Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

65 Mau a Chipulumutso m’Chipangano Chakale

Kuyambira pachiyambi pomwe Mulungu analenga zinthu zonse, wandionetsa ine chikondi chake chachikulu. Analenganso mwamuna ndi mkazi kuti akhale paubwenzi naye.

Ngakhale titachimwa, Mulungu m’chifundo chake anasankha kundikhululukira ine osandilola kuti nditayike. Kale, chikhululukiro cha Mulungu chinkafuna nsembe ya nyama yopanda chilema, ndipo kudzera m’nsembeyi Ambuye anakhazikitsanso pangano lake ndi Nowa, lonjeza kuti sadzawononganso dziko lapansi chifukwa cha kuipa kwa anthu.

Nthawi zonse, Mulungu amayesetsa kundiyendetsa ine kubwera kwa Iye. Koma ambiri anasiya malamulo a Mulungu ndipo anatayika.

Kale, Ambuye anathandiza anthu ndipo nthawi zonse anali nafe, akutionetsa momwe angatipulumutsire. M’Chipangano Chakale, anthu ankayembekezera Mesiya, ndipo Mulungu anakwaniritsa malonjezo ake ngakhale asanatumize Mpulumutsi wathu.

Monga mmene lemba la Genesis 49:18 limati, “Ndikuyembekezera chipulumutso chanu, Yehova.”


Genesis 49:18

“Ndikuyembekeza chipulumutso chanu, Inu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 14:13

Apo Mose adayankha anthuwo kuti, “Musaope! Limbikani, ndipo muzingopenya zimene Chauta achite lero lino pofuna kukupulumutsani. Aejipito amene mukuŵaona lerowo, simudzaŵaonanso.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 13:16

Kulimba mtima kwanga ndiye kudzandipulumutse, poti munthu woipa sangafike pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 15:2

Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 2:1

Hana adapemphera nati, “Mtima wanga ukukondwa chifukwa cha zimene Chauta wandichitira, Ndikuyenda ndi mdidi chifukwa cha Chauta. Pakamwa panga pakula nkuseka adani anga monyodola. Ndakondwa kwambiri chifukwa mwandipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 11:13

Koma Saulo adati, “Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene aphedwe lero lino, pakuti lero Chauta wagwira ntchito yopulumutsa Aisraele.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 19:5

Paja adaaika moyo wake pa minga pakupha Goliyati Mfilisti uja. Pambuyo pake Chauta adachita zazikulu pakupambanitsa Aisraele pa nkhondo. Inu mudaona zimenezo ndi kukondwera nazo. Chifukwa chiyani tsono mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa, pofuna kumupha Davideyu?”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:5

Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 7:7

Koma ine ndidzadalira Chauta. Ndidzaika mtima pa Mulungu Mpulumutsi wanga. Mulungu wanga adzandimva.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 80:19

Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, tibwezereni mwakale. Mutiwonetse nkhope yoŵala, kuti ife tipulumuke.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 33:22

Pakuti Chauta ndiye muweruzi wathu. Chauta ndiye wotilamula, Chauta ndiye mfumu yathu, ndiye amene adzatipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:7

Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga, zonsezo zili kwa Mulungu. Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu, ndiye kothaŵira kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 3:15

Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkazi, padzakhala chidani pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake. Idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaluma chidendene chake.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:17-18

Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse.

Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:1

Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 12:3

“Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 17:14

Inu Chauta, chiritseni ndipo ndidzachiradi. Pulumutseni ndipo ndidzapulumukadi. Ndinu amene ndimakutamandani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 103:12

Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 19:25

“Mtheradi ndikudziŵa kuti Momboli wanga alipo, ndipo pa nthaŵi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 3:8

Mumatipulumutsa ndinu, Inu Chauta. Madalitso anu akhale pa anthu anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 79:9

Tithandizeni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, kuti dzina lanu likhale ndi ulemerero. Tipulumutseni, ndipo mutikhululukire zochimwa zathu, kuti dzina lanu lilemekezeke.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:19

Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo
Yona 2:9

Koma ine ndidzapereka nsembe kwa Inu ndi mau okuthokozani. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita ndithu. Chipulumutso nchochokera kwa Inu Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 22:47

“Chauta ndiwamoyo. Litamandike thanthwe langa, alemekezeke Mulungu wanga, thanthwe londipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:1

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:1-2

Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.

Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.

Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,

chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake.

Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 12:2

“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:39

Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 12:1

Tsiku limenelo aliyense mwa inu adzati: “Ndikukuthokozani Inu Chauta, pakuti ngakhale mudaandipsera mtima, mkwiyo wanu udaleka, ndipo mwandilimbitsa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 51:12

Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 45:22

“Inu anthu onse a pa dziko lapansi, tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke. Paja Ine ndine Mulungu, palibenso wina ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 18:30

“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:16

Yang'aneni mtumiki wanune mwa kukoma mtima kwanu, pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:20

Mulungu wathu ndi Mulungu wotilanditsa, ndi Mulungu, Ambuye amene amatipulumutsa ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 25:9

Tsiku limenelo aliyense adzati, “Uyu ndiye Mulungu wathu! Tidamkhulupirira kuti adzatipulumutsa. Iyeyu ndiye Chauta. Tidamkhulupirira, tsopano tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa choti watipulumutsadi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:39-40

Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:11

Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 45:17

Koma Israele amampulumutsa ndi Chauta, ndipo chipulumutso chake chidzakhalapo mpaka muyaya, Anthu ake sadzaŵachititsa manyazi konse, sadzakhala onyozeka konse.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 46:4

Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 3:22

“Bwererani kwa Ine, inu anthu anga osakhulupirika. Ndidzakuchiritsani kuti mukhale okhulupirika.” Inu mukuti, “Tikubwera kwa Inu, poti ndinu Chauta, Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 36:26-27

Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu.

Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:14-16

Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.

Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.

Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:14

Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga. Ndiye mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:81

Moyo wanga wafooka podikira chipulumutso chanu, ndikukhulupirira mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 130:7-8

Iwe Israele, khulupirira Chauta. Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.

Adzaombola Israele ku machimo ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 146:7

Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 7:7-9

Koma ine ndidzadalira Chauta. Ndidzaika mtima pa Mulungu Mpulumutsi wanga. Mulungu wanga adzandimva.

Inu adani athu musatiseke. Tidagwa inde, koma tidzadzukanso. Ngakhale tikhale mu mdima, Chauta ndiye nyale yathu.

Tachimwira Chauta, nchifukwa chake tiyenera kupirira mkwiyo wake, mpaka atazenga mlandu wathu ndi kuugamula. Koma pambuyo pake adzatiloŵetsa m'kuŵala, ndipo tidzaona chipulumutso chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 9:9

Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni. Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu. Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu. Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu, bulu wake kamwana tsono.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 7:18-19

Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika.

Mudzatichitiranso chifundo. Mudzapondereza pansi zolakwa zathu, mudzataya machimo athu onse pansi pa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 14:13-14

Apo Mose adayankha anthuwo kuti, “Musaope! Limbikani, ndipo muzingopenya zimene Chauta achite lero lino pofuna kukupulumutsani. Aejipito amene mukuŵaona lerowo, simudzaŵaonanso.

Chauta ndiye amene akumenyereni nkhondo. Inuyo simuchitapo kanthu konse.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:22

Chauta amaombola moyo wa atumiki ake. Palibe wothaŵira kwa Iye amene adzalangidwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 30:19-20

Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo,

Tsono inuyo ndi zidzukulu zanu mudzabwerera kwa Chauta, ndipo mau ake amene ndikukupatsani leroŵa mudzaŵamvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:41

Chauta, mundikonde ndi chikondi chanu chosasinthika, mundipulumutse monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:1-2

“Atonthozeni mtima, atonthozeni mtima anthu anga,” akutero Mulungu wanu.

Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake.

Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.

Kodi ndani adayesa kuchuluka kwa madzi am'nyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyesa kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani adayesa dothi lonse la dziko lapansi ndi dengu? Ndani adayesa kulemera kwa mapiri ndi magomo pa sikelo?

Ndani adalamulirapo maganizo a Chauta? Ndani adamphunzitsapo kanthu ngati mlangizi wake?

Kodi Chauta adapemphapo nzeru kwa yani, kuti adziŵe zinthu? Ndani adamuphunzitsa kuweruza molungama? Ndani adamphunzitsa kudziŵa zinthu? Ndani adamlangiza njira ya kumvetsa zinthu?

Mitundu ya anthu ili ngati kadontho ka madzi mu mtsuko, ilinso ngati fumbi chabe pa sikelo. M'manja mwa Chauta zilumba nzopepuka ngati fumbi.

Nkhalango ya ku Lebanoni siingakwanitse nkhuni zosonkhera moto, nyama zam'menemo sizingakwanire kuperekera nsembe yootcha.

Mitundu yonse ya anthu si kanthu konse pamaso pa Chauta, Iye amaziyesa zachabe ndi zopandapake.

Kodi Mulungu mungathe kumuyerekeza ndi yani? Kodi mungamufanizire ndi chiyani?

Likakhala fano, ndi munthu waluso amene amalipanga, kenaka mmisiri wa golide amalikuta ndi golide, nalipangira ukufu wasiliva.

“Muŵalankhule mofatsa anthu a ku Yerusalemu. Muŵauze kuti nthaŵi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndaŵalanga moŵirikiza chifukwa cha machimo ao.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:7

Ndidzapita kuti, pofuna kupewa Mzimu wanu, kapena pofuna kuthaŵa nkhope yanu?

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:10

Chauta ali ngati nsanja yolimba, munthu wokhulupirira amathaŵiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 143:10

Phunzitseni, kuti ndizichita zofuna Inu, pakuti ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoweli 2:32

Ndipo aliyense amene adzatama dzina la Chauta mopemba, adzapulumuka. Monga Iye adanenera, kudzakhala ena opulumuka ku phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo mwa otsalawo padzapezeka ena amene Chauta adzaŵaitana.

Mutu    |  Mabaibulo
Habakuku 3:18

komabe kwanga nkukondwerera mwa Chauta, kwanga nkusangalala chifukwa cha Mulungu Mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 2:10-11

“Inu anthu a ku Ziyoni, imbani mokondwa, chifukwa ndikubwera, ndikudzakhala pakati panu,” akutero Chauta.

Nthaŵi imeneyo anthu a mitundu yambiri adzabwera kwa Chauta, adzasanduka anthu ake, ndipo Iye adzakhala pakati panu. Apo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 59:1

Chauta si wosoŵa mphamvu, kuti angalephere kukupulumutsani, ndipo si gonthi, kuti nkupanda kumva zimene mukupempha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 53:5-6

Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.

Tonse tidaasokera ngati nkhosa. Aliyense mwa ife ankangodziyendera. Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Wopulumutsa! Lero ndikufuulirani inu, ndikuyang'ana nkhope yanu kuti ndikuyamikireni chifukwa ndinu Mulungu wa chipulumutso changa, ndi amene mumayenda patsogolo panga ngati chimphona champhamvu, mukumenyera nkhondo zanga. Monga momwe munatulutsira Aisraeli m'dziko la udziko la Igupto ndi dzanja lanu lamphamvu ndi lotambasuka, zikomo Atate, chifukwa simuswa mawu anu ndi mapangano anu. Zikomo chifukwa cha lonjezo la Mpulumutsi ndi Munthu Womasula. Kuyambira kale lomwe dziko lisanakhaleko, munaganizira kale za chipulumutso cha anthu, pakuti monga momwe imfa inadzera mwa munthu mmodzi, chiukiriro nachonso chidzera mwa munthu mmodzi. Zikomo Atate chifukwa kumene uchimo unachuluka, chisomo chinachulukirapo. Mulungu wanga, ulemerero ndi ulemu zonse zikhale zanu. M'dzina la Yesu. Ameni.