Tsiku lililonse ndimasankha kukhala moyera, podziwa kuti ndine munthu wopanda ungwiro, ndili ndi zofooka zanga. Koma ndikudziwanso kuti m'magazi a Khristu ndapeza chilungamo ndi chikhululukiro chifukwa cha chisomo chake.
Kukhala moyera si nkhani yokambirana, ndi moyo umene tiyenera kusankha. Tikufuna kuwonetsa chiyero cha Mulungu, chifukwa umboni wathu udzakhala chitsanzo kwa anthu otizungulira.
Mulungu amafuna chiyero m'tchalitchi chake ndi mtima wopanda chidetso. Kudziwa chiyero cha Mulungu kumatithandiza kumudziwa Iye bwino.
Kumbukira kuti moyo woyera padziko lapansi umatikhazika moyo wosatha kumwamba. Zikomo Mulungu!
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Muzikhala oyera pamaso panga, pakuti Ine Chauta ndine woyera, ndipo ndakupatulani pakati pa anthu onse kuti mukhale anthu anga.
Iye adatipulumutsa, ndipo adatiitana kuti tikhale anthu ake. Sadachite zimenezi chifukwa choti ife tidaachita zabwino ai, koma chifukwa mwiniwakeyo adaazikonzeratu motero, ndiponso chifukwa mwa Khristu Yesu adatikomera mtima nthaŵi isanayambe.
Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.
Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse. Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”
Tsono, inu okondedwa, popeza kuti tili ndi malonjezo ameneŵa, tiyeni tidzichotsere zinthu zonse zodetsa thupi lathu kapena mtima wathu. Ndipo pakuwopa Mulungu tiziyesetsa ndithu kukhala oyera mtima.
“Palibe woyera wina wofanafana ndi Chauta, palibe wina koma Iye yekha. Palibe thanthwe lina lotchinjiriza lofanafana ndi Mulungu wathu.
Kumeneko kudzakhala mseu waukulu wotchedwa “Mseu Wopatulika.” Ochimwa sadzayendamo, ndipo zitsilu sizidzasokera m'menemo.
Mosakayika konse, Malamulo a Mose ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo lamulo lililonse mwa Malamulowo ndi loyera, lolungama ndi labwino.
Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Tsono mudziyeretse, ndipo mukhale oyera pakuti Ine ndine woyera. Musadziipitse ndi chinthu chokwaŵa pansi chilichonse. Pakuti Ine ndine Chauta, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale oyera, pakuti Ine ndine woyera.”
Koma tsopano mwamasulidwa ku uchimo, ndipo ndinu otumikira Mulungu. Phindu lake ndi kuyera mtima, ndipo potsiriza pake kulandira moyo wosatha.
Motero Iye adzalimbitsa mitima yanu kuti idzakhale yangwiro ndi yoyera pamaso pa Mulungu Atate athu, pamene Ambuye Yesu adzabwerenso pamodzi ndi oyera ake onse.
Umu ndimo m'mene ndidzaonetsere kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Choncho ndidzadziŵika kwa anthu a mitundu yonse. Tsono adzadziŵadi kuti Ine ndine Chauta.”
Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.
Enanu munali otere kale, koma mudayeretsedwa, mudasanduka anthu a Mulungu, ndipo mudapezeka olungama pamaso pake. Zimenezi zidachitika m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndiponso mwa Mzimu wa Mulungu wathu.
Mulungu Atate adakusankhani, monga Iye adaziganiziratu kuyambira pa chiyambi, kuti Mzimu Woyera akuyeretseni ndipo kuti mumvere Yesu Khristu, ndi kutsukidwa ndi magazi ake. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wonka nuchulukirachulukira.
Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Ndi msampha kwa munthu kupereka chinthu kwa Chauta mosaganiza bwino, chifukwa mwina atha kusintha maganizo atalumbira kale.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.
Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu.
Ndipo chifukwa cha iwoŵa ndikudzipereka kwa Inu, kuti iwonso akhale odzipereka moonadi kwa Inu.”
Tikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto. Mulungu adakupatulani mwa Khristu Yesu, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake, pamodzi ndi anthu onse amene ponseponse amatama dzina la Ambuye Yesu Khristu mopemba. Iye ndiye Mbuye wathu ndi Mbuye waonso. Nanga ali kuti anthu anzeru? Ali kuti aphunzitsi a Malamulo a Mose? Ali kuti anthu onyadira nzeru zamakono zapansipano? Monga Mulungu sadaonetse kuti kudalira nzeru zapansipano nkopusa? Pakuti mwa nzeru zake Mulungu adakonzeratu kuti anthuwo asamdziŵe ndi nzeru zao. Koma kudamkomera Mulungu kupulumutsa anthu okhulupirira ndi mau opusa amene timalalika. Ayuda amafuna kuwona zozizwitsa, pamene Agriki amafunafuna nzeru. Koma ife timalalika Khristu amene adapachikidwa pa mtanda. Kwa Ayuda mau ameneŵa ndi okhumudwitsa, pamene kwa anthu a mitundu ina mauŵa ndi opusa. Koma amene Mulungu adaŵaitana, kaya ndi Ayuda kaya ndi Agriki, onsewo amazindikira kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru ya Mulungu. Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu. Abale, taganizani m'mene munaliri pamene Mulungu adakuitanani. Pakati panu panalibe ambiri amene anthu ankaŵayesa anzeru. Panalibenso ambiri amphamvu, kapena obadwa m'mabanja omveka. Koma Mulungu adasankha zimene anthu amaziyesa zopusa, kuti Iye anyazitse nazo anthu anzeru. Adasankhanso zimene anthu amaziyesa zofooka, kuti Iye anyazitse nazo anthu amphamvu. Ndipo zimene anthu amaziyesa zachabe, zonyozeka ndi zosakhala zenizeni, Mulungu adazisankha kuti athetse mphamvu zinthu zimene iwowo amayesa kuti ndiye zenizeni. Mulungu adachita zimenezi kuti pasakhale wina aliyense woti nkumadzitukumula pamaso pake. Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama. Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa.
Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.
Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi opanda cholakwa pamaso pake.
Munthu aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi pa Khristu, amadzisandutsa woyera monga momwe Khristuyo ali woyera.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta, inu anthu ake oyera mtima, mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera.
Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera, njenjemerani pamaso pake, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Uthenga umene tidamva kwa Iye, ndipo timaulalika kwa inu, ndi wakuti Mulungu ndiye kuŵala, ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye. M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse. Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu. Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika. Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.
Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa.
Nyamukani, nyamukani, chokaniko msanga ku Babiloniko, musakhudze kanthu konyansa pa chipembedzo. Tulukanimo ndipo mudziyeretse, inu amene mukunyamula ziŵiya zopatulikira Chauta.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.
Popeza kuti zonsezi zidzasungunuka motero, nanga simuyenera kukhala anthu angwiro m'makhalidwe anu ndiponso osamala za Mulungu? Muziyembekeza tsiku la Ambuye ndi kugwira ntchito zofulumizitsa kudza kwake. Pa tsikulo zakumwamba zidzayaka moto ndi kusungunuka, ndipo zinthu zonse nazonso zidzasungunukira m'motomo.
kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,
“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?
Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu.
Inu ndinu mtundu wopatulika wa Chauta, Mulungu wanu. Mulungu adasankha inu kuti mukhale anthu ake pakati pa anthu onse a pa dziko lapansi.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Tikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto. Mulungu adakupatulani mwa Khristu Yesu, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake, pamodzi ndi anthu onse amene ponseponse amatama dzina la Ambuye Yesu Khristu mopemba. Iye ndiye Mbuye wathu ndi Mbuye waonso.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Chifukwa chakuti Yesu Khristu adachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako.
Ndani angayenere kukwera phiri la Chauta? Ndani angaime m'malo ake oyera? Ndi amene amachita zabwino ndi manja ake, ndipo amaganiza zabwino mumtima mwake. Ndi amene salingalira zonama, ndipo salumbira monyenga.
Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta. Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu. Ndili ndi nzeru kupambana okalamba, pakuti ndimatsata malamulo anu. Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu. Sindisiyana nawo malangizo anu, pakuti Inu mudandiphunzitsa mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga. Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga. Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza kuti ndidzamvera malangizo anu olungama. Ndazunzika koopsa, Chauta, patseni moyo, molingana ndi mau anu aja. Chauta, landirani mapemphero anga oyamika, ndipo mundiphunzitse malangizo anu. Moyo wanga uli m'zoopsa nthaŵi zonse, komabe sindiiŵala malamulo anu. Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni. Anthu oipa anditchera msampha, komabe sindisokera kuchoka m'njira ya malamulo anu. Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga. Mtima wanga muuphunzitse kuti uzikonda malamulo anu nthaŵi zonse. Ndimadana nawo anthu apaŵiripaŵiri, koma ndimakonda mau anu. Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu. Chokereni inu, anthu ochita zoipanu, kuti ine ndizitsata malamulo a Mulungu wanga. Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika. Chirikizeni kuti ndipulumuke, kuti nthaŵi zonse ndizitsata malamulo anu. Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu, zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake. Anthu onse oipa a pa dziko lapansi, mumaŵayesa ngati zakudzala, nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu. Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu. Thupi langa limanjenjemera chifukwa chokuwopani, ndimachita mantha ndi kuweruza kwanu. Ndachita zimene zili zolungama ndi zabwino. Musandisiye m'manja mwa ondizunza. Lonjezani kuti mudzandichitira zabwino mtumiki wanune, musalole anthu osasamala za Mulungu kuti andizunze. Maso anga atopa chifukwa cha kuyembekeza chipulumutso chanu, chifukwa cha kudikira kuti malonjezo anu olungama aja achitikedi. Komereni mtima mtumiki wanune, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Ndine mtumiki wanu, mundipatse nzeru zomvetsa, kuti ndizidziŵa malamulo anu. Yakwana nthaŵi yakuti Inu Chauta muchitepo kanthu, popeza kuti anthu aphwanya malamulo anu. Koma ine ndimasamala malamulo anu kupambana golide, golide wosungunula bwino. Malamulo anu onse amalungamitsa mayendedwe anga. Ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. Malamulo anu ndi abwino, nchifukwa chake ndimaŵatsata ndi mtima wanga wonse. Ndimalalika ndi mau anga malangizo onse a pakamwa panu. Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru. Ndimapuma mwaŵefuŵefu nditatsekula pakamwa, chifukwa ndimalakalaka malamulo anu. Yang'aneni, ndipo mundikomere mtima monga m'mene mumachitira ndi anthu okukondani. Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira. Pulumutseni kwa anthu ondizunza, kuti ndizitsata malamulo anu. Yang'anireni ine mtumiki wanu ndi chikondi chanu, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Maso anga akudza misozi yambiri ngati mitsinje, chifukwa anthu satsata malamulo anu. Ndinu olungama Chauta, ndipo kuweruza kwanu nkolungama. Malamulo amene mwatipatsa, ndi olungama ndi okhulupirika ndithu. Changu changa chikuyaka ngati moto mumtima mwanga, chifukwa adani anga amaiŵala mau anu. Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse. Malonjezo anu ndi otsimikizika, ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda. Ine ndine wamng'ono ndi wonyozeka, komabe sindiiŵala malamulo anu. Kulungama kwanu nkwamuyaya, ndipo malamulo anu ndi oona. Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe, koma malamulo anu amandisangalatsa. Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya, patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo. Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu. Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu. Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu. Ndimakhala maso usiku wonse, ndikusinkhasinkha za malonjezo anu. Imvani liwu langa chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Inu Chauta, sungani moyo wanga chifukwa cha chilungamo chanu. Ndidzasinkhasinkha za malamulo anu, ndipo ndidzatsata njira zanu. Anthu ankhanza ondizunza akuyandikira. Iwo ali kutali ndi malamulo anu. Koma Inu Chauta muli pafupi, ndipo malamulo anu onse ndi oona. Poŵerenga malamulo anu ndidadziŵa kale lomwe kuti Inu mudaŵakhazikitsa mpaka muyaya. Yang'anani masautso anga, ndipo mundipulumutse, popeza kuti sindiiŵala malamulo anu. Munditchinjirize pa mlandu wanga, ndipo mundiwombole. Mundipatse moyo molingana ndi malonjezo anu aja. Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu. Chifundo chanu nchachikulu, Inu Chauta, mundipatse moyo molingana ndi chilungamo chanu. Anthu ondizunza ndiponso adani anga ngochuluka, koma sindisiyana nawo malamulo anu. Ndimanyansidwa ndikamayang'ana anthu osakhulupirika, chifukwa satsata malamulo anu. Onani m'mene ndimakondera malamulo anu, sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika Ndidzakondwera ndi malamulo anu, ndipo mau anu sindidzaŵaiŵala. mau anu ndi oona okhaokha, malangizo anu onse olungama ngamuyaya. Mafumu amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umaopa mau anu. Ndimakondwa ndi mau anu monga munthu amene wapeza chuma chambiri. Ndimadana ndi anthu abodza, zoonadi, ndimanyansidwa nawo, koma ndimakonda malamulo anu. Ndimakutamandani kasanunkaŵiri pa tsiku, chifukwa cha malangizo anu olungama. Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa. Ndimakhulupirira kuti mudzandipulumutsa, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu. Mzimu wanga umatsata malamulo anu, pakuti ndimaŵakonda ndi mtima wanga wonse. Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu, pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona. Kulira kwanga kumveke kwa Inu, Chauta. Mundipatse nzeru zomvetsa potsata mau anu aja. Komereni mtima ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo ndi kusunga mau anu. Kupempha kwanga kumveke kwa Inu. Mundipulumutse potsata malonjezo anu. Pakamwa panga padzakutamandani, chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu. Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu, chifukwa malamulo anu onse ndi olungama. Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza, chifukwa ndatsata malamulo anu. Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa. Lolani kuti ndikhale moyo, kuti ndizikutamandani, ndipo malangizo anu azindithandiza. Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu. Tsekulani maso anga kuti ndiwone zodabwitsa zochokera m'malamulo anu. Ndine munthu wongokhala nawo pa dziko lapansi, musandibisire malamulo anu. Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse, Mtima wanga wafooka chifukwa cholakalaka malangizo anu nthaŵi zonse. Inu mumadzudzula onyada, amene ali otembereredwa, amene amasiya malamulo anu. Mundichotsere zonyoza zao zondinyodola, chifukwa ndasunga malamulo anu. Ngakhale mafumu andichitire upo woipa, ine mtumiki wanu ndidzasinkhasinkhabe za malamulo anu. Malamulo anu amandikondwetsa, ndiwo amene amandilangiza. Ndangoti thapsa m'fumbi. Bwezereni moyo monga momwe mudalonjezera. Pamene ndidasimba za njira zanga, Inu mudandiyankha. Phunzitseni malamulo anu. Mundidziŵitse mfundo za malamulo anu, ndipo ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zodabwitsa. Ndafookeratu ndi chisoni. Limbitseni monga momwe mudalonjezera. Mundichotse m'njira zondisokeza, kuti ndisayendemo. Mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu. amene sachita zolakwa, koma amayenda m'njira za Chauta.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Adafuna kuti akauimike pamaso pake uli waulemerero, wopanda banga kapena makwinya, kapena kanthu kena kalikonse kouipitsa, koma uli woyera ndi wangwiro kotheratu.
Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu? Ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera? Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Dzuka, dzuka, vala dzilimbe iwe Ziyoni. Vala zovala zako zabwino, iwe Yerusalemu, mzinda woyera. Anthu osaumbalidwa ndi onyansa pa chipembedzo sadzaloŵanso pa zipata zako.
Pakuti anthu amene Mulungu adaŵasankhiratu, Iye adaŵapatulanso kale kuti akhale monga Mwana wake, kuti choncho Mwanayo akhale woyamba mwa abale ambiri.
Ndikukulamula kuti, mopanda cholakwa kapena chokayikitsa, utsate bwino zonse zimene udalamulidwa, mpaka Ambuye athu Yesu Khristu adzabwerenso.
Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake.
Popeza kuti zonsezi zidzasungunuka motero, nanga simuyenera kukhala anthu angwiro m'makhalidwe anu ndiponso osamala za Mulungu?
Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Inu okondedwa, ndife ana a Mulungu tsopano. Mulungu sadatiwonetsebe chimene tidzakhale. Koma tikudziŵa kuti Iye akadzaoneka, tidzakhala ofanafana naye, pakuti tidzamuwona monga momwe aliri.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
“Choncho tsopano ndikukuikani m'manja mwa Mulungu, mau ake oonetsa kukoma mtima kwake akusungeni bwino. Mauwo ali ndi mphamvu zakukulitsa mpingo, ndi kukupatsani madalitso onse aja amene Mulungu akusungira anthu ake.