Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


102 Mau a Mulungu Okhudza Kudzozedwa ndi Mafuta

102 Mau a Mulungu Okhudza Kudzozedwa ndi Mafuta

Lembani izi, Mulungu ndiye amatilimbitsa ife pamodzi ndi inu mwa Khristu, ndipo anatipaka mafuta. Iyenso anatisindikiza, natipatsa Mzimu m’mitima yathu monga chikole. 2 Akorinto 1:21-22

Suli pano padziko lapansi mwangozi. Mulungu waika chinthu chapadera mkati mwako, zomwe zikutanthauza kuti pali cholinga chamuyaya chokhala ndi dzina lako, kuyambira kale lomwe dziko lisanakhaleko. N’chifukwa chake, uzikumbukira nthawi zonse kuti amene anakutcha ndiye amakugwira, amene anakudzoza ndiye amakupatsa mphamvu ndi nzeru zochitira zofuna zake.

Kumbukira nthawi zonse kuti kuyitanidwa komwe Mulungu wakupatsa sikungasinthike. Pali chizindikiro pa iwe chosonyeza kuti ndiwe mwana wa Mulungu, wosankhidwa kuonetsa ulemerero wake ndi mphamvu zake. Chifukwa chake, yenda molimba mtima podziwa kuti suli wekha ndipo Mzimu Woyera amakutsogolera nthawi zonse.

Usawope zomwe anthu angakuchitire. Lankhula zomwe Mulungu wakuuza ndipo chita zonse zomwe akulamula, chifukwa kukhalapo kwake kudzakhala nawe.




Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:14

Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:22-25

Chauta adauzanso Mose kuti, “Utenge zonunkhira bwino kwambiri zokwanira makilogaramu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogaramu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa kinamoni, makilogaramu atatu a nzimbe zonunkhira bwino, makilogaramu asanu ndi limodzi a kasiya (zonsezo potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu). Ndipo muwonjeze mafuta okwanira malita anai a olivi. Tsono zonsezi udzapangire mafuta odzozera. Udzaziphatikize pamodzi monga momwe amachitira munthu wopanga zonunkhira. Mafuta amenewo adzakhale mafuta oyera, odzozera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 1:9

Mudakonda chilungamo nkudana ndi zosalungama. Nchifukwa chake Ine, Mulungu wanu, ndakukwezani nkukudzozani ndi mafuta osonyeza chimwemwe, kupambana anzanu ena onse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 29:7

Tsono utenge mafuta odzozera aja ndi kuŵatsanyulira kumutu kwake kuti umdzoze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 6:13

Ankatulutsa mizimu yoipa yocholuka, ndiponso ankadzoza mafuta anthu odwala ambiri nkumaŵachiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 8:10-12

Pambuyo pake Mose adatenga mafuta odzozera, nadzoza chihema chamsonkhano pamodzi ndi zonse zimene zinali m'menemo, ndipo adazipatula. Adawazako mafuta ena kasanu ndi kaŵiri pa guwa, nalidzoza guwalo pamodzi ndi zipangizo zake zonse. Adadzozanso mkhate pamodzi ndi phaka lake, kuti zikhale zopatulika. Mafuta ena odzozerawo adaŵathira pamutu pa Aroni, namdzoza, ndi kumsandutsa wopatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:14-15

Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye. Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:46

Iwe sudandidzoze kumutu kwanga ndi mafuta, koma iyeyu wadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:27

Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:30

Kenaka udzamdzoze Aroni pamodzi ndi ana ake, ndi kuŵapatula kuti akhale ansembe onditumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:15

Tsono uŵadzoze monga momwe udadzozera bambo wao, kuti akhale ansembe onditumikira Ine. Kudzozedwako kudzaŵasandutsa ansembe pa mibabwo ndi mibadwo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 8:12

Mafuta ena odzozerawo adaŵathira pamutu pa Aroni, namdzoza, ndi kumsandutsa wopatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 16:13

Samuele adatenga nsupa ya mafuta, namdzoza pamaso pa abale ake. Ndipo mzimu wa Chauta udamloŵa Davide mwamphamvu kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake. Pambuyo pake Samuele adanyamuka napita ku Rama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:5

Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona. Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta, mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 14:8

Iyeyu wachita zimene akadatha kuchita. Wadzozeratu thupi langa ndi mafuta onunkhira, kuti alikonzeretu lisanaikidwe m'manda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 28:41

Zovala zimenezi uveke mbale wako Aroni ndi ana ake. Tsono uŵadzoze, uŵapatse udindo ndi kuŵapatula, kuti akhale ansembe onditumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 1:39

Kumeneko wansembe Zadoki adatenga nsupa ya mafuta ya ku hema la Chauta, nadzoza Solomoni. Pomwepo adaliza lipenga, ndipo anthu onsewo adafuula kuti, “Achite kufa ndi ukalamba mfumu Solomoni!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:9

“Pambuyo pake utenge mafuta odzozera aja, udzoze Nyumba ya Mulungu ndi zonse za m'menemo. Uipereke kwa Mulungu Nyumbayo, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, kuti idzakhale yoyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 2:4

Tsono anthu a ku Yuda adafika, ndipo kumeneko adadzoza Davide kuti akhale mfumu yao. Davide atamva kuti ndi anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene adaika Saulo m'manda,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:10

Koma ine mwandilimbitsa ngati njati. Mwandidzoza ndi mafuta atsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 19:16

Yehu mwana wa Nimisi ukamdzoze kuti akhale mfumu ya ku Israele. Ndipo Elisa, mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola, ukamdzoze kuti akhale mneneri woloŵa m'malo mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 8:30

Tsono Mose adatengako mafuta odzozera aja ndi magazi amene anali pa guwa, nawaza Aroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zao. Umu ndimo m'mene Mose adapatulira Aroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 133:2

Ndi ngati mafuta amtengowapatali oŵathira pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aroni, oyenderera mpaka ku khosi la mkanjo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:3

Tsono Maria adatenga mafuta onunkhira zedi a narido weniweni, amtengowapatali, okwanira theka la lita, nayamba kudzoza mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake. M'nyumba monsemo mumvekere guu ndi fungo la mafutawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:17

Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m'maso nkudzola mafuta kumutu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 21:10-12

“Munthu amene ali mkulu wa ansembe onse, amene adamdzoza pa mutu ndi mafuta, ndiponso amene adapatulidwa pakumuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake, kapena kung'amba zovala zake kusonyeza kuti ali pamaliro. Asakaloŵe kumene kuli munthu wakufa aliyense ndi kudziipitsa, ngakhale mtembo wa bambo wake kapena wa mai wake. Asatuluke m'malo oyera kapena kuipitsa malo oyera a Mulungu wake, pakuti mafuta odzozera a Mulungu wake amene adamdzoza nawo ali pa iye. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:20

Koma inuyo, mudadzozedwa ndi Woyera uja, ndipo nonse mukudziŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 6:15

Aperekenso dengu la buledi wosafufumitsa, makeke a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa topyapyala ndi topaka mafuta, pamodzi ndi zopereka zake za zakudya ndi zachakumwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 29:21

Utengeko magazi otsalira pa guwa ndiponso mafuta ena odzozera, uwaze Aroni ndi zovala zake. Uwazenso ana ake ndi zovala zao. Tsono iyeyo ndi ana ake adzakhala opatulika, pamodzi ndi zovala zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:8

mafuta anyale, zonunkhira zopangira mafuta odzozera, ndiponso zopangira lubani wonunkhira bwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:21-22

Mulungu ndi amene amatikhazikitsa pamodzi nanu mwa Khristu. Ndiye amene adatidzoza, natisindikiza chizindikiro chake, ndi kuika Mzimu Woyera m'mitima mwathu ngati chikole.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 10:1

Tsono Samuele adatenga nsupa ya mafuta nathira mafutawo pamutu pa Saulo. Ndipo adamumpsompsona nati, “Chauta akukudzoza kuti ukhale mfumu ya anthu ake Aisraele. Udzalamulira anthu a Chauta ndi kuŵapulumutsa kwa adani oŵazungulira. Chizindikiro chakuti Chauta wakudzoza kuti ukhale mfumu yolamulira anthu ake, ndi ichi:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 45:7

Mumakonda chilungamo ndipo mumadana ndi zoipa. Nchifukwa chake Mulungu, Mulungu wanu, wakusankhani. Wakudzozani ndi kukusangalatsani kupambana anzanu ena onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 31:11

mafuta odzozera ndiponso lubani wa fungo lokoma, zonsezo zokhalira malo oyera. Adzapange zinthu zonsezi monga ndakulamulira iwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:26-29

Udzadzoze chihema chamsonkhanocho ndi mafuta amenewo. Udzadzozenso bokosi lachipangano, tebulo ndi zipangizo zake zonse, choikaponyale pamodzi ndi zida zake, guwa lofukizirapo lubani, guwa lopserezapo zopereka, pamodzi ndi zipangizo zake, ndiponso beseni losambiramo lija ndi phaka lake lomwe. Zonsezi udzazipatula mwa njira imeneyi, ndipo zidzakhala zoyera kopambana. Ndipo chilichonse chokhudza zimenezi chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:6

mafuta a nyale, zonunkhira za mafuta odzozera, ndiponso lubani wa fungo lokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:13-15

Aroniyo umuveke zovala zopatulika. Umdzoze, ndipo umpatule kuti akhale wansembe wonditumikira Ine. Ana ake abwerenso, ndipo uŵaveke miinjiro. Tsono uŵadzoze monga momwe udadzozera bambo wao, kuti akhale ansembe onditumikira Ine. Kudzozedwako kudzaŵasandutsa ansembe pa mibabwo ndi mibadwo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 29:1-2

“Pofuna kumpatula Aroni ndi ana ake, kuti akhale ansembe onditumikira, uchite izi: Utenge ng'ombe yamphongo ndi nkhosa zamphongo ziŵiri zopanda chilema. “Pambuyo pake ubwere ndi ng'ombe yamphongo pakhomo pa chihema chamsonkhano. Tsono Aroni ndi ana ake asanjike manja ao pamutu pa ng'ombeyo. Kenaka muiphe ng'ombeyo pamaso pa Chauta, pa khomo la chihema chamsonkhano. Utengeko magazi a ng'ombeyo, ndipo uŵapake ndi chala chako pa nyanga za guwa. Tsono magazi otsalawo uŵatsanyulire patsinde pa guwalo. Pambuyo pake utenge mafuta onse okuta matumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ndiponso imso ziŵiri, pamodzi ndi mafuta ozikuta. Zonsezi uzipereke, ndipo uzitenthere pa guwalo. Koma nyama yake, chikumba chake ndi ndoŵe zake, ukazitenthere kunja kwa mahema. Chopereka chimenechi ndicho cha nsembe yopepesera machimo. “Utenge imodzi mwa nkhosa ziŵiri zamphongo zija, ndipo Aroni ndi ana ake aamuna asanjike manja ao pamutu pa nkhosayo. Tsono uiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza pa mbali zonse za guwa. Nkhosayo uiduledule, ndipo utatsuka matumbo ndi miyendo yake, uziike mosanjikiza pamwamba pa nthuli zake ndi mutu. Ndipo upsereze nkhosa yonseyo paguwapo. Imeneyo idzakhala nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta. Idzakhala nsembe ya fungo lokoma yopereka pa moto kwa Chauta. “Tsono utenge nkhosa yamphongo inayo. Aroni ndi ana ake aamuna asanjike manja ao pamutu pa nkhosayo. Utengenso buledi wosafufumitsa, makeke osatupitsa, osakaniza ndi mafuta, ndiponso mitanda ya buledi yopsapsalala yopaka mafuta. Zimenezi uzipange ndi ufa wosalala watirigu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 35:25

Mpingo umpulumutse munthu wopha mnzakeyo m'manja mwa mbale wa munthu wakufayo. Ndipo um'bweze munthuyo ku mzinda wake wothaŵirako kumene adathaŵira. Adzakhala komweko mpaka mkulu wa ansembe onse atamwalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 9:6

Pamenepo Yehuyo adanyamuka nakaloŵa m'nyumba. Ndipo mneneri uja adathira mafuta pamutu pa Yehu nati, “Chauta, Mulungu wa Israele, akuti akukudzozani inu kuti mukhale mfumu ya Aisraele, anthu a Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:15-18

Wansembe atapeko mafuta pang'ono, nkuŵathira m'dzanja lake lakumanzere. Ndipo aviike chala chake cha ku dzanja lamanja m'mafuta amene ali m'dzanja lakumanzerewo, ndi kuwazako mafutawo ndi chala chake kasanu ndi kaŵiri pamaso pa Chauta. Mafuta otsala m'dzanja la wansembeyo, aŵapakeko pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu woyeretsedwa uja, ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pamene anali atapaka magazi aja a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija. Mafuta otsala m'dzanja la wansembe, aŵathire pamutu pa munthu woti ayeretsedwe uja. Ndimo m'mene wansembe amchitire munthuyo mwambo wompepesera pamaso pa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 39:37

choikaponyale cha golide wabwino kwambiri, nyale zake pamodzi ndi zipangizo zake, mafuta anyale;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:31-33

Tsono Aisraele onse udzaŵauze kuti, ‘Ameneŵa ndiwo adzakhale mafuta anga oyera odzozera pa mibadwo yanu yonse. Musadzadzozere anthu wamba, ndipo musadzapangenso mafuta ena ofanafana nawo. Ameneŵa ngoyera ndipo kwa inu adzakhalabe oyera ndithu. Munthu aliyense amene adzapange mafuta ena ofanafana nawo, kapena kudzozera munthu aliyense amene sali wansembe, adzamchotsa pakati pa anthu anzake.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 19:15-16

Apo Chauta adamuuza kuti, “Bwerera, tsata njira yopita ku chipululu cha ku Damasiko. Ukakafika kumeneko, ukadzoze Hazaele kuti akhale mfumu ya ku Siriya. Yehu mwana wa Nimisi ukamdzoze kuti akhale mfumu ya ku Israele. Ndipo Elisa, mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola, ukamdzoze kuti akhale mneneri woloŵa m'malo mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 9:16

“Maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, ndidzakutumizira munthu wa ku dera la Benjamini, udzamudzoze kuti akhale mfumu ya anthu anga Aisraele. Adzapulumutsa anthu kwa Afilisti. Ndaona kuzunzika kwao, ndipo ndamva kulira kwao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:28

Adaperekanso zonunkhira, mafuta anyale, mafuta odzozera ndiponso lubani wa fungo lokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 2:1

“Munthu wina aliyense akabwera kudzapereka chopereka cha chakudya kwa Chauta, nsembeyo ikhale ya ufa wosalala. Ufawo authire mafuta ndi lubani,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:24-25

makilogaramu asanu ndi limodzi a kasiya (zonsezo potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu). Ndipo muwonjeze mafuta okwanira malita anai a olivi. Tsono zonsezi udzapangire mafuta odzozera. Udzaziphatikize pamodzi monga momwe amachitira munthu wopanga zonunkhira. Mafuta amenewo adzakhale mafuta oyera, odzozera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 4:16

“Eleazara mwana wa wansembe Aroni, azisamala mafuta a nyale, lubani wonunkhira, chopereka cha chakudya choperekedwa nthaŵi zonse, ndi mafuta odzozera. Aziyang'anira malo opatulika ndi zonse za m'kati mwake, ndiponso chipinda chopatulika kwambiri ndi zipangizo zake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 105:15

Adati, “Musakhudze odzozedwa anga, musaŵachite choipa aneneri anga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:7

Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta onunkhira amtengowapatali. Adayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 7:12

akaipereka chifukwa cha kuthokoza, pamodzi ndi nsembe yothokozerayo apereke makeke osafufumitsa, osakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wosakaniza bwino ndi mafuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 6:17

Atatero, apereke nkhosa yamphongo kwa Chauta, kuti ikhale nsembe yachiyanjano, pamodzi ndi dengu la buledi uja wosafufumitsa. Kenaka aperekenso chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 28:15

Kenaka anthu amene taŵatchula maina aja, adanyamuka natenga akapolowo. Amene anali maliseche adaŵaveka zovala zimene adaafunkha. Adaŵaveka, naŵapatsa nsapato. Adaŵapatsa zakudya ndi zakumwa. Tsono atanyamula anthu onse ofooka pa abulu, adabwera nawo kwa abale ao ku Yeriko, mzinda wamigwalangwa. Kenaka adabwerera ku Samariya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:6

Tsopano ndikudziŵa kuti Chauta adzathandiza wodzozedwa wake. Adzamuyankha ali ku malo ake oyera kumwamba, pakumpambanitsa kwathunthu ndi dzanja lake lamanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 4:14

Tsono iye adati, “Ameneŵa ndi anthu aŵiri odzozedwa aja, amene amatumikira Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:20

“Ndampeza Davide mtumiki wanga, ndamdzoza ndi mafuta anga oyera,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 10:27

Tsiku limenelo ndidzakusanjulani katundu wa Aasiriya pa mapewa anu, ndi goli lao m'khosi mwanu, golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 141:5

Munthu wolungama angathe kundimenya kapena kundidzudzula chifukwa andimvera chifundo, koma ndisalandire ulemu kwa anthu oipa, pakuti ndimapemphera motsutsana ndi ntchito zao zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 27:20

“Uŵalamule Aisraele kuti akupatse mafuta aolivi opsinyidwa bwino, oyatsira nyale, kuti ziziyaka kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 39:38

guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani wa fungo lokoma, nsalu yotsekera pa chipata choloŵera m'chihema,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:10-11

Tsono udzozenso guwa loperekapo nsembe zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake zomwe. Guwalo ulipereke kwa Mulungu, kuti likhale loyera ndipo lidzakhaladi loyera kopambana. Udzoze beseni losambira, pamodzi ndi phaka lake lomwe, ndipo ulipereke kwa Mulungu, kuti likhale loyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:26-29

Kenaka wansembe athireko mafuta m'dzanja lake lamanzere, awazeko mafutawo kasanu ndi kaŵiri ndi chala cha ku dzanja lamanja pamaso pa Chauta. Apakekonso mafuta omwewo pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pomwe anali atapaka magazi a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija. Mafuta otsala amene ali m'dzanja la wansembe aŵapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo, kuti amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:16

Mose adachita zonse, monga momwe Chauta adamlamulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 28:3

Ulamule anthu onse aluso, onse amene ndaŵapatsa nzeru, kuti asoke zovala za Aroni zozivala pamene udzampatule kuti akhale wansembe wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 8:1-2

Chauta adauza Mose kuti, Pambuyo pake Mose adatenga mafuta odzozera, nadzoza chihema chamsonkhano pamodzi ndi zonse zimene zinali m'menemo, ndipo adazipatula. Adawazako mafuta ena kasanu ndi kaŵiri pa guwa, nalidzoza guwalo pamodzi ndi zipangizo zake zonse. Adadzozanso mkhate pamodzi ndi phaka lake, kuti zikhale zopatulika. Mafuta ena odzozerawo adaŵathira pamutu pa Aroni, namdzoza, ndi kumsandutsa wopatulika. Kenaka adabwera ndi ana a Aroni aja naŵaveka miinjiro, naŵamanga malamba m'chiwuno, ndi kuŵaveka zikofiya kumutu. Pambuyo pake Mose adabwera ndi ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aroni ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo. Kenaka Mose adaipha natenga magazi ake ndi kuŵapaka ndi chala chake pa nyanga za guwa molizungulira, ndipo adaliyeretsa. Adathiranso magazi patsinde pa guwalo nalipatula. Motero adachita mwambo wopepesera machimo. Tsono Mose adatenga mafuta onse akumatumbo ndi mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ndi imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe, ndipo adazitenthera paguwapo. Koma ng'ombe yamphongo ija, chikopa chake, nyama yake, ndi ndoŵe yake, zonsezi adazitenthera kunja kwa mahema, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Pambuyo pake adapereka nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza, ndipo Aroni ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa nkhosayo. Kenaka Mose adaipha nathira magazi ake pa guwa mozungulira. “Utenge Aroni ndi ana ake. Utengenso zovala, mafuta odzozera, ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziŵiri zamphongo, ndipo utengenso dengu la buledi wosafufumitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 1:39-40

Kumeneko wansembe Zadoki adatenga nsupa ya mafuta ya ku hema la Chauta, nadzoza Solomoni. Pomwepo adaliza lipenga, ndipo anthu onsewo adafuula kuti, “Achite kufa ndi ukalamba mfumu Solomoni!” Namwaliyo anali wokongola kwambiri. Tsono adakhala wosamala mfumu ndi kumaitumikira. Koma mfumuyo sidakhale naye malo amodzi namwaliyo. Anthuwo adapita namamtsatira pambuyo akuliza zitoliro ndi kukondwerera kwambiri, kotero kuti dziko lidagwedezeka chifukwa cha phokosolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:12

“Pambuyo pake ubwere ndi Aroni ku chipata cha chihema chamsonkhano, pamodzi ndi ana ake omwe, ndipo onsewo asambe kumeneko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 28:18

Yakobeyo adadzuka m'maŵa kwambiri, natenga mwala uja adaatsamirawu, nauimiritsa kuti ukhale mwala wachikumbutso. Tsono adauthira mafuta mwalawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:25-28

Tsono zonsezi udzapangire mafuta odzozera. Udzaziphatikize pamodzi monga momwe amachitira munthu wopanga zonunkhira. Mafuta amenewo adzakhale mafuta oyera, odzozera. Udzadzoze chihema chamsonkhanocho ndi mafuta amenewo. Udzadzozenso bokosi lachipangano, tebulo ndi zipangizo zake zonse, choikaponyale pamodzi ndi zida zake, guwa lofukizirapo lubani, guwa lopserezapo zopereka, pamodzi ndi zipangizo zake, ndiponso beseni losambiramo lija ndi phaka lake lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:15-16

Wansembe atapeko mafuta pang'ono, nkuŵathira m'dzanja lake lakumanzere. Ndipo aviike chala chake cha ku dzanja lamanja m'mafuta amene ali m'dzanja lakumanzerewo, ndi kuwazako mafutawo ndi chala chake kasanu ndi kaŵiri pamaso pa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:3-4

Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera. Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’ “Pamene Mwana wa Munthu adzabwera ndi ulemerero wake, pamodzi ndi angelo onse, adzachita kukhalira pa mpando wake wachifumu. Adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse pamaso pake, ndipo adzaŵalekanitsa monga momwe mbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Nkhosa adzazikhazika ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi ku dzanja lake lamanzere. Tsono Iyeyo ngati Mfumu adzauza a ku dzanja lamanjawo kuti, ‘Bwerani kuno inu odalitsidwa a Atate anga. Loŵani mu ufumu umene adakukonzerani chilengedwere dziko lapansi. Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’ Apo olungama aja adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, ife nkukupatsani chakudya, kapena muli ndi ludzu, ife nkukupatsani chakumwa? Ndi liti tidaakuwonani muli mlendo, ife nkukulandirani kunyumba kwathu, kapena muli wamaliseche, ife nkukuvekani? Ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife nkudzakuchezetsani?’ Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m'nsupa zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 37:29

Adapanganso mafuta oyera odzozera, ndiponso zofukizira za fungo lokoma. Mapangidwe ake adachita monga momwe ankachitira mmisiri wopanga zonunkhira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 39:37-38

choikaponyale cha golide wabwino kwambiri, nyale zake pamodzi ndi zipangizo zake, mafuta anyale; guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani wa fungo lokoma, nsalu yotsekera pa chipata choloŵera m'chihema,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:29-30

Mafuta otsala amene ali m'dzanja la wansembe aŵapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo, kuti amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta. Tsono wansembeyo atuluke kunja kwa mahema, ndipo amuwonetsetse wodwalayo. Ngati wakhateyo apezeke kuti wachira, Tsono malinga ndi m'mene adapezeramo, apereke njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:10

Aroni azidzachita mwambo wopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Ndi magazi a nyama zija za nsembe zopepesera machimo azidzayeretsera guwa limeneli kamodzi pa chaka. Zimenezi zizidzachitikanso m'mibadwo yanu yonse. Guwa limeneli lidzakhala loyera kwambiri, lopatulikira Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:8-9

mafuta anyale, zonunkhira zopangira mafuta odzozera, ndiponso zopangira lubani wonunkhira bwino, miyala ya mtundu wa onikisi ndi ina yokoma yoika pa chovala chaunsembe cha efodi ndiponso pa chovala chapachifuwa.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 7:10

Ndipo chopereka chilichonse cha chakudya chosakaniza ndi mafuta kapena chouma, chikhale cha ana onse a Aroni. Anawo aigaŵane molingana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:27-29

awazeko mafutawo kasanu ndi kaŵiri ndi chala cha ku dzanja lamanja pamaso pa Chauta. Apakekonso mafuta omwewo pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pomwe anali atapaka magazi a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija. Mafuta otsala amene ali m'dzanja la wansembe aŵapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo, kuti amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:28

Apakekonso mafuta omwewo pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pomwe anali atapaka magazi a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:23-24

“Utenge zonunkhira bwino kwambiri zokwanira makilogaramu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogaramu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa kinamoni, makilogaramu atatu a nzimbe zonunkhira bwino, makilogaramu asanu ndi limodzi a kasiya (zonsezo potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu). Ndipo muwonjeze mafuta okwanira malita anai a olivi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 18:8

Chauta adauzanso Aroni kuti, “Pa zopereka kwa Ine, ndakupatsa zotsala zimene amasunga, ndiye kuti zinthu zimene Aisraele amapatulira Ine. Ndakupatsa zimenezi kuti zikhale gawo lako ndi la ana ako, kuti zikhale zanu mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:10-13

“Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, wodwalayo atenge anaankhosa amphongo aŵiri opanda chilema, atengenso mwanawankhosa mmodzi wamkazi, wa chaka chimodzi, wopanda chilema, ndi chochepereka cha chakudya wosalala wolemera makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta, ndiponso mafuta okwanira limodzi mwa magawo atatu a lita. Wansembe amene ayeretse wodwalayo, aimiritse munthu woti ayeretsedweyo ali ndi zopereka zake zonse, pamaso pa Chauta, pakhomo pa chihema chamsonkhano. Wansembe atengeko mwanawankhosa wamphongo mmodzi ndi kumpereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja. Aziweyule, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta. Mwanawankhosayo amuphere pamalo pomwe amaphera nyama yoperekera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, ndiye kuti pa malo oyera aja, pakuti chopereka chopepesera kupalamula ndi chake cha wansembe, monga momwe chimakhalira chopereka chopepesera machimo. Zoperekazo nzoyera kopambana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 133:1-2

Ati kukoma ndi kukondweretsa ati, anthu akakhala amodzi mwaubale! Ndi ngati mafuta amtengowapatali oŵathira pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aroni, oyenderera mpaka ku khosi la mkanjo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:19-20

Pambuyo pake wansembe apereke nsembe yopepesera machimo, kuti achite mwambo wompepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Kenaka wansembeyo aphe nyama yoperekera nsembe yopsereza, “Lamulo la munthu wakhate pa tsiku la kuyeretsedwa kwake nali: Abwere naye kwa wansembe. ndipo aipereke pamodzi ndi chopereka cha chakudya pa guwa. Atatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu wodwalayo, ndipo pamenepo munthuyo adzakhala woyeretsedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:3

Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 18:8-9

Chauta adauzanso Aroni kuti, “Pa zopereka kwa Ine, ndakupatsa zotsala zimene amasunga, ndiye kuti zinthu zimene Aisraele amapatulira Ine. Ndakupatsa zimenezi kuti zikhale gawo lako ndi la ana ako, kuti zikhale zanu mpaka muyaya. Mwa zopereka zoyera kopambana zimene sadazitenthe pa guwa, zanu zikhale izi: chepereka chonse cha chakudya, nsembe zao zonse zopepesera machimo ndi nsembe zao zonse zopepesera kupalamula, zimene amapereka kwa Ine, zonsezo zikhale zoyera kwa iwe ndi kwa ana ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:10-12

“Anthu onse aluso pakati panupa abwere, ndipo apange zonse zimene Chauta adalamula. Apange chihema cha Chauta, hema lake pamodzi ndi chophimbira chake, ngoŵe zake zokoŵera, mafulemu ake, mitanda yake, nsanamira zake pamodzi ndi masinde ake omwe. Apangenso bokosi lachipangano ndi mphiko zake, chivundikiro chake cha bokosilo ndi nsalu zotchinga bokosilo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:6-8

mafuta a nyale, zonunkhira za mafuta odzozera, ndiponso lubani wa fungo lokoma. Ulandirenso miyala yokoma ya onikisi, ndiponso miyala ina yoti uike pa chovala chaunsembe cha efodi, ndi pa chovala chapachifuwa. Ndipo andipangire chihema chopatulika kuti Ine ndidzakhale pakati pao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:34

Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:21-24

“Koma munthu wodwalayo akakhala wosauka, kuti alibe zonsezo, apereke mwanawankhosa wamphongo kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula. Aipereke moweyula manja, kuti achite mwambo wompepesera. Aperekenso kilogaramu limodzi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, kuti ukhale nsembe yaufa, pamodzi ndi mafuta okwanira limodzi mwa magawo atatu a lita. Aperekenso njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, monga m'mene angathere. Imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo, inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pakhomo pa chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta, kuti munthuyo ayeretsedwe. Wansembe atenge mwanawankhosa woperekera nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:1-3

Tsono Chauta adauza Mose kuti, Tsono udzozenso guwa loperekapo nsembe zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake zomwe. Guwalo ulipereke kwa Mulungu, kuti likhale loyera ndipo lidzakhaladi loyera kopambana. Udzoze beseni losambira, pamodzi ndi phaka lake lomwe, ndipo ulipereke kwa Mulungu, kuti likhale loyera. “Pambuyo pake ubwere ndi Aroni ku chipata cha chihema chamsonkhano, pamodzi ndi ana ake omwe, ndipo onsewo asambe kumeneko. Aroniyo umuveke zovala zopatulika. Umdzoze, ndipo umpatule kuti akhale wansembe wonditumikira Ine. Ana ake abwerenso, ndipo uŵaveke miinjiro. Tsono uŵadzoze monga momwe udadzozera bambo wao, kuti akhale ansembe onditumikira Ine. Kudzozedwako kudzaŵasandutsa ansembe pa mibabwo ndi mibadwo.” Mose adachita zonse, monga momwe Chauta adamlamulira. Motero pa tsiku loyamba la mwezi woyamba chaka chachiŵiri, malo opatulika adautsidwa. Poutsa malowo, Mose adakhazika masinde ake pansi, ndipo adautsa mafulemu ake, nalumikiza mitanda yake, nautsanso nsanamira zake zija. Pambuyo pake adautsa chihema pamwamba pa malo opatulikawo, nachiphimba ndi chophimbira chake cha chihema, monga momwe Chauta adamlamulira. “Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, uutse chihema chamsonkhano. Tsono adatenga miyala yaumboni ija naiika m'bokosi muja. Adapisa mphiko zija m'mphete za bokosilo, naika chivundikiro pamwamba pake. Kenaka adaika bokosilo m'malo opatulika, ndipo adaika nsalu zochingira. Motero adachinga bokosi laumboni, monga momwe Chauta adamlamulira. Tsono m'chihema chamsonkhanomo adaikamo tebulo, chakumpoto kwa malo opatulika, kunja kwa nsalu yochinga ija, ndipo pamwamba pa tebulolo adaikapo buledi, monga momwe Chauta adamlamulira. M'chihema chamsonkanomo adaikamo choikaponyale mopenyana ndi tebulo chakumwera kwake kwa malo opatulika. Tsono pa choikaponyalecho adaikapo nyale, kuti zikhale pamaso pa Chauta, monga momwe Iye adalamulira Mose. M'chihema chamsonkhanomo adaikamo guwa lagolide patsogolo pa nsalu yochinga. Adafukiza lubani wa fungo lokoma paguwapo, monga momwe Chauta adamlamulira. Pa khomo la malo opatulika adaikapo nsalu yochinga. Ndipo adaika guwa la nsembe zopsereza pa khomo la chihema chamsonkhano. Pa guwa limenelo adaperekapo nsembe zopsereza ndiponso chopereka cha chakudya, monga momwe Chauta adamlamulira. Bokosi m'mene muli miyala yaumboni uliike m'menemo, ndipo bokosilo uliphimbe ndi nsalu kuti ulichinge.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:1-3

Atatsala masiku asanu ndi limodzi kuti chifike chikondwerero cha Paska, Yesu adadza ku Betaniya, kumene kunali Lazaro uja amene Iye adamuukitsa kwa akufa. Motero akulu a ansembe adaapangana zoti aphe ndi Lazaro yemwe, pakuti chifukwa cha iyeyo anthu ambiri ankaŵachokera nkumakhulupirira Yesu. M'maŵa mwake anthu ambirimbiri amene anali atabwera ku chikondwerero cha Paska chija, adamva kuti Yesu akubwera ku Yerusalemu. Motero adatenga nthambi za kanjedza natuluka kukamchingamira. Ankafuula kuti, “Ulemu kwa Mulungu! Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye! Idalitsidwe Mfumu ya Israele!” Tsono Yesu adapeza mwanawabulu nakwerapo, monga akunenera Malembo kuti, “Usaope, iwe mzinda wa Ziyoni. Ona, Mfumu yako ilikudza, yakwera pa mwanawabulu.” Pa nthaŵi imeneyo ophunzira ake sadazimvetse zimenezo. Koma Yesu atauka ndi ulemerero, iwo adakumbukira kuti zimenezi zidalembedwa kunena za Iye, ndipo kuti adamchitiradi zimenezi. Paja pamene Yesu adaaitana Lazaro kuti atuluke m'manda nkumuukitsa kwa akufa, panali anthu ambirimbiri. Tsono iwowo ankasimba m'mene adaaziwonera. Nchifukwa chake anthu onsewo adakamchingamira, popeza kuti anali atamva kuti Iye adaachita chizindikiro chozizwitsa chimenechi. Pamenepo Afarisi adayamba kuuzana kuti, “Mukuwonatu kuti sitikuphulapo kanthu konse. Onani anthu onse akumthamangira.” Adamkonzera Yesu chakudya kumeneko, ndipo Marita ankaŵatumikira. Lazaro anali mmodzi mwa amene ankadya naye pamodzi. Koma panali Agriki ena pakati pa anthu amene adaakapembedza pa chikondwererocho. Iwowo adapita kwa Filipo, amene kwao kunali ku Betsaida wa ku Galileya, nakampempha kuti, “Pepani bambo, timati tidzaone Yesu.” Filipo adakauza Andrea, ndipo Andrea pamodzi ndi Filipoyo adakauza Yesu. Yesu adati, “Yafika nthaŵi yoti Mwana wa Munthu alandire ulemerero wake. Kunena zoona, mbeu ya tirigu imakhalabe imodzi yomweyo ngati siigwa m'nthaka nkufa. Koma ikafa, imabala zipatso zambiri. Munthu amene amakonda moyo wake, adzautaya, koma amene saikapo mtima pa moyo wake pansi pano, adzausungira ku moyo wosatha. Ngati munthu anditumikira Ine, anditsatire, motero kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Munthu akanditumikira Ine, Atate anga adzamlemekeza.” “Tsopano mtima wanga wavutika. Nanga ndinene chiyani? Kodi ndinene kuti, ‘Atate, mundipulumutse ku nthaŵi iyi?’ Iyai, kwenikweni ndidadzera nthaŵi imeneyi. Atate, onetsani ulemerero wa dzina lanu.” Pamenepo kudamveka mau ochokera kumwamba akuti, “Ndauwonetsa ulemererowo ndipo ndidzauwonetsanso.” Panali khamu la anthu pamenepo. Tsono pamene adamva mauwo, adati, “Kwagunda bingu.” Koma ena adati, “Mngelo walankhula naye.” Tsono Maria adatenga mafuta onunkhira zedi a narido weniweni, amtengowapatali, okwanira theka la lita, nayamba kudzoza mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake. M'nyumba monsemo mumvekere guu ndi fungo la mafutawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:6-7

mafuta a nyale, zonunkhira za mafuta odzozera, ndiponso lubani wa fungo lokoma. Ulandirenso miyala yokoma ya onikisi, ndiponso miyala ina yoti uike pa chovala chaunsembe cha efodi, ndi pa chovala chapachifuwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 2:10

Chauta adzatswanya adani ake, adzaŵaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba. Chauta adzaŵaweruza mpaka ku mathero a dziko lapansi. Koma adzalimbikitsa mfumu yake, adzakuza mphamvu za wodzozedwa wake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 2:2-3

ndipo abwere nawo kwa ansembe, ana a Aroni. Atapeko ufa wosakaniza ndi mafuta uja dzanja limodzi, ndi lubani wake yense. Tsono wansembe atenthe zimenezo pa guwa, kusonyeza kuti nsembeyo yaperekedwa kwa Chauta, ndi nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta. Zotsala za chopereka cha chakudyacho zikhale za Aroni pamodzi ndi ana ake. Chimenecho ndicho chigawo chopatulika kopambana, chifukwa chatapidwa pa nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:29-30

Motero Aisraele onse, amuna ndi akazi omwe, amene adafuna ndi mtima wao wonse kupereka zao ku ntchito zimene Chauta adalamula kudzera mwa Mose, adabwera ndi zopereka zao kwa Chauta. Pa tsiku la Sabata limenelo, musamasonkha ndi moto womwe m'nyumba mwanu.” Pambuyo pake Mose adauza Aisraele kuti, “Chauta wasankhula Bezalele, mwana wa Uri, mdzukulu wa Huri, wa fuko la Yuda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:22

Adati, “Musaŵakhudze odzozedwa anga, musaŵachite choipa aneneri anga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:5-6

Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona. Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta, mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira. Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga. Ndidzakhala m'Nyumba mwanu moyo wanga wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Yesu, ndimakukondani ndi mtima wanga wonse, ndimakutamandani chifukwa cha ukulu ndi kukongola kwanu. Ndinu Mulungu wanga, kuyambira m'mimba mwa mayi wanga munandisankha ndipo munaika cholinga chosatha mwa ine. Ndingaleke bwanji kukudalitsani? Mzimu wanga umakondwerera ukulu wanu chifukwa cha chikondi chanu chomwe mwandionetsa, ndipo m'mawa uliwonse mumandikomera mtima. Mzimu Woyera, ndimadzigonjera pansi pa mapazi anu ndipo ndikuvomereza kuti zonse zomwe ndili nazo ndi chifukwa cha inu. Palibe chomwe ndingadzitamandire nacho; ulemerero wonse ndi wanu. Lero ndikupemphani kuti mundithandize kukhala wolimba m'maitanidwe anu. Musandilole kupatuka ku chifuniro chanu. Ndikufuna kukhala mwa inu kuti ndikwaniritse ntchito yomwe munandipatsa, chifukwa munandipaka mafuta kuti ndilalikire uthenga wanu ndikulimbitsa thupi lanu. Mundipatse nzeru zanu ndi luntha lanu, ndipo mundionetse njira yoyenera kutsata. Zikomo chifukwa cha zonse, chifukwa cha chisomo ndi chiyanjo chanu. Ndimakutamandani chifukwa cha amene muli ndi zonse zomwe mwatichitira. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa