyenera kumlemekeza mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:36-38

Adatumikira mafano ao amene adasanduka msampha kwa iwo.

Adapereka nsembe ana ao aamuna ndi aakazi kwa mizimu yoipa.

Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 29:13

Ambuye adati, “Anthu aŵa amati amapemphera kwa Ine, koma mau ao ndi opanda tanthauzo, ndipo mitima yao ili kutali ndi Ine. Chipembedzo chao ndi kungotsata chabe malamulo ongoŵaloŵeza pamtima, malamulo ochokera kwa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 115:4-8

Koma mafano ao ndi asiliva ndi agolide, opangidwa ndi manja a anthu.

Pakamwa ali napo, koma salankhula. Maso ali nawo, koma sapenya.

Makutu ali nawo, koma saamva. Mphuno ali nazo, koma sanunkhiza.

Manja ali nawo, koma akakhudza, samva kanthu. Miyendo ali nayo, koma sayenda, ndipo satulutsa ndi liwu lomwe kukhosi kwao.

Anthu amene amapanga mafanowo amafanafana nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 22:15

Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:20

Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 10:1-5

Inu Aisraele, imvani mau amene Chauta akukuuzani,

Koma Chauta ndiye Mulungu woona, Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo ndiponso Mfumu yamuyaya. Dziko lapansi limagwedezeka ndi ukali wa Chauta. Anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.

Anthuwo mukaŵauze kuti, “Milungu imene sidalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzaonongeka ponseponse, pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.”

Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba.

Iye akalankhula, kumamveka mkokomo wa madzi kumwamba, ndiye amene amadzetsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amang'animitsa mphezi za mvula, amakunthitsa mphepo kuchokera kumene amaisunga.

Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza mwa iwo mulibe konse moyo.

Mafanowo ngachabechabe, ayenera kuŵaseka, ndipo pamene anthuwo adzalangidwe, mafanowo adzaonongeka.

Koma Iye uja amene ali choloŵa cha Yakobe sali ngati mafanowo, Iye ndiyedi Mlengi wa zonse. Aisraele ndi anthu ake amene Iye adaŵasankha, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.

Tolatolani katundu wanu, osamsiyanso pansi, inu amene adani akuzingani ndi zithando zankhondo.

Chauta akunena kuti, “Tsopano ndichotsa anthu onse a m'dziko lino. Ndidzaŵagwetsa m'mavuto, mpaka aŵamve ndithu.”

Ali apa amvekere, “Kalanga ine chifukwa cha kupweteka koopsa! Bala langa ndi lomvetsa chisoni. Kale ndinkati chimenechi ndi chilango changa, ndingochipirira basi.”

Chauta akuti, “Musatsate makhalidwe a anthu a mitundu ina. Musachite mantha ndi zizindikiro zozizwitsa zamumlengalenga, ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha zimenezi.

Hema langa laonongeka, zingwe zake zonse zaduka. Ana anga andisiya ndipo kulibenso. Palibenso wina woti nkundikhomera hema, kapena woti nkufunyulula nsalu zake.

Paja abusa ndi opusa, sapempha nzeru kwa Chauta. Nchifukwa chake zinthu sizidaŵayendere bwino, ndipo nkhosa zao zidabalalika.

Tamvani, kukubwera mphekesera. Kumpoto kukuchokera chinamtindi chosokosa chodzasakaza mizinda ya Yuda, kuti isanduke bwinja, mokhala nkhandwe basi.

Inu Chauta, ndikudziŵa kuti moyo umene ali nawo munthu si wake. Munthu sangathe kudzitsogolera yekha.

Langizeni, Inu Chauta, koma mwachilungamo. Musandikwiyire kuti mungandiwononge.

Ukali wanu uyakire mitundu imene sikudziŵani, ndiye kuti anthu amene satama dzina lanu mopemba. Iwo adasakaza anthu anu ndi kuŵaononga kotheratu ndipo dziko lao adalisandutsa bwinja.

Ndithudi, miyambo ya anthu a mitundu inayo nzopanda pake. Iwo aja amakadula mtengo ku nkhalango, munthu waluso namausema ndi nsompho.

Anthu ena amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide, kenaka nkuchikhomerera ndi misomali, kuti chisagwedezeke.

Mafano aowo ali ngati kangamunthu woopsera mbalame m'munda wa minkhaka, sangathe nkulankhula komwe. Ayenera kuŵanyamula, poti sangayende okha. Musaŵaope, chifukwa sangakuchiteni choipa. Alibenso mphamvu zochitira zabwino.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 10:14

Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza mwa iwo mulibe konse moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 17:35

Chauta adaachita nawo Aisraele chipangano naŵalamula kuti, “Musapembedze milungu ina kapena kuilambira kapena kuitumikira, kapena kuiperekera nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 14:4-5

Tsono uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ngati Mwisraele wina aliyense aika mtima pa mafano ake, naikanso maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, kenaka nkupita kwa mneneri, Ineyo Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha moyenerana ndi kuchuluka kwa mafano ake.

Ndidzatero kuti mwina mwake nkukopanso mitima ya Aisraele amene andisiya chifukwa cha mafano ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 14:6

“Nchifukwa chake uŵauze Aisraele kuti Ineyo Ambuye Chauta ndikunena kuti, ‘Lapani, mulekane nawo mafano anu. Muzisiye zonyansa zanu zonse.’

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 4:9

Tsono adamuuza kuti, “Zonsezi ndidzakupatsani mukagwada pansi ndi kundipembedza.”

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:30-31

“Tsono uŵauze Aisraele kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Kodi mudzadziipitsa monga momwe makolo anu adachitira ndi kusokera popembedza milungu yao yonyansa?

Pamene mubwera ndi mphatso zanu, ndi kumapereka ana anu kuti akhale nsembe zopsereza, mumadziipitsa potumikira mafano anu ambirimbiri mpaka lero lino. Kodi Aisraele inu, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Pali Ine ndemwe Chauta wamoyo, sindidzalola zoterezi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:36-39

Adatumikira mafano ao amene adasanduka msampha kwa iwo.

Adapereka nsembe ana ao aamuna ndi aakazi kwa mizimu yoipa.

Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo.

Adadzidetsa ndi ntchito zao, nakhala osakhulupirika pa zochita zao ngati mkazi wachigololo.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 19:10

Apo ndidadzigwetsa ku mapazi ake kuti ndimpembedze. Koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ndiponso ngati abale ako amene amachitira Yesu umboni. Iwe pembedza Mulungu.” Pajatu kuchitira Yesu umboni ndiye thima la uneneri.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 2:20-23

Mudafa pamodzi ndi Khristu, ndiye kuti simulamulidwanso ndi miyambo ya dziko lapansi. Tsono bwanji mukuchita ngati kuti moyo wanu ukudalirabe zapansipano? Bwanji mukuŵamvera malamulo onga aŵa akuti,

“Usagwire chakuti”, “Usakhudze chakuti”?

Malamulo ameneŵa ndi zophunzitsa zimenezi ndi za anthu chabe, ndipo zimangokhudza zinthu zimene zimatha, anthu akamazigwiritsa ntchito.

Kwinaku mauwo amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamula anthu zambiri pa za kupembedza, za kudzichepetsa ndi za kuzunza thupi lao. Komabe malamulowo alibe phindu, ndipo sathandiza konse kugonjetsa khalidwe longosangalatsa thupi.

Mutu    |  Mabaibulo
Oweruza 7:2

Chauta adauza Gideoni kuti, “Anthu uli nawoŵa andichulukira kwambiri, kuti ndigonjetse Amidiyani, chifukwa Aisraele angamandipeputse Ine ndi kumanena kuti, ‘Tadzipulumutsa ndi mphamvu zathu.’

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 4:23-24

Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza.

Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.”

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 17:29

“Tsono popeza kuti tili ngati ana a Mulungu, sitiyenera kuganiza kuti umulungu wake umafanafana ndi fano lagolide kapena lasiliva kapena lamwala, lopangidwa mwa luso ndi nzeru za munthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 6:6-8

Kodi nditenge chiyani kuti ndifike pamaso pa Chauta, kuti ndikapembedze Mulungu Wakumwamba? Kodi nditenge anaang'ombe a chaka chimodzi kuti ndipereke nsembe zopsereza?

Kodi Chauta adzakondwera ndi nkhosa zamphongo zikwi zingapo kapena mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndidzapereke mwana wanga wachisamba chifukwa cha zolakwa zanga? Kodi mwana wanga adzakhale nsembe yolipira tchimo langa?

Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 13:14-15

Chinkanyenganso anthu okhala pa dziko lapansi ndi zozizwitsa zimene chidaaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Chinkauza anthu okhala pa dziko lapansiwo kuti apange fano lolemekezera chilombo chimene chidaavulazidwa ndi lupanga, koma nkukhalabe moyo.

Chidaaloledwa kuuzira mpweya wopatsa moyo mu fano la chilombo choyamba chija, kuti mpaka lizilankhula, ndi kuphetsa aliyense wosalipembedza.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:13-15

Musabwere nazonso nsembe zanu zachabechabe. Utsi wake umandinyansa. Sindingapirire misonkhano yanu yamapemphero, kapenanso zikondwerero za pokhala mwezi ndi za Sabata, sindingapirire mapemphero oipitsidwa ndi machimo.

Zikondwerero zanu za pokhala mwezi ndi masiku anu oyera ndimadana nazo. Zasanduka katundu wondilemera, ndatopa nako kuŵapirira.

Mukamatambasula manja anu popemphera, sindidzayang'anako. Ngakhale muchulukitse mapemphero anu chotani, sindidzasamalako, chifukwa manja anu ndi odzaza ndi magazi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 10:12

Sikuti timayesa kudzilinga kapena kudziyerekeza ndi ena amene amadzichitira okha umboni. Amapusa chabe pakungodziyesa ndi muyeso waowao, ndi kudzilinganiza ndi anzao a m'gulu lao lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 4:10

Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 2:18-19

Wina aliyense asakuletseni kupata mphothoyo. Iwo aja amakonda kudziwonetsa ngati odzichepetsa, popembedza amatamanda angelo. Amaika mtima pa zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amadzitukumula popanda chifukwa, popeza kuti amangotsata nzeru za anthu,

osakangamira Khristu amene ali mutu wa Mpingo. Komatu mwa Khristu thupi lonse limalandira mphamvu, ndi kulumikizika pamodzi mwa mfundo zake ndi mitsempha yake. Motero thupi limakula monga momwe Mulungu afuna kuti likulire.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 10:14-15

Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza mwa iwo mulibe konse moyo.

Mafanowo ngachabechabe, ayenera kuŵaseka, ndipo pamene anthuwo adzalangidwe, mafanowo adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 13:15

Chidaaloledwa kuuzira mpweya wopatsa moyo mu fano la chilombo choyamba chija, kuti mpaka lizilankhula, ndi kuphetsa aliyense wosalipembedza.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 2:22

Nanga iwe wonena kuti, “Osamachita chigololo,” bwanji iwenso umachita chigololo? Iwe amene umanyansidwa ndi mafano, bwanji umaba za m'nyumba zopembedzeramo mafanowo?

Mutu    |  Mabaibulo
Malaki 1:14

Atembereredwe munthu wonyenga amene amayesa kuchita zimene adalumbirira popereka nsembe yoipa kwa Chauta, pamene ali nayo nkhosa yamphongo yabwino m'khola.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ine ndine Mfumu yaikulu, ndipo dzina langa nlochititsa mantha pakati pa anthu a mitundu yonse.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:21-23

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.

Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’

Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:1

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 12:29-31

Chauta, Mulungu wanu, akadzaononga mitundu ina imene mudzalanda dziko lao, inu mudzakhala ndi kukhazikika m'dzikomo.

Mukagwetse maguwa ao, ndipo miyala yao yoimiritsa, imene amaiyesa yopembedzerapo, mukaiphwanyephwanye. Mukatenthe mafano ao a Aserimu. Mukaonongenso mafano ao ofanizira milungu yao, ndipo mukafafanize ndi dzina lomwe la milunguyo konsekonse.

Chauta ataiwononga mitunduyo inu mukuwona, mukachenjere kuti musakatsate zipembedzo zao. Musadzayese kufunsafunsa za milungu yao kuti, “Kodi mitundu ya anthu iyi imapembedza bwanji milungu yao, kuti ifenso tichite chimodzimodzi?”

Musadzapembedze Chauta, Mulungu wanu, mofanafana ndi m'mene iwo amapembedzera milungu yaoyo. Iwo adachita zoipa zoopsa zambiri zimene Chauta amadana nazo, mpaka kutentha ana ao aamuna ndi aakazi pa moto pakuŵapereka kwa milungu yao.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:15

Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:11-15

Chauta akuti, “Kodi ndili nazo chiyani nsembe zanu zochuluka? Zandikola nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi za mafuta a nyama zonenepa. Sindikuŵafunanso magazi a ng'ombe zamphongo ndi a anaankhosa ndi a atonde.

“Ndani amakulamulani kuti mubwere nazo zimenezi pamaso panga? Ndani amakuuzani kuti muzipondaponda m'mabwalo a Nyumba yanga?

Musabwere nazonso nsembe zanu zachabechabe. Utsi wake umandinyansa. Sindingapirire misonkhano yanu yamapemphero, kapenanso zikondwerero za pokhala mwezi ndi za Sabata, sindingapirire mapemphero oipitsidwa ndi machimo.

Zikondwerero zanu za pokhala mwezi ndi masiku anu oyera ndimadana nazo. Zasanduka katundu wondilemera, ndatopa nako kuŵapirira.

Mukamatambasula manja anu popemphera, sindidzayang'anako. Ngakhale muchulukitse mapemphero anu chotani, sindidzasamalako, chifukwa manja anu ndi odzaza ndi magazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 45:20-21

Chauta akuti, “Musonkhane pamodzi ndipo mubwere. Musendere pafupi, inu nonse amene mudapulumuka kwa anthu a mitundu ina! Ndi opanda nzeru amene amanyamula mafano amitengo, namapemphera kwa milungu imene singathe kuŵapulumutsa.

Kambani, fotokozani mlandu wanu. Mupatsane nzeru nonse pamodzi. Kodi ndani adaneneratu zimene zidzachitika? Ndani adaloseratu kalekale zimenezo? Kodi si Ineyo, Chautane? Ndithu, kupatula Ine palibe Mulungu wina, Mulungu wachilungamo ndi wopulumutsa. Palibenso wina aliyense kupatula Ine.”

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:28-29

Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha.

Paja Mulungu wathu ndi moto wopsereza.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:20-21

Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana.

Simungathe kumwera m'chikho cha Ambuye nkumweranso m'chikho cha Satana. Simungathe kudyera pa tebulo la Ambuye nkudyeranso pa tebulo la Satana.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 32:16-17

Adamchititsa nsanje ndi mafano ao achilendo, ndipo zonyansa zimene adachita zidamkwiyitsa.

Iwo adapereka nsembe kwa mizimu yoipa, imene siili milungu konse, milungu imene Aisraele sadaidziŵe nkale lonse, milungu yongobwera kumene, milungu imene makolo ao sankailemekeza konse.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 6:16-17

Kodi Nyumba ya Mulungu nkufanana bwanji ndi mafano? Pajatu ife ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo, monga Mulungu mwini adanena kuti, “Ndidzakhazikika mwa iwo, ndi kukhala nawo. Ndidzakhala Mulungu wao, iwo adzakhala anthu angaanga.”

Nchifukwa chake Ambuye akuti, “Tulukani pakati pao, ndi kudzipatula. Musakhudze kanthu kosayera, ndipo ndidzakulandirani.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:4

Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 4:1

Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:5

Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 24:24

Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:1

Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:11-14

Chauta akuti, “Kodi ndili nazo chiyani nsembe zanu zochuluka? Zandikola nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi za mafuta a nyama zonenepa. Sindikuŵafunanso magazi a ng'ombe zamphongo ndi a anaankhosa ndi a atonde.

“Ndani amakulamulani kuti mubwere nazo zimenezi pamaso panga? Ndani amakuuzani kuti muzipondaponda m'mabwalo a Nyumba yanga?

Musabwere nazonso nsembe zanu zachabechabe. Utsi wake umandinyansa. Sindingapirire misonkhano yanu yamapemphero, kapenanso zikondwerero za pokhala mwezi ndi za Sabata, sindingapirire mapemphero oipitsidwa ndi machimo.

Zikondwerero zanu za pokhala mwezi ndi masiku anu oyera ndimadana nazo. Zasanduka katundu wondilemera, ndatopa nako kuŵapirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 8:16-18

Kenaka adapita nane ku bwalo lam'kati la Nyumba ya Chauta. Kumeneko, ku khomo loloŵera ku Nyumba ya Chauta, pakati pa khonde ndi guwa, kunali anthu aamuna ngati 25. Adaafulatira Nyumba ya Chautayo, nkhope zao zitaloza chakuvuma, ndipo ankapembedza dzuŵa choyang'ana kuvuma.

Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziwona zimenezi? Ayuda sakukhutira nazo zonyansa akuchita panozi. Koma akufalitsanso zandeu m'dziko lonse. Motero akuutsa ukali wanga, akundipsetsa mtima ndi zochita zao.

Tsono Ine ndidzaŵalanga ndili wokwiya. Sindidzaŵayang'ana ndi maso achifundo, ndipo sindidzaŵalekerera. Ngakhale adzalire mofuula kwa Ine, sindidzaŵamvera ai.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:24

“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:16

Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 1:6-9

Ndikudabwa kuti mukupatuka msangamsanga motere, kusiya Mulungu amene adakuitanani mwa kukoma mtima kwa Khristu, ndipo kuti mukutsata uthenga wabwino wina.

Koma palibe konse uthenga wabwino wina. Pali anthu ena amene akukusokonezani, ndipo akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wonena za Khristu.

Koma aliyense, kaya ndife kaya ndi mngelo wochokera Kumwamba, akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi uja tidakulalikiraniwu, ameneyo akhale wotembereredwa.

Ndikubwereza kunena zimene tidaanenanso kale, kuti munthu aliyense akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi Uthenga Wabwino umene mudalandira uja, iyeyo akhale wotembereredwa.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga, dzina lanu ndi loyera ndi loopsa, palibe chofanana ndi kuyera kwanu! Ndikubwerera kwa inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu chifukwa ndikufuna kukulemekezani ndi moyo wanga wonse ndi maganizo anga. Ndikukupemphani kuti mudzilemekeze pa moyo wanga, kuti kulikonse kumene ndikupita ndikhale ndi moyo woyera. Ndipo njira yanga yabwino yolalikirira ena isakhale ndi mawu okha, komanso ndi moyo wanga. Mawu anu amati: "Kuopa Yehova ndiko chiyanzitso cha nzeru; kudziwa Woyera ndiwo luntha." Atate, ndilimbitseni kuti ndikhalebe wolimbika m'pemphero. Ndithandeni kuti ndisadzisunge ndi dziko ndipo ndikhale wokonzeka kubwera kwa Ambuye wanga Yesu. Atate, mwandipanga m'chifaniziro chanu, ndithandizeni kuti ndikhale umboni wa kusintha kwanu kudzera mwa Mzimu Woyera, kuti umboni wanga waukulu wa chikondi ndi ulemu kwa inu ukhale kukhala moyo woopa Mulungu ndi wodzipereka kwa inu. M'dzina la Yesu. Amene.