Njira ya moyo, ndiyendayenda ine ndekha. Nthawi zina njira imakhala yowala ndipo nthawi zina imakhala yamdima komanso yovuta.
Baibulo limandiphunzitsa kuti ndine woyang'anira zisankho zanga ndi njira zomwe ndimasankha. M'buku la Miyambo, mawu oti "njira" atchulidwa maulendo opitilira makumi asanu ndi limodzi. Mawuwa sakutanthauza kokha njira yeniyeni, komanso njira ya moyo wanga.
Mfumu yanzeru Solomoni imatilimbikitsa kuti: "Samalira mayendedwe a mapazi ako, ndipo njira zako zonse zikhale zolungama" (Miyambo 4:26). Apa, udindo uli pa ine kuti ndiyang'ane ndikusankha njira yolungama.
Njira ya chitsiru ndi ya munthu wanzeru zimasiyana kwambiri. Chitsiru chimayenda ngati munga minga yodzaza ndi zopinga. Mosiyana ndi izi, munthu wanzeru amayenda panjira yosalala, yopanda zopinga, akumwetulira (Miyambo 15:19).
Mtundu wa njira yanga si ngozi. Umadalira zisankho zanga ndi maganizo anga. Ngati nditaya njira za Mulungu, ndi chifukwa chosankha kutsatira chifuniro changa m'malo modalira Ambuye.
Baibulo limatichenjeza kuti: "Mtima wa munthu ukuganiza njira yake, koma Yehova ndiye wolamulira mayendedwe ake" (Miyambo 16:9).
Ngati ndikuona kuti ndikuchoka panjira za Mulungu, sinachedwe kuti ndikonzenso njira yanga. Ndiyenera kuzindikira udindo wanga ndikuvomereza zotsatira za zisankho zanga. Ndiyenera kusiya kuimba mlandu ena ndikuvomereza kuti Ambuye adzandifunsa za njira yanga.
Ndiyenera kudalira Ambuye, kufunafuna nzeru zake ndikutsatira malamulo ake. Ngakhale nditalakwitsa, chikondi ndi chisomo cha Mulungu zilipo kuti zinditsogolere kubwerera panjira yolungama.
Monga momwe wamasalmo ananenera: "Ntsogolereni mapazi anga m’mawu anu, ndipo musalole choipa chilichonse kundilamulira" (Salmo 119:133).
Choncho, poyenda ulendo wanga, ndikuyenera kukumbukira kuti ndine woyang'anira njira yanga. Ndiyenera kusankha mwanzeru ndikukhulupirira Ambuye kuti anditsogolere ku moyo wabwino womwe wandikonzera.
Munali ngati nkhosa zosokera, koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang'anirani.
Tonse tidaasokera ngati nkhosa. Aliyense mwa ife ankangodziyendera. Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu.
Koma ai, anthu onse ndi osokera, onsewo ndi oipa chimodzimodzi. Palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino, ai, palibiretu ndi mmodzi yemwe.
“Anthu anga anali ngati nkhosa zotayika. Abusa ao adaŵasokeza ndi kuŵayalukitsa ku mapiri. Ankangoyendayenda ku zitunda ndi ku mapiri, mpaka kuiŵala kwao.
“Tsono mukuganiza bwanji? Munthu atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nkutayika, kodi sangasiye 99 zina zija m'phiri nkukafunafuna imodzi yotayikayo? Ndithu ndikunenetsa kuti ataipeza, chimwemwe chake chokondwerera imeneyo chimapambana chokondwerera zina zija zimene sizidatayike. Chonchonso Atate anu amene ali Kumwamba safuna kuti ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa atayike.
“Ndani mwa inu ali ndi nkhosa 100, imodzi itatayikapo, sangasiye nkhosa zina zonse 99 zija ku busa, nkukafunafuna yotayikayo mpaka ataipeza? Ndipo ataipeza, amaisenza pamapewa pake mokondwa. Pofika kwao, amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndaipeza nkhosa yanga idaatayika ija.’ ” Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.”
“Tsono Alevi amene adaandisiya kutali pa nthaŵi imene Aisraele adaasokera potsata mafano, adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwao.
Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera. Ndipo adazindikira kukoma kwa mau a Mulungu, ndi mphamvu za nthaŵi imene inalikudzafika. Tsono akamkana Mulungu tsopano, akuchita ngati kumpachika iwo omwe Mwana wa Mulungu, ndi kumnyozetsa poyera.
Chimenechi chikhale chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene adamvera malamulo anga, osatsata Aisraele pamene adaasokera, monga m'mene adaachitira Alevi.
Chifukwatu ngati anthu apulumuka ku zodetsa za dziko lino lapansi, pakudziŵa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, pambuyo pake nkugwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zoipa zomwezo, potsiriza adzakhala oipa koposa m'mene analiri poyamba. Kukadakhala bwino kwa iwo akadakhala osadziŵa njira ya chilungamo, koposa kuileka atadziŵa lamulo loyera limene Mulungu adaŵapatsa. Pakutero akutsimikiza kuti ngwoona mwambi uja wakuti, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndi wina ujanso wakuti, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhuliranso m'matope.”
“Tsoka kwa iwo pakuti andisiya Ine. Aonongeke chifukwa chakuti andipandukira. Ndimafuna kuŵapulumutsa, koma amangolankhula zabodza za Ine.
uli ndi chikhulupiriro ndiponso ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa. Ena sadamvere pamene mtima wao unkaŵatsutsa, motero chikhulupiriro chao chidaonongeka. Ndikulembera iwe Timoteo, mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro. Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu akukomere mtima, akuchitire chifundo ndi kukupatsa mtendere. Mwa iwowo wina ndi Himeneo, wina Aleksandro, anthu amene ndaŵapereka kwa Satana kuti aphunzire kusanyoza Mulungu mwachipongwe.
Pamenepo zindikirani kuti Mulungu ndi wachifundodi, komanso ndi waukali. Kwa anthu amene adagwa, ndi wokwiya, koma kwa inu ndi wachifundo, malinga mukasamala chifundo chake. Ngati simuchita zimenezi, adzakudulani inunso.
Tsono ndidaukwiyira mbadwowo, ndipo ndidati, ‘Nthaŵi zonse amasokera mumtima mwao, sanaphunzirebe njira zanga.’
Pa nthaŵi imeneyo ambiri adzataya chikhulupiriro chao, azidzaperekana nkumadana. Kudzaoneka aneneri onama ambiri, amene azidzasokeza anthu ambiri. Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
Anthuwo adachita kuchoka pakati pathu, komabe sanali a gulu lathu kwenikweni. Pakuti akadakhala a gulu lathu, bwenzi akali nafebe. Koma adatichokera, kuti aonekere poyera kuti panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene anali wa gulu lathu.
Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza, Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu. dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
Ngati ukhumudwitsa mbale wako pakudya chakudya cha mtundu wakutiwakuti, ndiye kuti sukuyendanso m'chikondi. Usamuwononge ndi chakudya chako munthu amene Khristu adamufera.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Abale, mchenjere, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woipa ndi wosakhulupirira, womlekanitsa ndi Mulungu wamoyo. Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.
“Bwererani kwa Ine, inu anthu anga osakhulupirika. Ndidzakuchiritsani kuti mukhale okhulupirika.” Inu mukuti, “Tikubwera kwa Inu, poti ndinu Chauta, Mulungu wathu.
Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.
Muzidziyesa nokha inuyo kuti mutsimikize ngati mukusungadi chikhulupiriro chanu. Muzidzifunsitsa nokha. Simudziŵa nanga kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Ngati si choncho, mwalephereratu.
Munthu wosalungama adzalandira zoyenerera ntchito zake, koma munthu wabwino adzalandira mphotho ya ntchito zake.
Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Koma Ine ndakupempherera, kuti usaleke kundikhulupirira. Ndipo iweyo utatembenuka mtima, ukaŵalimbitse abale akoŵa.”
Tsono ndidati, “Inu Chauta, ndakuchimwirani, mundikomere mtima, muchiritse moyo wanga.”
Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu.
Pambuyo pake adauza onse amene anali pamenepo kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake tsiku ndi tsiku nkumanditsata.
Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake.
Onse amene ali kutali ndi Inu adzaonongeka, Inu mumaŵaononga amene ali osakhulupirika kwa Inu. Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera. Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse.
Pajatu kale ifenso tinali opusa, osamvera, ndi osokezedwa. Tinali akapolo a zilakolako zoipa ndi zisangalatso zamitundumitundu. Masiku onse tinkakhalira kuchita zoipa ndi kaduka, anthu kudana nafe, ndipo ife tomwe kumadana.
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna. Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’ Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’
Paja nthaŵi idzafika pamene anthu azidzakana chiphunzitso choona. M'malo mwake, chifukwa cholakalaka kumva zoŵakomera zokha, adzadzisankhira aphunzitsi ochuluka omaŵauza zimene iwo akufuna. Adzafulatira choona, osafunanso kuchimva, ndipo adzangotsata nthano chabe.
Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.
Koma anthu amene amatsata njira zao zokhotakhota, Chauta adzaŵapirikitsira kumene kuli anthu ochita zoipa. Mtendere ukhale ndi Israele.
Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai.
Ndakhala ndikukuuzani kaŵirikaŵiri, ndipo tsopano ndikubwerezanso molira misozi, kuti pali ambiri amene mayendedwe ao akutsimikiza kuti amadana ndi mtanda wa Khristu. Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha.
Nkhosa zofooka simudazilimbikitse, zodwala simudazichiritse, zopweteka simudazimange mabala ake, zosokera simudazibweze, ndipo zotayika simudazifunefune. Koma munkaziŵeta mozunza ndi mwankhalwe.
“Koma munthu wabwino akasanduka woipa, namachita zonyansa za mitundu yonse zimene anthu amachita, kodi munthu woteroyo nkukhala ndi moyo? Iyai, ntchito zake zonse zabwino sizidzakumbukika. Wapalamula, wachimwa, adzafa basi.
Ndikuŵachitira umboni kuti ndi achangudi pa zinthu za Mulungu, koma changu chake sadachimvetse bwino m'mene chiyenera kukhalira.
Ena adakhala mu mdima ali ndi chisoni, anali am'ndende ozunzika m'maunyolo achitsulo, pakuti adaatsutsa mau a Mulungu, adaakana monyoza malangizo a Wopambanazonse.
“Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ndi womwaza.
Inu amene mukuyesa kusanduka olungama pakutsata Malamulowo, mudadzipatula nokha kusiya Khristu. Pamenepo mudalekana ndi madalitso aulere a Mulungu.
Iwowo adasokera nkusiya choona. Amaphunzitsa kuti kuuka kwa akufa kudachitika kale. Motero amasokoneza chikhulupiriro cha anthu ena.
Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.
Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.
Mbeu zogwera pa nthaka yapathanthwe zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nkuŵalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangokhulupirira kanthaŵi pang'ono chabe, mwakuti pa nthaŵi ya kuyesedwa, amabwerera m'mbuyo.
Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.” Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda. Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola. Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.
Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa. Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse. Koma tsono muzikhala okhazikika kolimba pa maziko a chikhulupiriro chanu, osasunthika pa chiyembekezo chofumira ku Uthenga Wabwino umene mudamva. Uthenga Wabwinowu walalikidwa kwa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo Mulungu ndiye adandipatsa ine, Paulo, ntchito yoti ndiwulalike.
Ngakhale pakati pa inu nomwe, padzauka ena olankhula zonama nkumakopa ophunzira kuti aŵatsate.
Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino. Mulungu kumwambako waŵerama, akuyang'ana anthu pansi pano, kuti aone ngati angakhalepo mmodzi wanzeru wofunitsitsa Mulungu. Koma ai anthu onse ndi osokera, onsewo ndi oipa chimodzimodzi. Palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino, ai, palibiretu ndi mmodzi yemwe.
Chauta si wosoŵa mphamvu, kuti angalephere kukupulumutsani, ndipo si gonthi, kuti nkupanda kumva zimene mukupempha. Timapapasapapasa ngati anthu akhungu, tili ngati anthu opanda maso. Timaphunthwa masana ngati usiku. Ndife amoyo ndithu, komabe tili ngati anthu akufa. Tonse timabangula ngati zimbalangondo, ndipo timalira modandaula ngati nkhunda. Timayembekeza kuweruza kolungama, koma sitikupeza. Timadikiranso chipulumutso, koma chili nafe kutali. Inu Chauta, takuchimwirani kwambiri. Machimo athu akutitsutsa, zolakwa zathu zili pa ife, ndipo sitingakanepo nchimodzi chomwe. Takupandukirani, takukanani, Inu Chauta, ndipo takana kukutsatani. Tapanikiza anzathu, takupandukirani Inu. Maganizo athu ndi abodza, mau athu ndi onama. Kuweruza kolungama kwalekeka, ndipo kuchita zaungwiro kwaiŵalika. Zoona sizikupezekanso m'mabwalo a milandu, ndipo chilungamo sichikutha kupezeka kumeneko. Zoona zikusoŵa kumeneko, ndipo wina aliyense akapanda kuchita nawo zoipa, amapeza mavuto.” Chauta adaziwona zimenezi ndipo zidamunyansa kuti palibe chilungamo. Chauta adaona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe adadabwa kuti palibe wochitapo kanthu. Tsono adapambana ndi mphamvu zakezake, ndipo adadzilimbitsa ndi kulungama kwake. Adavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake adavala chisoti chachipulumutso. Adavala kulipsira ngati mkanjo, ndipo mkwiyo udakhala ngati chofunda chake, Chauta adzalanga adani a anthu ake molingana ndi zochita zao: adzaonetsa ukali kwa omuukira, ndipo adzalipsira adani ake. Adzalanga ngakhale okhala m'maiko akutali. Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho. Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho saamva zimene inu mumanena.
Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
Tsono popeza kuti iwo sadalabadireko za kumvera Mulungu, Mulunguyo adaŵasiya m'maganizo ao opusa, kotero kuti amachita zosayenera.
Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.
Nchifukwa chake abale, chitani changu koposa kale kutsimikiza kuti Mulungu adakuitanani ndipo adakusankhani. Mukatero simudzagwa konse.
Agalatiya opusa inu, adakulodzani ndani? Pamene tidakulalikirani Yesu Khristu, tidamuwonetsa poyera pamaso panu ngati wopachikidwa pa mtanda.
Munthu wochita zabwino amatsogolera anzake pa njira yokhoza, koma njira ya munthu woipa imaŵasokeretsa.
Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithudi, pali Ine ndemwe, sindikondwa ndikaona munthu woipa alikufa. Ndikadakonda kuti aleke kuchimwako kuti akhale ndi moyo. Inu Aisraele, muferanji? Tembenukani, lekani zoipa zimene mukuchita.
Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.
Paja mau a Mulungu akuti, “Ngati wolungama yemwe adzapulumuka movutikira, nanga munthu wochimwa, wonyozera za Mulungu, adzatani?”
Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’
Koma wopemphayo apemphe mokhulupirira, ndi mosakayika konse. Paja munthu wokayikakayika ali ngati mafunde apanyanja, amene amavunduka ndi kuŵinduka ndi mphepo. Munthu wotere asamaganiza kuti nkudzalandira kanthu kwa Ambuye ai; pakuti iyeyo ndi wa mitima iŵiri, ndi wosakhazikika pa zochita zake zonse.
Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu wonse ukhale wolunzana naye. Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri. Chenjerani kuti wina aliyense angakusokonezeni ndi mau olongosola nzeru zapatali. Ameneŵa ndi mau onyenga chabe. Paja nzeru zimenezi zimangochokera ku miyambo ya anthu, ndi ku maganizo ao okhudza zapansipano, osati kwa Khristu ai.
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta. Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu. Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino, opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu. Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.
Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa.
Nkofunika ndithu kuti pakhale kusiyana maganizo pakati panu, kuti amene ali okhoza pakati panu adziŵike.
Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.
Nchifukwa chake tsono, zimene tidamva, tizizisamala kwambiri, kuwopa kuti pang'ono ndi pang'ono tingazitaye.
Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya. Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.
Komabe panali aneneri ena onama ngakhale pakati pa Aisraele omwe. Momwemonso pakati pa inu padzaoneka aphunzitsi onama. Iwowo adzaloŵetsa mwachinsinsi zophunzitsa zonama ndi zoononga, ngakhale kukana kumene Mbuye wao amene adaŵaombola, ndipo motero adzadziitanira chiwonongeko mwamsanga.
Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziŵa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba kuti sindimdziŵa.
Mulungu sadaŵalekerere Ayuda, amene ali ngati nthambi zenizeni za mtengo. Kodi tsono mukuyesa kuti adzakulekererani inuyo? Pamenepo zindikirani kuti Mulungu ndi wachifundodi, komanso ndi waukali. Kwa anthu amene adagwa, ndi wokwiya, koma kwa inu ndi wachifundo, malinga mukasamala chifundo chake. Ngati simuchita zimenezi, adzakudulani inunso.
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni. Tayani zoipa zanu zonse zakale zimene mudachimwira Ine. Mukhale ndi mtima watsopano ndi nzeru zatsopano. Nanga muferenji, inu anthu a ku Israele? Sindikondwera nayo imfa ya munthu wina aliyense. Nchifukwa chake lapani, kuti mukhale ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Adatsala pang'ono kundichotsa pa dziko lapansi, komabe sindidaleke kutsata malamulo anu.
Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.
Kusiyana kwake pakati pa ana a Mulungu ndi ana a Satana kumaoneka motere: aliyense wosachita chilungamo, ndiponso wosakonda mnzake, sali mwana wa Mulungu.
Tsono musataye kulimba mtima kwanu, pakuti kumabweretsa mphotho yaikulu. Pafunikadi kupirira, kuti muchite zimene Mulungu akufuna, kuti motero mukalandire zimene adalonjeza.
Koma zikadzanyeka ndi moto, sadzalandira mphotho. Inde mwiniwakeyo adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wangopulumuka m'moto.
Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino, osalola kuti adani anu azikuwopsezani pa kanthu kalikonse. Zimenezi zidzaŵatsimikizira kuti iwowo adzaonongeka, koma inu mudzapulumuka. Mulungu ndiye amene adzakuchitirani zimenezi.
“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Koma tsopano mukumdziŵa Mulungu, makamaka ndinene kuti Mulungu ndiye akudziŵa inu. Nanga bwanji mukubwereranso ku miyambo yachabe ndi yopanda phindu ija? Bwanji mukufuna kukhalanso akapolo ake?
Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.
Tsono inu okondedwa, popeza kuti mwazidziŵiratu zimenezi, chenjerani kuti zolakwa za anthu ochimwa zingakusokeretseni ndipo mungagwedezeke kenaka nkugwa.
Kodi iweyo ndiwe yani kuti uweruze wantchito wamwini kuti walakwa? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza, popeza kuti Ambuye angathe kumkhozetsa. Ena amaganiza kuti tsiku lakutilakuti ndi loposa masiku ena, koma pamene ena akuganiza kuti masiku onse nchimodzimodzi. Aliyense achite monga momwe watsimikizira kwenikweni mumtima mwake.
Pambuyo pake Yesu adaŵauza kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya usiku uno. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa za msambiwo zidzangoti balala.’
Ngwodala munthu amene amadalira Chauta, munthu amene sapatukira ku mafano kapena kutsata milungu yonama.
Tsono mbuye wake adzangoti mbwe mwadzidzidzi, pa tsiku limene iye sakumuyembekeza. Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu osakhulupirika.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Munthu wodzipatula mwa anzake amangotsata zomkomera iyeyo, amangofuna kutsutsana ndi zimene onse akudziŵa kuti ndi zoona.
Tsono mudzati, “Koma nthambi zija zidakadzuka kuti andilumikizepo ineyo pamtengopo.” Mulungu sadaŵataye anthu ake amene Iye adaŵasankha kale. Monga simudziŵa mau aja a m'Malembo, pamene mneneri Eliya akudandaula kwa Mulungu kuti aŵalange Aisraele? Paja adati, Nzoona, iwo adakadzukadi chifukwa sadakhulupirire, ndipo inu pakukhulupirira, mukukhala mu mtengo tsopano. Komatu tsono musamadzitame, makamaka muzichita mantha.
Ndikudabwa kuti mukupatuka msangamsanga motere, kusiya Mulungu amene adakuitanani mwa kukoma mtima kwa Khristu, ndipo kuti mukutsata uthenga wabwino wina. Koma palibe konse uthenga wabwino wina. Pali anthu ena amene akukusokonezani, ndipo akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wonena za Khristu.
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Anthu osasamala za Mulungu amandinyoza kwathunthu, komabe sindisiyana nawo malamulo anu.
Monga inu simudziŵa kuti pa mpikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti nkukalandira mphothoyo. Aliyense wothamanga pa mpikisano wa liŵiro amadziletsa pa zonse. Iwowo amachita zimenezi kuti akalandire mphotho ya nkhata yamaluŵa yotha kufota. Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota. Nchifukwa chake ndimathamanga monga munthu wodziŵa kumene walinga. Ndiponso ndikamachita mpikisano womenyana, sindichita ngati munthu amene angomenya mophonya. Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.
“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.
Ndidalankhula mwankhaŵa kuti, “Andipirikitsira kutali ndi Inu.” Koma Inu mudamva kupempha kwanga pamene ndidakudandaulirani kuti mundithandize.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Tikanena kuti timayanjana naye, pamene tikuyendabe mu mdima, tikunama, ndipo zochita zathu nzosagwirizana ndi zoona. Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Mulungu wathu ndi Mulungu wotilanditsa, ndi Mulungu, Ambuye amene amatipulumutsa ku imfa.
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye. M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse. Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu. Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika. Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.
Muzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene munkalakalaka pamene munali osadziŵa. Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse. Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka. Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita. Koma ngati Mzimu Woyera akutsogolerani, ndiye kuti sindinunso akapolo a Malamulo a Mose.
Sadziŵa chilungamo chochokera kwa Mulungu, koma adayesa kupezeka kuti ngolungama pamaso pake mwa njira yaoyao, osagonjera chilungamo chochokera kwa Mulungu.
Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Tsono ndi momwemonso makono. Patsala Aisraele oŵerengeka amene Mulungu adaŵasankha mwa kukoma mtima kwake. Komatu ngati adaŵasankha chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye kuti si chifukwa cha zimene iwo adaachita. Zikadatero, kukoma mtima kwake sikukadakhalanso kukoma mtima ai.
Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe.
Iwo sadaonongeretu mitundu ina ya anthu monga m'mene Chauta adaaŵalamulira, koma adasakanizana ndi mitundu inayo naphunzira kuchita zoipa zomwe anthu enawo ankachita.
Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.
Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo. Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola. Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu.
Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
Amadzinyenga m'maganizo mwake, kotero kuti tchimo lake sangathe kulizindikira ndi kudana nalo.
Ndi wodala munthu amene amaopa Chauta nthaŵi zonse, koma woumitsa mtima wake adzagwa m'tsoka.
Paja munthu wopanda zimenezi ndiye kuti ngwakhungu, sangathe kuwona patali, ndipo waiŵala kuti adamtsuka machimo ake akale.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano. Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa. Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai. Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu. Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye Munthu mmodzi uja, Yesu Khristu. Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri. Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo. Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuŵapatsa moyo. Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Phunzitseni njira zanu, Inu Chauta, kuti ndiziyenda m'zoona zanu. Mundipatse mtima wosagaŵikana, kuti ndiziwopa dzina lanu.
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,
Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti ngati kukhulupirika kwanu sikuposa kukhulupirika kwa aphunzitsi a Malamulo ndi kwa Afarisi, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.
Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.
Inu Chauta, ndikudziŵa kuti kuweruza kwanu nkolungama, ndipo mwandilanga potsata kukhulupirika kwanu.
Ugule choona, ndipo usachigulitse. Ugulenso nzeru, mwambo ndiponso mtima womvetsa zinthu.
Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”
Cholinga changa pokupatsa malangizo ameneŵa, nchakuti pakhale chikondi chochokera mu mtima woyera, mu mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndiponso m'chikhulupiriro chopanda chiphamaso.