Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -



44 Mau a Chipulumutso Ngati Chatayika

44 Mau a Chipulumutso Ngati Chatayika

Ndikufuna ndikuuzeni nkhani yofunika kwambiri. Yesu, yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye amene amatipatsa chipulumutso ndi chikhululukiro cha machimo kudzera m’dzina lake lokha. Sitipulumutsidwa chifukwa cha ntchito zathu kuti tisadzitame, koma chifukwa cha chisomo chake. Chipulumutso ndi mphatso yamtengo wapatali yomwe tiyenera kuyisamalira ndi kuyiyamikira, chifukwa winawake anapereka moyo wake kuti apulumutse miyoyo yathu ku gehende.

Ndikofunika kukhala paubwenzi ndi Mzimu Woyera mumtima mwathu, kuti tifune kukhala naye tsiku ndi tsiku. Kupita kutchalitchi kumatithandiza kukhalabe olungama pamene timalandira chakudya chauzimu chomwe chimatilimbikitsa, chimatipangitsa kukhala atsopano, chimatitonthoza, ndiponso chimatiwongolera.

Kuti tipeze chipulumutso, tiyenera kukhulupirira Yesu ndi kusonyeza chikhulupiriro chathu mwa kumvera malamulo ake. Tchalitchi chiyenera kukhala choyera nthawi zonse, chodzazidwa ndi Mzimu Woyera. Ngakhale sitikudziwa tsiku kapena ola, kubwera kwa Mpulumutsi wathu kuli pafupi.

Palibe chodabwitsa kuposa chikhululukiro, chisomo, ndi chipulumutso chomwe Mulungu amatipatsa. Tiyeni tilankhule za Khristu ndi kugawana utheni wabwino wa chipulumutso!




Aroma 13:11

Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:22

Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:5

Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:11-13

Kudzaoneka aneneri onama ambiri, amene azidzasokeza anthu ambiri. Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:8

Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:12

Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:19-20

Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza, Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu. dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:21-23

Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa. Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse. Koma tsono muzikhala okhazikika kolimba pa maziko a chikhulupiriro chanu, osasunthika pa chiyembekezo chofumira ku Uthenga Wabwino umene mudamva. Uthenga Wabwinowu walalikidwa kwa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo Mulungu ndiye adandipatsa ine, Paulo, ntchito yoti ndiwulalike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:4-6

Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera. Ndipo adazindikira kukoma kwa mau a Mulungu, ndi mphamvu za nthaŵi imene inalikudzafika. Tsono akamkana Mulungu tsopano, akuchita ngati kumpachika iwo omwe Mwana wa Mulungu, ndi kumnyozetsa poyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:39

Ifetu sindife anthu oti nkumabwerera m'mbuyo ndi kutayika ai, ndife anthu okhulupirira, kuti tipulumuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:9

Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 2:13

Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:13

Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:1-3

Nchifukwa chake tsono, zimene tidamva, tizizisamala kwambiri, kuwopa kuti pang'ono ndi pang'ono tingazitaye. Paja Mulungu amene ndi Mlengi wa zonse ndipo zonse zimalinga kwa Iye, adafuna kufikitsa ana ake ambiri ku ulemerero. Tsono kudaamuyenera kuti mwa njira ya zoŵaŵa, amsandutse Yesu mtsogoleri wangwiro woŵatsogolera ku chipulumutso. Amene amayeretsa anthuyo, ndiponso anthu amene amayeretsedwawo, onse Tate wao ndi mmodzi. Nchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuŵatchula abale ake, ponena mau akuti, “Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu. Ndidzakutamandani pa msonkhano wa anthu anu.” Amanenanso kuti, “Ndidzakhulupirira Mulungu.” Penanso amanena kuti, “Ine ndili pano, pamodzi ndi ana amene Mulungu adandipatsa.” Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe adasanduka munthu wonga iwowo. Adachita zimenezi kuti ndi imfa yake aononge Satana amene anali ndi mphamvu yodzetsa imfa. Pakutero adafunanso kuti aŵamasule amene pa moyo wao wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa. Paja nchodziŵikiratu kuti sadatekeseke ndi angelo ai koma ndi zidzukulu za Abrahamu. Nchifukwa chake adaayenera kusanduka wofanafana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe onse wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, ndipo kuti pakutero achotse machimo a anthu. Tsono popeza kuti iye yemwe adazunzikapo ndi kuyesedwapo, ndiye kuti angathe kuŵathandiza anthu amene amayesedwa. Mau amene Mulungu adalankhula kudzera mwa angelo anali okhazikika ndithu, kotero kuti aliyense amene sadaŵamvere kapena amene adaŵanyoza, adalangidwa monga momwe kudamuyenerera. Nanga ife tingapulumuke bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiwo amene adalankhula poyamba za chipulumutsochi, kenaka amene adamva mau aowo, adatitsimikizira kuti ndi oona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:17

Tsono inu okondedwa, popeza kuti mwazidziŵiratu zimenezi, chenjerani kuti zolakwa za anthu ochimwa zingakusokeretseni ndipo mungagwedezeke kenaka nkugwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:5

Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:16

Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:26-27

Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:5-6

“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu. Ngati munthu sakhala mwa Ine, amamtaya kunja monga nthambi yodulidwa, ndipo amauma. Nthambi zotere amazitola, naziponya pa moto ndipo zimapsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:20-22

Chifukwatu ngati anthu apulumuka ku zodetsa za dziko lino lapansi, pakudziŵa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, pambuyo pake nkugwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zoipa zomwezo, potsiriza adzakhala oipa koposa m'mene analiri poyamba. Kukadakhala bwino kwa iwo akadakhala osadziŵa njira ya chilungamo, koposa kuileka atadziŵa lamulo loyera limene Mulungu adaŵapatsa. Pakutero akutsimikiza kuti ngwoona mwambi uja wakuti, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndi wina ujanso wakuti, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhuliranso m'matope.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:17

Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:8-9

Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:21-23

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna. Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’ Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:12

Tsono amene akuganiza kuti waimirira molimba, achenjere kuti angagwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:12

Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:6

Ngati munthu sakhala mwa Ine, amamtaya kunja monga nthambi yodulidwa, ndipo amauma. Nthambi zotere amazitola, naziponya pa moto ndipo zimapsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 7:25

Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:1

Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:1

Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:22

Pamenepo zindikirani kuti Mulungu ndi wachifundodi, komanso ndi waukali. Kwa anthu amene adagwa, ndi wokwiya, koma kwa inu ndi wachifundo, malinga mukasamala chifundo chake. Ngati simuchita zimenezi, adzakudulani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:28

Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:20

Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:4

Inu amene mukuyesa kusanduka olungama pakutsata Malamulowo, mudadzipatula nokha kusiya Khristu. Pamenepo mudalekana ndi madalitso aulere a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:13

Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:27

Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:8

Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 7:10

Ankafuula mokweza mau kuti, “Chipulumutso nchochokera kwa Mulungu wathu wokhala pa mpando wachifumu, ndiponso kwa Mwanawankhosa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:21

Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:5

Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:32-33

“Aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba. Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziŵa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba kuti sindimdziŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:13

Mbeu zogwera pa nthaka yapathanthwe zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nkuŵalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangokhulupirira kanthaŵi pang'ono chabe, mwakuti pa nthaŵi ya kuyesedwa, amabwerera m'mbuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:12

Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye. Ngati ife timkana, Iyenso adzatikana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:6-8

Iye adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Anthu amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pakuchita ntchito zabwino molimbikira, Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha. Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wathu Wamuyaya, Mwini Mphamvu Zonse, m'dzina la Yesu ndikukuthokozani chifukwa cha mpingo wanu waulemerero. Ndikukupemphani kuti mpingo uwu ukhale woyera ngati mkwatibwi wopanda banga, wopanda chidetso, wokhazikika m'pemphero. Ambuye Yesu, tikhale mpingo wogwirizana, wolimba m'chikhulupiriro, woyang'anira kubwera kwanu. Atate, monga thupi la Khristu, ndikupemphani kuti tikhale mpingo wovala zida zanu, mumphamvu yanu. Kuti tikhale oyang'anira, akupemphera, ndi kusamalira chipulumutso chathu. Monga momwe Mawu anu akunenera: "Mumasungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kuti mukafike pa chipulumutso chokonzeka kuwululidwa nthawi yomaliza." M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa