Mtima wanga ukukondwera kwambiri tikamadziwa kuti tili ogwirizana mwa Khristu. Tiyenera kukhala odzichepetsa, ofatsa, oleza mtima, ndi okhala bwino wina ndi mnzake. Tili ngati ziwalo za thupi limodzi, thupi lauzimu la Khristu.
Baibulo limatiuza mu Aefeso 2:15-16 kuti Khristu “anachotsa udani pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina mwa kufa kwake pamtanda. Iye anabweretsa mtendere pakati pa magulu awiriwa ndi kuwagwirizanitsa kukhala thupi limodzi, logwirizana ndi Mulungu.” Uku ndiko kuzama kwa chikondi chake kwa ife.
Ndimakumbukira pemphero la Yesu asanapite pamtanda, pomwe anapempherera ife tonse, kuti “onse akhale amodzi; monga Inu, Atate, muli mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akhale amodzi mwa Ife; kuti dziko likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. Ine ndawapatsa ulemerero umene Inundipatsa Ine, kuti akhale amodzi, monganso Ife tiri amodzi” (Yohane 17:21-22). Ndi pemphero lamphamvu loti tidzipendere nawo tsiku ndi tsiku.
Tiyeni tizitsatira chitsanzo cha Khristu, ndi kukhala ogwirizana mwa chikondi chake. Ndi chikhumbo changa kuti ife tonse tiyesetse kukhala ogwirizana, monga momwe Iye anatifunira.
Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.
Inu ndinu mboni, Mulungu yemwe ndi mboninso, kuti mkhalidwe wathu pakati pa inu okhulupirira unali wangwiro, wolungama, ndi wopanda cholakwa.
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.
M'dzina la Khristu Yesu mundiperekereko moni kwa aliyense wamumpingo. Akukupatsani moni abale amene ndili nawo pamodzi kuno.
Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
Zoonadi ntchito imeneyi yomwe mukuchitira anthu a Mulungu, siingoŵathandiza pa zosoŵa zao, komanso chotsatira chake china nchakuti anthu ochuluka adzathokoza Mulungu kwambiri.
Koma tsopanoli ndikupita ku Yerusalemu kukapereka chithandizo kwa anthu a Mulungu kumeneko.
Kunena za zopereka zothandizira akhristu a ku Yerusalemu, inunso muchite monga momwe ndidalongosolera m'mipingo ya ku Galatiya.
Tikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto. Mulungu adakupatulani mwa Khristu Yesu, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake, pamodzi ndi anthu onse amene ponseponse amatama dzina la Ambuye Yesu Khristu mopemba. Iye ndiye Mbuye wathu ndi Mbuye waonso. Nanga ali kuti anthu anzeru? Ali kuti aphunzitsi a Malamulo a Mose? Ali kuti anthu onyadira nzeru zamakono zapansipano? Monga Mulungu sadaonetse kuti kudalira nzeru zapansipano nkopusa? Pakuti mwa nzeru zake Mulungu adakonzeratu kuti anthuwo asamdziŵe ndi nzeru zao. Koma kudamkomera Mulungu kupulumutsa anthu okhulupirira ndi mau opusa amene timalalika. Ayuda amafuna kuwona zozizwitsa, pamene Agriki amafunafuna nzeru. Koma ife timalalika Khristu amene adapachikidwa pa mtanda. Kwa Ayuda mau ameneŵa ndi okhumudwitsa, pamene kwa anthu a mitundu ina mauŵa ndi opusa. Koma amene Mulungu adaŵaitana, kaya ndi Ayuda kaya ndi Agriki, onsewo amazindikira kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru ya Mulungu. Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu. Abale, taganizani m'mene munaliri pamene Mulungu adakuitanani. Pakati panu panalibe ambiri amene anthu ankaŵayesa anzeru. Panalibenso ambiri amphamvu, kapena obadwa m'mabanja omveka. Koma Mulungu adasankha zimene anthu amaziyesa zopusa, kuti Iye anyazitse nazo anthu anzeru. Adasankhanso zimene anthu amaziyesa zofooka, kuti Iye anyazitse nazo anthu amphamvu. Ndipo zimene anthu amaziyesa zachabe, zonyozeka ndi zosakhala zenizeni, Mulungu adazisankha kuti athetse mphamvu zinthu zimene iwowo amayesa kuti ndiye zenizeni. Mulungu adachita zimenezi kuti pasakhale wina aliyense woti nkumadzitukumula pamaso pake. Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
Ndikulembera inu nonse amene muli ku Roma, amene Mulungu amakukondani, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake. Mulungu Atate athu ndi Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”
“Koma inuyo anthu asati azikutchulani aphunzitsi, pakuti muli ndi Mphunzitsi mmodzi yekha, ndipo nonsenu muli pa chibale.
Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.”
Ndilikudza kwa Inu. Ine sindikhalanso pansi pano ai, koma iwoŵa akhala pansi pano. Atate oyera, asungeni iwoŵa m'dzina lanu limene mudandipatsa, kuti akhale amodzi monga ife.
Ndikuŵapempherera kuti iwo onse akhale amodzi. Monga Inu Atate mumakhala mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife. Motero anthu onse adzakhulupirira kuti mudandituma. Ulemerero womwewo umene mudandipatsa, ndaŵapatsanso iwoŵa. Akhale amodzi monga Ife tili amodzi. Ine ndikhale mwa iwo, Inu mwa Ine, kuti akhale amodzi kwenikweni. Motero anthu onse adzazindikira kuti mudandituma ndinu, ndipo kuti mumaŵakonda monga momwe mumandikondera Ine.
Onseŵa ankalimbikira kupemphera ndi mtima umodzi, pamodzi ndi akazi ena, ndi Maria amai ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.
Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m'nyumba imodzi.
Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi. Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao.
Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “Zimene ndiri nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse. Atumwi ankachita umboni ndi mphamvu yaikulu kuti Ambuye Yesu adaukadi kwa akufa, ndipo onse Mulungu ankaŵakomera mtima kwambiri.
Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Khonde la Solomoni.
Tsono titasonkhana, tavomerezana kusankha anthu ndi kuŵatuma kwa inu. Adzabwera pamodzi ndi okondedwa athu Barnabasi ndi Paulo.
M'thupi lathu limodzi lomweli tili ndi ziwalo zambiri, ndipo ziwalozo zili ndi ntchito zosiyanasiyana. Momwemonso ife, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, olumikizana mwa Khristu, ndipo tonse, aliyense pa mbali yake, ndife ziwalo zolumikizana.
Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.
Tsono wobzala sasiyana ndi wothirira, ndipo aliyense adzalandira mphotho yake molingana ndi ntchito imene adaigwira. Komabe ife ndife okhaokha ogwira ntchito ya Mulungu, inuyo ndinu munda wa Mulungu, ndinunso nyumba ya Mulungu.
Popeza kuti mkate ndi umodzi wokha, ife tonse, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, chifukwa tonse timagaŵana mkate umodzi womwewo.
Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.
Komatu ziwalo nzambiri, ngakhale thupi ndi limodzi lokha. Motero diso silingauze dzanja kuti, “Ndilibe nawe ntchito.” Ndiponso mutu sungauze mapazi kuti, “Ndilibe nanu ntchito.”
Adachita zimenezi kuti pasakhale kugaŵikana m'thupi, koma kuti ziwalo zonse zizisamalirana. Chiwalo chimodzi chikamamva kuŵaŵa, ziwalo zonse zimamvanso kuŵaŵa. Chiwalo chimodzi chikamalandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwa nao. Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu,
Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.
Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa. Iye adathetsa Malamulo a Mose pamodzi ndi malangizo ake ndi miyambo yake. Adachita zimenezi kuti kuchokera ku mitundu iŵiri ija, alenge mtundu umodzi watsopano, wokhala mwa Iye, kuti choncho adzetse mtendere. Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu.
Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera.
Chinsinsicho nchakuti mwa Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda. Pamodzinso ndi Ayuda ali ziwalo za thupi limodzi, ndipo mwa Khristu Yesu amalandira nao lonjezo la Mulungu.
Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako. Iye amene adaatsika, ndi yemweyo amene adakwera, nabzola Kumwamba konse, kuti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu. Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga amene amasokeretsa anthu ndi kuchenjera kwao Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi. Tsono m'dzina la Ambuye ndikukuuzani, ndipo ndikunenetsa, kuti musayendenso monga amachitira akunja potsata maganizo ao achabe. Nzeru zao zidachita chidima, sangalandire nao konse moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene udadza mwa iwo kaamba ka kuuma mtima kwao. Mitima yao idaludzulala ndipo adangodzipereka ku zonyansa, kuti azichita zoipa zilizonse mosadziletsa. Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai, ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu. Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni. Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu. Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni. Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa. M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo. ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.
Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu Woyera mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene Mulungu adakuitanirani. Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi. Pali Mulungu mmodzi amene ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, ndipo ali mwa onse.
Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu.
Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.
Yuwodiyayo ndi Sintikeyo ndaŵapemba, chonde akhale omvana, popeza kuti ndi abale mwa Ambuye. Mulungu Atate athu alemekezedwe mpaka muyaya. Amen. M'dzina la Khristu Yesu mundiperekereko moni kwa aliyense wamumpingo. Akukupatsani moni abale amene ndili nawo pamodzi kuno. Akukupatsani moni anthu onse a Mulungu amene ali kuno, makamakanso ogwira ntchito ku nyumba ya Mfumu ya ku Roma. Ambuye Yesu Khristu akudalitseni. Ndiponso iwe, mnzanga weniweni pa ntchito yathuyi, bwanji uŵathandize azimaiŵa. Paja ameneŵa pofalitsa Uthenga Wabwino akhala akugwira ntchito kolimba pamodzi ndi ine ndi Klemensi ndi antchito anzanga ena onse, amene maina ao ngolembedwa m'buku la amoyo.
Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake. Ndiye chiyambi chake, Woyambirira mwa ouka kwa akufa, kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu.
Ndikufuna kuti zimenezi ziŵalimbitse mtima, ndipo azilunzana pamodzi m'chikondi, azikhala odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu. Motero adzatha kudziŵa mozama chinsinsi cha Mulungu chonena za Khristu.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.
Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima. Onetsetsani kuti wina aliyense mnzake akamchita choipa, asabwezere choipacho. Koma nthaŵi zonse muziyesetsa kuchitira zabwino anzanu ndi anthu ena onse.
Tiyenera kuthokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale. Nkoyeneradi kutero, chifukwa chikhulupiriro chanu chikunka chikukulirakulira kwambiri pamodzi ndi kukondana kwanu pakati pa inu nonse.
Munthu wachikulire usamdzudzule mokalipa, koma umchenjeze monga ngati bambo wako. Amuna achinyamata uzikhalitsana nawo ngati abale ako. Akhale mai woti anthu amamchitira umboni wakuti amachitadi ntchito zabwino. Akhale woti ankalera ana ake bwino, ankalandira bwino alendo, ankasambitsa mapazi a anthu a Mulungu, ndipo ankathandiza anthu amene anali m'mavuto. Akhalenso mai woti ankadzipereka pa ntchito zonse zabwino. Koma azimai amasiye a zaka zochepera uzikana kuŵalemba m'gulu limeneli. Pajatu zilakolako zao zikayamba kuŵavutitsa nkuŵalekanitsa ndi Khristu, amangofuna kukwatiwanso. Pamenepo amapezeka olakwa, chifukwa chosasunga lonjezo lao loyamba. Kuwonjezera pamenepo, amagwa m'chizoloŵezi cha kungokhala khale, motero amangoyendayenda ku nyumba za anthu. Tsonotu samangokhala khale chabe ai, amachitanso miseche nkumaloŵera za eni, ndi kukhala omalankhula zimene samayenera kulankhula. Nchifukwa chake nkadakonda kuti azimai amasiye a zaka zochepera azikwatiwanso, abale ana, ndipo azisamala bwino panyumba pao, kuti adani athu asapeze mpata wotisinjirira. Paja alipo kale azimai amasiye ena amene adapatukapo nkumatsata Satana. Koma ngati mai wina aliyense wachikhristu ali ndi achibale amene ali azimai amasiye, aziŵasamala iyeyo, osasenzetsa mpingo katundu wakeyo. Motero mpingo udzatha kusamala azimai amasiye opanda oŵathandiza. Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa. Paja Malembo akuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe imene ikupuntha tirigu.” Penanso akuti, “Wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake.” Usamamvere mau oneneza mkulu wa mpingo, pokhapokha ngati pali mboni ziŵiri kapena zitatu. Azimai achikulire uzikhalitsana nawo ngati amai ako, ndipo azimai a zaka zochepa uzikhalitsana nawo ngati alongo ako, m'kuyera mtima kwenikweni.
Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere. Uzikana matsutsano opusa ndi opanda nzeru, paja ukudziŵa kuti zotere zimautsa mikangano.
Uziŵakumbutsa anthu onse kuti azigonjera akulu oweruza ndi olamulira. Aziŵamvera ndipo azikhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino. Munthu woyambitsa mipatuko, utamdzudzula kaŵiri konse, usakhale nayenso nkanthu. Paja ukudziŵa kuti munthu wotere ngwosokonezeka ndipo ngwochimwa. Mwini wake yemwe amadziimba mlandu yekha. Ndikadzamtuma Aritema kapena Tikiko kwanuko, uchite chotheka kudzandipeza ku Nikopoli, chifukwa ndatsimikiza kuti ndikakhala kumeneko nyengo yachisanu ikubwerayi. Uyesetse kuthandiza Zena, katswiri wa malamulo uja ndiponso Apolo, kuti apitirize ulendo wao. Uwonenso kuti asasoŵe kanthu. Anthu athunso aziphunzira kudzipereka pa ntchito zabwino, kuti azithandiza pamene pali kusoŵa kwenikweni. Azitero kuti moyo wao usakhale wopanda phindu. Onse amene ali nane kuno akuti moni. Uperekeko moni kwa onse amene amatikonda chifukwa cha chikhulupiriro. Mulungu akukomereni mtima nonse. Uŵauze kuti asamakamba zoipa za wina aliyense, apewe kukangana, akhale ofatsa, ndipo nthaŵi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.
Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso. Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.
Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso. Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.
Mwayeretsa mitima yanu pakumvera choona, kotero kuti muzikondana ndi akhristu anzanu mosanyenga. Nchifukwa chake muzikondana ndi mtima wonse, mosafookera.
Inunso mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake. M'menemo muzitumikira ngati ansembe opatulika, pakupereka nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa. Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.
Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.” Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni.
Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.
Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu. Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake? Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu. Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene.
Inu okondedwa, ngati Mulungu adatikonda kwambiri chotere, ifenso tiyenera kumakondana. Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife.
Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone. Lamulo limene Iye adatipatsa ndi lakuti, wokonda Mulungu azikondanso mbale wake.
Tsono ife tiyenera kumaŵathandiza anthu otere, kuti tigwirizane nawo pa ntchito yofalitsa choona.
Koma inu okondedwa, muzithandizana kuti uzikulirakulira moyo wanu, umene udakhazikika pa maziko a chikhulupiriro chanu changwiro. Muzipemphera ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mudzisunge m'chikondi cha Mulungu podikira moyo wosatha, umene Ambuye athu Yesu Khristu adzakupatseni mwa chifundo chake.
Koma ena muŵapulumutse pakuŵalanditsa ku moto. Enanso muŵachitire chifundo, koma mwamantha, muzidana ngakhale ndi chovala chao chomwe choipitsidwa ndi machimo.
Ndine, Yohane, mbale wanu, ndipo ngati mnzanu wokhulupirira Yesu, ndili nanu limodzi mu ufumu wa Mulungu, komanso m'masautso ndi m'kupirira kosatepatepa. Ndidaponyedwa pa chilumba cha Patimosi, chifukwa cha kulalika mau a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni.
“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, ndidzampatsako chakudya chobisika cha mana. Ndidzampatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziŵa iye yekha, osati wina aliyense.”
Amene adzapambane, ndidzamsandutsa mzati wokhazikika m'Nyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso, ndipo pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga, ndi la mzinda wa Mulungu wanga. Mzindawo ndi Yerusalemu watsopano, wotsika Kumwamba kuchokera kwa Mulungu wanga. Pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano.
Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu.
Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.
Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Muzikumbukira am'ndende, ngati kuti mukuzunzikira nawo limodzi m'ndendemo. Muzikumbukira ovutitsidwa, pakuti inunso muli ndi thupi.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.
Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu.
Munthu aliyense wokhulupirira kuti Yesu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, iyeyo ndi mwana wa Mulungu. Ndipo aliyense wokonda nakubala, amakonda ndi mwana wake yemwe.