Mtanda uwu ndi chizindikiro cha nsembe yaikulu ya Yesu yopulumutsa anthu. Ndi chikondi chachikulu chomwe sichinachitikepo. Ndi umboni wa chikhululukiro chomwe sitinayenerere. Ndi Mulungu wokonda mbadwo woipa ndi wauchimo mwachilendo.
Mtanda umatikumbutsa kuti, ngakhale pakati pa mavuto ndi zowawa, pali chiyembekezo chomwe chimatilimbitsa. Mu mtanda muli kuwala pakati pa mdima, ndi chitonthozo chochokera mu lonjezo la moyo wosatha.
Kuyang'ana mtanda kumatipangitsa kuti tidzipende tokha ndikudzifunsa za tanthauzo la zochita zathu. Kumatilimbikitsa kuganizira za chikondi cha Mulungu chosatha ndi kufunitsitsa kwake kutipatsa mwayi wachiwiri. Ndi kudzera mu mtanda momwe timapezera chikhululukiro ndi kubwezeretsedwa ubwenzi ndi Mlengi wathu.
Mtanda umatilimbikitsa kutsegula mitima yathu ndikupereka miyoyo yathu monga nsembe, monga momwe Yesu anachitira. Umatipangitsa kudzikana tokha ndikutsatira mapazi ake, kubweretsa uthenga wake wachikondi ndi chifundo padziko lapansi.
Kuganizira za mtanda kutitsogolere kukhala moyo wotsatira malamulo a Mulungu, kusonyeza chifundo, chikhululukiro, ndi chikondi kwa anansi athu. Pa sitepe iliyonse yomwe timaponda, tipeze mphamvu zonyamula mtanda wathu ndikutsatira njira ya Yesu, podziwa kuti chikondi chake chosasinthika chimatiyandikira nthawi zonse.
Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.
Atatero Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata.
Ndakhala ndikukuuzani kaŵirikaŵiri, ndipo tsopano ndikubwerezanso molira misozi, kuti pali ambiri amene mayendedwe ao akutsimikiza kuti amadana ndi mtanda wa Khristu.
Koma ine sindinganyadire kanthu kena kalikonse, koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu basi. Popeza kuti Iye adafa pa mtanda, tsopano zapansipano kwa ine zili ngati zakufa, ndipo inenso kwa zapansipano, ndili ngati wopachikidwa.
Pafupi ndi mtanda wa Yesu padaaimirira amai ake, ndi mbale wa amai akewo, Maria mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa ku Magadala.
Iye atasenza mtanda wake, adatuluka naye mu mzinda kupita ku malo otchedwa “Malo a Chibade cha Mutu” (pa Chiyuda amati “Gologota.”)
Mulungu wa makolo athu adaukitsa Yesu kwa akufa, Iye amene inu mudaamupha pakumpachika pa mtanda.
Pamene ankatuluka mumzindamo, adakumana ndi munthu wina, dzina lake Simoni, wa ku Kirene. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu.
Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m'mene Iye amadziŵiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Pambuyo pake adauza onse amene anali pamenepo kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake tsiku ndi tsiku nkumanditsata.
Koma ndidaatsimikiza kuti pamene ndili pakati panu, ndiiŵale zina zonse, kupatula Yesu Khristu yekha, koma tsono amene adapachikidwa pa mtanda.
Pamene adafika ku malo otchedwa Chibade cha Mutu, adapachika Yesu komweko pa mtanda. Komwekonso adapachika zigaŵenga zija, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere.
Paja Khristu adandituma, osati kuti ndizibatiza ai, koma kuti ndizilalika Uthenga Wabwino. Ndipo ndiyenera kumaulalika mosagwiritsa ntchito luso lake la ulaliki, kuwopa kuti mtanda wa Khristu ungatheretu mphamvu.
Pilato adalemba chidziŵitso nachiika pamtandapo. Adaalembapo kuti, “Yesu wa ku Nazarete, Mfumu ya Ayuda.”
Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lao lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake.
Tidziŵa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo.
Asilikali adamtenga Yesu napita naye kuti akampachike. Pa njira adagwira munthu wina wa ku Kirene, dzina lake Simoni. Iye ankachokera ku midzi. Adamsenzetsa mtanda wa Yesu kuti aunyamule, azitsatira pambuyo pa Yesuyo.
Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.”
Atatero Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata. Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?
Yesu atalandira vinyo wosasayo adati, “Zonse ndakwaniritsa.” Kenaka adaŵeramitsa mutu, napereka mzimu.
Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu.
Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
“Ndithudi, iye adapirira masautso amene tikadayenera kuŵamva ifeyo, ndipo adalandira zoŵaŵa zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumlanga, ndi kumkantha ndi kumsautsa.
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.
Chimene ndikufuna nchakuti ndidziŵe Khristu, ndiponso mphamvu zimene zidamuukitsa kwa akufa. Ndikufunanso kumva zoŵaŵa pamodzi naye ndi kufanafana naye pa imfa yake.
Pambuyo pake Yesu adaitana khamu la anthu pamodzi ndi ophunzira aja kuti adze pafupi naye, ndipo adaŵauza kuti, “Munthu wofuna kutsana Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata.
Mulungu adachita zimene Malamulo a Mose sadathe kuzichita, chifukwa khalidwe la anthu lopendekera ku zoipa lidaŵafooketsa. Iye adatsutsa uchimo m'khalidwe lopendekera ku zoipalo, pakutuma Mwana wakewake, ali ndi thupi longa la ife anthu ochimwa, kuti m'thupilo adzagonjetse uchimowo.
Motero Ine ndidzampatsa ulemu woyenerera akuluakulu. Adzagaŵana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza kuti adapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo. Adasenza machimo a anthu ambiri, ndipo adaŵapempherera ochimwawo kuti akhululukidwe.
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
“Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye mwini. Si Mfumu ya Aisraele nanga? Atsiketu tsopano pamtandapo kuti timkhulupirire.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Paja adaakuuzani kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja mwa anthu ochimwa, kupachikidwa pa mtanda, ndi kuuka kwa akufa patapita masiku atatu.’ ”
Koma ife timalalika Khristu amene adapachikidwa pa mtanda. Kwa Ayuda mau ameneŵa ndi okhumudwitsa, pamene kwa anthu a mitundu ina mauŵa ndi opusa.
Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti, “Atate ndikupereka mzimu wanga m'manja mwanu.” Atanena zimenezi, adatsirizika.
Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.
Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
Chifukwa chakuti Yesu Khristu adachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako.
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu: “Ngati tidafa pamodzi naye, tidzakhala moyonso pamodzi naye.
Koma kunena za ine, abale, ngati ndikulalikabe kuti anthu aziwumbalidwa, nanga bwanji ndikuzunzidwabe? Ndikadalalikabe kuti anthu aziwumbalidwa, sibwenzi ndikuŵakhumudwitsa pakulalika mtanda wa Khristu.
Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera. Nanga pamenepo ifenso timakhaliranji m'zoopsa nthaŵi zonse? Abale anga, imfa ndimayenda nayo tsiku ndi tsiku. Ndikunenetsa zimenezi chifukwa ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu. Nanga pamene ndidalimbana ndi zilombo ku Efeso, ndidapindulapo chiyani, ngati ndinkatsata maganizo a anthu chabe? Ndiyetu ngati akufa sauka, tizingochita monga amanenera kuti, “Tiyeni tizidya ndi kumwa, pakuti maŵa tikufa.” Musadzinyenge. “Paja kuyanjana ndi anthu ochimwa kumaononga khalidwe.” Mudzidzimuke mumtima mwanu, ndipo muleke kuchimwa. Ena mwa inu sadziŵa Mulungu konse. Ndikukuuzani zimenezi kuti muchite manyazi. Koma kapena wina nkufunsa kuti, “Kodi akufa adzauka bwanji? Kodi adzakhala ndi thupi lotani?” Ati kupusa ati! Mbeu imene umafesa, siingamere ndi kukhala moyo itapanda kufa. Ndipo chimene ufesa, si mmera umene udzatuluka ai, koma ndi njere chabe, kaya ndi ya tirigu, kapena ya mtundu wina uliwonse. Koma Mulungu amaisandutsa mmera monga momwe Iye akufunira, mbeu iliyonse mmera wakutiwakuti. Mnofu sukhala wa mtundu umodzi. Pali mnofu wina wa anthu, wina wa nyama, wina wa mbalame, ndi wina wa nsomba. Adaikidwa m'manda, mkucha wake adauka, monga Malembo anenera.
M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi.
Paja Iye adakupatsani mwai, osati wakungokhulupirira Khristu ai, komanso wakumva zoŵaŵa chifukwa cha Iye.
Ndidaperekera msana wanga kwa ondimenya, ndiponso masaya anga kwa ondimwetula ndevu. Sindidaŵabisire nkhope ondinyoza ndi ondithira malovu.
Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu.
Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai, adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Anali wofooka pamene adapachikidwa pa mtanda, komabe tsopano ali moyo mwa mphamvu ya Mulungu. Ifenso ndife ofooka mwa Iye, koma tidzakhala amoyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, pogwira ntchito yathu pakati panu.
Iwo adatifera kuti tikakhale ndi moyo pamodzi naye, ngakhale pamene tili amoyo kapena titafa kale.
Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu.
Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu.
Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo.
Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?”
Anthu ambiri atamuwona adadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika, kotero kuti siinkachitanso ngati ya munthu. Maonekedwe ake sanalinso ngati a munthu.
Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adaŵafera, nauka kwa akufa chifukwa cha iwowo.
Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.
Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Adati, “Atate, ngati mukufuna, mundichotsere chikho chamasautsochi. Komabe muchite zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Motero mwa Khristu Mulungu adaŵalanda zida maufumu ndi maulamuliro onse, ndipo pamaso pa onse, adaŵayendetsa ngati akaidi pa mdipiti wokondwerera kupambana kwake.
Iyeyo adadzipereka kuti akhale momboli wa anthu onse. Umenewu unali umboni umene udaperekedwa pa nthaŵi yake.
Iye uja anthu adamnyoza ndipo adamkana. Anali munthu wamasautso, wozoloŵera zoŵaŵa. Anali ngati munthu amene anzake amaphimba kumaso akamuwona. Anthu adamnyoza, ndipo ife sitidamuyese kanthu.
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.
Kufa kumene adafako kunali kufa kolekana ndi uchimo, ndipo adafa kamodzi kokhako. Tsono moyo umene ali nawo tsopano ndi moyo woperekedwa kwa Mulungu.
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Akukomereninso mtima ndi kukupatsani mtendere Yesu Khristu, mboni yokhulupirika, amene ali woyambirira kulandira moyo waulemerero, amenenso ali Mfumu yolamula mafumu onse a pa dziko lapansi. Iyeyo amatikonda, ndipo ndi magazi ake adatimasula ku machimo athu.
Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi.
“Tsono anthu a pa banja la Davide ndi anthu onse a ku Yerusalemu ndidzaŵadzaza ndi mtima wachifundo ndi wakupemphera. Motero adzati atamuyang'ana amene adambaya, adzamlira kwabasi monga muja amamlirira mwana akakhala mmodzi yekha. Adzamliradi kwambiri monga muja amamlirira mwana wachisambamu.
Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse.
Komatu tikuwona kuti Yesu, amene pa kanthaŵi pang'ono adaasanduka wochepera kwa angelo, adalandira mphotho ya ulemerero ndi ulemu chifukwa adamva zoŵaŵa za imfa. Zidatero chifukwa mwa kukoma mtima kwake Mulungu adaafuna kuti afere anthu onse.
Yesuyo adaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha zochimwa zathu, ndipo adauka kwa akufa kuti tipezeke olungama pamaso pa Mulungu.
Agalatiya opusa inu, adakulodzani ndani? Pamene tidakulalikirani Yesu Khristu, tidamuwonetsa poyera pamaso panu ngati wopachikidwa pa mtanda.
Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere.
Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.” Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthaŵi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.”
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera.
Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa choŵeramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji? Chifukwa chiyani simukundithandiza mpang'ono pomwe, chifukwa chiyani simukumva mau a kubuula kwanga?
Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi opanda cholakwa pamaso pake.
Mkulu wa asilikali ndiponso amene anali naye polonda Yesu, ataona chivomezi chija ndi zina zonse zimene zidaachitika, adachita mantha kwambiri nati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.”
Sindiisandutsa yopandapake mphatso yaulere ya Mulungu. Pakuti ngati munthu atha kusanduka wolungama pamaso pa Mulungu pakutsata Malamulo, ndiye kuti Khristu adafa pachabe.
Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.
Koma Yesu adavutikabe koopsa mu mtima, nkumapemphera kolimba kuposa kale. Ndipo thukuta limene ankadza linali ngati madontho akuluakulu a magazi ogwera pansi.]
Yesu ameneyu sali ngati akulu a ansembe ena aja. Palibe chifukwa chakuti tsiku ndi tsiku azipereka nsembe poyamba chifukwa cha machimo ake, kenaka chifukwa cha machimo a anthu. Zimenezi adachitiratu kamodzi kokha, pakudzipereka yekha ngati nsembe.