Ndikufuna ndikuuzeni nkhani yofunika kwambiri. Kale, panali malo opatulika otchedwa Malo Oyera, omwe anali mbali ya Kachisi. Malo Oyera amenewa anali ogawanika pakati: Malo Oyera ndi Malo Oyeretsa. Ansembe okha ndi omwe ankalowedwa m’Malo Oyera tsiku ndi tsiku kuti akachite ntchito zawo zotumikira Mulungu. Wina aliyense wosaloledwa kulowamo, makamaka wosadetsedwa, akanatha kufa nthawi yomweyo.
Koma Mulungu, m’chikondi chake chachikulu, nthawi zonse amafuna kuti tikhale paubwenzi naye. Tinali titalekanitsidwa ndi machimo athu, koma tsopano Yesu Khristu, Mkulu wa Ansembe wathu, wadzipereka yekha kukhala nsembe yochimwira machimo athu kamodzi kokha.
Chifukwa cha nsembe imeneyi, chophimba chomwe chinkatilekanitsa ndi Malo Oyera chinang’ambika! Tsopano palibe chotilepheretsa kufika kwa Atate wathu wakumwamba ndikumulambira. Kale zinali zosatheka kuti munthu wamba alowe m’Malo Oyera, koma tsopano, chifukwa cha Yesu, tili ndi mwayi wokhala m’chiyero ndi kutsukidwa ku machimo athu ndi mwazi wake wamtengo wapatali wotayidwa pa Mtanda wa pa Gologota.
Tiyeni tiyesetse kukhala mwamtendere ndi anthu onse ndiponso m’chiyero, chifukwa lemba limati popanda chiyero palibe amene adzaona Ambuye (Ahebri 12:14). Zikomo, Mpulumutsi wathu wokondedwa, chifukwa chotilola kusangalala ndi kukhalapo kwanu masiku ano.
Wolamula gulu lankhondo la Chauta uja adamuyankha kuti, “Vula nsapato zako. Malo amene ukuimirirapoŵa ngoyera.” Yoswa adachitadi zimene adamuuzazo.
Imvani kupempha kwanga, pamene ndikulirira Inu kuti mundithandize, pamene ndikukupembedzani pokweza manja anga ku malo anu opatulika kopambana.
Chipinda chopatulika chija adachikonza m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, kuti aikemo Bokosi lachipangano la Chauta.
Guwalo ulikhazike patsogolo pa nsalu yochinga bokosi lachipangano, patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa bokosi lachipangano. Pa malo ameneŵa ndi pamene ndizidzakumana nawe.
Kenaka adapanga malo opatulika kwambiri. M'litali mwake anali a mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwa nyumbayo. M'mimba mwake analinso a mamita asanu ndi anai. Adakuta malo opatulikawo ndi golide wosalala wokwanira matani makumi aŵiri.
Ukoloŵeke nsalu yochingayo ku ngoŵezo ndipo uike bokosi lachipangano lija m'kati momwemo, kuseri kwa nsalu yochingayo. Nsalu yochingayo idzalekanitsa malo opatulika ndi malo opatulika kopambana.
Kumbuyo kwa Nyumbayo adadula chipinda kutalika kwake mamita asanu ndi anai. Adachimanga ndi matabwa amkungudza kuyambira pansi mpaka ku siling'i. Chipindachi adachimanga m'kati mwa Nyumbayo, kuti chikhale chipinda chopatulika cham'kati, malo opatulika kopambana.
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Pamene ndidzabwezeranso anthu ufulu, kudzamvekanso mau ku dziko la Yuda ndi ku mizinda yake. Mau ake adzakhala akuti, ‘Chauta akudalitse iwe malo achilungamo, ndiponso iwe phiri loyera.’
Ukoloŵeke nsalu yochingayo ku ngoŵezo ndipo uike bokosi lachipangano lija m'kati momwemo, kuseri kwa nsalu yochingayo. Nsalu yochingayo idzalekanitsa malo opatulika ndi malo opatulika kopambana. Uike chivundikiro chija pa bokosi lachipangano ku malo opatulika kopambanawo.
Kenaka adaika bokosilo m'malo opatulika, ndipo adaika nsalu zochingira. Motero adachinga bokosi laumboni, monga momwe Chauta adamlamulira.
Bokosi m'mene muli miyala yaumboni uliike m'menemo, ndipo bokosilo uliphimbe ndi nsalu kuti ulichinge.
Chivundikiro cha bokosicho udzachiike pamwamba pa bokosilo, ndipo m'bokosimo udzaikemo miyala iŵiri ija ya Malamulo imene ndidzakupatse. Ndizidzakumana nawe kumeneko, ndipo kuchokera pamwamba pa chivundikirocho, pakati pa akerubi ali pamwamba pa bokosiwo, ndidzakuuza malamulo okhudza anthu anga Aisraele.
M'chigawo chopatulikacho uyese malo a makilomita 12 ndi theka m'litali mwake, makilomita asanu muufupi mwake. Pamenepo padzakhala malo opatulika, malo oyera kwambiri.
Ku malo opatulika kwambiriko adapangako akerubi aŵiri achitsulo, ndipo adaŵakuta ndi golide.
Pambuyo pake adayesa chipinda chenichenicho napeza kuti m'litali mwake ndi muufupi mwake munali mamita khumi. Apo adandiwuza kuti, “Chimenechi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”
Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika.
Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera akuphunzitsa kuti njira yoloŵera m'Malo Opatulika Kopambana ndi yosatsekukabe pamene chipinda choyamba chija chilipobe.
Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni mbale wako kuti asamaloŵa nthaŵi iliyonse ku malo opatulika kwambiri, kuseri kwa nsalu yochinga, pamaso pa chivundikiro chokhala pamwamba pa Bokosi lachipangano, kuti angafe, chifukwa Ine ndidzaonekera mu mtambo pamwamba pa chivundikirocho.
Motero adaikuta Nyumba yonseyo ndi golide mpaka idatha. Guwa lansembe la m'chipinda chopatulika nalonso adalikuta ndi golide.
Paseri pa chochinga chachiŵiri panali chipinda chotchedwa “Malo Opatulika Kopambana”. Chipindachi chinali ndi guwa lagolide lofukizirapo lubani. M'chipindamo munalinso bokosi lachipangano. Bokosi lonselo linali lokutidwa ndi golide. M'bokosimo munali kambiya kagolide m'mene munali mana uja, ndi ndodo ya Aroni, ija idaaphukayi. Munalinso miyala iŵiri ija yolembedwapo mau a chipangano.
“Tsono Aroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu. Magazi ake aloŵe nawo kuseri kwa nsalu yochinga, ndi kuchita nawo monga momwe adachitira ndi magazi a ng'ombe, pakuwaza magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho. Akatero ndiye kuti wachita mwambo wopepesera malo oyera chifukwa cha kuipitsidwa kwa Aisraele, ndiponso chifukwa cha kusamvera kwao, ndiye kuti machimo ao onse. Achite chimodzimodzi ndi chihema chamsonkhano chokhala ndi iwo pakati pa machimo ao.
Njira zanu, Inu Mulungu, nzoyera. Kodi alipo mulungu winanso wamkulu ngati Mulungu wathu?
Chipinda chopatulika chija adachikonza m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, kuti aikemo Bokosi lachipangano la Chauta. Nyumba imene mfumu Solomoni adamangira Chauta muutali mwake inali ya mamita 27, muufupi mwake inali ya mamita asanu ndi anai, ndipo msinkhu wake unali wa mamita pafupi 13 ndi theka. Chinali cha mamita asanu ndi anai ponseponse, m'litali mwake, m'mimba mwake ndiponso mumsinkhu mwake. Ndipo adachikuta ndi golide weniweni. Adapanganso guwa lansembe la matabwa amkungudza.
Ndizidzakumana nawe kumeneko, ndipo kuchokera pamwamba pa chivundikirocho, pakati pa akerubi ali pamwamba pa bokosiwo, ndidzakuuza malamulo okhudza anthu anga Aisraele.
Tsono ansembe adafika nalo Bokosi lachipangano la Chauta lija ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana naliika kunsi kwa mapiko a akerubi.
Tsono ansembe adafika nalo ndi Bokosi lachipangano la Chauta ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana, naliika kunsi kwa mapiko a akerubi.
Chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi.
Tsono adatenga miyala yaumboni ija naiika m'bokosi muja. Adapisa mphiko zija m'mphete za bokosilo, naika chivundikiro pamwamba pake. Kenaka adaika bokosilo m'malo opatulika, ndipo adaika nsalu zochingira. Motero adachinga bokosi laumboni, monga momwe Chauta adamlamulira.
dzuŵa litangoti bii kuda. Pamenepo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati. za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa, ndi za chiweruzo chotsiriza. Koma tiyeni tipitirire mpaka tikafike pa kukhwima kwenikweni. Yesu adatitsogolera kale nkuloŵamo chifukwa cha ife. Iye adasanduka mkulu wa ansembe onse wamuyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Ndipo Aroni akamaloŵa m'malo opatulika, azivala chovala chapachifuwa cholembedwa maina onse a ana a Israele, kuti Chauta azidzaŵakumbukira.
Paseri pa chochinga chachiŵiri panali chipinda chotchedwa “Malo Opatulika Kopambana”. Chipindachi chinali ndi guwa lagolide lofukizirapo lubani. M'chipindamo munalinso bokosi lachipangano. Bokosi lonselo linali lokutidwa ndi golide. M'bokosimo munali kambiya kagolide m'mene munali mana uja, ndi ndodo ya Aroni, ija idaaphukayi. Munalinso miyala iŵiri ija yolembedwapo mau a chipangano. Pamwamba pa bokosilo panali zithunzi za akerubi oonetsa ulemerero wa Mulungu. Mapiko ao adaaphimbira pa chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nkosatheka tsopano lino kufotokoza zonzezi tsatanetsatane.
Pa masiku asanu ndi aŵiri uzipereka nsembe zoyeretsera guwalo, ndipo uzilipatula. Pambuyo pake guwalo lidzakhala loyera kwathunthu, ndipo chilichonse chimene chidzakhudze guwalo chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.
Koma m'chipinda chachiŵiri chija ndi mkulu wa ansembe onse yekha amene amaloŵamo, nayenso ndi kamodzi kokha pa chaka, ndipo saloŵamo popanda kutenga magazi. Magaziwo ngokapereka kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini, ndiponso chifukwa cha machimo ochita anthu mosazindikira bwino.
Koma Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso changwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano. Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha.
Paja Khristu sadaloŵe m'malo opatulika omangidwa ndi anthu, malo ongofanizira malo enieni opatulika a Kumwamba. Iye adapita Kumwamba kwenikweniko, kuti tsopano aziwonekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.
Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake.
Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Pamenepo mudatsekuka m'Nyumba ya Mulungu Kumwamba, ndipo bokosi lachipangano lidaoneka m'Nyumbamo. Kenaka kudachita mphezi, phokoso, mabingu ndi chivomezi, ndipo kudagwa matalala akuluakulu.