Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -



60 Mauvesi a Chipulumutso ndi Moyo Wosatha

60 Mauvesi a Chipulumutso ndi Moyo Wosatha

Ndili mwana wake wa Mulungu, ndikukumbukira kuti kale tinali titatayika, osadziwa komwe tikupita. Tsogolo lathu linkaoneka ngati nyanja yamoto, malo a zowawa zosatha, odzaza ndi kulira ndi kutaya mtima.

Koma Mulungu, m’chikondi chake chachikulu ndi chifundo, anatumiza Mwana wake kuti adzatipulumutse. Iye anatulutsa chigamulo chimene chinali pa ife. Yesu, Mpulumutsi wathu, anatsegula njira yoti tidzakhale naye kosatha.

Cholowa chathu ndi ichi, umboni wa ubwino ndi chikondi cha Mulungu, kutipulumutsa ku mphamvu ya uchimo. Monga momwe lemba la Aroma 3:23-24 limatiuza, “onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo akuyesedwa olungama mfulu mwa chisomo chake, mwa chiwombolocho chimene chili mwa Khristu Yesu.”

Tiyeyese kusunga nsembe yaikulu imeneyi, mwa kumvera mawu ake ndi kuchita chifuniro chake. Tiyeni tipitirizebe kuyenda m’njira yake, ndi kukhala moyo wotsatira mfundo zake. Mmenemo tidzapeza mtendere ndi machiritso, ndi kukonzekera nyumba yokongola imene Mulungu watikonzera.

Tiyeni tikhale moyo woyera, kuti tsiku lina tidzamuone Mulungu maso ndi maso, ndi kumulambira kosatha.




Aroma 10:9

Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:13

Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:16

Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:47

Paja Ambuye adatilamula kuti, “ ‘Ndakuika kuti uunikire anthu akunja, kuti mwa iwe ndipulumutse dziko lonse lapansi.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:10

Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzafunafuna ndi kudzapulumutsa amene adatayika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:10

Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:31

Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:16-17

Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:12

Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:1

Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 7:10

Ankafuula mokweza mau kuti, “Chipulumutso nchochokera kwa Mulungu wathu wokhala pa mpando wachifumu, ndiponso kwa Mwanawankhosa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:16

Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:8-9

Motero Yesu, ngakhale anali Mwana wa Mulungu, adaphunzira kumvera pakumva zoŵaŵa. Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:21

Pamenepo aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba, adzapulumuka.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:21

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:19

Mukadzalimbikira, ndiye mudzapate moyo wanu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:23

Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:6

Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:9

Iye adatipulumutsa, ndipo adatiitana kuti tikhale anthu ake. Sadachite zimenezi chifukwa choti ife tidaachita zabwino ai, koma chifukwa mwiniwakeyo adaazikonzeratu motero, ndiponso chifukwa mwa Khristu Yesu adatikomera mtima nthaŵi isanayambe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:28

Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:10

Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:8-9

Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:35-36

Inu mwanditchinjiriza ndi chishango chanu chachipulumutso. Dzanja lanu lamanja landichirikiza, mwandikweza ndi chithandizo chanu. Mudandikuzira njira yanga kuti ndiyendemo bwino, choncho mapazi anga sadaterereke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:9

Paja Mulungu sadatisankhe kuti tidzaone mkwiyo wake, koma kuti tidzalandire chipulumutso kwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:39

Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:5

Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:44

Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene adandituma samkoka. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:5

Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:8-9

Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:7

Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga, zonsezo zili kwa Mulungu. Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu, ndiye kothaŵira kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:18

Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:12

Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 7:25

Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:25

Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:20

Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:10

Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:11-12

Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake. Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:24

“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:11-13

Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake. Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo. Inu amene mumakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu, ndakulemberani zimenezi kuti mudziŵe kuti muli ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:16

Komabe tikudziŵa kuti munthu sangapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo, koma pakukhulupirira Yesu Khristu. Ifenso tidakhulupirira Khristu Yesu kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira Khristu, osati chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Pakuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:16-17

Munthu wina wachinyamata adadza kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndizichita chabwino chanji kuti ndikalandire moyo wosatha?” Yesu adamuyankha kuti, “Bwanji ukundifunsa za chimene chili chabwino? Wabwino ndi Mmodzi yekha. Ngati ufuna kukaloŵa ku moyo, uzimvera Malamulo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:6-7

Adandiwuzanso kuti, “Kwatha! Alefa ndi Omega ndine. Ndiye kuti, Woyamba ndi Wotsiriza ndine. Aliyense womva ludzu, ndidzampatsa mwaulere madzi a pa kasupe wa madzi opatsa moyo. Aliyense amene adzapambane, adzalandira zimenezi, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wake, iye adzakhala mwana wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:3-5

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:28

Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:1

Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:25

Ndipo chimene adalonjeza nchimenechi: moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:40

Pakuti chimene Atate anga afuna nchakuti munthu aliyense amene aona Mwanayo namkhulupirira, akhale ndi moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:13-14

Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:13-14

Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza. Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adaŵaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:39-40

Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 11:25-26

Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:15

Aliyense wovomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye, ndipo iye amakhala mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:19

Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:10

Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:2

ndi kuŵapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha. Mulungu amene sanama, adalonjeza moyo wosathawu nthaŵi isanayambe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wachilungamo ndi wokhulupirika, ulemerero ndi ulemu zikhale kwa Inu! Ambuye Yesu, ndikukuthokozani chifukwa cha nsembe yanu pa mtanda, kutenga malo anga ndi kulipira mtengo umene ine sindingathe kulipira. Zikomo potsegulira njira yatsopano yotchedwa chipulumutso kwa anthu onse. Zikomo Yesu, chifukwa cha nsembe yanu yangwiro mwalipira ngongole yanga, mwandiwombola ndi kundipulumutsa, ndipo tsopano ndine womasuka ku chiweruzo chilichonse. Mawu anu amati: "Ndipo anafuula ndi mawu aakulu, nanena, Chipulumutso chikhale cha Mulungu wathu, wakukhala pa mpando wachifumu, ndi cha Mwanawankhosa." Yesu wanga wabwino, ndikukuthokozani chifukwa chondikondera kotero kuti lero nditha kulengeza kuti mulimonse mmene zinthu zilili, Inu ndinu yankho. Nsembe yanu pa mtanda sinali yachabe, kudzera mmenemo ndapeza chipulumutso, chikhululukiro, machiritso, ndipo mwandiyanjanitsa ndi Atate. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa